Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Zimene Owerenga Amafunsa . . .

Kodi Si Ndinu Mkhristu Ngati Simukhulupirira Zoti Kuli Milungu Itatu mwa Mulungu Mmodzi?

Kodi Si Ndinu Mkhristu Ngati Simukhulupirira Zoti Kuli Milungu Itatu mwa Mulungu Mmodzi?

Buku lina lakusekondale lonena za zipembedzo zopezeka padziko lonse (World Religions in Denmark), lomwe linatulutsidwa m’chaka cha 2007, linanena kuti Mboni za Yehova ndi kagulu ka Akhristu amene amayesetsa kutsatira Baibulo kwambiri. Pa zipembedzo zikuluzikulu za ku Denmark, Mboni za Yehova zili pa nambala 3.

Koma bishopu wa mpingo wa Danish National Church anadzudzula kwambiri munthu amene analemba bukuli chifukwa chofotokoza za Mboni za Yehova m’buku lakelo. Kodi chifukwa chiyani anatero? Bishopuyo anati: “Sindinayambe ndakumanapo ndi katswiri wa zachipembedzo amene amaona kuti a [Mboni za Yehova] ndi Akhristu. Iwo amakana chiphunzitso chofunika kwambiri pa ziphunzitso zachikhristu chakuti kuli milungu itatu mwa Mulungu mmodzi.”

Mlembi wa bukuli, yemwe ndi katswiri wa maphunziro a zachipembedzo, dzina lake Annika Hvithamar, ananena kuti anthu akafunsidwa kuti afotokoze chifukwa chake amadziona kuti ndi Akhristu, samayankha kuti ndi chifukwa chakuti amakhulupirira kuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi. Komanso mbali ina ya bukuli, yomwe ili ndi kamutu kakuti, “Kodi Ndinu Mkhristu?” ili ndi mawu akuti: “Chiphunzitso chakuti kuli milungu itatu mwa Mulungu mmodzi ndi chimodzi mwa ziphunzitso zovuta kumvetsa kwambiri zachikhristu. Nthawi zonse zimavuta kufotokozera Akhristu amene sanapite kusukulu zophunzitsa ubusa chifukwa chake timati Mulungu wa Akhristu ndi mmodzi basi osati milungu itatu.”

“Chiphunzitso chakuti kuli milungu itatu mwa Mulungu mmodzi ndi chimodzi mwa ziphunzitso zovuta kumvetsa kwambiri zachikhristu”

Komatu zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza Mulungu ndiponso Yesu ndi zomveka bwino kwambiri. Ndiponso mawu akuti utatu kapena chiphunzitso chakuti kuli milungu itatu mwa Mulungu mmodzi sizipezeka n’komwe m’Mawu a Mulungu. Baibulo limanena momveka bwino kuti Yesu Khristu ndi Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu. (Akolose 1:15) Limanenanso kuti Yesu ndi “mkhalapakati . . . pakati pa Mulungu ndi anthu.” (1 Timoteyo 2:5) Koma ponena za Atate, Baibulo limati: “Inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”​—Salmo 83:18.

Mboni za Yehova zimaona kuti kukhulupirira Yesu n’kofunika kwambiri. (Yohane 3:16) Pa chifukwa chimenechi, iwo amatsatira lamulo la Yesu lakuti: “Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo utumiki wako wopatulika uyenera kupita kwa iye yekha basi.’” (Mateyo 4:10) Motero, munthu aliyense amene amayesetsa kutsatira malamulo a Yesu ndi woyenerera kutchedwa Mkhristu.