Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kumwamba N’kotani?

Kodi Kumwamba N’kotani?

 Kodi Kumwamba N’kotani?

ANTHU ena amaganiza kuti n’zosatheka kudziwa zoona zenizeni za kumwamba chifukwa palibe amene anatsika kumwamba kuti adzatiuze mmene kulili. Mwina anthu amenewa amaiwala kuti Yesu ananena kuti: “Ndinatsika kuchokera kumwamba.” (Yohane 6:38) Yesu anauzanso atsogoleri ena achipembedzo kuti: “Inu ndinu ochokera pansi pano; ine ndine wochokera kumwamba.” (Yohane 8:23) Kodi Yesu ananena kuti kumwamba ndi kotani?

Yesu anatsimikizira anthu kuti kumwamba n’kumene Yehova amakhala. Iye anatchula Mulungu kuti, “Atate wanga wa kumwamba.” (Mateyo 12:50) Komabe, Yesu ankagwiritsira ntchito mawu akuti “kumwamba” potanthauza zinthu zinanso. Mwachitsanzo, iye anagwiritsa ntchito mawu akuti “kumwamba” kutanthauza mumlengalenga pamene anati: “Yang’anirani mbalame za kumwamba.” (Mateyo 6:26, Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu) Komabe, Yehova amakhala kumwamba kwambiri kupitirira mlengalenga. Baibulo limati: “Akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi.”​—Yesaya 40:22.

Kodi “Atate wa kumwamba” amakhala pamodzi ndi nyenyezi? Thambo limene timaonali, limatchedwanso kuti “kumwamba” m’Malemba Oyera. Mwachitsanzo, munthu wina amene analemba nawo buku la Masalmo anati: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mum’kumbukira?”​—Salmo 8:3, 4.

Yehova Mulungu sakhala m’thambo limene analenga monganso kalipentala sakhala m’kabati imene wakhoma. Choncho, pamene Mfumu Solomo ankapereka kwa Yehova kachisi wa ku Yerusalemu, anati: “Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo ndi m’mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.” (1 Mafumu 8:27) Ngati Yehova samakhala kuthambo limene timaonali, ndiye kumwamba kumene iye amakhalako ndi kuti?

Pogwiritsa ntchito makina amphamvu oonera zinthu zakutali, anthu aphunzira zambiri zokhudza zinthu zakuthambo zimene timaonazi ndipo ena amapita m’mwamba kwambiri kupitirira thambo limene timaonali. Koma zimene Baibulo limanena ndi zoona. Limati: “Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” (Yohane 1:18) Yesu anafotokoza chifukwa chake ponena kuti: ‘Mulungu ndi Mzimu.’​—Yohane 4:24.

Mzimu ndi chinthu chamoyo koma choposa anthu. Mzimu ndi wosakhudzika kapena kuoneka ndi maso chifukwa ulibe zinthu zooneka monga mnofu ndi magazi. Choncho pamene Yesu ananena kuti poyamba ankakhala limodzi ndi Atate “kumwamba,” ankatanthauza kuti anali ndi moyo waulemerero kwambiri kuposa moyo wa chinthu chilichonse chooneka ndi maso. (Yohane 17:5; Afilipi 3:20, 21) Malo amenewa, omwe Yesu ankakhala ali mzimu limodzi ndi Atate wake, ndi amene Baibulo limati “Kumwamba.” Kodi kumwamba kumeneku n’kotani? Nanga kumachitika zotani?

 Kumagwiridwa Ntchito Yosangalatsa

Baibulo limafotokoza kuti kumwamba kumagwiridwa ntchito zosiyanasiyana. Limanena kuti pali zolengedwa zauzimu zokhulupirika zambirimbiri zimene zimakhala kumwambako. (Danieli 7:9, 10) Chilichonse cha zolengedwa zauzimu zimenezi n’chosiyana ndi zinzake zonse. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Pa zolengedwa zonse zooneka ndi maso, palibe chilichonse chimene chimafanana ndendende ndi chinzake, choncho sitingakayike kuti kumwamba nakonso kuli zolengedwa zosiyanasiyana. Koma chochititsa chidwi n’chakuti, ngakhale kuti zolengedwa zakumwambazi n’zosiyanasiyana, zimagwira ntchito limodzi mogwirizana. Zimenezi n’zosilirika kwambiri tikayerekezera ndi mmene zilili padziko pano chifukwa anthu ambiri samachita zinthu mogwirizana.

Taonani mmene Baibulo limafotokozera ntchito imene imachitika kumwamba. “Lemekezani [tamandani, NW] Yehova, inu angelo ake; amphamvu zolimba, akuchita mawu ake, akumvera liwu la mawu ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chom’kondweretsa Iye.” (Salmo 103:20, 21) Choncho, kumwamba kumagwiridwa ntchito yambiri. Tikukhulupirira kuti ntchito imeneyi ndi yosangalatsa kwambiri.

Angelo akhala akutumikira Mulungu mosangalala kuyambira kale kwambiri dzikoli lisanalengedwe. Malemba amanena kuti, Yehova atalenga dziko lapansi, ana a Mulungu ‘anaimba limodzi mokondwera,’ ndipo “anafuula ndi chimwemwe.” (Yobu 38:4, 7) Mmodzi mwa ana a Mulungu akumwamba anali ndi mwayi wogwira ntchito limodzi ndi Mulungu polenga zinthu zonse. (Akolose 1:15-17) Poona kuti kumwamba kumagwiridwa ntchito yosangalatsa chonchi, mwina mungakhale ndi mafunso ena okhudza kumwamba ndiponso anthu.

Kodi Anthu Analengedwa kuti Azikakhala Kumwamba?

Popeza kuti angelo ankatumikira Mulungu dzikoli lisanalengedwe, mwachionekere mwamuna ndi mkazi oyambirira sanalengedwe kuti azikakhala kumwamba. M’malomwake, Mulungu anauza banja loyambirirali kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28; Machitidwe 17:26) Adamu anali mtundu watsopano wa zamoyo zapadziko lapansi, zotha kudziwa Mulungu ndi kumutumikira mokhulupirika. Iye anafunika kukhala tate wa mtundu wa anthu amene kwawo kwenikweni ndi pano padziko lapansi. Ndipo Baibulo limati: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.”​—Salmo 115:16.

Mwachibadwa anthufe sitimafuna kufa chifukwa sitinalengedwe kuti tizifa. Mulungu anamuuza Adamu kuti imfa ndi chilango cha kusamvera. Adamu akanamvera Mulungu, sakanafa.​—Genesis 2:17; Aroma 5:12.

Chotero n’zosadabwitsa kuti Mulungu sanamuuze Adamu chilichonse chokhudza kupita kumwamba. Choncho, dziko lapansi si malo ongoyesera anthu pofuna kuwaona ngati ali oyenera kukakhala kumwamba. Anthu analengedwa kuti azikhala padziko lapansi kosatha, ndipo Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake chimenechi. Baibulo limalonjeza kuti “olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Apa zikuonekeratu kuti anthu sanalengedwe kuti azikakhala kumwamba. Ngati zili chonchi, n’chifukwa chiyani Yesu analonjeza atumwi ake kuti adzapita kumwamba? Kodi Yesu anatanthauza kuti anthu onse abwino adzapita kumwamba?