Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Amishonale Atumizidwa “Kumalekezero a Dziko Lapansi”

Amishonale Atumizidwa “Kumalekezero a Dziko Lapansi”

 Mwambo Womaliza Maphunziro a Gileadi​—Gulu la Nambala 127

Amishonale Atumizidwa “Kumalekezero a Dziko Lapansi”

YESU analamula ophunzira ake kuti akhale mboni “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Machitidwe 1:8) Mboni za Yehova zimaona kuti lamulo limeneli ndi lofunika kulitsatira.

Ndipo kwa zaka zoposa 65 zapitazi, amishonale ophunzitsidwa ku Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo athandiza kupititsa patsogolo ntchito yolalikira m’mayiko oposa 200. Loweruka pa 12 September, 2009, amishonale atsopano okwana 56, amene akhala akugwira ntchito yolalikira kwa zaka zambiri, anamaliza maphunziro awo. Maphunzirowa anali a miyezi isanu ndipo anachitikira kusukulu ya amishonale imene ili ku Patterson, ku New York, m’dziko la America.

Mphamvu ya Maganizo Anu

Stephen Lett, yemwe ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anali tcheyamani pa mwambowu ndipo anakambira ophunzirawo nkhani ya mutu wakuti, “Muzikagwiritsira Ntchito Maganizo Anu Mwanzeru.” Poyamba anachenjeza ophunzirawo za njira zinayi zimene sayenera kugwiritsa ntchito maganizo awo. Mfundo zitatu zoyambirira zinali zakuti: (1) Osamaganiza kuti zinthu zingamakuyendereni bwino kwambiri chifukwa chokhala ndi zinthu zakuthupi, (2) osamaganizira za zinthu zolakwika, ndiponso (3) osamada nkhawa kwambiri poganizira za mavuto amene mungakumane nawo mawa. (Miyambo 18:11; Mateyo 5:28; 6:34) Pofotokoza mfundo yachitatuyi, m’baleyo ananena kuti munthu amene amada nkhawa kwambiri amadziunjikira mavuto chifukwa amatenga mavuto a dzulo ndiponso a mawa n’kuwaphatikiza ndi a lero. Kenako M’bale Lett anati: “Umenewu ndi mtolo wolemetsa.” Kodi mfundo yachinayi inali yotani? Ophunzirawo anachenjezedwa kuti asamaganize kuti moyo wawo wakale unali wabwino kwambiri asanayambe ntchito yaumishonale. Kuchita zimenezi kungawalepheretse kusangalala ndi zinthu zabwino zimene akazipeze kumayiko amene angatumizidwe.

Kenako M’bale Lett analimbikitsa ophunzirawo kuti azigwiritsa ntchito maganizo awo m’njira zabwino zinayi. Iye anati: (1) Muzioneratu zinthu zimene zingaike pangozi moyo wanu wauzimu ndi wakuthupi, ndipo muzipewa tsokalo, (2) mukamawerenga Baibulo, muzikhala ngati mukuona zimene zikuchitikazo ndipo muziganizira kuti mukuchita nawo zimene zikufotokozedwazo, (3) muziona kuti munthu aliyense amene mungalankhule naye m’dziko limene mukupita angathe kukhala mtumiki wa Yehova, ndiponso (4) mukamalalikira munthu muziganizira mmene zikanakhalira ngati inuyo mukanakhala iyeyo.​—Miyambo 22:3.

Ubwino Wophunzitsa Ena

David Splane, yemwenso ali m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Zinthu Zimenezi Uziphunzitse kwa Anthu Okhulupirika.” Nkhani imeneyi inachokera pa 2 Timoteyo 2:2. Pamene mtumwi Paulo ankalangiza Timoteyo kuti aziphunzitsa anthu okhulupirika, cholinga chake chinali chakuti Timoteyo awaphunzitse anthu amenewa mfundo za choonadi komanso kuwalimbikitsa kuti nawonso aziphunzitsa anthu ena. M’baleyu anawauza ophunzirawo kuti pakufunikira amuna ambiri oti azitsogolera ntchito zachikhristu. Kodi anthu amenewa ayenera kuphunzitsidwa panthawi iti ndiponso motani? M’bale Splane analimbikitsa amishonalewo kuti aziyamba kuphunzitsa amuna amenewa zimenezi akangoyamba kuphunzira nawo Baibulo.

Koma kodi amishonale angaphunzitse bwanji anthu amene akuwaphunzitsa Baibulo kuti akhale zitsanzo zabwino pa nkhani ya kukhulupirika? M’baleyo anafotokoza zinthu zingapo zimene amishonalewo angachite. Amishonale amafunika kuphunzitsa amunawa kukonzekera bwino phunziro lawo la Baibulo. Kenako, ophunzirawo akayamba kupita kumisonkhano ya mpingo, ayenera kuphunzitsidwa mmene angakonzekerere pawokha  nkhani za m’Baibulo zimene akaphunzire kumisonkhanoyo. M’bale Splane anati: “Ngati munthu sakutha kuphunzira Baibulo payekha, sangathenso kuphunzitsa anthu ena.” M’baleyo ananenanso kuti amishonale angathe kuthandiza ophunzira atsopano kuti azisunga nthawi, azithandiza ndi ndalama zawo ntchito yolalikira, ndiponso kuti azigonjera abale amene panopo akutsogolera mu mpingo. Iye anafotokoza kuti njira yabwino yophunzitsira anthu amenewa ndiyo kuwasonyeza chitsanzo chabwino.

Kukhala Mboni za Yehova Ndi Mwayi Wapadera

M’bale Guy Pierce, yemwenso ali m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani imene inachokera pa mawu a Yesu amene ali pa Machitidwe 1:8. Mutu wake unali wakuti, “Mudzakhala Mboni Zanga.” Iye anakumbutsa ophunzirawo kuti m’nthawi ya atumwi, mtundu wa Aisiraeli unataya mwayi wokhala mboni za Yehova. Mwayi umenewu unaperekedwa ku mtundu wobereka zipatso za Ufumu. (Mateyo 21:43) Mpingo wa Akhristu odzozedwa ndiwo unakhala mtundu umenewu. M’baleyu anatchula mawu a mtumwi Petulo, amene ananena kuti “mtundu woyera” wa Akhristu odzozedwa uzidzalengeza kulikonse zabwino zopambana za Yehova. (1 Petulo 2:6-9) Choncho, ponena kuti “mudzakhala mboni zanga,” Yesu sankatanthauza kuti Akhristu adzakhala mboni za iyeyo basi, osatinso mboni za Yehova. Ndiponso Yesu mwiniyo amatchedwa “Mboni Yokhulupirikayo.” (Chivumbulutso 1:5; 3:14) Iye ndi Mboni ya Yehova yoyamba ndiponso chitsanzo chimene ife timatsatira.​—1 Petulo 2:21.

M’bale Pierce anauza ophunzirawo kuti, masiku ano mawu a Yesu opezeka pa Machitidwe 1:8 ndi ofunika kwambiri. Iye anatero chifukwa chakuti ulosi wa pa Chivumbulutso 11:15 wakwaniritsidwa m’njira yochititsa chidwi kwambiri. Ufumu wa Mesiya wa Mulungu wakhazikitsidwa. Tsopano ntchito yolalikira za Ufumuwu ikugwiridwa “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Machitidwe 1:8) M’baleyu anatsindika mfundo yakuti amishonale amachitira umboni za Yehova ndi Ufumu wake basi, osati za iwowo kapena za moyo umene anali nawo poyamba, za chikhalidwe chawo, kapenanso za dziko lawo. Iye analimbikitsa ophunzirawo kuti akayesetse kuphunzitsa “anthu ambiri mmene angakathere m’nthawi imene yatsalayi.”

Mfundo Zina Zofunika za Pamwambowu

Alex Reinmueller, yemwe amathandizira Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku, anakamba nkhani yakuti “Yehova Adzakulimbitsani Mtima.” M’baleyu ananena kuti amishonalewo akamadalira mphamvu za Yehova, Iye adzawathandiza kudziwa zimene amachita bwino, kuvomereza zimene amalakwitsa, kuthana ndi zimene amaopa, ndiponso kutumikira Mulungu ndi mtima wawo wonse.

Sam Roberson ndi William Samuelson, omwe ali mu Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu, nawonso anakambira nkhani ophunzirawo. M’bale Roberson anakamba nkhani ya mutu wakuti “Ndili Nawe” yomwe inachokera pa Yesaya 41:10. Iye ananena kuti ngakhale kuti amishonalewo akakumana ndi mavuto, akapezanso madalitso ambiri. Iwo angathe kupirira mavutowa ngati atatsanzira Mfumu Davide, amene ankapemphera mofuula kwa Atate wake wachikondi. (Salmo 34:4, 6, 17, 19) M’bale Samuelson anatsindika mfundo yakuti m’pofunika kupitiriza kukulitsa luso loganiza bwino. Amishonale amene amachita zimenezi amapewa kuchita zosayenera ena akawanenera zoipa ndipo sakhumudwa msanga.​—Miyambo 2:10, 11.

Jim Mantz, yemwe amathandizira Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku, anafunsa mafunso abale atatu. Wina ndi wa mu Komiti ya Nthambi ya dziko la Republic of Georgia, wina wa ku Honduras, ndipo wina ndi wa m’Komiti ya Dziko la Republic of Tajikistan. Abale amenewa akuidziwa bwino ntchito ya umishonale ndipo analangiza amishonalewa zimene angachite kuti azikagwirizana ngakhale ndi anthu ovuta kucheza nawo poyesetsa “kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:21) Mark Noumair, mlangizi winanso wa sukulu ya amishonale, anatsogolera zokambirana ndi ophunzirawa, pamene iwo anafotokoza zinthu zimene anakumana nazo polalikira pamene anali kusukuluyi. Mbali imeneyi inali ndi mutu wochititsa chidwi kwambiri wakuti “Inde, Ndikufuna Kuthandiza Nawo.”

Tcheyamani anamalizitsa mwambowu ponena mawu a mu nyimbo yatsopano ya Chingelezi yakuti “Muziganizira Moyo Wanu Zinthu Zonse Zikadzakhala Zatsopano.” Anthu 6,509 amene anabwera kudzaonerera mwambowu anabwerera kwawo ali otsimikiza mtima kuposa kale lonse zoti akachitire umboni za Yehova ndi za Mwana wake “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”

 [Tchati/​Mapu patsamba 31]

ZA OPHUNZIRAWO

Mayiko amene ophunzira achokera: 8

Ophunzira: 56

Mabanja: 28

Avereji ya zaka zakubadwa: 33.6

Avereji ya zaka zimene akhala Mboni kuchokera pamene anabatizidwa: 18.3

Avereji ya zaka zimene akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse: 13.6

[Mapu]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ophunzirawa anatumizidwa kumayiko 22 amene ali pansipa.

KUMENE AMISHONALE ANATUMIZIDWA

ALBANIA

BOLIVIA

BURUNDI

CAMBODIA

CHILE

CONGO, DEM. REP.

COSTA RICA

CÔTE D’IVOIRE

CURAÇAO

GUYANA

HAITI

JAMAICA

MOLDOVA

MOZAMBIQUE

NEPAL

NICARAGUA

PANAMA

PARAGUAY

PERU

SERBIA

TANZANIA

UGANDA

[Chithunzi patsamba 31]

Gulu la Nambala 127 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pamndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mumzera uliwonse mayina tawandandalika kuyambira la munthu amene ali kumanzere kupita kumanja.

(1) Marshall, T.; Prudent, L.; Mashburn, A.; Rosenström, S.; Testa, A.; Takeyama, M.; Sisk, M.

(2) Grooms, K.; Miura, S.; Camacho, M.; Rozas, S.; Burch, M.; Meza, I.; Young, G.; Geraghty, S.

(3) Bonilla, C.; Knaller, D.; Parrales, R.; Hotti, S.; Takada, A.; Tournade, M.; Sopel, C.

(4) Miura, Y.; Parrales, K.; Prudent, K.; Colburn, S.; Willis, L.; Vääränen, A.; Sisk, B.; Takada, R.

(5) Grooms, J.; Vääränen, M.; Geraghty, B.; Stackhouse, R.; Wilson, A.; Bonell, E.; Camacho, D.; Meza, R.; Bonell, M.

(6) Takeyama, S.; Testa, G.; Colburn, T.; Mashburn, C.; Willis, W.; Tournade, L.; Burch, J.; Stackhouse, J.

(7) Wilson, J.; Young, J.; Marshall, E.; Rozas, M.; Knaller, J.; Hotti, N.; Rosenström, A.; Sopel, J.; Bonilla, O.