Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zodabwitsa Zimene Zinachitika pa Pentekosite

Zodabwitsa Zimene Zinachitika pa Pentekosite

 Zoti Achinyamata Achite

Zodabwitsa Zimene Zinachitika pa Pentekosite

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kuona mmene anthuwo akumvera.

ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI MACHITIDWE 2:1-21, 38-41.

N’chiyani chomwe chimabwera m’maganizo mwanu mukamawerenga nkhani yonena za ‘mkokomo wa mphepo yamphamvu’ ndiponso za “malawi ooneka ngati malilime a moto”?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti anthu ankanena chiyani podabwa ophunzira akuyankhula zinenero zachilendo?

․․․․․

Malinga ndi mmene afotokozera m’vesi 13, kodi mukuganiza kuti nkhope za anthu odabwawo zinkaoneka bwanji?

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Kodi mwambo wa Pentekosite unali wotani, ndipo unakhudza bwanji gulu la anthu amene anasonkhana ku Yerusalemu? (Deuteronomo 16:10-12)

․․․․․

Kodi Petulo anasonyeza bwanji ulemu polankhula ndi anthuwo, ndipo anatani kuti akambe nkhani yokhudza anthu onsewo? (Machitidwe 2:29)

․․․․․

Kodi kulankhula molimba mtima kwa Petulo kunasiyana bwanji ndi zimene iye ananena poyamba m’bwalo la Mkulu wa Ansembe? (Mateyo 26:69-75)

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .

Kufunika kopeza nkhani imene ikukhudza omvera athu ndi kulankhula nawo mwaulemu powauza zikhulupiriro zathu za m’Baibulo.

․․․․․

Kukhala Mboni yolimba mtima ya Yehova, ngakhale kuti mwina panopo timachita mantha.

․․․․․

M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ZITI ZIMENE ZAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Kuti mudziwe zambiri, werengani Nsanja ya Olonda ya September 15, 1996, tsamba 8 ndi 9.