Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndalama Zimathandiza Munthu Kukhala Wosangalaladi?

Kodi Ndalama Zimathandiza Munthu Kukhala Wosangalaladi?

 Kodi Ndalama Zimathandiza Munthu Kukhala Wosangalaladi?

SONIA anabadwira ku Spain ndipo ali mwana, ankapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova ndi mayi ake. Koma atakula, anasamukira ku London, m’dziko la England ndipo anayamba ntchito yothandiza makampani kungongola ndi kungongoza ndalama.

Sonia ankasangalala ndi ntchito imeneyi ndipo ankaikonda kwambiri. Iye ankapeza ndalama zambiri chifukwa ankagwira ntchito ndi makampani akuluakulu ndipo zinthu zinkamuyendera bwino kwambiri. Nthawi zonse, Sonia ankagwira ntchito kwa maola 18 patsiku ndipo nthawi zina ankangogona kwa maola awiri kapena atatu okha. Pamoyo wake wonse, iye ankangoganiza za ntchito yake basi. Kenako zinthu zinasintha mwadzidzidzi. Iye anadwala matenda okupha ziwalo, mwina chifukwa chopanikizika ndi ntchito. Panthawiyi n’kuti ali ndi zaka 30 zokha.

Sonia anafa ziwalo za mbali imodzi ya thupi lake moti anasiya kulankhula ndipo madokotala ankakayikira zoti iye angadzayambenso kuyankhula. Mayi ake atamva zoti iye akudwala, nthawi yomweyo ananyamuka ulendo wopita ku England kuti azikamusamalira. Sonia atayambiranso kuyenda, tsiku lina mayi ake anamuuza kuti: “Ndikupita kumisonkhano yampingo. Tiye tipite tonse chifukwa sindingakusiye wekha.” Sonia anavomera ndipo anasangalala kwambiri ndi zimene anaona kumeneko.

Iye ananena kuti: “Zonse zimene ndinamva kumeneko zinali zoona zokhazokha ndiponso zinali zosangalatsa kwambiri. Ndinasangalala kwambiri mmodzi mwa anthu amene anandipatsa moni paulendo wanga woyamba kufika pa Nyumba ya Ufumu atandiuza kuti azindiphunzitsa Baibulo. Anthu amene ndinkacheza nawo kale anali atasiya kundiyendera, koma anzanga atsopanowa ankandisamalira mwachikondi.”

Patapita nthawi, Sonia anayambanso kuyankhula ndiponso analimbikira kwambiri kuphunzira Baibulo. Chaka chisanathe n’komwe, iye anabatizidwa. Ambiri mwa anzake atsopanowa ankagwira ntchito yolalikira nthawi zonse ndipo iye ankaona kuti iwo akusangalala kwambiri. Choncho, Sonia anaganiza kuti: ‘Inenso ndikufuna ndikhale ngati anzangawa chifukwa ndikufuna kutumikira Yehova Mulungu ndi mphamvu zanga zonse.’ Panopa, Sonia amagwira ntchito yolalikira nthawi zonse.

Kodi Sonia anaphunzirapo chiyani pa zimene zinachitikazi? Iye anati: “Ngakhale kuti ndinkapeza ndalama zambiri, ndinkapanikizika komanso ndinkakhala mwamantha chifukwa cha kusadalirika kwa ntchitoyo. Zimenezi zinkachititsa kuti ndizida nkhawa komanso ndisamasangalale. Tsopano ndazindikira kuti chinthu chofunika kwambiri pamoyo n’kukhala paubwenzi wabwino ndi Yehova, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba. Panopa ndinedi wosangalala kwambiri.”

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa kuchoka pa chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo.” (1 Timoteyo 6:10) Mogwirizana ndi zimene zinamuchitikira, Sonia amakhulupirira kuti mawu amenewa ndi oona.