Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Mukhale Wolemera?

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Mukhale Wolemera?

 Kodi Mulungu Amafuna Kuti Mukhale Wolemera?

‘Mulungu amafuna kuti mulemere. Amafuna kuti mukhale ndi magalimoto ambiri ndiponso ntchito yabwino. Chofunika ndi kungomukhulupirira basi ndi kum’patsa ndalama zambiri.’

NYUZIPEPALA ina ya ku Brazil inanena kuti zipembedzo zina zakumeneko zimalimbikitsa maganizo amenewa ndipo anthu ambiri amakhulupiriradi zimenezi. Ponena za kafukufuku wina amene anachitika ku America pakati pa anthu amene amati ndi Akhristu, magazini ina inati: “Anthu 61 pa 100 aliwonse amakhulupirira kuti Mulungu amafuna kuti anthu akhale olemera. Ndipo anthu 31 pa 100 aliwonse, . . . amakhulupirira kuti ngati munthu akupereka kwa Mulungu ndalama zambiri, Mulungu amadalitsanso munthuyo ndi ndalama zambiri.”​—Time.

Anthu ambiri a ku mayiko a ku Latin-America, monga Brazil, amakhulupirira kuti Mulungu amafuna kuti anthu akhale olemera. Choncho iwo amakhamukira m’matchalitchi omwe amaphunzitsa zoti Mulungu amapatsa anthu chuma. Koma kodi Mulungu analonjezadi kuti anthu amene amam’tumikira adzawapatsa chuma? Kodi atumiki onse a Mulungu akale anali olemera?

N’zoona kuti tikawerenga Malemba Achiheberi timaona kuti ambiri mwa anthu amene Mulungu anawadalitsa anali olemera. Mwachitsanzo, lemba la Deuteronomo 8:18, limati: “Mukumbukire Yehova Mulungu wanu, popeza ndi iyeyu wakupatsani mphamvu ya kuwonera chuma.” Zimenezi zinatsimikizira Aisiraeli kuti ngati angamvere Mulungu, iye adzalitsa mtundu wawo ndi chuma.

Nanga kodi Mulungu ankadalitsa mtumiki wake aliyense payekha? Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, anali wolemera kwambiri. Satana atawononga chuma cha Yobu, Yehova anam’bwezera chumacho ‘mowirikiza.’ (Yobu 1:3; 42:10) Nayenso Abulahamu anali wolemera kwambiri. Lemba la Genesis 13:2, limanena kuti iye “anali wolemera ndithu ndi ng’ombe ndi siliva ndi golidi.” Magulu ankhondo a mafumu anayi a m’dera la kummawa atagwira Loti, yemwe anali m’bale wake, Abulahamu anatsogolera ‘anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu.’ (Genesis 14:14) Banja la Abulahamu liyenera kuti linali lalikulu kwambiri chifukwa iye anali ndi “anyamata ake” amphamvu okwana 318. Apa zikuonekeratu kuti iye anali wolemera kwambiri chifukwa anali ndi nkhosa ndiponso ng’ombe zambiri komanso ankatha kusamalira banja lalikulu chonchi.

Ndithudi, atumiki ambiri a Mulungu, omwe anali okhulupirika, monga Abulahamu, Isaki, Yakobo, Davide ndiponso Solomo, anali olemera. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu amapereka chuma kwa munthu aliyense amene amamulambira? Nanga munthu akakhala wosauka, kodi zimatanthauza kuti Mulungu sakumudalitsa? Nkhani yotsatirayi iyankha mafunso amenewa.