Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chuma Chimene Mulungu Amapereka

Chuma Chimene Mulungu Amapereka

 Chuma Chimene Mulungu Amapereka

NGATI inuyo muli wokhulupirika kwa Mulungu, kodi iye angakudalitseni ndi chuma? Mwina, koma osati ndi chuma chimene inu mukuganizira. Taganizirani chitsanzo cha Mariya, mayi wa Yesu. Mngelo Gabiriele anaonekera kwa iye n’kumuuza kuti anali ‘wodalitsika koposa’ m’maso mwa Mulungu ndiponso kuti adzabereka Mwana wa Mulungu. (Luka 1:28, 30-32) Komatu Mariya anali wosauka. Yesu atabadwa, iye anapereka nsembe ya “njiwa ziwiri kapena maunda awiri a nkhunda.” Zimenezi zinali nsembe zimene anthu osauka ankapereka kwa Yehova.​—Luka 2:24; Levitiko 12:8.

Popeza kuti Mariya anali wosauka, kodi zikutanthauza kuti Mulungu sankamudalitsa? Ayi, si choncho. Tikutero chifukwa iye atapita kukacheza kwa m’bale wake Elizabeti, Baibulo limati: “Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera. Choncho anafuula ndi mawu amphamvu nati: ‘Wodalitsika ndiwe [Mariya] mwa akazi onse, n’chodalitsikanso chipatso cha mimba yako!’” (Luka 1:41, 42) Mariya anali ndi mwayi wokhala mayi wa Mwana wokondedwa wa Mulungu.

Nayenso Yesu anali wosauka. Iye anabadwira m’banja losauka ndipo anakhala wosauka kwa moyo wake wonse wapadziko lapansi. Nthawi ina, anauza munthu wina yemwe ankafuna kukhala wophunzira wake kuti: “Nkhandwe zili nawo mapanga ndipo mbalame za m’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamiritsa mutu wake.” (Luka 9:57, 58) Komabe, kubwera kwa Yesu Khristu padziko lapansi kunathandiza kuti ophunzira ake apeze chuma cha mtengo wapatali kwambiri. Ponena za Yesu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Anakhala wosauka kuchitira inu, kuti inuyo mulemere kudzera m’kusauka kwake.” (2 Akorinto 8:9) Kodi Yesu anapereka chuma chotani kwa ophunzira ake? Nanga masiku ano akupereka chuma chotani?

Chuma Chimene Yesu Amapereka

Nthawi zambiri munthu wachuma sakhala ndi chikhulupiriro chifukwa amadalira kwambiri chumacho m’malo modalira Mulungu. Yesu anati: “Zidzakhalatu zovuta zedi kuti anthu a ndalama adzalowe mu ufumu wa Mulungu!” (Maliko 10:23) Apa zikuonekeratu kuti chuma chimene Yesu anapereka kwa otsatira ake sichinali ndalama.

 Ndipo Akhristu ambiri a m’nthawi ya atumwi anali osauka. Mwachitsanzo, munthu wina yemwe anabadwa wolumala atapempha Petulo kuti am’patse ndalama, iye anayankha kuti: “Siliva ndi golide ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: M’dzina la Yesu Khristu Mnazarete, yenda!”​—Machitidwe 3:6.

Zimene wophunzira Yakobe ananena zimasonyezanso kuti anthu ambiri mumpingo wachikhristu anali osauka. Iye analemba kuti: “Tamverani abale anga okondedwa. Mulungu anasankha osauka m’zinthu za dziko kuti akhale olemera m’chikhulupiriro ndi olandira cholowa cha ufumu umene anaulonjeza kwa omukonda, sanatero kodi?” (Yakobe 2:5) Komanso, mtumwi Paulo ananena kuti si anthu ambiri “anzeru mwa kuthupi” kapena “amphamvu” kapena “a m’mabanja achifumu” amene anaitanidwa kuti akhale mumpingo wachikhristu.​—1 Akorinto 1:26.

Ngati chuma chimene Yesu anapatsa otsatira ake sichinali ndalama, kodi anawapatsa chuma chotani? M’kalata yopita ku mpingo wa ku Simuna, Yesu anati: “Ndikudziwa chisautso chako ndi umphawi wako, koma ndiwe wolemera.” (Chivumbulutso 2:8, 9) Ngakhale kuti Akhristu a ku Simuna anali osauka, iwo anali ndi chuma cha mtengo wapatali kuposa siliva ndi golide. Iwo anali olemera chifukwa anali ndi chikhulupiriro ndiponso anali okhulupirika kwa Mulungu. Ndipo chikhulupiriro ndi cha mtengo wapatali chifukwa “sichikhala ndi anthu onse.” (2 Atesalonika 3:2) Ndiponso Mulungu amaona kuti anthu opanda chikhulupiriro ndi osauka.​—Chivumbulutso 3:17, 18.

Chuma Chimene Chimabwera Chifukwa cha Chikhulupiriro

N’chifukwa chiyani chikhulupiriro chili chamtengo wapatali? Anthu omwe ali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu amapindula ndi “chuma cha kukoma mtima ndi kusakwiya msanga ndi kuleza [mtima] kwake.” (Aroma 2:4) Komanso ‘amakhululukidwa machimo’ awo chifukwa amakhulupirira nsembe ya dipo  ya Yesu. (Aefeso 1:7) Kuwonjezera apo, amakhalanso ndi nzeru zimene anthu a chikhulupiriro amapeza ‘m’mawu a Khristu.’ (Akolose 3:16) Iwo akamapemphera kwa Mulungu mwa chikhulupiriro, “mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira,” umateteza mitima ndiponso maganizo awo. Zimenezi zimathandiza kuti anthuwo akhale osangalala.​—Afilipi 4:7.

Komanso anthu amene amakhulupirira Mulungu kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu, akuyembekezera kudzalandira moyo wosatha. Pankhani imeneyi, Yesu Khristu ananena mawu odziwika bwino kwambiri akuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ndipo munthu amakhulupirira kwambiri zimenezi akaphunzira za Atate ndiponso Mwana wake. Izi zili choncho chifukwa Yesu ananenanso kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”​—Yohane 17:3.

Ngakhale kuti nthawi zambiri Mulungu amadalitsa anthu mwauzimu, amawadalitsanso kuti akhale ndi mtendere wa m’maganizo ndiponso moyo wosangalala. Mwachitsanzo, taonani zimene zinachitikira bambo wina wa ku Brazil dzina lake Dalídio. Iye anali chidakwa asanaphunzire zoona zenizeni zokhudza Mulungu. Ndipo khalidwe limeneli linkasokoneza kwambiri banja lake. Komanso, anali ndi mavuto ambiri a zachuma. Kenako, iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo zimenezi zinathandiza kuti asinthe kwambiri khalidwe lake.

Zimene Dalídio anaphunzirazo zinam’thandiza kuti asiye makhalidwe ake oipa. Iye anapita patsogolo kwambiri mwauzimu moti ananena kuti: “Poyamba, ndinkangokhalira kuyenda m’malo omwera mowa; koma tsopano ndimayenda nyumba ndi nyumba.” Iye anayamba kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu nthawi zonse. Zimenezi zinam’thandiza kuti akhale ndi thanzi labwino komanso kuti azikhala ndi ndalama. Dalídio anati: “Ndalama zimene ndinkamwera mowa tsopano ndimazigwiritsa ntchito kuthandizira ena komanso pogula zinthu zofunika pamoyo.” Ndiponso iye tsopano wapeza anzake abwino ocheza nawo omwenso amakonda zinthu zauzimu. Komanso amasangalala kwambiri chifukwa ali ndi mtendere wa mumtima womwe sakanakhala nawo akanakhala kuti sanadziwe Mulungu.

Chitsanzo china cha munthu amene anakhala ndi moyo wosangalala atayamba kukhulupirira Yehova Mulungu, ndi Renato. Mukamuona masiku ano mmene amasangalalira, simungakhulupirire kuti iye anakumana ndi zokhoma kwambiri atangobadwa kumene. Mayi ake anamuika m’thumba n’kukamutaya pansi pa mpando womwe unali m’mbali mwa njira. Panthawiyi, iye anali atakalikakalika ndiponso anali asanamudule mchombo. Azimayi awiri omwe ankadutsa pamalowo anaona thumbalo likusunthasuntha. Poyamba, iwo ankaganiza kuti munthu wina wasiyamo mphaka. Koma ataona kuti m’thumbalo munali mwana wakhanda, anam’tenga mofulumira n’kupita naye kuchipatala.

Mmodzi mwa azimayiwo anali wa Mboni za Yehova ndipo anauza nkhaniyi mayi wina, dzina lake Rita, yemwenso anali wa Mboni. Rita anali atapita padera kangapo konse ndipo anali ndi mwana mmodzi yekha wamkazi. Iye ankafunitsitsa mwana wamwamuna, choncho anaganiza zotenga Renato kuti akhale mwana wake.

 Rita anauza Renato adakali mwana kuti iye sanali mayi ake enieni. Komabe, ankamusamalira mwachikondi ndipo anam’phunzitsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pamoyo wake. Motero pamene iye amakula, anayamba kukonda kwambiri Baibulo. Renato anayamba kuyamikira kwambiri chifukwa cha mmene anapulumutsidwira ali mwana. Nthawi zonse iye amagwetsa misozi akamawerenga zimene wamasalmo Davide analemba kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.”​—Salmo 27:10.

Poyamikira zonse zimene Yehova anamuchitira, Renato anabatizidwa m’chaka cha 2002, ndipo m’chaka chotsatira, anayamba kugwira ntchito yolalikira nthawi zonse. Mpaka pano, iye sadziwa makolo ake enieni ndipo mwina sadzawadziwa n’komwe. Komabe, Renato amaona kuti mphatso yamtengo wapatali kwambiri imene iye walandira ndi kudziwa ndiponso kukhulupirira Yehova, yemwe ndi Atate ake achikondi.

Mwina nanunso mumafunitsitsa kukhala paubwenzi ndi Mulungu, umene ungachititse kuti mukhale ndi moyo wosangalala kwambiri. Mwayi wokhala paubwenzi ndi Yehova Mulungu komanso Mwana wake, Yesu Khristu ndi wa aliyense, kaya wolemera kapena wosauka. Ubwenzi umenewu mwina sungakuthandizeni kuti mukhale ndi ndalama zambiri koma ungakuthandizeni kukhala ndi mtendere wamumtima komanso moyo wosangalala, zimene simungagule ndi ndalama. Ndithudi, mawu a pa lemba la Miyambo 10:22, ndi oona. Mawuwo amati: “Madalitso a Yehova alemeretsa, saonjezerapo chisoni.”

Yehova Mulungu amakonda kwambiri anthu amene akubwera kwa iye ndipo anati: “Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.” (Yesaya 48:18) Iye akulonjeza kuti anthu amene amabwera kwa iye ndi maganizo ndiponso zolinga zoyenera adzawadalitsa kwambiri. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Mphoto ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.”​—Miyambo 22:4.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Kukhulupirira Mulungu kumathandiza munthu kukhala ndi mtendere wamumtima komanso moyo wosangalala

[Chithunzi patsamba 5]

Ngakhale kuti banja limene Yesu anabadwira linali losauka, Mulungu analidalitsa kwambiri