Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipembedzo Zonse N’zabwino?

Kodi Zipembedzo Zonse N’zabwino?

PADZIKOLI pali zipembedzo zambirimbiri. Ndipo zotsatira za kafukufuku wina waposachedwapa, zasonyeza kuti padziko lonse lapansi pali zipembedzo zikuluzikulu zokwanira 19, ndiponso pali zipembedzo zing’onozing’ono 10,000. Chifukwa cha kuchuluka kwa zipembedzo, anthu ali ndi mwayi wosankha chipembedzo chimene akufuna. Koma kodi pali vuto ngati mutasankha chipembedzo chilichonse?

Ena amanena kuti zipembedzo zili ngati njira zosiyanasiyana zopita pamwamba pa phiri limodzi. Motero, iwo amaona kuti zilibe kanthu ngati atasankha njira iliyonse chifukwa njira zonsezo zikupita kumalo amodzi. Iwo amati popeza kuti pali Mulungu Wamphamvuyonse mmodzi, ndiye kuti zipembedzo zonse zimatsogolera anthu kwa iye.

Kodi Zipembedzo Zonse Zimatsogolera Anthu kwa Mulungu?

Kodi Yesu Khristu, yemwe anali mphunzitsi wotchuka kwambiri pankhani zachipembedzo, ananenapo chiyani pankhani imeneyi? Iye anauza ophunzira ake kuti: “Lowani pachipata chopapatiza.” N’chifukwa chiyani anawauza zimenezi? Iye anafotokoza kuti: “Chipata cholowera kuchiwonongeko n’chachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. Koma chipata ndi chaching’ono ndi msewu ndi waung’ononso umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene aipeza njirayo.”​—Mateyo 7:13, 14, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza kuti zipembedzo zina zimatsogolera anthu “kuchiwonongeko”? Kapena kodi iye ankatanthauza kuti anthu osakhulupirira okha ndi amene ali pamsewu waukulu, pamene anthu okhulupirira Mulungu ndi amene ali pamsewu waung’ono wotsogolera ku moyo, mosatengera kuti ali m’chipembedzo chiti?

Atangonena kuti pali misewu iwiri yokha, Yesu ananena kuti: “Yang’anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma mkati mwawo ali afisi olusa.” (Mateyo 7:15, Buku Lopatulika Ndilo Mau a  Mulungu) Ndiyeno anati: “Siyense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.” (Mateyo 7:21, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Munthu amene amatchedwa mneneri kapena amene amanena kuti Yesu ndi “Ambuye” wake, ndiye kuti ndi wopembedza, osati wosakhulupirira. Choncho, pamenepa n’zoonekeratu kuti Yesu ankachenjeza kuti si zipembedzo zonse zimene zili zabwino ndiponso si aphunzitsi onse a zachipembedzo amene tiyenera kuwakhulupirira.

Kodi N’zotheka Kudziwa ‘Msewu Waung’ono’?

Popeza kuti si zipembedzo zonse zimene zimatsogolera anthu kwa Mulungu, kodi chipembedzo chabwino mungachidziwe bwanji? Taganizirani chitsanzo ichi: Yerekezerani kuti mwasochera mumzinda waukulu ndipo mwaganiza zoti mufunse njira. Munthu wina akukuuzani kuti mulowere kumanja ndipo wina akuti mulowere kumanzere. Koma wina akukuuzani kuti musankhe nokha njira iliyonse imene inuyo mukuona kuti ndi yabwino. Kenako, munthu wina amenenso ali paulendo akutenga mapu olondola n’kukuonetsani njira yoyenera. Ndiyeno akukupatsani mapuwo kuti muwagwiritse ntchito paulendo wanu. Kodi pamenepa mungakayike zoti mukafika kumene mukupita?

N’chimodzimodzinso pankhani yosankha chipembedzo chabwino, tiyenera kukhala ndi mapu olondola. Kodi pali mapu oterewa? Inde, alipo. Mapu amenewa ndi Baibulo, ndipo limati: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.”​—2 Timoteyo 3:16, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Muyenera kuti muli ndi Baibulo m’chilankhulo chanu lomwe mungagwiritse ntchito ngati mapu. Mboni za Yehova zimene zimafalitsa magazini ino, zinatulutsa Baibulo lolondola, lotchedwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu. Komabe, ngati siinu wa Mboni za Yehova, mwina mungakonde kugwiritsa ntchito Baibulo lina powerenga nkhani zofotokoza mmene mungadziwire chipembedzo chabwino ndi choipa. Choncho, m’nkhani ino ndiponso zitatu zotsatirazi, tagwiritsa ntchito mabaibulo amene anthu a zipembedzo zina amagwiritsa ntchito.

Mukamawerenga nkhanizi, yerekezerani zimene mukudziwa ndi zimene Baibulo likunena. Kumbukirani mawu a Yesu onena za mmene tingasiyanitsire chipembedzo chabwino ndi choipa. Iye anati: “Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma.” (Mateyo 7:17, 18, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Onani zipatso zabwino zitatu zokha zimene Baibulo limanena kuti zingatithandize kudziwa “mtengo wabwino.”