Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Ndizipereka Ndalama Zingati?

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Ndizipereka Ndalama Zingati?

 Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Ndizipereka Ndalama Zingati?

Baibulo limati: “Mulungu amakonda wopereka mokondwera.” (2 Akorinto 9:7) Anthu ambiri padziko lonse amawadziwa mawu amenewa. Komabe, anthu ena opembedza amaganiza kuti Mulungu amafuna kuti iwo azipereka ndalama zambiri zomwe sangakwanitse. Ndipotu zipembedzo zina zimanena kuchuluka kwa ndalama zimene anthu awo ayenera kumapereka. Ndalama zimenezi zimatchedwa chakhumi.

Kodi Baibulo limasonyezadi kuti munthu aziuzidwa ndalama zimene ayenera kupereka? Ngati silimasonyeza, ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ndizipereka ndalama zingati?’

Zopereka M’nthawi Yakale

M’Baibulo muli malangizo omveka bwino opita kwa Aisiraeli, onena za kuchuluka kwa zopereka zimene iwo ankafunika kupereka kwa Mulungu. (Levitiko 27:30-32; Numeri 18:21, 24; Deuteronomo 12:4-7, 11, 17, 18; 14:22-27) Zoperekazi zinali zoti munthu angakwanitse kupereka. Ndipo Yehova analonjeza kuti Aisiraeli akamvera malamulo ake, ‘adzawachulukitsira zokoma.’​—Deuteronomo 28:1, 2, 11, 12.

Komabe, nthawi zina Aisiraeli ankapereka zinthu zambiri kapena zochepa malinga n’kufuna kwawo. Mwachitsanzo, mfumu Davide atakonza zomanga kachisi wa Yehova, anthu ake anapereka “golidi [wokwana] matalente zikwi zisanu.” * (1 Mbiri 29:7) Ndiyeno siyanitsani zimenezi ndi zimene nthawi ina Yesu anaona ali padziko lapansi. Iye anaona “mkazi wina wamasiye wosauka akuponya timakobili tiwiri tating’ono” m’bokosi la pakachisi. Kodi mayiyu anapereka ndalama zingati? Anapereka ndalama yochepa kwambiri zedi pa ndalama zimene munthu ankalandira akagwira ntchito tsiku limodzi. Komabe, Yesu ananena kuti Mulungu anasangalala ndi ndalama yochepayo.​—Luka 21:1-4.

Kodi Akhristu Ayenera Kuuzidwa Ndalama Zimene Ayenera Kupereka?

Akhristu sali m’pangano la Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli. Choncho, iwo safunikira kuuzidwa kuchuluka kwa ndalama zimene ayenera kupereka kwa Mulungu. Komabe, Akhristu oona amasangalala ndi kupatsa ndipo Yesu Khristu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Mwakufuna kwawo, Mboni za Yehova zimapereka ndalama zothandizira ntchito yawo yolalikira yomwe ikuchitika padziko lonse. Zoperekazi zimathandiza pantchito yosindikiza mabuku ndi magazini ngati imene mukuwerengayi. Ndalamazi zimathandizanso pantchito yomanga ndi kukonzanso malo awo olambirira omwe amatchedwa kuti Nyumba ya Ufumu. Koma ndalamazi sizigwiritsidwa ntchito polipira anthu ogwira ntchitoyi. Anthu ena omwe anadzipereka kuti nthawi zonse ntchito yawo izikhala yolalikira, amalandira ndalama yochepa yolipirira thiransipoti ndi zinthu zina. Koma anthuwa sachita kupempha kuti azipatsidwa ndalamazi. Ndipotu a Mboni za Yehova ambiri salandira ndalama iliyonse pantchito yawo yolalikira. Koma amagwira ntchito kuti azipeza zofunika pamoyo wawo monga mmene Paulo anachitira pogwira ntchito yosoka mahema.​—2 Akorinto 11:9; 1 Atesalonika 2:9.

Nanga ngati munthu akufuna kupereka ndalama zothandiza pantchito imene Mboni za Yehova zikugwira, kodi ayenera kupereka ndalama zingati? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Aliyense achite mwa kutsimikiza kwa mtima wake, osati monyinyirika kapena mokakamizika ayi, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.”​—2 Akorinto 8:12; 9:7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Mu 2008, golide wolemera magalamu 28, mtengo wake unali madola 871, zimenezi zikutanthauza kuti mtengo wa golide amene anaperekedwa pantchitoyi unali wokwana madola 4,794,855,000.