Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pali Munthu Amene Amasamaladi za Ine?

Kodi Pali Munthu Amene Amasamaladi za Ine?

 Kodi Pali Munthu Amene Amasamaladi za Ine?

Kodi nthawi zina mumaona kuti muli nokhanokha popanda wina wokuthandizani, kapenanso amene akumvetsa mavuto amene mukukumana nawo? Mwina mumaonanso kuti ngakhale kuti anthu akudziwa mavuto anu, koma sakusamala za inu.

TIKAMAKUMANA ndi mavuto ambirimbiri pamoyo wathu, nthawi zina tingaone ngati mavutowo sadzatha. Mwina tingafike poganiza kuti mavutowo ndi aakulu kwambiri moti sitingathe kuwapirira. Nthawi zambiri tingaganize choncho tikamavutika maganizo, tikamadwala matenda aakulu kapenanso tikavulala kwambiri pangozi. Zinthu ngati zimenezi zingatichititse kuona ngati palibe amene angatithandize kapena kutitonthoza. Choncho tingadzifunse kuti, ‘Kodi pali munthu amene amasamaladi za ine?’

“Mulungu wa Chitonthozo Chonse” Amasamala za Ife

Baibulo limati Mulungu ndi “Tate wa chifundo chachikulu ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.” (2 Akorinto 1:3) Mulungu, yemwe dzina lake ndi Yehova, amadziwa kuti timafunika kutonthozedwa. Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “chitonthozo” m’njira zosiyanasiyana kwa nthawi zopitirira 100. Ndipo zimenezi zimatitsimikizira kuti Mulungu amadziwa mavuto athu ndiponso amafunitsitsa kutitonthoza. Kudziwa zimenezi kumatithandiza kukhulupirira kuti Yehova Mulungu amatisamalira ngakhale kuti anthu ena angaoneke kuti sakumvetsa kapenanso sasamala za mavuto athu.

Malemba amasonyeza kuti Yehova amasamalira munthu aliyense payekha. Baibulo limati: “Maso a Yehova ali ponseponse, nayang’anira oipa ndi abwino.” (Miyambo 15:3) Komanso lemba la Yobu 34:21 limati: “Maso ake ali pa njira ya munthu ali yense, napenya moponda mwake monse.” Yehova amaona zimene timachita, kaya zabwino kapena zoipa. Iye amadziwanso zimene zikutichitikira ndiponso mmene angatithandizire. Mawu amene mneneri Hanani anauza Mfumu Asa ya Yuda, akutsimikizira mfundo imeneyi. Mneneriyo anati: “Pakuti maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”​—2 Mbiri 16:7, 9.

Yehova amatiyang’anira pa chifukwa chinanso. Yesu anafotokoza kuti: “Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.” (Yohane 6:44) Yehova amasamala za ife, moti amafufuza mumtima mwathu kuti aone ngati tili ofunitsitsa kum’dziwa ndipo iye angatithandize. Mwachitsanzo, m’dziko la Dominican Republic, mayi wina yemwe ankadwala khansa, anagonekedwa m’chipatala kuti achitidwe opaleshoni. Iye anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize kupeza chipembedzo choona. Posakhalitsa mwamuna wake anam’bweretsera kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? * Mwamunayo anapatsidwa kabukuka ndi anthu ena a Mboni za Yehova amene anabwera kunyumba kwake m’mawa wa tsiku lomwelo. Mayiyo atawerenga kabukuko, anazindikira kuti Mulungu wayankha pemphero lake. Iye anavomereza kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo pasanapite miyezi 6, anadzipereka kwa Mulungu n’kubatizidwa.

M’buku la Masalmo, timapeza mawu ambiri  ogwira mtima a Mfumu Davide komanso Aheberi ena amene analemba nawo bukuli. Mawuwa amasonyeza kuti Yehova amasamalira atumiki ake mwachikondi. Pa lemba la Salmo 56:8, timapezapo mawu a Mfumu Davide amene anachonderera Mulungu kuti: “Sungani misozi yanga m’nsupa yanu. Kodi siikhala m’buku mwanu?” Mawu amenewa akusonyeza kuti Davide ankadziwa kuti Yehova amadziwa mavuto amene iye ankakumana nawo, komanso mmene iye akumvera. Yehova ankadziwa ululu umene Davide ankamva ndiponso mavuto amene anam’chititsa kuti azilira. Zoonadi, Mlengi wathu amayang’anira anthu onse amene amayesetsa kuchita chifuniro chake, “amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”

Salmo 23 nalonso limafotokoza kuti Mulungu amatisamalira mwachikondi. Mawu oyamba a Salmo limeneli amayerekezera Mulungu ndi m’busa wachikondi. Mawuwa amati: “Yehova ndiye m’busa wanga; sindidzasowa.” Abusa a nkhosa ku Middle East, amasamalira nkhosa zawo mwachikondi kwambiri ndipo nkhosa iliyonse amaitchula dzina. Tsiku lililonse m’busa amaitana nkhosa iliyonse ndipo amaisisita mwachikondi, kenako amafufuza kuti awone ngati yavulala. Akapeza kuti nkhosa inayake ili ndi bala, amaipaka mafuta kapenanso mankhwala kuti balalo lipole mwansanga. Akaona kuti nkhosa ina ikudwala, m’busayo amaimwetsa mankhwala, ndipo amaithandiza kuti iimirire kuopera kuti ikagona pansi ikhoza kufa. Kunena zoona, zimene m’busayu amachita zikusonyeza mmene Yehova amasamalirira anthu amene amamudalira.

Pemphero Ndiponso Kuuka kwa Akufa Ndi Umboni Woti Mulungu Amatisamalira

Masalmo amenewa sikuti anangolembedwa kuti tiziwerenga ndiponso kusangalala nawo  chabe. Koma amasonyeza mmene atumiki okhulupirika a Mulungu ankapempherera mochokera pansi pa mtima. Iwo ankapemphera kuti Yehova awathandize ndipo ankapempheranso pomuthokoza chifukwa chakuti iye akuyankha mapemphero awo komanso akuwadalitsa. Mapemphero awowa akusonyeza kuti atumiki a Mulungu amenewa ankakhulupirira kuti iye akuwasamalira. Kuwerenga ndiponso kuganizira kwambiri mapemphero ochokera pansi pamtima amenewa kungatithandize kuti nafenso tizidalira kwambiri Mulungu. Yehova amalola kuti tizipemphera kwa iye ndipo zimenezi ndi umboni wakuti iye amatisamalira.

Komabe nthawi zina tikakumana ndi mavuto timasowa chonena m’pemphero. Kodi pamenepa, ndiye kuti Yehova sangadziwe za mavuto athuwo? Lemba la Aroma 8:26 limati: “Mofananamo, mzimu umatithandiza pa zofooka zathu; pakuti chimene tiyenera kupempherera monga mmene tiyenera kupemphera sitikuchidziwa, koma mzimu umachonderera m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza.” Lembali likutiuza kuti mapemphero a atumiki akale amene analembedwa m’Baibulo, angatikhudze chifukwa nafenso tingakhale ndi mavuto ofanana ndi awo. Komanso likutiuza kuti Yehova, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” angayankhe mapemphero athu.​—Salmo 65:2.

Umboni winanso wakuti Mulungu amasamalira wina aliyense wa ife ndi wakuti akufa adzauka. Yesu Khristu anati: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu [a Yesu] ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Mawu achigiriki amene anawagwiritsa ntchito palembali anawamasulira molondola kuti “manda a chikumbutso,” osati “manda” chabe. Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu amakumbukira chilichonse chokhudza munthu amene anamwalira.

Kuti Mulungu adzaukitse munthu, ndiye kuti ayenera kudziwa chilichonse chokhudza munthuyo, monga maonekedwe ake, makhalidwe ndiponso maganizo ake. (Maliko 10:27) Mulungu amakumbukirabe ndipo saiwala ngakhale pang’ono munthu amene anamwalira ngakhale patapita zaka zambiri chotani. (Yobu 14:13-15; Luka 20:38) Choncho Yehova Mulungu amakumbukira chilichonse chokhudza anthu mabiliyoni ambirimbiri omwe anamwalira. Ndipotu zimenezi ndi umboni woti Mulungu amasamalira munthu aliyense payekha.

Yehova Amapereka Mphoto

Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu azitisamalira mwachikondi? Choyamba tiyenera kusonyeza kuti timam’dalira, timamukhulupirira ndiponso timamumvera. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti munthu akakhala ndi chikhulupiriro, Mulungu amamusamalira. Iye anati: “Popanda chikhulupiriro n’kosatheka kum’kondweretsa Mulungu. Pakuti amene akum’fikira Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amakhala wopereka mphoto kwa anthu om’funafuna ndi mtima wonse.”​—Aheberi 11:6.

Kuti tisonyeze kuti timakhulupirira Mulungu m’pofunika kuchita zinthu ziwiri. Choyamba, tiyenera kukhulupirira kuti “iye alikodi,” ndiponso kuti ndi Wolamulira Wamkulu, yemwe tiyenera kumumvera ndiponso kumulambira. Chachiwiri, tiyenera kukhulupirira kuti iye ndi “wopereka mphoto kwa anthu om’funafuna ndi mtima wonse.” Munthu wa chikhulupiriro chenicheni sakayikira kuti Mulungu amasamala za anthu onse amene amafuna kuchita chifuniro chake ndipo sakayika kuti adzawapatsa mphoto. Mukamaphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kucheza ndi anthu amene amam’mvera, inunso mudzakhala ndi chikhulupiriro cholimba chimene chidzachititsa kuti Mulungu akudalitseni ndiponso kuti azikukondani.

Masiku ano, ambiri amakhulupirira kuti Mulungu sasamala za anthu. Koma monga mmene taonera, Baibulo likusonyezeratu kuti Mulungu amasamalira kwambiri anthu amene amamukhulupirira ndi mtima wonse. Ngakhale kuti masiku ano timakumana ndi mavuto ambiri monga, nkhawa ndiponso kukhumudwa, sitiyenera kutaya mtima chifukwa Yehova Mulungu amatisamalira. Ndipotu iye akutipempha mwachikondi kuti: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza; nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”​—Salmo 55:22.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Kabukuka kanafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 29]

Malemba Amene Angakuthandizeni Kukhulupirira Kuti Mulungu Amakusamalirani Mwachikondi

“Pakuti maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi iye.”​—2 MBIRI 16:9

“Sungani misozi yanga m’nsupa yanu; kodi siikhala m’buku mwanu?”​—SALMO 56:8

“Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.”​—SALMO 23:1

“Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.”​—SALMO 65:2

“Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu.”​—YOBU 14:15

“Amene akum’fikira Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amakhala wopereka mphoto kwa anthu om’funafuna ndi mtima wonse.”​—AHEBERI 11:6

“Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza; nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”​—SALMO 55:22