Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kubadwa Mwatsopano Kuli N’cholinga Chotani?

Kodi Kubadwa Mwatsopano Kuli N’cholinga Chotani?

 Kodi Kubadwa Mwatsopano Kuli N’cholinga Chotani?

ANTHU ambiri amaganiza kuti munthu ayenera kubadwanso kuti adzalandire chipulumutso. Koma taonani zimene Yesu ananena zokhudza cholinga cha kubadwa mwatsopano. Iye anati: “Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwanso.” (Yohane 3:3) Choncho, munthu ayenera kubadwanso kuti akalowe mu Ufumu wa Mulungu osati kuti adzapeze chipulumutso. Komabe, ena anganene kuti mawu akuti kulowa mu Ufumu ndiponso kupeza chipulumutso akutanthauza chinthu chimodzi. Koma zimenezi si zoona. Kuti timvetse kusiyana kwake, tiyeni tikambirane kaye tanthauzo la mawu akuti “Ufumu wa Mulungu.”

Ufumu ndi boma, ndipo mawu akuti “Ufumu wa Mulungu” akutanthauza “boma la Mulungu.” Baibulo limatiuza kuti Yesu Khristu, yemwe amatchedwanso “mwana wa munthu,” ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo palinso ena amene adzalamulire naye. (Danieli 7:1, 13, 14; Mateyo 26:63, 64) Kuwonjezera pamenepa, masomphenya amene mtumwi Yohane anaona amasonyeza kuti anthu amene adzalamulire ndi Khristu amasankhidwa kuchokera “mu fuko lililonse, lilime, mtundu, ndi dziko lililonse,” ndipo “adzalamulira dziko lapansi monga mafumu.” (Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6) Mawu a Mulungu amatiuzanso kuti anthu amene adzalamulire monga mafumu amapanga “kagulu” ka anthu okwana 144,000 “amene anagulidwa padziko lapansi.”​—Luka 12:32; Chivumbulutso 14:1, 3.

Kodi likulu la Ufumu wa Mulungu lili kuti? “Ufumu wa Mulungu” umatchedwanso “ufumu wa kumwamba.” Zimenezi zikusonyeza  kuti Yesu limodzi ndi olamulira anzake amalamulira kuchokera kumwamba. (Luka 8:10; Mateyo 13:11) Choncho, Ufumu wa Mulungu ndi boma la kumwamba lolamulidwa ndi Yesu Khristu pamodzi ndi olamulira anzake osankhidwa kuchokera mwa anthu.

Nanga kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anati munthu ayenera kubadwanso kuti “akalowe mu Ufumu wa Mulungu”? Ankatanthauza kuti munthu ayenera kubadwanso kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba. Choncho, cholinga cha kubadwa mwatsopano ndicho kukonzekeretsa kagulu ka anthu amenewa kuti ayenerere kukalamulira kumwamba.

Pofika pano, taona kuti kubadwa mwatsopano n’kofunika kwambiri, kumachititsidwa ndi Mulungu, ndiponso kuti kumakonzekeretsa kagulu ka anthu kuti ayenerere kukalamulira kumwamba. Koma kodi chimachitika n’chiyani kuti munthu abadwe mwatsopano?

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Cholinga cha kubadwa mwatsopano ndicho kukonzekeretsa kagulu ka anthu kuti ayenerere kukalamulira kumwamba

[Chithunzi patsamba 7]

Yesu Khristu pamodzi ndi olamulira anzake osankhidwa kuchokera mwa anthu ndi amene amapanga Ufumu wa Mulungu