Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chiwembu Chibwerera Eni Ake

Chiwembu Chibwerera Eni Ake

 Zoti Achinyamata Achite

Chiwembu Chibwerera Eni Ake

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera. Nkhaniyi ikhale ngati ikuchitika panopa.

ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI DANIELI 6:1-28.

Kodi mukuganiza bwanji? Kodi Dariyo ndi munthu wotani? Fotokozani mmene akuonekera. Kodi mawu ake akumveka bwanji? (Werenganinso mavesi 14, 16, 18-20.)

․․․․․

Kodi dzenjelo likuoneka bwanji? Ndipo fotokozani mmene mikangoyo ikuonekera.

․․․․․

Fotokozani zimene mukuganiza kuti zinachitika mu mphindi zoyambirira, dzenje la mikango litatsekedwa Danieli ali momwemo.

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

N’chifukwa chiyani akalonga a Dariyo anachitira nsanje Danieli? (Werenganinso vesi 3.)

․․․․․

N’chifukwa chiyani Danieli anapemphera poyera pomwe akanatha kupemphera mobisa? (Werenganinso vesi 10 ndi 11.)

․․․․․

Mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Dariyo anaona kuti lamulo lokhudza kupemphera linali labwino? (Werenganinso vesi 7.)

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .

Kulimba mtima mukamatsutsidwa.

․․․․․

Kufunika kwa pemphero.

․․․․․

Mmene Yehova amasamalira atumiki ake okhulupirika.

․․․․․

M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ZITI ZIMENE ZAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․