Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zokhudza Mmene Tiyenera Kukhalira ndi Ena

Zokhudza Mmene Tiyenera Kukhalira ndi Ena

 Zimene Tikuphunzira kwa Yesu

Zokhudza Mmene Tiyenera Kukhalira ndi Ena

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala okoma mtima?

Kodi mumakhala wokoma mtima ngakhale pamene anthu sakukusonyezani kukoma mtima? Ngati tikufuna kutsanzira Yesu, tifunika kukhala okoma mtima ngakhale kwa anthu amene amatida. Yesu anati: “Kodi mukamakonda okhawo amene amakukondani, mudzapeza phindu lotani? Pakuti ngakhale ochimwa amakonda amene amawakonda. . . . Mosiyana ndi zimenezo, inu pitirizani kukonda adani anu . . . , ndipo mudzakhala ana a Wam’mwambamwamba, chifukwa iye ndi wachifundo kwa osayamika ndi kwa oipa.”​—Luka 6:32-36; 10:25-37.

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhululuka?

Tikachimwa timafuna kuti Mulungu atikhululukire. Yesu anaphunzitsa kuti tiyenera kupemphera kuti Mulungu atikhululukire. (Mateyo 6:12) Koma ananena kuti Mulungu adzatikhululukira ngati ifenso timakhululukira anzathu. Iye anati: “Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanu wa kumwamba adzakhululukiranso inu; koma ngati simumakhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanu sadzakukhululukirani zolakwa zanu.”​—Mateyo 6:14, 15.

 Mmene mabanja angakhalire osangalala

Ngakhale kuti Yesu sanakwatire, pali zinthu zambiri zimene tingaphunzire kwa iye zothandiza kuti tikhale ndi banja losangalala. Anatisiyira chitsanzo mwa zolankhula zake komanso zochita zake. Taonani mfundo zitatu izi:

1. Mwamuna ayenera kukonda mkazi wake monga thupi lake. Yesu anapereka chitsanzo choti amuna okwatira azitsatira. Polankhula ndi ophunzira ake, iye anati: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana wina ndi mnzake.” Kodi anati tizikondana motani? Iye anati: “Mmene ine ndakukonderani.” (Yohane 13:34) Posonyeza kuti mfundoyi imakhudzanso amuna okwatira, Baibulo limati: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu, monga Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo . . . Mwa njira imeneyi amuna akonde akazi awo monga matupi awoawo. Amene akonda mkazi wake adzikonda iye mwini, pakuti palibe munthu anadapo thupi la iye mwini; koma amalidyetsa ndi kulisamala, mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo.”​—Aefeso 5:25, 28, 29.

2. Anthu okwatirana azikhala okhulupirika m’banja. Kugonana ndi munthu amene si mkazi kapena mwamuna wako ndi kulakwa pamaso pa Mulungu ndipo kumasokoneza banja. Yesu ananena kuti: “Kodi simunawerenge . . . ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake ndipo adzaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho, chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse . . . Ine ndikukuuzani kuti aliyense wosudzula mkazi wake ndi kukwatira wina achita chigololo, kupatulapo ngati am’sudzula chifukwa cha dama.”​—Mateyo 19:4-9.

3. Ana ayenera kumvera makolo. Yesu ali mwana, ankamvera makolo ake ngakhale kuti iye anali wangwiro pomwe makolo akewo anali opanda ungwiro. Ponena za Yesu ali ndi zaka 12, Baibulo limati: “Pamenepo ananyamuka nawo[makolo ake] limodzi kubwerera ku Nazarete, ndipo anapitiriza kuwamvera.”​—Luka 2:51; Aefeso 6:1-3.

N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira mfundo zimenezi?

Ponena za mfundo zimene anaphunzitsa otsatira ake, Yesu anati: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, mudzakhala osangalala mukamazichita.” (Yohane 13:17) Kuti tikhale Akhristu enieni m’pofunika kutsatira malangizo amene Yesu anapereka okhudza mmene tiyenera kukhalira ndi anthu ena. Iye anati: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.”​—Yohane 13:35.

Kuti mumve zambiri werengani mutu 14 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Fanizo la Yesu la mwana wolowerera limatiphunzitsa kuti m’pofunika kukhala okoma mtima komanso okhululuka.​—Luka 15:11-32

[Chithunzi patsamba 17]

Anthu okwatirana ayenera kukhala okhulupirika m’banja