Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Phunzitsani Ana Anu

Samueli Anapitirizabe Kuchita Zabwino

Samueli Anapitirizabe Kuchita Zabwino

KODI unaonapo anthu ena akuchita zoipa?​— * Kalelo, Samueli anaona ena akutero. Komatu kumene ankakhala Samueli kunali kosayenera kuchitirako zoipa. Iye ankakhala ku kachisi, kapena kuti malo olambirirako Mulungu, mumzinda wa Silo. Zimenezi zinachitika zaka 3,000 zapitazo. Ndiye tiye tione kuti zinatheka bwanji kuti Samueli azikhala kukachisi.

Samueli asanabadwe, mayi ake dzina lawo Hana, ankafunitsitsa atakhala ndi mwana. Mayi akewo atafika ku kachisi anapemphera kwa Mulungu za nkhaniyi. Anapemphera mochoka pansi pamtima moti milomo yawo inayamba kunjenjemera. Ndiye ataona zimenezi, mkulu wa ansembe, dzina lake Eli, anaganiza kuti akunjenjemera chifukwa choledzera. Koma atadziwa kuti amanjenjemera chifukwa cha vuto lawolo, anawadalitsa n’kuwauza kuti: “Mulungu wa Israyeli akupatse chopempha chako.”​—1 Samueli 1:17.

Kenaka, Samueli anabadwa, ndipo mayi akewo anasangalala kwambiri moti anauza amuna awo, a Elikana, kuti: ‘Mwanayu akangosiya kuyamwa, ndidzam’pititsa ku kachisi kuti akatumikire Mulungu.’ Ndipo iwo anachita zimenezi Samueli atakwanitsa zaka zinayi kapena zisanu.

Panthawiyi n’kuti Eli atakalamba ndipo ana ake Hofeni ndi Pinehasi sankalambira Yehova m’njira yoyenera. Nthawi zina mpaka ankachita zachiwerewere ndi akazi amene ankabwera kukachisiko. Kodi ukuganiza kuti bambo awo anayenera kuchita chiyani atadziwa zimenezi?​— Anayenera kuwalanga n’kuwaletsa kuti asadzachitenso zoipazo.

Samueli ali mwana ankakhala kukachisi nthawi zonse, ndipo n’zotheka kuti amadziwa khalidwe loipa la ana a Eliwo. Koma kodi Samueli anatengera khalidwe lawolo?​— Ayi, iye anapitirizabe kuchita zinthu zabwino zimene makolo ake anam’phunzitsa. Moti n’zosadabwitsa kuti Yehova anakwiya naye Eli. Anachita  kutumiza mneneri wake kuti akawauze kuti alanga banja lake lonse, makamaka ana ake oipawo.​—1 Samueli 2:22-36.

Samueli anapitirizabe kutumikira pakachisi limodzi ndi Eli. Kenaka tsiku lina usiku, Samueli ali mtulo anamva munthu akumuitana. Iye anadzuka n’kupita kwa Eli, koma Eli anamuuza kuti sanamuitane. Kenaka Samueli anamvanso kuitana. Zimenezi zitachitikanso kachitatu, Eli anauza Samueli kuti akamvanso mawuwo anene kuti: “Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva.” Samueli atanena zimenezi Yehova anamuuza mawu. Kodi ukudziwa zimene anamuuza?​—

Mawu ake anali omwe aja onena kuti Iye akufuna kulanga banja la Eli. M’mawa mwake Samueli anachita mantha kumuuza Eli zimene Yehova ananena. Koma Eli anam’chonderera Samueli kuti: “Anakuuza chinthu chanji? Usandibisire ine.” Kenaka Samueli anauza Eli zonse zimene Yehova ananena kuti achita, monga mmene anali atanenera kale kudzera mwa mneneri wake. Eli atamva zimenezi anayankha kuti “Yehova; achite chom’komera pamaso pake.” Kenaka, patsogolo pake Hofeni ndi Pinehasi anaphedwa, ndipo Eli naye anafa.​—1 Samueli 3:1-18.

Koma “Samueli anakula, Yehova nakhala naye.” N’kutheka kuti panthawiyi Samueli anali mnyamata, ndipo anali asanakwanitse zaka 20. Munthu akakhala pa msinkhu umenewu amafunika kuchita zinthu mosamala kwambiri. Kodi ukuganiza kuti zinali zophweka kuti Samueli azichita zabwino ngakhale kuti anzake ankachita zoipa?​— Ayi, sizinali zophweka. Komatu Samueli anatumikirabe Yehova mokhulupirika kwa moyo wake wonse.​—1 Samueli 3:19-21.

Nanga bwanji iweyo? Kodi ukadzakula ukufuna kudzakhala ngati Samueli? Kodi umafuna kumachita zinthu zabwino ngati Samueli? Kodi umafuna kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa komanso zimene makolo ako amakuphunzitsa? Ngati umatero uzidziwa kuti Yehova ndiponso makolo ako adzasangalala nawe.

^ ndime 3 Ngati mukuwerengera ana nkhaniyi, kamzereka n’kokuuzani kuti muime kuti anawo ayankhe funsolo.