Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Posachedwapa Dzikoli Liwonongekeratu?

Kodi Posachedwapa Dzikoli Liwonongekeratu?

 Kodi Posachedwapa Dzikoli Liwonongekeratu?

Sankhani yankho limene mukuona kuti ndi lolondola la funso ili.

Kodi n’chiyani chimene mukuona kuti chichitika padzikoli m’tsogolo muno?

(a) zinthu ziyamba kuyenda bwino

(b) zinthu sizisintha

(c) zinthu ziipiraipira

KODI mumadzilimbitsa mtima poganiza kuti zinthu ziyamba kuyenda bwino m’tsogolo muno? Ngati mumatero mumachita bwino kwambiri. Ofufuza apeza kuti anthu amene amaganiza choncho amachita bwino kusukulu ndiponso amakhala athanzi labwino. Ofufuza ena amene akhala akufufuza zimenezi kwa zaka zambiri, anapeza kuti amuna amene amaganiza kuti zinthu ziyamba kuyenda bwino kawirikawiri sadwala matenda a mtima kuyerekezera ndi amene anataya mtima. Zimene anapezazi n’zogwirizana ndi zimene Baibulo linanena kalekale, kuti: “Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.”​—Miyambo 17:22.

Komabe, anthu ambiri amaona kuti palibe chowalimbitsa mtima akaganizira zimene akatswiri a sayansi akunena zokhudza tsogolo la dziko lathu lino. Taganizirani zina mwa nkhani zoterezi zimene zikufalitsidwa kwambiri.

Dzikoli Lili Pangozi

M’chaka cha 2002, bungwe lina lodziwika kwambiri pankhani yoona zachilengedwe linachenjeza kuti ngati anthu sachitapo kanthu pa vuto la zachuma, pangakhale “mavuto  amene angasokoneze kwambiri nyengo ndiponso zachilengedwe za padziko lonse.” Bungwelo linanenanso kuti umphawi wa padziko lonse, kudyerana masuku pamutu, ndiponso kuwononga zachilengedwe kungabweretse mavuto ambiri okhudza “chilengedwe, chikhalidwe ndiponso chitetezo.”​—Stockholm Environment Institute Synthesis Report.

M’chaka cha 2005, bungwe la United Nations linatulutsa lipoti la zimene linapeza pa kafukufuku wake wina yemwe anatenga zaka zinayi. Kafukufukuyu anali woona mmene zachilengedwe zikusinthira padziko lonse ndipo anachitidwa ndi akatswiri oposa 1,360 ochokera m’mayiko 95. Lipoti limene anatulutsa pa kafukufukuyo linali ndi mawu ochenjeza akuti: “Zochita za anthu zikusokoneza kwambiri zachilengedwe padziko lonse moti tayamba kukayikira ngati dzikoli lipitirirabe kukhala ndi zinthu zokwanira aliyense m’tsogolo muno.” Lipotili linati, kuti tipewe zoopsazi m’pofunika “kusintha kwakukulu pankhani ya malamulo, mabungwe ndiponso zochita za anthu. Komabe kusintha kotereku sikunayambe.”​—Millennium Ecosystem Assessment Synthesis Report.

Anna Tibaijuka, yemwe ndi mkulu woyang’anira bungwe lina loona za malo, anatchula nkhawa imene ofufuza ambiri ali nayo. Iye anati: “Tikapanda kuchitapo kanthu, tidzanong’oneza bondo.”​—United Nations Human Settlements Programme.

Musataye Mtima

Nawo a Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magazini ino, amakhulupirira kuti posachedwapa pachitika zinthu zimene zidzasinthiratu dzikoli. Kungoti iwo sakayika ngakhale pang’ono kuti kusintha kwake sikudzakhala kowononga dzikoli. Kusinthako kudzakhala koyala maziko a moyo wabwino kwambiri, woposa moyo uliwonse umene anthu anakhalapo nawo. N’chifukwa chiyani amakhulupirira zimenezi? N’chifukwa choti amakhulupirira malonjezo a m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Taonani chitsanzo chimodzi cha malonjezo amenewa: “Katsala kanthawi ndipo oipa adzatha psiti: Inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Salmo 37:10, 11.

Kodi mukuona kuti zimenezi n’zongolakalaka chabe? Musanayankhe funso limeneli taganizirani mfundo iyi: Zaka masauzande ambiri zapitazo, Baibulo linanena molondola kuti masiku athu ano kudzachitika mavuto akuluakulu. Mavuto ake ndi amene akuwononga dziko ndiponso kuvutitsa anthu masiku ano. Werengani malemba amene asonyezedwa m’nkhani yotsatirayi, ndipo onani ngati akugwirizanadi ndi zimene mukuona padziko pano. Mukatero, mungathe kuyamba kukhulupirira kwambiri kuti zimene Baibulo limanena zokhudza m’tsogolo ndi zoonadi.