Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chiyani Chingathe “Kutilekanitsa ndi Chikondi cha Mulungu”?

Kodi N’chiyani Chingathe “Kutilekanitsa ndi Chikondi cha Mulungu”?

 Yandikirani Mulungu

Kodi N’chiyani Chingathe “Kutilekanitsa ndi Chikondi cha Mulungu”?

Aroma 8:38, 39

PALIBE munthu amene safuna kukondedwa. Tonse timamva bwino tikaona kuti abale athu ndiponso anzathu amatikonda. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthufe timakhumudwitsana n’kudana pa zifukwa zosadziwika bwino. Achibale ndiponso anzathu angathe kutikhumudwitsa kwambiri, kutisala, kapena kusiya kutiyendera. Komatu pali munthu wina amene chikondi chake n’chosakayikitsa. Lemba la Aroma 8:38, 39 limafotokoza bwino mmene Yehova Mulungu amakondera anthu amene amamulambira.

Mtumwi Paulo anati: “Ndatsimikiza.” Kodi pamenepa ankatanthauza kuti watsimikiza chiyani? Kuti palibe chingathe “kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu.” Ponena kuti “kutilekanitsa,” Paulo anasonyeza kuti sanali kungonena za iyeyo ayi, koma akunenanso za anthu onse amene amatumikira Mulungu mokhulupirika, kuphatikizapo ifeyo. Pofuna kugogomezera mfundo yake, Paulo anatchulapo zinthu zingapo zimene sizingaletse chikondi cha Yehova kufika kwa atumiki ake odzipereka.

“Imfa, kapena moyo.” Chikondi cha Yehova pa anthu ake sichitha anthuwo akafa. Potsimikizira chikondi chake, Mulungu amakumbukira anthu amenewa ndipo adzawaukitsa kuti akhalenso ndi moyo m’dziko lolungama limene likubwera. (Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:3, 4) Chikondi cha Mulungu kwa anthu amene amamulambira mokhulupirika sichitha ngakhale zinthu zitakhala bwanji pa moyo wawo m’dongosolo linolo.

“Angelo, kapena maboma.” Anthu amatha kutengeka mosavuta ndi anthu opatsidwa ulemu kapena akuluakulu aboma, koma Yehova satero ayi. Ngakhale angelo amphamvu, ngati mngelo amene anakhala Satana, sangathe kuchititsa Mulungu kuleka kukonda anthu amene amam’lambira. (Chivumbulutso 12:10) Ngakhale maboma, amene amatsutsa Akhristu oona sangasinthe mmene Mulungu amaonera atumiki ake.​—1 Akorinto 4:13.

“Zinthu zimene zilipo, kapena zinthu zam’tsogolo.” Chikondi cha Mulungu sichizirala pakapita nthawi. Palibe chilichonse chimene chingachitike kwa atumiki ake, panopo ngakhale m’tsogolo, chomwe chingalepheretse Mulungu kuwasonyeza chikondi.

“Mphamvu.” Paulo akutchula za “mphamvu” pambuyo poti watchula “angelo” ndi “maboma.” Mawu a Chigiriki amene anawagwiritsa ntchito pano ali ndi matanthauzo angapo. Ngakhale zili choncho, mfundo yaikulu pamenepa ndi yakuti: Palibe mphamvu yamtundu uliwonse, kumwamba kapena padziko pano, imene ingaletse chikondi cha Yehova kufika kwa anthu ake.

“Msinkhu, kapena kuya.” Yehova amawakondabe anthu ake ngakhale akumane ndi mavuto otani pamoyo wawo.

“Cholengedwa china chilichonse.” Ponena mawu amenewa, Paulo anatanthauza kuti palibiretu chilichonse chimene chingalekanitse anthu olambira Yehova mokhulupirika ku chikondi chake.

Mosiyana ndi chikondi cha anthu, chimene chikhoza kusintha komanso kuzirala, chikondi cha Mulungu pa anthu amene amam’tsatira mokhulupirika sichisintha ndipo n’chosatha. Ndithudi, kudziwa zimenezi kumatilimbikitsa kuyandikira kwa Yehova ndi kuyesetsa kuchita zinthu zosonyeza kuti timam’konda.