Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dziko Lapansili Likhalapobe Mpaka Kalekale?

Kodi Dziko Lapansili Likhalapobe Mpaka Kalekale?

 Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Dziko Lapansili Likhalapobe Mpaka Kalekale?

Dziko lathuli silidzaonongeka ndi masoka a chilengedwe. N’chifukwa chiyani sitikukayikira zimenezi? Chifukwa chakuti Yehova analonjeza kuti dzikoli “silidzagwedezeka ku nthawi yonse.” (Salmo 104:5) Baibulo limanena kuti: “Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.”​—Mlaliki 1:4.

Lemba la Salmo 104:5 limatsindika mfundo yakuti dziko lapansi lidzakhalapobe. Mawu awiri achiheberi amene anagwiritsidwa ntchito pa lembali amatsimikizira mfundo imeneyi. Oyamba ndi akuti ʽoh·lamʹ kutanthauza kuti “kosatha” ndipo achiwiri ndi akuti ʽadh kutanthauza kuti “kwa muyaya.” Mawu akuti ʽoh·lamʹ angamasuliridwenso kuti “kwa zaka zambiri” kapena kuti “mpaka kalekale.” Buku lina lotanthauzira mawu achiheberi limene Harkavy analemba, limasonyeza kuti mawu oti ʽadh amatanthauza “nthawi yaitali, kosatha, kapena kwa muyaya.” (Students’ Hebrew and Chaldee Dictionary) Mawu achiheberi awiri amenewa amatsimikizira mfundo yakuti dzikoli lidzakhalapobe mpaka kalekale. Tiyeni tione zifukwa zitatu zolembedwa m’Baibulo zotsimikizira kuti dzikoli lidzakhalapobe mpaka kalekale.

Chifukwa choyamba n’chakuti Mulungu analenga dzikoli kuti anthu akhalemo. Iye anafuna kuti likhale paradaiso wokongola kwambiri osati malo opanda ntchito. Pofotokoza za Yehova, lemba la Yesaya 45:18 limati: “Analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; iye analiumba akhalemo anthu.”

Chifukwa chachiwiri n’chakuti Mulungu analonjeza kale kuti anthu amene amamumvera adzakhala m’dzikoli kosatha mwamtendere. Lemba la Mika 4:4 limanena kuti: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.” Motero malinga ndi chifuniro cha Mulungu, dziko lapansi liyenera kukhalapo kosatha kuti anthu akhalemo. Kupanda kutero ndiye kuti lonjezo lake silikwaniritsidwa.​—Salmo 119:90; Yesaya 55:11; 1 Yohane 2:17.

Chifukwa chachitatu n’chakuti Mulungu wapatsa anthu udindo wosamalira dzikoli. Mawu a Mulungu amati: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” (Salmo 115:16) Kodi pali bambo wachikondi amene angapereke mphatso yokongola kwa mwana wake kenako n’kuiwononga? Ayi ndithu palibe. Choncho, Yehova sangawononge dziko ndi anthu okhalamo chifukwa “Mulungu ndiye chikondi.”​—1 Yohane 4:8.

Posonyeza kuti mawu a Atate ake ndi odalirika, Yesu anati: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Ndipo Mulungu amene sanganame walonjeza kuti “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:29; Tito 1:2.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Globe: Based on NASA photo