Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Nkhondo Yothetsa Nkhondo Zonse”

“Nkhondo Yothetsa Nkhondo Zonse”

 “Nkhondo Yothetsa Nkhondo Zonse”

‘Ndikukutsimikizirani kuti iyi ikhala nkhondo yomaliza, nkhondo yothetsa nkhondo zonse.’ ANATERO PULEZIDENTI WOODROW WILSON WA KU UNITED STATES (1913-1921).

IZI ndi zinthu zimene mtsogoleri wa dziko ameneyu, anali kuyembekezera zaka 90 zapitazo kuti zichitika nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha. Nkhondo imeneyi inali yoopsa kwambiri ndipo asilikali ankakhulupirira kuti akamenya nkhondo imeneyi modzipereka kwambiri, adzathetsa nkhondo zonse. Koma nkhondo sizinathe ndipo pali mavuto ambiri.

Pulezidenti Wilson anapupuluma polonjeza zimenezi chifukwa patapita zaka 20, nkhondo yachiwiri yapadziko lonse inayamba. Anthu ambiri anafa ndipo zinthu zambiri zinawonongedwa pa nkhondoyi kuposa zimene zinawonongedwa pa nkhondo yoyamba. M’kati mwa zaka 20 zimenezi, anthu anapita patsogolo kwambiri pa luso lopanga zida za nkhondo zoopsa zedi. Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itangotha, atsogoleri a padziko lonse anazindikira kuti nkhondo ina ingathe kuyambika nthawi iliyonse.

M’chaka cha 1945, mkulu wa asilikali a dziko la United States dzina lake Douglas MacArthur anati: “Uwu ndi mwayi wathu womaliza woti tithetse nkhondo padziko lonse. Koma ngati sitipeza njira ina yabwino kwambiri yoyendetsera zinthu, nkhondo ya Aramagedo ikhoza kuyamba nthawi iliyonse.”

Mkulu wa asilikaliyu ankadziwa bwino zimene zinachitika mizinda ya ku Japan, ya Nagasaki ndi Hiroshima, itaphulitsidwa ndi mabomba a nyukiliya, chakumapeto kwa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Kuwonongedwa kwa mizinda imeneyi kunachititsa kuti mkulu wa asilikaliyu aganize kuti Aramagedo ndi nkhondo ya zida za nyukiliya imene idzaseseratu anthu onse padziko lapansi.

 Anthu padziko lonse akuda nkhawa chifukwa akuona kuti, nthawi iliyonse nkhondo ya zida za nyukiliya ikhoza kuyambika. Pofika mu 1960, mayiko amphamvu kwambiri padziko lonse anali atagwirizana zoti, ngati dziko lina litaputa linzake ndi zida za nyukiliya adzabwezerana. Panganoli linapereka chilolezo chowononga dera la anthu ndi la mafakitale. Anagwirizananso kuti dziko limene lachitiridwa za mtopola lizibwezera dziko lililonse limene lili m’panganolo ngakhale silikukhudzidwa n’komwe ndi nkhaniyo. Koma pangano limeneli, lomwe ankati cholinga chake chinali kubweretsa mtendere, linachititsa kuti anthu ambiri azikhala mwa mantha.

Masiku ano, zida za nyukiliya zikuchulukirachulukira ndipo anthu ambirimbiri akufabe pa nkhondo. Ndipo ambiri ali ndi mantha chifukwa akuona kuti nkhondo ya zida za nyukiliya itha kuyambika nthawi ina iliyonse. Ngakhale kuti anthu ambiri akulakalaka kuti nkhondo ithe, ndi anthu ochepa chabe amene amakhulupirira kuti mapangano amene mayiko amachita angathetse nkhondo.

Komabe, Baibulo limanena za nkhondo ina yapadera kwambiri yomwe idzathetsa nkhondo zonse. Ndipo limati nkhondoyi ndi Aramagedo, imene anthu ambiri amaganiza kuti ndi nkhondo ya zida za nyukiliya. Koma kodi zidzatheka bwanji kuti nkhondo ya Aramagedo idzathetse nkhondo zonse? Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

DTRA Photo

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Nagasaki, Japan, 1945: USAF photo