Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani mu Gulu la Ana a Mulungu

Khalani mu Gulu la Ana a Mulungu

 Khalani mu Gulu la Ana a Mulungu

PATATHA zaka 30 kuchokera pamene nkhondo ya ku Korea inatha, bungwe lofalitsa nkhani pa TV ndi pa wailesi linayambitsa pulogalamu yothandiza anthu kupezanso achibale awo omwe analekana nawo panthawi ya nkhondo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Anthu oposa 11,000 anakumananso ndi abale awo. Ndipo anthuwa anasangalala kwambiri moti anakumbatirana ndiponso anakhetsa misozi. Nyuzipepala ina ya ku Korea (Korea Times) inati: “Nthawiyi inali yoyamba kuti anthu ochuluka a ku Korea akhetse misozi yambiri ndi kusangalala panthawi imodzi.”

Ku Brazil, Cézar ali mwana wakhanda anaperekedwa ku banja lina polipira ngongole. Patatha zaka 10, iye anasangalala kwambiri kukumananso ndi mayi ake enieni ndipo anachoka kwa makolo ake om’lera omwe anali olemera kwambiri.

Anthu apachibale amasangalala kwambiri akaonananso pambuyo poti anasowana kwa nthawi yaitali. Baibulo limafotokoza momveka bwino zinthu zomvetsa chisoni zimene zinachititsa kuti anthu asiyane ndi banja la Mulungu. Ndipo limafotokozanso zimene Mulungu wachita kuti anthu agwirizanenso naye mosangalala. Kodi wachita zotani? Kodi inuyo mungatani kuti mugwirizane ndi Mulungu mosangalala?

Banja la Mulungu Linalekanitsidwa

Ponena za Mlengi wathu Yehova Mulungu, wamasalmo anati: “Chitsime cha moyo chili ndi inu.” (Salmo 36:9) Yehova ndiye Tate wa banja lalikulu kwambiri m’chilengedwe chonse. Banja limeneli ndi la zolengedwa zokhulupirika ndiponso za nzeru zomwe zili m’magulu awiri, za kumwamba ndi za padziko lapansi. Kumwamba kuli angelo omwe ndi ana ake auzimu ndipo padziko lapansi pali anthu omwe akufunika kudzakhala ana ake.

Pamene munthu woyamba kulengedwa, Adamu, sanamvere Mulungu monga mmene nkhani yapitayi yafotokozera, anthu onse analekanitsidwa momvetsa chisoni ndi Atate wachikondi yemwe ndi Mlengi. (Luka 3:38) Izi zili chonchi chifukwa chakuti kusamvera Mulungu kwa Adamu kunachititsa kuti iye ndiponso ana ake ataye mwayi wokhala ana a Mulungu. Kudzera mwa mtumiki wake Mose, Mulungu anafotokoza zotsatira za kusamvera kumeneku. Iye anati: “Anam’chitira zovunda sindiwo ana [a Mulungu]  chirema n’chawo.” “Chirema,” kapena kuti uchimo, chinalekanitsa anthu kwa Mulungu yemwe ndi woyera ndiponso wangwiro m’njira zake zonse. (Deuteronomo 32:4, 5; Yesaya 6:3) Motero, anthu onse anakhala ngati ana amasiye, kapena kuti opanda bambo.​—Aefeso 2:12.

Potsindika mmene anthu alili otalikirana ndi Mulungu, Baibulo limati anthu amene ali kunja kwa banja la Mulungu ndi “adani” ake. (Aroma 5:8, 10) Popeza anthu anasiya Mulungu, Satana akuwalamulira mwa nkhanza ndiponso akuvutika ndi zotsatirapo za uchimo komanso kupanda ungwiro. (Aroma 5:12; 1 Yohane 5:19) Kodi n’zotheka kuti anthu ochimwa akhale m’banja la Mulungu? Kodi anthu opanda ungwiro angakhaledi ana a Mulungu ngati mmene Adamu ndi Hava analili asanachimwe?

Kusonkhanitsa Ana Olekanitsidwa

Mwachikondi, Yehova anakonza njira yothandizira anthu opanda ungwiro amene amam’konda. (1 Akorinto 2:9) Mtumwi Paulo anati: “Mulungu akuyanjanitsa dziko ndi iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthuwo machimo awo.” (2 Akorinto 5:19) Monga mmene nkhani yapitayi yasonyezera, Yehova Mulungu anapereka Yesu Khristu kukhala dipo la machimo athu. (Mateyo 20:28; Yohane 3:16) Mtumwi Yohane analemba moyamikira kuti: “Taonani mtundu wa chikondi chimene Atate watikonda nacho, potitcha ife ana a Mulungu.” (1 Yohane 3:1) Motero, iye anatsegula njira yoti anthu omvera akhalenso m’banja la Yehova.

Anthu onse omwe ali m’banja la Mulungu adzakhala ogwirizana kwambiri moyang’aniridwa ndi Atate wawo wakumwamba. Baibulo limati anthu amenewa alipo magulu awiri, chifukwa limati: “Chinsinsicho n’chogwirizana ndi zokomera [Mulungu] ndi zimene anafuna mu mtima mwake, kuti akakhazikitse dongosolo lake ikadzatha nyengo yonse ya nthawi zoikika. Dongosolo limenelo ndilo kusonkhanitsanso zinthu zonse pamodzi mwa Khristu, zinthu za kumwamba ndi zinthu za padziko lapansi.” (Aefeso 1:9, 10) N’chifukwa chiyani Mulungu anachita zinthu mwa dongosolo limeneli?

Zimene Yehova wachita poika ana ake m’magulu awiri n’zothandiza kwambiri kuti banja lake likhale logwirizana. Ndipo zimenezi si zovuta kumvetsa. Banja la Mulungu ndi lalikulu kwambiri moti tingaliyerekezere ndi anthu okhala m’dziko. M’dziko lililonse, anthu ochepa amasankhidwa kuti apange boma lolamulira kuti anthu ena onse akhale mwa bata ndi mtendere. Palibe boma la anthu limene lingabweretse mtendere weniweni koma ndi Mulungu yekha amene angachite zimenezi kwa anthu ake. Gulu loyamba lomwe ndi “zinthu za kumwamba,” ndi la ana a Mulungu omwe Yehova wawasankha kuti apange boma, kapena kuti Ufumu kumwamba. Ali kumwambako, iwo “adzalamulira dziko lapansi monga mafumu.”​—Chivumbulutso 5:10.

Ana a Mulungu a Padziko Lapansi

Yehova akusonkhanitsanso “zinthu za padziko lapansi” zomwe ndi anthu mamiliyoni ambiri, n’cholinga choti adzakhale ana ake padzikoli. Popeza iye ndi Tate wachikondi, amawaphunzitsanso njira zake zachikondi kuti akhale ogwirizana bwino ngakhale ali ochokera m’mitundu yosiyanasiyana. Ngakhale anthu omwe ndi achiwawa, odzikonda, achiwerewere ndiponso osamvera Mulungu, akulimbikitsidwa kuti ‘ayanjanenso ndi Mulungu.’​—2 Akorinto 5:20.

Nanga bwanji anthu amene amakana kuyanjananso ndi Mulungu kuti akhale ana ake? Anthu oterowo, Yehova adzawalanga n’cholinga choti banja lake likhale la mtendere ndi logwirizana. Padzakhala “tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 3:7) Mulungu adzawononga anthu onse osamvera padzikoli. Ndiyeno anthu omvera adzasangalala ndi mtendere wochuluka.​—Salmo 37:10, 11.

Kenako padzakhala zaka 1,000 za mtendere, zomwe anthu onse okonda Mulungu adzabwereranso kukhala angwiro monga momwe Adamu analili poyamba. Ndipo panthawiyi nawonso akufa adzaukitsidwa. (Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 20:6; 21:3, 4) Motero Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Chilengedwecho [kapena kuti anthu] chidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda ndi kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”​—Aroma 8:21.

 Kuyanjanitsidwa ndi Atate Wathu

Cézar ndiponso anthu ambirimbiri a ku Korea omwe tawatchula kumayambiriro kwa nkhani ino anachita zonse zimene akanatha kuti akumanenso ndi achibale awo. Anthu a ku Korea aja anafunika kumvera pulogalamu ija ndipo Cézar anachoka kwa makolo ake om’lera. Mofanana ndi zimenezi, inunso mufunika kuyesetsa kuchita zilizonse zomwe mungathe kuti muyanjanenso ndi Atate wanu wakumwamba, Yehova Mulungu, ndiponso kuti mukhale m’banja lake. Kodi inuyo mufunika kuchita chiyani?

Kuti Mulungu akhale Atate wanu ndiponso kuti mukhale naye paubwenzi wabwino, mufunika kuphunzira mawu ake omwe ndi Baibulo. Ndipo zimenezi zidzakuthandizani kum’khulupirira kwambiri ndiponso kukhulupirira malonjezo ake. Mudzazindikira kuti zimene Mulungu amakuuzani kuti muchite ndi zinthu zopindulitsa inu nomwe. Mudzafunikiranso kutsatira malangizo a Mulungu chifukwa Baibulo limauza Akhristu kuti: “Mulungu akuchita nanu ngati ana ake. Ndi mwana wanji amene atate wake sam’langa?”​—Aheberi 12:7.

Kuchita zimenezi kudzasintha moyo wanu wonse. Baibulo limanena kuti: “Mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo choona ndi kukhulupirika.” (Aefeso 4:23, 24) Ndiyeno tsatirani malangizo a mtumwi Petulo akuti: “Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa.”​—1 Petulo 1:14.

Gwirizanani ndi Banja Lanu Lenileni

Cézar atapeza amayi ake, anasangalala kwambiri atadziwa kuti iye anali ndi mchimwene ndiponso mlongo wake. Mofanana ndi zimenezi, mukamayesetsa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wanu wakumwamba, mudzazindikira kuti muli ndi abale ndi alongo ambirimbiri mumpingo wachikhristu. Mukamacheza nawo, mudzayamba kukondana nawo kwambiri kuposa achibale anu enieni.​—Machitidwe 28:14, 15; Aheberi 10:24, 25.

Tikukulimbikitsani kuti mugwirizanenso ndi Atate wanu wakumwamba, komanso abale ndi alongo anu achikhristu. Mudzasangalala kwambiri ngati mmene Cézar ndi anthu ena ambirimbiri ku Korea anasangalalira atakumananso ndi achibale awo.

[Chithunzi patsamba 8]

Cézar ali ndi zaka 19, ndipo ali limodzi ndi amayi ake

[Zithunzi patsamba 10]

Chitani zimene mungathe kuti mukhale pa ubwenzi ndi Mulungu