Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pankhani ya Mulungu Woona

Pankhani ya Mulungu Woona

 Zimene Tikuphunzira kwa Yesu

Pankhani ya Mulungu Woona

Kodi Mulungu ali ndi dzina?

Yesu anaphunzitsa kuti Mulungu ali ndi dzina. Iye anati: “Choncho inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.’” (Mateyo 6:9) Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. (Salmo 83:18) Ponena za ophunzira ake, Yesu anapemphera kwa Atate wake kuti: “Dzina lanu ndalidziwitsa kwa iwo.”​—Yohane 17:26.

Kodi Yehova ndi ndani?

Yesu anati Yehova ndi “Mulungu yekha woona” chifukwa Iye ndiye Mlengi. (Yohane 17:3) Yesu anati: “Kodi simunawerenge kuti iye amene analenga iwo pachiyambi pomwe anapanga iwo mwamuna ndi mkazi?” (Mateyo 19:4) Yesu ananenanso kuti: “Mulungu ndiye Mzimu.” (Yohane 4:24) N’chifukwa chake sitingathe kuona Mulungu.​—Eksodo 33:17-20.

 Kodi Mulungu amafuna kuti tizichita chiyani?

Munthu wina atafunsa Yesu kuti lamulo lalikulu ndi liti, iye anayankha kuti: “Loyamba n’lakuti, ‘Imva Isiraeli iwe, Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi, ndipo uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse, ndi mphamvu zako zonse.’ Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.’”​—Maliko 12:28-31.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mulungu?

Yesu anati: “Ndimakonda Atate.” Kodi anasonyeza bwanji chikondi chake? Iye anati: “Ndikuchita izi kutsatira lamulo limene Atateyo anandipatsa.” (Yohane 14:31) Iye ananenanso kuti: “Ndimachita zinthu zom’kondweretsa nthawi zonse.” (Yohane 8:29) Tingasangalatse Mulungu mwa kuphunzira za iye. Yesu popempherera ophunzira ake, anati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona.”​—Yohane 17:3; 1 Timoteyo 2:4.

Kodi tingatani kuti tiphunzire za Mulungu?

Njira imodzi yodziwira Mulungu ndiyo kuona zinthu zimene analenga. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Onetsetsani mbalame za mlengalenga, pajatu sizifesa kapena kukolola kapena kututira m’nkhokwe ayi; komabe Atate wanu wa kumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu a mtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” Kodi pamenepa mfundo ya Yesu inali yotani? Tisalole kuti nkhawa ya zinthu zimene timafunika pamoyo wathu itilepheretse kutumikira Mulungu.​—Mateyo 6:26-33.

Njira yabwino kwambiri imene tingam’dziwire bwino Yehova ndi kuphunzira Mawu ake, Baibulo. Yesu ananena kuti Malemba ndi “mawu a Mulungu.” (Luka 8:21) Yesu anati kwa Mulungu: “Mawu anu ndiwo choonadi.”​—Yohane 17:17; 2 Petulo 1:20, 21.

Yesu anathandiza anthu kuphunzira za Yehova. Ponena za Yesu, wophunzira wake wina anati: “Kodi mitima yathu sinali kunthunthumira pamene anali kulankhula nafe mu msewu, muja anali kutisanthulira Malemba momveka bwino?” (Luka 24:32) Kuti tiphunzire za Mulungu tiyenera kukhala odzichepetsa ndiponso ofunitsitsa kuphunzira. Yesu anati: “Mukapanda kutembenuka ndi kukhala ngati ana aang’ono, simudzalowa konse mu ufumu wa kumwamba.”​—Mateyo 18:3.

N’chifukwa chiyani timakhala osangalala tikadziwa Mulungu?

Mulungu amatithandiza kuti tizindikire cholinga cha moyo wathu. Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyo 5:3) Yehova amatiphunzitsa zimene tingachite kuti tikhale osangalala. Yesu anati: “Osangalala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”​—Luka 11:28; Yesaya 11:9.

Kuti mudziwe zambiri, onani mutu 1 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 16]

“Dzina lanu ndalidziwitsa kwa iwo.”​—Yohane 17:26

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Tingaphunzire za Yehova mwa kuona zimene analenga ndiponso kuphunzira Baibulo