Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Phunzitsani Ana Anu

Maliko Sanafooke

Maliko Sanafooke

MALIKO analemba limodzi mwa mabuku anayi a m’Baibulo ofotokoza za moyo wa Yesu. Buku lake ndi laling’ono ndiponso losavuta kwambiri kuwerenga. Kodi Maliko anali ndani? Kodi ukuganiza kuti Maliko ankamudziwa Yesu?​— * Tiye tione mavuto amene Malikoyu anakumana nawo ndiponso tione chifukwa chimene iye sanasiyire Chikhristu.

Nthawi yoyamba imene Maliko akutchulidwa m’Baibulo ndi pamene mfumu Herode Agripa anaika mtumwi Petulo m’ndende. Tsiku lina usiku mngelo anam’masula Petulo, ndipo atangotuluka anapita ku Yerusalemu kwa Mariya omwe anali amayi ake a Maliko. Zimenezi zinachitika patapita zaka pafupifupi 10 kuchokera pamene Yesu anaphedwa pa Pasika mu 33 C.E.​—Machitidwe 12:1-5, 11-17.

Kodi ukudziwa chifukwa chake Petulo anapita ku nyumba kwa Mariya?​— Mwina chifukwa choti ankadziwana ndi abale ake a Mariya ndiponso ankadziwa kuti ophunzira a Yesu ankachitira misonkhano ku nyumba imeneyi. Baranaba yemwe anali msuweni wa Maliko anali atakhala kale wophunzira, mwina kuyambira pa Phwando la Pentekosite mu 33 C.E. Zinthu zabwino zimene Baranaba ankachitira ophunzira atsopano zinalembedwa m’Baibulo. Choncho, Yesu ayenera kuti ankamudziwa Baranaba pamodzi ndi azakhali ake Mariya ndiponso mwana wawo Maliko.​—Machitidwe 4:36, 37; Akolose 4:10.

Maliko analemba mu uthenga wake wabwino kuti usiku umene Yesu anamangidwa, panali mnyamata wina amene anangofunda nsalu “popanda chovala china mkati.” Adani atam’gwira Yesu, Maliko analemba kuti mnyamata ameneyu anathawa. Kodi ukuganiza kuti mnyamatayu ayenera kuti anali ndani?​— Ayenera kuti anali Maliko amene. Motero Yesu ndi atumwi ake atachoka kwa Maliko pausiku umenewo, n’kutheka kuti Maliko anangofunda nsalu yake n’kuyamba kuwatsatira.​—Maliko 14:51, 52.

Maliko analidi wochokera ku banja lokonda kwambiri zinthu zauzimu. Zikuoneka kuti iye analipo pamene mzimu woyera unatsanuliridwa pa atumwi pa Pentekosite mu 33 C.E., ndipo ankacheza kwambiri ndi atumiki okhulupirika a Mulungu, monga Petulo. Maliko ankayendanso ndi msuweni wake Baranaba, amene anathandiza Saulo kuti adziwane ndi Petulo patatha zaka zitatu kuchokera nthawi imene Yesu anaonekera kwa Saulo m’masomphenya. Patapita zaka zingapo, Baranaba anapita ku Tariso kuti akamuyang’ane Saulo.​—Machitidwe 9:1-15, 27; 11:22-26; 12:25; Agalatiya 1:18, 19.

M’chaka cha 47 C.E., Baranaba ndi Saulo anasankhidwa kuti akhale amishonale.  Pantchito yawoyi, iwo anam’tenga Maliko koma pazifukwa zina zimene sizinafotokozedwe, Maliko anawasiya n’kubwerera kwawo ku Yerusalemu. Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri Saulo amene anayamba kudziwika ndi dzina lake la Chiroma lakuti Paulo. Ndipo Paulo sanaiwale zimene Maliko anachitazi.​—Machitidwe 13:1-3, 9, 13.

Paulo ndi Baranaba atabwerako ku ulendo wawo wa umishonalewu ananena kuti zinthu zinawayendera bwino kwambiri. (Machitidwe 14:24-28) Patapita miyezi ingapo, anthu awiriwa anagwirizana kuti ayenderenso anthu amene anatembenuka mtima paulendo woyamba umene anawalalikira. Baranaba anafuna kuti am’tengenso Maliko, koma kodi ukudziwa zimene Paulo anaganiza?​— Iye “anaona kuti n’kosayenera” chifukwa Maliko anawasiya n’kubwerera kwawo paulendo woyamba uja. Koma zimene zinachitika pambuyo pake zinamumvetsa Maliko chisoni.

Paulo ndi Baranaba anapsetsana mitima, ndipo “panabuka mkangano woopsa” umene unachititsa kuti apatukane. Baranaba anam’tenga Maliko kukalalikira ku Kupuro, ndipo Paulo anam’tenga Sila kukachezeranso ophunzira atsopano, monga anagwirizanirana ndi Baranaba. Zimenezi zinamumvetsatu Maliko chisoni kwabasi chifukwa Paulo ndi Baranaba anasemphana maganizo chifukwa cha iye.​—Machitidwe 15:36-41.

Sitikudziwa chimene chinam’chititsa Maliko kubwerera kwawo pa ulendo woyamba uja. Koma n’kutheka kuti anali ndi chifukwa chomveka. Komabe, Baranaba anali ndi chikhulupiriro chonse kuti Maliko sachitanso zimene anachita pa ulendo woyambawo. Ndipo ndi mmenedi zinakhalira, Maliko sanabwerere kwawo. Patapita nthawi iye anapitanso paulendo waumishonale ndi Petulo ku Babulo, komwe kunali kutali kwambiri  ndi kwawo. Ali kumeneko, Petulo anatumiza moni, ndipo anati: “Mwana wanga Maliko, [nayenso] akupereka moni.”​—1 Petulo 5:13.

Petulo ndi Maliko ankagwirizana kwambiri chifukwa anatumikira limodzi Mulungu. Umboni wa zimenezi timaupezanso tikamawerenga uthenga wabwino wa Maliko. M’buku limeneli, Maliko analongosola bwino zimene anauzidwa ndi Petulo yemwe ankaona zochita za Yesu. Mwachitsanzo, tikawerenga nkhani yonena za namondwe yemwe anachitika pa nyanja ya Galileya, Maliko analemba nkhani imeneyi momveka bwino chifukwa anatchula kumene Yesu anagona m’bwatomo ndiponso chimene anatsamira. Amene akanadziwa bwino zinthu zimenezi ndi asodzi okha, monga Petulo. Tiye tiwerengere limodzi nkhani imeneyi m’Baibulo pa Mateyo 8:24; Maliko 4:37, 38; ndi Luka 8:23 kuti tione kusiyana kwake.

Kenaka, mtumwi Paulo ali m’ndende ku Roma, anayamikira Maliko chifukwa chom’thandiza mokhulupirika. (Akolose 4:10, 11) Ndipo Paulo atamangidwa kachiwiri, analembera kalata Timoteyo ndi kum’pempha kuti amubweretse Maliko. Pauloyo anati “iye ndi wofunika ponditumikira.” (2 Timoteyo 4:11) Ndithudi, Maliko anatumikira Mulungu mwapadera kwambiri chifukwa choti sanafooke.

^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana wanu, mukapeza pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.