Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufufuza Mayankho

Kufufuza Mayankho

 Kufufuza Mayankho

“Ngakhale anthu masiku ano atakhala ndi moyo wabwinopo, chifukwa chokhala ndi zinthu monga nyumba zabwino ndi magalimoto apamwamba komanso mawailesi a ma CD, angadzifunsebe kuti: ‘Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’ Nanga n’chifukwa chiyani anthu amadzivutitsa kuti apeze zinthu zonsezi?”​—Anatero pulofesa David G. Myers, yemwe ndi katswiri wa zamaganizo pa Hope College, ku Holland, m’mzinda wa Michigan, ku America.

KODI inuyo mungayankhe bwanji mafunso amene anafunsa katswiri ameneyu? Anthu ena angaganize kuti kuthera nthawi yambiri akufufuza mayankho a mafunso amenewa kulibe phindu. Komabe, kunyalanyaza mafunso amenewa kuli ngati kunyalanyaza kamwala kamene kali mu nsapato yanu. Mungathe kupitiriza kuyenda, koma kamwalako kazikusowetsani mtendere.

Ngati inuyo munadzifunsapo za cholinga cha moyo, simuli nokha. Bungwe lina lofufuza za makhalidwe a anthu (World Values Survey), linapeza kuti anthu ochuluka m’mayiko ambiri amafunsa za “tanthauzo ndi cholinga cha moyo.” Kafukufuku ameneyu ndi mmodzi mwa akafukufuku aakulu kwambiri okhudza makhalidwe a anthu amene mabungwe achita.

Koma ngati mukufuna kuti mukhale ndi mtendere weniweni wa mu mtima, mufunika kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri otsatirawa.

Kodi tinachokera kuti?

Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?

Kodi m’tsogolomu muli zotani?

Kodi mayankho odalirika a mafunso ofunikawa mungawapeze kuti? M’malo mongofotokoza maganizo a anthu, nkhani zotsatirazi zifotokoza mayankho opezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Tikukulimbikitsani kuti Baibulo lanu likhale pafupi powerenga nkhanizi kuti muone nokha zimene limanena.