Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?

Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?

 Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA YANKHO LA FUNSOLI? Mfundo yakuti moyo ulibe tanthauzo ndiponso cholinga ndi imodzi mwa zinthu zimene zimativutitsa kwambiri anthu maganizo. Koma, munthu amene amadziwa bwino kwambiri cholinga cha moyo amatha kupirira mavuto ndipo sataya mtima. Viktor E. Frankl yemwe ndi katswiri wa zamaganizo amenenso anapulumuka pa nkhanza zoopsa za Anazi analemba kuti: “Ndinganene kuti palibe chinthu chimene chingathandize munthu kupirira mavuto aakulu, kuposa kudziwa mfundo yakuti moyo wake uli ndi cholinga.”

Komabe, anthu amaganiza zosiyanasiyana pankhani imeneyi. Ambiri amaganiza kuti aliyense angasankhe yekha cholinga cha moyo. Komabe, anthu ena amene amakhulupirira zoti anthufe tinachita kusanduka amaphunzitsa kuti moyo ulibe cholinga chilichonse.

Komatu, njira yabwino yodziwira cholinga cha moyo ndi kufunsa amene anatipatsa moyo, yemwe ndi Yehova Mulungu. Taganizirani zimene Mawu ake amanena pankhani imeneyi.

Zimene Baibulo Limanena

Baibulo limaphunzitsa kuti Yehova Mulungu anali ndi cholinga chinachake polenga mwamuna ndi mkazi. Yehova anapereka lamulo lotsatirali kwa makolo athu oyambawo.

Genesis 1:28. “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.”

Mulungu anafuna kuti Adamu ndi Hava ndiponso ana awo asandutse dziko lonse lapansi kukhala paradaiso. Iye sanafune kuti anthu azikalamba ndi kumwalira komanso kuti aziwononga chilengedwe. Komabe, chifukwa chakuti makolo athu sanasankhe bwino zinthu, anatipatsira uchimo ndi imfa. (Genesis 3:2-6; Aroma 5:12) Ngakhale zili choncho, cholinga cha Yehova sichinasinthe. Posachedwapa dzikoli lidzakhala paradaiso.​—Yesaya 55:10, 11.

Yehova anatilenga kuti tizitha kuganiza ndi kuchita zinthu kuti tikwaniritse cholinga chake. Iye sanatilenge kuti tizidzidalira tokha. Taonani momwe malemba otsatirawa akufotokozera bwino cholinga chimene Mulungu ali nacho kwa ife.

Mlaliki 12:13. “Mawu atha, zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”

Mika 6:8. “Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”

Mateyo 22:37-39. “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu koposa komanso loyamba. Lachiwiri, lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.’”

Baibulo Limatithandiza Kukhala ndi Mtendere wa Mumtima

Makina aliwonse kuti agwire ntchito bwino afunika kugwiritsidwa ntchito imene anapangidwira. Mofananamo, kuti ife tipewe kudzivulaza tokha kaya m’maganizo kapena mumtima ngakhalenso mwakuthupi, tiyenera kutsatira malangizo a Mlengi wathu. Taonani mmene kudziwa cholinga cha Mulungu kungatithandizire  kukhala ndi mtendere wa mumtima pamoyo wathu m’mbali zotsatirazi.

Posankha zinthu zimene akuona kuti n’zofunika kwambiri, anthu ambiri masiku ano amathera nthawi yawo yonse akufunafuna chuma. Komabe, Baibulo limachenjeza kuti “anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mu msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopanda nzeru ndi zopweteka.”​—1 Timoteyo 6:9, 10.

Koma anthu amene amakonda Mulungu osati ndalama amadziwa zimene zimapangitsa munthu kukhala wosangalala. (1 Timoteyo 6:7, 8) Iwo amadziwa kufunika kolimbikira ntchito komanso amazindikira kuti ali ndi udindo wopeza zinthu zofunika pamoyo wawo. (Aefeso 4:28) Komabe iwo amaganiziranso kwambiri zimene Yesu anachenjeza kuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri; pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”​—Mateyo 6:24.

Choncho, anthu amene amakonda Mulungu amaona kuti chinthu chofunika kwambiri pamoyo wawo ndicho kuchita chifuniro chake osati ntchito yawo kapena kufunafuna chuma. Iwo amadziwa kuti Yehova Mulungu adzawasamalira ngati kuchita chifuniro chake kuli chinthu chofunika kwambiri pamoyo wawo. Ndipotu, Yehova amaona kuti ndi udindo wake kuchita zimenezi.​—Mateyo 6:25-33.

Anthu ambiri pochita zinthu ndi ena, amangofuna kuti zawo zokha ziyende. Masiku ano, dzikoli silili pamtendere makamaka chifukwa choti anthu ambiri ndi “odzikonda, . . . opanda chikondi chachibadwa.” (2 Timoteyo 3:2, 3) Anthu ena akakhumudwitsidwa kapena ena akapanda kuvomereza maganizo awo, ‘amapsa mtima, amakwiya, amalalata ndiponso amanena mawu achipongwe.’ (Aefeso 4:31) Izi sizibweretsa mtendere wa mumtima koma ‘zimangoputa makani.’​—Miyambo 15:18.

Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene amamvera lamulo la Mulungu lokonda anansi awo monga amadzikondera okha, amakhala “okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.” (Aefeso 4:32; Akolose 3:13) Ngakhale ena atapanda kuwakomera mtima, iwo amayesetsa kutsanzira Yesu amene pochitiridwa chipongwe “sanabwezere zachipongwe.” (1 Petulo 2:23) Mofanana ndi Yesu, amadziwa kuti kutumikira ena n’kosangalatsa, ngakhale kuchitira anthu amene sangayamikire n’komwe. (Mateyo 20:25-28; Yohane 13:14, 15; Machitidwe 20:35) Yehova Mulungu amapereka mzimu wake woyera kwa anthu amene amatsanzira Mwana wake, ndipo mzimu umenewu umawathandiza kukhala pamtendere weniweni.​—Agalatiya 5:22.

Komabe, kodi mmene inuyo mumaonera za m’tsogolo zimakhudza bwanji mtendere wanu wa mumtima?

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Munthu afunika kudziwa bwinobwino cholinga cha moyo

[Chithunzi patsamba 7]

Yesu amatiphunzitsa mmene tingapezere mtendere wa mumtima