Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Azimayi Khalani ndi Moyo Wosangalala

Azimayi Khalani ndi Moyo Wosangalala

 Azimayi Khalani ndi Moyo Wosangalala

MASIKU ano, padziko lonse azimayi ambiri ali pantchito. M’mayiko olemera, chiwerengero cha azimayi amene ali pantchito chatsala pang’ono kufanana ndi cha azibambo. Ndipo m’mayiko osauka, nthawi zambiri azimayi amagwira ntchito zakumunda kwa maola ochuluka kuti athandize mabanja awo.

Azimayi ambiri amagwira ntchito komanso amafunika kusamalira banja lawo ndi kugwira ntchito za pakhomo. Azimayi amenewa amayenera kupeza ndalama zoti agulire chakudya, zovala, apeze malo ogona komanso amafunika kuphika, kuchapa ndi kusamalira pa nyumba.

Ndipo azimayi achikhristu amafunikanso kuphunzitsa ana awo zinthu zauzimu. Cristina yemwe ali ndi ana aang’ono awiri anati: “Kunena zoona, kugwira ntchito komanso kusamalira banja n’kovuta makamaka ngati munthu uli ndi ana aang’ono. Zimakhala zovuta kwambiri kuwasamalira mokwanira.”

N’chifukwa chiyani azimayi ambiri ali pantchito? Kodi iwo amakumana ndi mavuto otani? Nanga kuti mzimayi akhale wosangalala, kodi zimadalira kuti akhale pantchito?

Chifukwa Chake Azimayi Amagwira Ntchito

Azimayi ambiri n’ngofunikadi kugwira ntchito chifukwa cha mmene zinthu zilili pamoyo wawo. Ena alibe mwamuna woti azipezera banjalo ndalama. Mabanja ena amaona kuti ndalama za munthu mmodzi sizokwanira kusamalirira banjalo.

Koma si azimayi onse amene amagwira ntchito chifukwa cha mavuto azachuma. Azimayi ambiri ndithu amagwira ntchito pofuna kuti anthu aziwalemekeza. Ena amagwira ntchito kuti azikhala ndi ndalama zawozawo kapena kuti azigula zofuna zawo. Ena amangogwira ntchitoyo chifukwa choti amaidziwa bwino komanso amaikonda.

Azimayi ena amagwira ntchito chifukwa chotsanzira anzawo. Ngakhale kuti anthu ambiri amadziwa kuti azimayi apantchito amatopa kwambiri, iwo nthawi zambiri sawamvetsetsa ndipo amawanyoza azimayi amene sali pantchito. Mayi wina ananena mosabisa kuti: “N’zovuta kufotokozera anthu ena chifukwa chake suli pantchito. Zimene anthu ena amanena ngakhalenso zochita zawo zimachita kusonyezeratu kuti akukunena kuti ‘ukungowonongeka.’” Mzimayi winanso  dzina lake Rebeca yemwe ali ndi mwana wa zaka ziwiri anati: “Ngakhale kuti anthu masiku ano amadziwa kuti azimayi ayenera kusamalira ana awo pakhomo, ndimaona kuti anthuwa amaona azimayi amene sali pantchito kuti ndi otsika.”

Kodi Zoona Zake N’ziti?

M’madera ena padziko lapansili, ofalitsa nkhani amasonyeza kuti “mzimayi weniweni” ndi amene ali pantchito yapamwamba, yamalipiro bwino, wodziwa kutchena ndiponso wodzidalira. Ndi amene amati akangofika panyumba, amatha kuthana ndi vuto lililonse limene ana ake ali nalo, kuthandiza mwamuna wake pazinthu zimene walakwitsa ndiponso kuthana ndi mavuto onse apanyumba. Koma zoona zake n’zakuti, ndi azimayi ochepa chabe amene angakhaledi ndi moyo wotere.

Kunena zoona, ntchito zambiri zimene azimayi amagwira n’zonyozeka ndiponso n’zamalipiro ochepa. Ndipo nthawi zambiri azimayi amenewa amakhumudwa chifukwa ntchito zawozo sizimawapatsa mpata wogwiritsa ntchito mokwanira luso lawo. Buku lina lonena za moyo wa anthu (Social Psychology) limati: “Ngakhale kuti anthu masiku ano akulimbikitsa kuti pasakhale kusiyana pakati pa amuna ndi akazi, azibambo ndi amene amapeza ntchito zapamwamba ndiponso za malipiro abwino. Azimayi amene amaganiza kuti azilemekezedwa akakhala pantchito, nthawi zambiri amakhumudwa.” Nyuzipepala ina ya ku Spain (El País) inati: “Ponena za azimayi, kwapezeka kuti iwo ndi amene amavutika kwambiri maganizo poyerekeza ndi azibambo chifukwa ambiri mwa azimayi amene ali pantchito amafunikanso kugwira ntchito zapakhomo.”

Zimene Amuna Angachite Kuti Athandize Azimayi

Kunena zoona, mayi wachikhristu ayenera kusankha yekha kugwira ntchito kapena ayi. Komabe, ngati ndi wokwatiwa, iye ndi mwamuna wake ayenera kusankha zochita atakambirana bwinobwino nkhaniyi.​—Miyambo 14:15.

Nanga bwanji ngati banjalo litaganiza kuti chifukwa cha mavuto azachuma amene ali nawo, onse afunika kugwira ntchito? Ngati zili choncho mwamuna wanzeru adzaganizira mfundo ya m’Baibulo iyi: “Inunso amuna, pitirizani kukhala nawo mowadziwa bwino, kupatsa ulemu mkazi monga chiwiya chosalimba, kuti mapemphero anu asatsekerezedwe, pakutinso mudzalandira nawo limodzi mphatso yachisomo ya moyo.” (1 Petulo 3:7) Mwamuna angasonyeze kulemekeza mkazi wake mwakuchita zinthu mom’ganizira pozindikira kuti nayenso amatopa. Ngati n’kotheka, mwamuna angathandize mkazi wake ntchito za pakhomo. Mofanana ndi Yesu, mwamuna angazipereke kugwira ntchito zing’onozing’ono ngakhale zimene zikuoneka ngati zochititsa manyazi. (Yohane 13:12-15) M’malo mwake, mwamunayo angaone kuti umenewu ndi mwayi wake wosonyeza kuti amam’konda mkazi wake. Ndipo mkaziyo adzayamikira kwambiri zimenezi.​—Aefeso 5:25, 28, 29.

Mosakayikira, m’pofunika kuchita zinthu mogwirizana ngati onse awiri mwamuna ndi mkazi ali pantchito. Nyuzipepala ina ya ku Spain (ABC) inatsindika mfundo imeneyi pakafukufuku amene bungwe lina loona nkhani za m’banja (Institute of Family Matters) linachita. Nyuzipepalayi inanena kuti mabanja ambiri ku Spain akutha osati kokha chifukwa choti “anthu sapembedza kapena alibe makhalidwe abwino,” koma chifukwanso cha mfundo ziwiri izi: “Kugwira ntchito kwa azimayi komanso chifukwa chakuti amuna sathandiza akazi awo ntchito za pakhomo.”

Udindo Wofunika Kwambiri wa Azimayi Achikhristu

Ngakhale kuti Yehova anapatsa azibambo udindo waukulu wophunzitsa ana awo, azimayi achikhristu amadziwa kuti nawonso ali ndi udindo waukulu, makamaka mwanayo akakhala wakhanda. (Miyambo 1:8; Aefeso 6:4) Yehova ankauza azimayi ndi azibambo omwe pamene ankapereka malangizo kwa Aisiraeli kuti aziphunzitsa ana awo Chilamulo. Iye anadziwa kuti kuphunzitsa ana kumafuna nthawi ndiponso kuleza mtima makamaka ana akamakula.  Choncho Mulungu anauza makolo kuti afunika kuphunzitsa ana awo kunyumba, poyenda mu msewu, podzuka ndiponso pogona.​—Deuteronomo 6:4-7.

Baibulo limanena motsindika kufunika kwa udindo umene azimayi ali nawo chifukwa limalamula ana kuti: ‘Usasiye malamulo a amayi ako.’ (Miyambo 6:20) Koma, mayi wokwatiwa ayenera kukambirana ndi mwamuna wake asanakhazikitse lamulo lililonse kwa ana ake. Komabe, vesili likusonyeza kuti azimayi ali ndi udindo wopanga malamulo. Ndipo ana amene amamvera zimene amayi awo owopa Mulungu amawaphunzitsa pankhani zauzimu ndi zamakhalidwe abwino, amapindula kwambiri. (Miyambo 6:21, 22) Mayi wina wa ana awiri dzina lake Teresa analongosola chifukwa chake salowa ntchito. Iye anati: “Ntchito yaikulu imene ndili nayo ndi yophunzitsa ana anga kutumikira Mulungu. Ndikufuna kuigwira bwino ntchito imeneyi.”

Azimayi Amene Anachita Bwino

N’zoonekeratu kuti Lemueli mfumu ya Isiraeli anapindula kwambiri ndi khama la amayi ake. “Uthenga” umene amayi ake “anam’phunzitsa” wakhala mbali ya Mawu a Mulungu ouziridwa. (Miyambo 31:1; 2 Timoteyo 3:16) Zimene amayi akewa ananena pofotokoza mkazi wabwino zimathandiza ana amuna kusankha bwino mkazi womanga naye banja. Komanso malangizo okhudza nkhani ya chiwerewere ndiponso kumwetsa mowa ndi othandiza kwambiri masiku ano monga analili panthawi imene ankalembedwa.​—Miyambo 31:3-5, 10-31.

M’nthawi ya Akhristu oyambirira, mtumwi Paulo anayamikira mayi wina wotchedwa Yunike chifukwa cha ntchito yabwino imene anaigwira pophunzitsa mwana wake Timoteyo. Popeza mwamuna wake sanali wolambira Yehova koma mwina ankalambira milungu yachigiriki, Yunike anafunika kuphunzitsa Timoteyo kuti akhulupirire “malemba opatulika.” Kodi Yunike anayamba liti kuphunzitsa Timoteyo Malemba? Nkhani ya m’Baibulo imati “kuyambira pamene [anali] wakhanda.” (2 Timoteyo 1:5; 3:14, 15) Mwachionekere Timoteyo anakonzekera ntchito ya umishonale chifukwa choti amayi ake anali okhulupirika, achitsanzo chabwino ndiponso ankamuphunzitsa.​—Afilipi 2:19-22.

Baibulo limanenanso za azimayi ena amene anali ochereza atumiki okhulupirika a Mulungu ndipo zimenezi zinathandiza ana awo kutsanzira atumikiwo. Mwachitsanzo, nthawi ndi nthawi mzimayi wina wa ku Sunemu ankalandira mneneri Elisa kunyumba kwake. Kenaka mwana wake atamwalira anaukitsidwa ndi Elisa. (2 Mafumu 4:8-10, 32-37) Taonaninso chitsanzo cha Mariya, mayi ake a Maliko yemwe analemba nawo Baibulo. Zikuoneka kuti iye anapereka nyumba yake ku Yerusalemu kuti ophunzira azichitiramo misonkhano. (Machitidwe 12:12) N’zosakayikitsa kuti kucheza ndi ophunzira komanso Akhristu ena amene amabwera nthawi zonse kunyumbako kunam’thandiza kwambiri Maliko.

Ndithudi, Yehova amayamikira kwambiri khama la azimayi okhulupirika amene amayesetsa kuphunzitsa ana awo mfundo za m’Baibulo. Iye amawakonda kwambiri azimayiwa chifukwa cha kukhulupirika kwawo ndi kuyesetsa kwawo kuphunzitsa zinthu zauzimu panyumba.​—2 Samueli 22:26; Miyambo 14:1.

Ntchito Yosangalatsa Kwambiri

Malemba amene takambiranawo akusonyeza kuti kusamalira bwino banja mwa kuthupi, mwauzimu ndi mwamaganizo kuli ndi madalitso apadera. Koma kuchita zimenezi si ntchito ya masewera. Ntchito imene azimayi amagwira pakhomo nthawi zambiri imakhala yolemetsa kwambiri kuposa ntchito ya munthu amene ali ndi udindo wapamwamba uliwonse pakampani.

Ndithudi, ngati mayi wakambirana ndi mwamuna wake ndipo waona kuti asiye ntchito kapena azingogwira ganyu, banjalo lingafunike kukhala moyo wosalira zambiri. Angafunikenso kupirira kunyozedwa ndi anthu ena amene sangamvetse chifukwa chake wachitira zimenezi. Koma zimenezi n’zimene zili zopindulitsa kwambiri. Mzimayi wina wa ana atatu dzina lake Paqui anasankha kumangogwira maganyu basi. Iye anati: “Ndimafuna kuti ndizikhala ndili  pakhomo ana anga akamachokera ku sukulu kuti azipeza wolankhula naye.” Kodi zimenezi zathandiza bwanji ana ake? Iye anapitiriza kuti: “Ndimawathandiza pa ntchito yawo ya kusukulu, ndipo pakakhala vuto ndimawathandiza nthawi yomweyo. Timalankhulana bwino chifukwa timachezera limodzi tsiku lililonse. Ndinakana kulowa ntchito chifukwa ndimasangalala kwambiri kukhala ndi ana anga.”

Azimayi ambiri achikhristu aona kuti ngati asiya ntchito n’kumangogwira maganyu n’cholinga choti azikhala nthawi yaitali panyumba, anthu onse m’banjamo amasangalala. Cristina yemwe tam’tchula kale uja anati: “Nditasiya ntchito ndinaona kuti banja lathu linkayenda bwino kwambiri kuposa kale. Ndimakhala ndi nthawi yocheza ndi ana anga ndiponso yothandiza mwamuna wanga m’njira zina zambiri. Ndinayamba kukonda kuphunzitsa ana anga ndipo ndimasangalala kuwaona akuchita bwino pa zimene ndikuwaphunzitsazo.” Koma Cristina amakumbukira bwino chinthu china chapadera kwambiri. Iye anapitiriza kuti: “Mwana wanga woyamba anaphunzira kuyenda ali ku sukulu yosamalira ana, koma mwana wanga wachiwiri ndinam’phunzitsa ndekha kuyenda kunyumba kwathu. Ndinasangalala kwambiri nthawi imene mwana wanga anayamba kuponya mwendo kenako ndinamuwakha atatsala pang’ono kugwa.”

Mfundo inanso yofunika kuiganizira ndiyoti nthawi zambiri banja silikhala ndi mavuto azachuma amene banjalo lingaganize kuti lidzakhala nawo ngati mayi asiya ntchito kapena akungogwira maganyu. Cristina uja anafotokoza kuti: “Malipiro anga ankatha ndi kulipirira kusukulu yosamalira ana ndiponso thiransipoti yokawatenga ndi kukawasiya anawa kusukuluko. Koma titaunika bwinobwino zimenezi, tinaona kuti ntchito yanga si inkabweretsa ndalama zowonjezereka panyumba.”

Mabanja ena ataona bwinobwino moyo wawo, apeza kuti mayi akamakhala pa khomo nthawi zonse banjalo limapindula kwambiri kuposa mayiyo akakhala pantchito. Ndipo mwamuna wa Cristina, dzina lake Paul anati: “Ndimasangalala kwambiri chifukwa mkazi wanga amakhala panyumba n’kumasamalira ana athu aang’ono awiri. Koma poyamba zinali zovuta kwambiri pamene tonse tinkagwira ntchito.” Kodi zimenezi zathandiza bwanji ana awowo? Paul anapitiriza kuti: “Sikuti anawo amangoona kuti akukondedwa basi, koma amaonanso kuti ndi otetezeka kwambiri ku makhalidwe oipa.” N’chifukwa chiyani banjali linaona kuti lifunika kumakhala ndi nthawi yochuluka pamodzi ndi ana awo? Paul anayankha kuti: “Ndikukhulupirira kuti makolofe tikamapanda kuphunzitsa ana athu, ndiye kuti winawake adzawaphunzitsa.”

Zoonadi, banja lililonse liyenera kupenda bwinobwino mmene zinthu zilili pamoyo wawo ndipo munthu wina asanyoze zimene mabanja ena asankha kuchita pankhaniyi. (Aroma 14:4; 1 Atesalonika 4:11) Komabe, ndi bwino kuganizira madalitso ambiri amene banja limakhala nawo ngati mzimayi sali pantchito kapena amangogwira ganyu. Ponena mwachidule maganizo ake pankhani imeneyi, Teresa amene tam’tchula kale uja anati: “Palibe chinthu chimene chimasangalatsa kwambiri kuposa kukhala ndi nthawi yochuluka yosamalira ndi kuphunzitsa ana akoako.”​—Salmo 127:3.

[Chithunzi patsamba 31]

Azimayi achikhristu amathandiza pantchito yofunika kwambiri yophunzitsa ana awo