Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chimene Anthu Ambiri Akupempha Padziko Lonse

Chimene Anthu Ambiri Akupempha Padziko Lonse

 Chimene Anthu Ambiri Akupempha Padziko Lonse

TAGANIZIRANI anthu mamiliyoni kapena mabiliyoni onse akupempha chinthu chofanana. Ndipo iwo akupempha chinthu chimenechi kwa yemwe ali ndi mphamvu kwambiri kuposa aliyense m’chilengedwe chonse. Komano ndi anthu ochepa kwambiri amene akudziwa chimene akupemphacho. Kodi zimenezi zingathekedi? Ee, n’zotheka ndipo n’zimene zikuchitika tsiku lililonse. Kodi anthu onsewa akupempha chiyani? Akupempha kuti Ufumu wa Mulungu ubwere.

Malinga ndi zimene ofufuza ena apeza, akuti padziko lonse pali zipembedzo pafupifupi 37,000 zachikhristu, ndipo anthu ake amati Mtsogoleri wawo ndi Yesu Khristu. Zipembedzo zimenezi zili ndi anthu opitirira 2 biliyoni. Ndipo ochuluka mwa anthu amenewa amapemphera pemphero limene kawirikawiri limatchedwa Pemphero la Atate Wathu kapena Pemphero la Ambuye. Kodi inuyo mumalidziwa pemphero limeneli? Monga mmene Yesu anaphunzitsira otsatira ake, pempheroli limayamba motere: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.”​—Mateyo 6:9, 10.

Ngakhale kuti papita zaka zambirimbiri, anthu akupempherabe mobwerezabwereza mawu amenewa m’matchalitchi awo. Amatchula mawu amenewa pamtima mobwerezabwereza popemphera m’mabanja awo, aliyense payekha, pa zisangalalo ndi pamavuto pomwe. Amatchulanso mawu amenewa ndi mtima wawo wonse ndipo ena ambiri aloweza mawu amenewa pa mtima ndipo amawanena mosaikirapo mtima n’komwe. Koma si anthu a Matchalitchi Achikhristu okhawa amene amafuna ndiponso kupempha kuti Ufumu wa Mulungu ubwere.

Chimene Anthu a Zipembedzo Zosiyanasiyana Akupempha

Anthu a chipembedzo chachiyuda ali ndi pemphero lawo la pamaliro lodziwika bwino, ngakhale kuti silimanena kwenikweni za imfa kapena chisoni. Pempheroli limati: “[Mulungu] abweretse Ufumu wake m’moyo wathu . . . mwamsanga.” * Pemphero  linanso lakale la m’sunagoge limatchula za chiyembekezo cha Ufumu wa Mesiya wochokera m’nyumba ya Davide.

Anthu enanso omwe si Akhristu akusangalala ndi nkhani ya Ufumu wa Mulungu. Malinga ndi nyuzipepala ina (ya The Times of India), mtsogoleri wotchuka wa chipembedzo china ku India wa m’zaka za m’ma 1800 amene ankafunitsitsa kugwirizanitsa Ahindu, Asilamu ndi Akhristu anati: “Ufumu weniweni wa Mulungu udzabwera pokhapokha ngati anthu azipembedzo za m’mayiko a kum’mawa ndi a ku madzulo atagwirizana.” Ndipo posachedwapa mphunzitsi wamkulu pa koleji ina ya Asilamu ku Strathfield, m’dziko la Australia anauza nyuzipepala ina kuti: “Mofanana ndi Asilamu onse, ndimakhulupirira kuti Yesu adzabweranso kudzakhazikitsa Ufumu weniweni wa Mulungu.”

Mosakayikira, pali anthu mabiliyoni ambiri amene amafuna ndiponso amapempha Ufumu wa Mulungu. Koma taonani mfundo yosangalatsa iyi.

Sitikukayika kuti mukudziwa kuti ife a Mboni za Yehova, amene timafalitsa magazini ino, timapita ku nyumba ndi nyumba m’dera lanu n’kumakambirana ndi anthu za m’Baibulo. Tikunena pano, tikugwira ntchito imeneyi m’mayiko oposa 236 m’zinenero zoposa 400. Nkhani yaikulu pa ntchito yathu yolalikira ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipotu, mutu wonse wa magazini ino ndi wakuti Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Nthawi zambiri timawafunsa anthu ngati amapempha Ufumu umenewu ndipo ambiri amati amapempha. Komabe, tikawafunsa kuti kodi Ufumu umenewu n’chiyani, ambiri amati “kaya, sindikudziwa,” kapena yankho lake limakhala losamveka ndiponso longokayikira.

Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri amapempha chinthu chimene sakuchidziwa n’komwe? Kodi n’chifukwa chakuti nkhani yokhudza Ufumu wa Mulungu ndi yovuta ndiponso yosamvetsetseka? Ayi sichoncho. Nkhani ya Ufumu yafotokozedwa bwino kwambiri ndiponso momveka bwino m’Baibulo. Komanso, uthenga wa m’Baibulo wonena za Ufumu ungakupatseni chiyembekezo chenicheni m’masiku ovuta ano. M’nkhani yotsatirayi tiona zimene Baibulo limalongosola ponena za chiyembekezo chimenechi. Ndiyeno tionanso kuti pemphero la Yesu loti Ufumu ubwere lidzayankhidwa liti.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mofanana ndi pemphero lachitsanzo la Yesu, pemphero la pamaliro lachiyudali limanenanso kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. Ngakhale kuti pali kusiyana maganizo pankhani yoti pempheroli linayamba mu nthawi ya Khristu kapena n’lakale kwambiri kuposa nthawi imeneyi, koma sitiyenera kudabwa kuti mbali zina za mapempherowa zikufanana. Yesu sanapereke pemphero lake lija ndi cholinga chakuti aphunzitse mfundo zatsopano. Mfundo iliyonse ya m’pempheroli inali yogwirizana kwambiri ndi Malemba amene Ayuda onse anali nawo panthawiyo. Yesu ankalimbikitsa Ayuda anzake kupempha zinthu zimene iwo ankapempha nthawi zonse.