Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Yehova?

Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Yehova?

“Timasonyeza chikondi, chifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.”—1 YOH. 4:19.

NYIMBO: 56, 138

1, 2. Kodi Yehova watithandiza bwanji kuti tizimukonda?

ANA amaphunzira zambiri poona zimene bambo awo amachita. Choncho bambo akamasonyeza chikondi, anawo amaphunzira kukhala achikondi. Ndiyeno mtumwi Yohane analemba kuti: “Timasonyeza chikondi, chifukwa [Mulungu] ndi amene anayamba kutikonda.” (1 Yoh. 4:19) Atate wathu wakumwamba amatisonyeza chikondi m’njira zambiri ndipo izi zimatilimbikitsa kumukonda.

2 N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mulungu ndi amene “anayamba kutikonda”? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:8) Munthu wachikondi chenicheni amadzipereka kwambiri, mwinanso kufika povutika kuti athandize anzake. Choncho tinganene kuti Yehova anasonyeza chikondi chosaneneka popereka Mwana wake kuti awombole anthu okhulupirika. Zimene anachitazi zinathandiza kuti anthufe tigwirizane naye ndiponso kuti tizimukonda.—1 Yoh. 4:10.

3, 4. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova?

3 Khalidwe lalikulu kwambiri la Yehova ndi chikondi. M’pake kuti Yesu ananena kuti lamulo lalikulu ndi lakuti: “Uzikonda  Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Yehova amasangalala kwambiri tikamamukonda ndi ‘mtima wathu wonse.’ Koma kukonda Yehova kumatanthauza zambiri osati mmene timamvera mumtima basi. Paja Yesu ananenanso kuti tiyenera kukonda Mulungu ndi moyo wathu wonse, maganizo athu onse ndiponso mphamvu zathu zonse. Zimene mneneri Mika analemba zimatsimikizira mfundo imeneyi.—Werengani Mika 6:8.

4 Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda kwambiri Yehova? Tiyenera kutsatira zimene Yesu ananena n’kumakonda Mulungu ndi zonse zimene tili nazo ndiponso mopanda malire. M’nkhani yapita ija tinaona njira zinayi zimene Yehova watisonyezera chikondi. Tsopano tiyeni tikambirane zimene tingachite kuti tizimukonda kwambiri komanso mmene tingasonyezere chikondicho.

TIZIYAMIKIRA ZIMENE YEHOVA AMATIPATSA

5. Tikaganizira zonse zimene Yehova watipatsa, kodi timafuna kuchita chiyani?

5 Kodi mukalandira mphatso mumachita chiyani? Muyenera kuti mumayamikira komanso kuigwiritsa ntchito bwino. Pa nkhani ya mphatso, mtumwi Yakobo anati: “Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, pakuti imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zonse zakuthambo, ndipo iye sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.” (Yak. 1:17) Nthawi zonse Yehova amatipatsa zinthu zofunika kuti tizikhala ndi moyo komanso kuti tizisangalala. Zimenezi zimatilimbikitsa kuti nafenso tizimukonda.

6. Kodi Aisiraeli ankayenera kuchita chiyani kuti Yehova aziwadalitsabe?

6 Kwa zaka zambiri, Yehova ankasamalira ndiponso kudalitsa Aisiraeli. (Deut. 4:7, 8) Koma iwo ankayenera kumvera Chilamulo cha Mulungu kuti azidalitsidwabe. Mwachitsanzo, ankayenera kupereka kwa Yehova “zipatso zoyamba kucha zabwino koposa.” (Eks. 23:19) Akamachita zimenezi ankasonyeza kuti amayamikira kwambiri chikondi cha Yehova komanso madalitso ake.—Werengani Deuteronomo 8:7-11.

7. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji ‘zinthu zathu zamtengo wapatali’ posonyeza kuti timakonda Yehova?

7 Ifenso tiyenera kusonyeza kuti timakonda Yehova pomupatsa ‘zinthu zathu zamtengo wapatali.’ (Miy. 3:9) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tikhoza kupereka chuma chathu kuti chithandize pa ntchito yolalikira m’dziko lathu kapena padziko lonse. Kaya timapereka zambiri kapena zochepa, timasonyezabe kuti timakonda Yehova. (2 Akor. 8:12) Koma pali njira zinanso zosonyezera kuti timamukonda.

8, 9. Kodi kukhulupirira lonjezo la Yehova kumasonyeza bwanji kuti timamukonda? Perekani chitsanzo.

8 Kumbukirani kuti Yesu ananena kuti tisamade nkhawa za chakudya kapena zovala koma tiziika patsogolo Ufumu. Paja Atate wathu wakumwamba analonjeza kuti azitipatsa zinthu zofunika pa moyo. (Mat. 6:31-33) Tikamakhulupirira kwambiri lonjezo limeneli timasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova. Tikutero chifukwa chakuti munthu sangakonde mnzake amene samukhulupirira. (Sal. 143:8) Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zolinga ndiponso zochita zanga zimasonyeza kuti ndimakondadi Yehova? Kodi zimene ndimachita tsiku lililonse zimasonyeza kuti ndimakhulupirira zoti Yehova adzandisamalira?’

9 M’bale wina dzina lake Mike ndi chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye ali wachinyamata  ankafunitsitsa kukatumikira Mulungu kudziko lina. Kenako anakwatira n’kukhala ndi ana awiri koma sanasinthe cholinga chakecho. Mike ndi banja lake analimbikitsidwa kwambiri ndi nkhani zokhudza kukatumikira kumene kulibe ofalitsa okwanira. Iwo anasankha zokhala ndi moyo wosalira zambiri ndipo anagulitsa nyumba yawo yaikulu n’kumakakhala m’nyumba yaing’ono. Kenako anachepetsa ntchito pakampani yake. Anaphunziranso zimene angachite kuti aziyendetsabe kampaniyo pogwiritsa ntchito Intaneti ali m’dziko lina. Ndiyeno iye ndi banja lake anasamukira kudziko lina. Atatumikira kumeneko kwa zaka ziwiri, Mike anati: “Taonadi kuti mawu a Yesu pa Mateyu 6:33 ndi oona.”

TIZIYAMIKIRA ZIMENE YEHOVA AMATIPHUNZITSA

10. Malinga ndi zimene zinachitikira Davide, kodi kuganizira kwambiri za Yehova kungatithandize bwanji?

10 Zaka zoposa 3,000 zapitazo, Mfumu Davide anachita chidwi kwambiri ndi zimene anaona kumwamba. Iye analemba kuti: “Zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu. Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.” Iye ataona kuti malamulo a Yehova ndi othandiza kwambiri, ananenanso kuti: “Chilamulo cha Yehova ndi changwiro, chimabwezeretsa moyo. Zikumbutso za Yehova ndi zodalirika, zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.” Pambuyo poganizira zonsezi, Davide anati: “Mawu a pakamwa panga ndi kusinkhasinkha kwa mtima wanga, zikukondweretseni, inu Yehova, Thanthwe langa ndi Wondiwombola.” Mfundo zimene Davide ananenazi zikusonyeza kuti ankagwirizana kwambiri ndi Mulungu.—Sal. 19:1, 7, 14.

11. Kodi kukonda Yehova kungatilimbikitse kuchita chiyani ndi zinthu zamtengo wapatali zimene watiphunzitsa? (Onani chithunzi patsamba 23.)

11 Masiku ano, timadziwa zinthu zambiri zimene Yehova analenga komanso zimene akuchita pokwaniritsa cholinga chake. Anthu m’dzikoli amalimbikitsa maphunziro apamwamba. Koma pali umboni wosonyeza kuti nthawi zambiri maphunzirowo amachititsa anthu kusiya kukonda Mulungu ndiponso kumukhulupirira. N’zoona kuti Yehova amafuna kuti tidziwe zinthu koma amatiuzanso kuti tipeze nzeru ndi luso lomvetsa zinthu. Iye amafuna kuti tizigwiritsa ntchito zimene watiphunzitsa m’njira yoti zitithandize komanso zithandize anthu ena. (Miy. 4:5-7) Cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Tikamachita khama kwambiri pouza anthu za Ufumu wa Mulungu komanso zolinga zake, timasonyeza kuti timakonda Yehova.—Werengani Salimo 66:16, 17.

12. Kodi mtsikana wina ananena zotani poyamikira Yehova?

12 Nawonso achinyamata akhoza kusonyeza kuti amakonda Yehova n’kumayamikira zimene amatiphunzitsa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Shannon. Iye ali ndi zaka 11 anapita ku msonkhano wachigawo wa mutu wakuti, “Kudzipereka Kwaumulungu.” Anapita limodzi ndi makolo ake komanso mng’ono wake wazaka 10. Ndiyeno pa nthawi ina msonkhano uli mkati, achinyamata onse anauzidwa kuti akakhale pamalo enaake. Iye anachita mantha koma anapitabe. Kenako anadabwa kuona kuti aliyense anapatsidwa buku lakuti, Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Kodi Shannon anamva bwanji atalandira bukuli? Iye anati: “Apa ndinazindikira kuti  Yehova alikodi ndipo amandikonda kwambiri ineyo pandekha.” Shannon anapitiriza kuti: “Anthufe tili ndi mwayi waukulu chifukwa chakuti Yehova Mulungu amatipatsa mphatso zamtengo wapatali.”

TIZIMVERA MALANGIZO A YEHOVA

13, 14. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikalandira malangizo ochokera kwa Yehova, ndipo n’chiyani chingatithandize pa nkhaniyi?

13 Baibulo limanena kuti: “Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda, monga momwe bambo amadzudzulira mwana amene amakondwera naye.” (Miy. 3:12) Ndiyeno kodi tiyenera kuchita chiyani tikalandira malangizo? Mtumwi Paulo ananena zoona pamene analemba kuti: “Zoonadi, palibe chilango chimene chimamveka chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa.” Ponena zimenezi sikuti ankatanthauza kuti chilango si chabwino chifukwa anapitiriza kuti: “Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere, chomwe ndi chilungamo.” (Aheb. 12:11) Ngati timakonda Yehova tidzapewa kunyalanyaza malangizo ake kapena kunyansidwa nawo. Nthawi zina kulandira malangizo kungakhale kovuta koma kukonda Yehova kungatithandize kukhala omvera.

14 M’nthawi ya Malaki, Ayuda ambiri sankamvera malangizo a Mulungu. Iwo ankadziwa lamulo lokhudza nsembe koma ankalinyalanyaza kwambiri moti Yehova anawadzudzula mwamphamvu. (Werengani Malaki 1:12, 13.) Kodi nkhaniyi inali yaikulu bwanji? Yehova anawauza kuti: “Ndidzakutumizirani temberero ndi kutemberera madalitso anu. Ndatemberera dalitso la aliyense wa inu chifukwa simunaganizire [lamulo langa] mumtima mwanu.” (Mal. 2:1, 2) Nkhaniyi ikusonyeza kuti pamakhala mavuto aakulu ngati munthu amanyalanyaza malangizo a Yehova.

Tizitsatira malangizo a Mulungu osati maganizo a anthu a m’dzikoli (Onani ndime 15)

15. Kodi tiyenera kupewa makhalidwe ati amene afala m’dzikoli?

15 Anthu ambiri masiku ano ndi odzikonda  ndipo safuna kuuzidwa zochita kapena kupatsidwa malangizo. Ngakhale anthu amene amalandira malangizo, amachita zimenezi monyinyirika. Koma Akhristufe timalangizidwa kuti tipewe kutengera “nzeru za nthawi ino.” M’malomwake tiyenera kuzindikira ndiponso kuchita zimene Mulungu amafuna. (Aroma 12:2) Gulu la Yehova limatipatsa malangizo pa nkhani zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, limatipatsa malangizo okhudza zosangalatsa, anthu amene timacheza nawo komanso mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu amene si amuna kapena akazi anzathu. Tikamatsatira malangizo amenewa ndi mtima wonse timasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova ndiponso timayamikira malangizo ake.—Yoh. 14:31; Aroma 6:17.

TIZIDALIRA YEHOVA KUTI AZITITETEZA NDIPONSO KUTIPULUMUTSA

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira zimene Yehova amafuna tisanasankhe zochita? (b) Kodi Aisiraeli anasonyeza bwanji kuti sankakonda kwenikweni Yehova komanso sankamudalira?

16 Ana akaona zinthu zochititsa mantha amathawira kwa makolo awo. Koma akamakula amayamba kudzidalira. Ngakhale zili choncho, ana amene amagwirizana kwambiri ndi makolo awo amakondabe kufunsa nzeru kwa makolowo asanasankhe zochita. N’chimodzimodzi anthufe ndi Yehova. Iye amalola kuti tizisankha tokha zochita, komabe tikamamukonda timaganizira zimene iye amafuna tisanasankhe zochitazo. Tikamamudalira adzatitsogolera ndi mzimu wake woyera.—Afil. 2:13.

17 Pa nthawi ya mneneri Samueli, Aisiraeli anagonjetsedwa ndi Afilisiti ndipo ankafunikira kwambiri thandizo la Yehova. Zitatero, Aisiraeliwo anati: “Tiyeni tikatenge likasa la pangano la Yehova ku Silo, kuti likhale pakati pathu ndi kutipulumutsa m’manja mwa adani athu.” Koma atachita zimenezi “panaphedwa amuna oyenda pansi a Isiraeli okwanira 30,000. Ngakhalenso likasa la Mulungu linalandidwa.” (1 Sam. 4:2-4, 10, 11) Mwina tingaganize kuti Aisiraeliwo ankadalira Yehova chifukwa chakuti anatenga Likasa pokamenyana ndi Afilisiti. Koma sanapemphe Yehova kuti awathandize. M’malomwake anatsatira nzeru zawo ndipo anakumana ndi zoopsa kwambiri.—Werengani Miyambo 14:12.

18. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kudalira Yehova?

18 Munthu wina amene analemba masalimo ankakonda kwambiri Yehova komanso kumudalira ndipo anati: “Yembekezera Mulungu, ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu. Inu Mulungu wanga, ine ndataya mtima. N’chifukwa chake ndakumbukira inu.” (Sal. 42:5, 6) Kodi inunso mumakonda kwambiri ndiponso kudalira Mulungu? N’kutheka kuti mwayankha kuti inde, koma mwina mukhoza kumudalira kwambiri kuposa mmene mumachitira panopa. Paja Baibulo limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”—Miy. 3:5, 6.

19. Kodi inuyo mudzasonyeza bwanji kuti mumakonda Yehova?

19 Yehova ndi amene anayamba kutikonda ndipo watiphunzitsa mmene tingamusonyezere chikondi. Tiyeni nthawi zonse tiziganizira chitsanzo chake pa nkhaniyi. Tiziyesetsanso kusonyeza kuti timamukonda ‘ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, maganizo athu onse ndi mphamvu zathu zonse.’—Maliko 12:30.