Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikumbumtima Chanu Chimakuthandizani Kusankha Zochita Mwanzeru?

Kodi Chikumbumtima Chanu Chimakuthandizani Kusankha Zochita Mwanzeru?

‘Cholinga chokulamulira zimenezi n’chakuti tikhale ndi chikondi chochokera mumtima woyera ndiponso m’chikumbumtima chabwino.’—1 TIM. 1:5.

NYIMBO: 57, 48

1, 2. Kodi ndi ndani amene anatipatsa chikumbumtima, nanga chimatithandiza bwanji?

POLENGA anthu, Yehova Mulungu anawapatsa ufulu woti azisankha okha zochita. Anawapatsanso chikumbumtima pofuna kuwathandiza kuti azisankha zinthu mwanzeru. Pamene tikuti chikumbumtima tikutanthauza mphamvu yachibadwa yotithandiza kuzindikira chabwino ndi choipa. Munthu akachigwiritsa ntchito bwino amachita zabwino n’kumapewa zoipa. Choncho chikumbumtima ndi umboni wakuti Yehova amatikonda ndiponso amafuna kuti anthu onse azichita zabwino mogwirizana.

2 Munthu aliyense padzikoli ali ndi chikumbumtima. (Werengani Aroma 2:14, 15.) N’chifukwa chake anthu ena amadana ndi zoipa n’kumachita zabwino ngakhale kuti sadziwa mfundo za m’Baibulo. Chikumbumtima chawo sichiwalola kuchita zinthu zimene n’zoipa kwambiri. Anthufe tikanakhala opanda chikumbumtima, dzikoli likanaipa kwambiri kuposa pamene lafikapa. Choncho timayamikira  kwambiri kuti Mulungu anatipatsa chikumbumtima.

3. Kodi chikumbumtima chingathandize bwanji kuti zinthu ziziyenda bwino mumpingo?

3 Anthu ambiri saganiza zophunzitsa chikumbumtima chawo. Koma atumiki a Yehova amafunitsitsa kuchiphunzitsa pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Amadziwa kuti kuchita zimenezi kungathandize kuti azisiyanitsa zabwino ndi zoipa komanso azigwirizana mumpingo. Koma kuti tiphunzitse chikumbumtima chathu pamafunika zambiri osati kungodziwa zimene Baibulo limanena. Tiyenera kukonda mfundo za m’Baibulo ndiponso kukhulupirira kuti n’zothandiza. Paja Paulo analemba kuti: “Cholinga chokulamulira zimenezi n’chakuti tikhale ndi chikondi chochokera mumtima woyera, m’chikumbumtima chabwino, ndiponso m’chikhulupiriro chopanda chinyengo.” (1 Tim. 1:5) Munthu akaphunzitsa chikumbumtima chake n’kumachitsatira, amayamba kukonda kwambiri Yehova ndipo chikhulupiriro chake chimalimba. Amasonyezanso kuti ali ndi mtima wabwino ndipo akufunitsitsa kusangalatsa Yehova.

4. Kodi chikumbumtima chathu tingachiphunzitse bwanji?

4 Koma kodi chikumbumtima chathu tingachiphunzitse bwanji? Tiyenera kuphunzira Baibulo nthawi zonse, kuganizira kwambiri zimene timawerenga ndiponso kupempha Yehova kuti atithandize kuzigwiritsa ntchito. Apa n’zoonekeratu kuti pamafunika zambiri osati kungowerenga kuti tidziwe malamulo ndi mfundo zina. Tiyenera kuphunzira n’cholinga choti tidziwe bwino Yehova, makhalidwe ake, zimene amakonda ndiponso zimene amadana nazo. Tikatero chikumbumtima chathu chimayamba kuzindikira mosavuta zimene Yehova amafuna. Pamapeto pake, timayamba kuona zinthu mmene iye amazionera.

5. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

5 Komano mwina tingadzifunse kuti: Kodi chikumbumtima chophunzitsidwa bwino chingatithandize bwanji kusankha zinthu mwanzeru? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza zimene ena asankha motsatira chikumbumtima chawo? Nanga chikumbumtimacho chingatilimbikitse bwanji kuchita khama pa ntchito zabwino? M’nkhaniyi tikambirana mafunso amenewa ndiponso mmene chikumbumtima chingatithandizire pa nkhani zitatu izi: (1) zaumoyo, (2) zosangalatsa ndi (3) utumiki.

TIZIKHALA OGANIZA BWINO

6. Kodi tiyenera kusankha zochita pa nkhani iti?

6 Baibulo limatilimbikitsa kupewa zinthu zimene zingawononge moyo wathu. Limatilimbikitsanso kupewa zinthu monga kudya ndi kumwa mopitirira malire. (Miy. 23:20; 2 Akor. 7:1) Kutsatira mfundo za m’Baibulo kungatithandize kukhala ndi moyo wathanzi koma sitingapeweretu kudwala kapena kukalamba. Masiku ano pali chithandizo chosiyanasiyana cha mankhwala ndipo tiyenera kusankha zochita pa nkhani imeneyi. Chifukwa cha zimenezi, m’mayiko ambiri abale ndi alongo amalemba makalata opita ku ofesi ya nthambi kuti afunse ngati ndi zoyenera kugwiritsa ntchito chithandizo chinachake cha mankhwala kapena ayi.

7. Kodi tingasankhe bwanji zochita pa nkhani ya mankhwala?

7 Abale a ku ofesi ya nthambi kapena mumpingo sangasankhire anthu zochita pa nkhani ya mankhwala. (Agal. 6:5) Ngakhale zili choncho, angauze munthuyo mfundo za Yehova zimene zingamuthandize kusankha zochita. Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amanena kuti Akhristu ayenera kupewa magazi. (Mac. 15:29) Choncho sayenera kulandira magazi athunthu kapena chimodzi mwa zigawo zake 4  zikuluzikulu. Lamuloli lingakhudzenso zimene munthu angasankhe pa nkhani ya tizigawo ting’onoting’ono ta magazi. * Koma kodi pali mfundo zinanso za m’Baibulo zimene zingatithandize kusankha bwino pa nkhani ya mankhwala?

8. Kodi lemba la 1 Atesalonika 5:6 lingatithandize bwanji kusankha zochita pa nkhani zaumoyo?

8 Lemba la Miyambo 14:15 limati: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” Pali matenda ena amene alibe mankhwala. Choncho tiyenera kusamala tikamva ena akuchemerera mankhwala enaake koma alibe umboni woti ndi othandizadi. Paulo analemba kuti: “Tikhalebe oganiza bwino.” (1 Ates. 5:6) Kuganiza bwino kungatithandizenso kuti tisamangoganizira za thanzi lathu mpaka kufika poiwala zinthu zina zokhudza kulambira Yehova. Tikayamba kuganizira kwambiri za thanzi lathu tikhoza kusiyanso kuganizira zofuna za ena. (Afil. 2:4) Tisamaiwale kuti m’dzikoli sitingapeweretu matenda. Tizikumbukiranso kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.—Werengani Afilipi 1:10.

Kodi timakakamiza ena kutsatira maganizo athu? (Onani ndime 9)

9. Kodi lemba la Aroma 14:13, 19 lingatithandize bwanji kuti tisasokoneze mgwirizano mumpingo?

9 Mkhristu woganiza bwino sangakakamize anthu kutsatira maganizo ake. Mwachitsanzo, banja lina ku Europe linkalimbikitsa kwambiri anthu kugwiritsa ntchito mankhwala enaake ndiponso zakudya zinazake. Ndiyeno abale ena mumpingo anayamba kuwamvera koma ena anakana. Koma patapita nthawi, abalewo anaona kuti zinthuzo sizikuwathandiza ndipo anakhumudwa. N’zoona kuti banjalo linali ndi ufulu wosankha kugwiritsa ntchito zinthu zimenezo. Koma silinaganize bwino kulimbikitsa anthu ena kuchita zimenezi chifukwa zinasokoneza mgwirizano mumpingo. Kale, Akhristu a ku Roma analinso ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya zakudya ndiponso zikondwerero zina. Kodi Paulo anawapatsa malangizo otani? Iye anati: “Wina amaona tsiku lina ngati loposa linzake, koma wina amaona tsiku lina mofanana ndi masiku ena onse. Choncho munthu aliyense akhale wotsimikiza ndi mtima wonse m’maganizo mwake.” Malinga ndi lembali, tiyenera kusamala kuti tisakhumudwitse anthu powakakamiza kutsatira maganizo athu.—Werengani Aroma 14:5, 13, 15, 19, 20.

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza zimene ena asankha? (Onani chithunzi patsamba 8.)

10 Ngati sitikumvetsa zimene Mkhristu mnzathu wasankha mogwirizana ndi chikumbumtima  chake, tisafulumire kumuweruza kapena kumukakamiza kuti asinthe. N’kutheka kuti akufunikira kuphunzitsabe chikumbumtima chake kapena mwina chikumbumtima chakecho chimamutsutsa pa zinthu zambiri. (1 Akor. 8:11, 12) Apo ayi, vuto lingakhale chikumbumtima chathu ndipo tingafunike kuchiphunzitsabe mfundo za Mulungu. Pa nkhani ngati za mankhwala aliyense ayenera kusankha yekha zochita kuti patsogolo asadzaimbe mlandu anthu ena.

TIZISANKHA BWINO ZOSANGALATSA

11, 12. Kodi tikamasankha zosangalatsa, tiyenera kukumbukira malangizo ati a m’Baibulo?

11 Yehova analenga anthu m’njira yoti azisangalala. Paja Solomo analemba kuti pali “nthawi yoseka” ndi “nthawi yodumphadumpha mosangalala.” (Mlal. 3:4) Koma pali zosangalatsa zina zimene si zabwino ndipo zina tikazichita nthawi yaitali kwambiri sizithandiza. Kodi chikumbumtima chathu chingatithandize bwanji kusankha bwino zosangalatsa?

12 Malemba amanena kuti tizipewa “ntchito za thupi” monga ‘zinthu zodetsa, khalidwe lotayirira, kupembedza mafano, kuchita zamizimu, udani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, kaduka, kumwa mwauchidakwa ndiponso maphwando aphokoso.’ Paulo ananena kuti “anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (Agal. 5:19-21) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi chikumbumtima changa chimandiuza kuti ndizipewa masewera achiwawa, olimbikitsa mtima wampikisano kapena wokonda dziko lathu? Nanga chimandichenjeza ndikafuna kuonera filimu yosonyeza zolaula kapena yolimbikitsa zinthu monga chiwerewere, kuledzera ndi kukhulupirira mizimu?’

13. Kodi malangizo a pa 1 Timoteyo 4:8 ndi pa Miyambo 13:20 angatithandize bwanji pa nkhani ya zosangalatsa?

13 M’Baibulo muli mfundo zinanso zimene zingatithandize kusankha bwino pa nkhani ya zosangalatsa. Mfundo ina ndi yakuti, “kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Tim. 4:8) Anthu ambiri amaona kuti masewera amathandiza thupi komanso maganizo. Koma ngati tikufuna kuchita masewera pagulu, tiyenera kusamala ndi anthu amene timachita nawo masewerawo. Paja lemba la Miyambo 13:20 limanena kuti: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Choncho chikumbumtima chathu chiyenera kutithandiza kusankha bwino anthu amene tingamachite nawo zosangalatsa.

14. Kodi mtsikana wina anaona kuti angatsatire bwanji Aroma 14:2-4?

14 M’bale wina dzina lake Christian ndi mkazi wake dzina lake Daniela ali ndi ana awiri achinyamata. M’baleyu anati: “Tsiku lina pochita Kulambira kwa Pabanja, tinakambirana nkhani ya zosangalatsa. Tinaona kuti pali zosangalatsa zina zabwino koma zina n’zoipa. Tinakambirananso kuti m’pofunika kusamala posankha anthu ocheza nawo. Mwana wathu wina wamkazi ananena kuti achinyamata ena a Mboni akakhala kusukulu, amapanga zosayenera pa nthawi yopuma. Ndiyeno iye ankakakamizika kuti azichita nawo. Tinakambirana kuti si bwino kumangotsatira anzathu koma aliyense ayenera kutsatira chikumbumtima chake posankha zosangalatsa ndiponso anthu ocheza nawo.”—Werengani Aroma 14:2-4.

Chikumbumtima chingatithandize kupewa mavuto (Onani ndime 14)

15. Kodi malangizo a pa Mateyu 6:33 angatithandize bwanji posankha zosangalatsa?

15 Posankha zosangalatsa tiyenera kuganiziranso nthawi. Kodi chimene mumaika  patsogolo n’chiyani? Kodi nthawi zambiri mumalephera kusonkhana, kulalikira ndiponso kuphunzira panokha chifukwa cha zosangalatsa? Paja Yesu anati: “Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mat. 6:33) Kodi chikumbumtima chanu chimakulimbikitsani kutsatira malangizo a Yesu amenewa?

TIMALIMBIKITSIDWA KULALIKIRA

16. Kodi chikumbumtima chathu chingatithandize bwanji pa ntchito yolalikira?

16 Chikumbumtima chikhoza kutilimbikitsanso kuchita ntchito zabwino osati kungopewa zoipa. Ntchito yabwino komanso yofunika kwambiri ndi yolalikira. Chikumbumtima cha Paulo chinkamulimbikitsa kugwira ntchito imeneyi. Iye anati: “Ndinalamulidwa kutero. Ndithudi, tsoka kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino!” (1 Akor. 9:16) Ifenso tikamatsanzira Paulo chikumbumtima chathu chimatiuza kuti tikuchita bwino. Tikamalalikira timathandizanso anthu ena kuti chikumbumtima chawo chiziwatsogolera bwino. Paulo ananena kuti: “Pamaso pa Mulungu, takhala chitsanzo chabwino kwa chikumbumtima cha munthu aliyense.”—2 Akor. 4:2.

17. Kodi mlongo wina anatsatira bwanji chikumbumtima chake?

17 Pamene mlongo wina dzina lake Jacqueline anali ndi zaka 16, ankaphunzira Biology kusukulu. Ndiyeno inafika nthawi yophunzira zoti zinthu zinangokhalako zokha. Iye anati: “Chikumbumtima changa sichinandilole kuyankhapo ngati mmene ndinkachitira nthawi zonse. Sindinkagwirizana ndi nkhaniyi ndipo ndinafotokozera aphunzitsi maganizo anga. Ndinadabwa kuona kuti sanadandaule nazo m’malomwake anandilola kuti ndifotokozere kalasi yonse zimene ndimakhulupirira pa nkhaniyi.” Jacqueline anamva bwino kwambiri chifukwa choti anatsatira chikumbumtima chake. Kodi nanunso chikumbumtima chimakulimbikitsani kuchita zabwino?

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuphunzitsa chikumbumtima chathu?

18 Zimakhala zosangalatsa kwambiri tikamayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo za Yehova. Ndiyeno chikumbumtima chathu chikhoza kutithandiza kuchita zimenezi. Koma chofunika ndi kuphunzira Mawu a Mulungu, kusinkhasinkha zimene taphunzirazo komanso kuzitsatira. Tikatero tidzaphunzitsa chikumbumtima chathu ndipo chidzayamba kutitsogolera bwino pa moyo wathu.

^ ndime 7 Onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, tsamba 29 mpaka 31.