Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ngati Kingsley Akukwanitsa, Kuli Bwanji Ine?”

“Ngati Kingsley Akukwanitsa, Kuli Bwanji Ine?”

KU SRI LANKA kunali munthu wina wosaona dzina lake Kingsley. Iye analinso ndi vuto losamva bwino ndipo ankayenda pa njinga ya olumala. Tsiku lina, Kingsley anawerenga Baibulo m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Iye anatchula bwinobwino liwu lililonse koma sankagwiritsa ntchito Baibulo lake.

Mwina mukudzifunsa kuti, Kodi zinatheka bwanji kuti Kingsley aphunzire za Yehova n’kufika polembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu? Tamvani zimene zinachitika.

Tsiku limene ndinayamba kukumana ndi Kingsley ndinadabwa kwambiri ndi chidwi chimene anali nacho. Iye anali ataphunzira ndi a Mboni angapo ndipo ankafunitsitsa kuphunzirabe. Anali ndi buku lakuti Chidziwitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha * la zilembo za anthu osaona koma linali lakutha. Iye anavomera kuti tiyambe kuphunzira koma panali mavuto awiri.

Vuto loyamba linali lakuti Kingsley ankakhala ndi anthu ambirimbiri m’nyumba yosungira okalamba ndi olumala. M’nyumbayi munkakhala phokoso ndiye poti Kingsley sankamva bwinobwino, ndinkafunika kukweza mawu kwambiri.  Aliyense m’nyumbamo ankamva zimene tinkakambirana pophunzira.

Vuto lachiwiri linali lakuti tinkafunika kuphunzira zinthu zochepa kwambiri ulendo uliwonse kuti athe kuzimvetsa n’kuzisunga mumtima. Kuti zinthu ziziyenda bwino, Kingsley ankakonzekera mwakhama kwambiri. Iye ankawerenga ndimezo mobwerezabwereza, kuoneratu malemba n’kupezeratu mayankho a mafunso. Pokambirana, iye ankafotokoza mayankho ake mokweza kwambiri ndipo ankachita zimenezi uku akumenya pansi. Tinkaphunzira kawiri pa mlungu ndipo phunziro lililonse linkatenga maola awiri.

ANKAPITA KU MISONKHANO NDIPO ANALEMBETSA M’SUKULU

Kingsley ndi Paul

Kingsley ankafunitsitsa kupita ku misonkhano koma sinali nkhani yophweka. Pankafunika kumukweza ndiponso kumutsitsa m’galimoto. Kenako n’kumukweza panjinga kupita naye m’Nyumba ya Ufumu. Koma abale ambiri ankamuthandiza ndipo ankachita kusinthana. Pa misonkhano, Kingsley ankakhala malo oti azimva bwino, ankamvetsera mwatcheru komanso ankapereka ndemanga.

Patapita nthawi, iye analembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Kutatsala milungu iwiri kuti akawerenge Baibulo koyamba, ndinamufunsa ngati akukonzekera. Anayankha mosakayikira kuti: “Inde ndakhala ndikukonzekera maulendo 30.” Ndinamuyamikira ndipo ndinamupempha kuti awerenge ine ndikumvetsera. Anatsegula Baibulo kenako n’kugwira patsamba loyenerera. Koma ndinaona kuti zala zake sizinkasuntha pamene ankawerenga. Iye anali ataloweza mavesi onse.

Sindinakhulupirire zimene ndinaonazo moti misozi inayamba kutuluka m’maso mwanga. Kenako ndinamufunsa kuti anakwanitsa bwanji kuloweza zonse atangokonzekera maulendo 30 okha. Iye anayankha kuti: “Iii, ndikunenatu maulendo 30 pa tsiku.” Iye anachita zimenezi kwa mwezi wathunthu mpaka analoweza mavesi onse.

Tsiku loti awerenge Baibulo linafika ndipo atamaliza kuwerenga anthu anaomba m’manja kwa nthawi yaitali mpaka ena misozi inayamba kulengeza. Izi zitachitika, mlongo wina amene anasiya kukamba nkhani m’sukulu chifukwa cha mantha, analembetsa kuti ayambirenso. Mlongoyu anati: “Ngati Kingsley akukwanitsa, kuli bwanji ine?”

Pa September 6, 2008, Kingsley anabatizidwa ataphunzira Baibulo kwa zaka zitatu. Iye ankatumikira Yehova mokhulupirika mpaka pamene anamwalira pa May 13, 2014. Kingsley sankakayikira ngakhale pang’ono kuti m’Paradaiso adzakhala wathanzi ndipo adzapitiriza kutumikira Mulungu. (Yes. 35:5, 6)—Yofotokozedwa ndi Paul McManus.

^ ndime 4 Bukuli linasindikizidwa mu 1995 koma pano anasiya kulisindikiza.