Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mukufunika Kupirira”

“Mukufunika Kupirira”

MLONGO wina dzina lake Anita * atangobatizidwa, mwamuna wake anayamba kuvuta kwambiri. Mlongoyu anati: “Ankandiletsa kupita ku misonkhano ndipo ankanena kuti ndisamayerekeze kutchula dzina la Mulungu. Ndikangotchula dzina loti Yehova ankalusa koopsa.”

Mwamuna wake sankamulola kuti aziphunzitsa ana ake kapena kuwatenga popita ku misonkhano. Choncho akafuna kuwaphunzitsa ankayesetsa kuti mwamunayo asadziwe.

Nkhani ya Anita ikusonyeza kuti kutsutsidwa ndi a m’banja lathu ndi vuto lalikulu kwambiri. Anthu ena akukumananso ndi mavuto monga matenda ndi imfa. Ena akuvutika chifukwa choti wachibale wawo wasiya kutumikira Yehova. Ndiyeno kodi n’chiyani chimathandiza Akhristu oterewa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova?

Kodi inuyo muyenera kuchita chiyani ngati mwakumana ndi vuto lalikulu? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mukufunika kupirira.” (Aheb. 10:36) Koma kodi n’chiyani chingatithandize kupirira?

TIZIPEMPHA YEHOVA KUTI ATITHANDIZE

Ngati mukukumana ndi vuto linalake, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kupirira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Ana. Tsiku lina mwamuna wake anamwalira mwadzidzidzi. Mwamunayu anali atakhala naye m’banja zaka 30. Ana anati: “Mwamuna wanga anangopita kuntchito koma sanabwereko. Anamwalira ali ndi zaka 52 zokha.”

N’chiyani chinathandiza mlongoyu kuti apirire? N’zoona kuti ntchito yake inkamutangwanitsa koma zinkamuwawabe mumtima. Iye anati: “Ndinkadandaulira Yehova kuchokera mu mtima kuti andithandize pa vuto loopsali.” Mlongoyu akuona kuti Yehova anayankhadi pemphero lake. Iye anati: “Mtendere wa Mulungu ndi umene unandithandiza kuti mtima wanga ukhale m’malo komanso kuti ndisasokonezeke maganizo. Sindikayikira kuti Yehova adzaukitsa mwamuna wanga.”—Afil. 4:6, 7.

Yehova akutilonjeza kuti adzamva mapemphero athu ndipo adzatithandiza kukhala okhulupirika. (Sal. 65:2) Dziwani kuti nanunso Yehova adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika ngakhale mutakumana ndi mavuto aakulu.

ABALE NDI ALONGO ANGAKUTHANDIZENI

Yehova amagwiritsanso ntchito abale ndi alongo kuti atithandize kupirira. Mwachitsanzo, Akhristu mumpingo wa ku Tesalonika atakumana ndi mavuto, Paulo anawauza kuti: “Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukuchitira.” (1 Ates. 2:14; 5:11) Popeza ankathandizana, anatha kupirira mavuto amene ankakumana nawo. Chitsanzo chawo chimatithandizanso kupirira mavuto athu. Kodi tingatsanzire bwanji Akhristu a ku Tesalonika?

Tizipeza anzathu apamtima mumpingo kuti tizilimbikitsana. (Aroma 14:19) Kulimbikitsana n’kofunika kwambiri pa nthawi ya mavuto. Mwachitsanzo, Paulo anakumana ndi mavuto ambiri koma Yehova anamuthandiza kupirira. Nthawi zina, Mulungu ankalimbikitsa Paulo pogwiritsa ntchito Akhristu anzake. Mwachitsanzo, Paulo ananena kuti abale ndi alongo ena a mumpingo wa Kolose ‘anamuthandiza ndi kumulimbikitsa.’ (Akol. 4:10, 11) Popeza ankakonda kwambiri Paulo, iwo ankamulimbikitsa pa nthawi ya mavuto. Mwina nanunso mukukumbukira abale ena amene anakulimbikitsani mutakumana ndi mavuto.

 TIZIPEMPHA AKULU KUTI ATITHANDIZE

Yehova amagwiritsanso ntchito akulu kuti atilimbikitse. Akuluwo amakhala ngati “malo obisalirapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho, ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi, ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.” (Yes. 32:2) N’zolimbikitsa kudziwa kuti akulu ndi okonzeka kutithandiza. Koma kodi mumalola kuti azikuthandizani? Iwo angakulimbikitseni kuti muthe kupirira.

Komabe akulu sangathetse mavuto anu onse. Iwo si angwiro ndipo ali ‘ndi zofooka ngati ife tomwe.’ (Mac. 14:15) Koma akatipempherera mtima wathu ukhoza kukhala m’malo. (Yak. 5:14, 15) M’bale wina ku Italy amene wakhala akuvutika ndi matenda enaake kwa zaka zambiri anati: “Akulu amandikonda kwambiri ndipo amabwerabwera kudzandilimbikitsa. Zimenezi zandithandiza kupirira.” Choncho mukakhala ndi vuto Yehova akufuna kuti muzipempha akulu kuti akuthandizeni.

TIZIKONDA KUCHITA ZINTHU ZOKHUDZA KULAMBIRA

Koma pali zinthu zina zimene tiyenera kuchita kuti tipirire. Tiyenera kukonda kuchita zinthu zokhudza kulambira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wazaka 39, dzina lake John. Iye anapezeka ndi matenda a khansa ndipo anati: “Sindinamvetse kuti ndapezeka ndi matendawa pa msinkhu umenewu.” Pa nthawiyi n’kuti mwana wake ali ndi zaka zitatu zokha. John anati: “Mkazi wanga ankafunika kusamalira mwana komanso ineyo. Ankafunikanso kundithandiza kuti ndipite kuchipatala.” Mankhwala amene John ankalandira ankachititsa kuti azifooka komanso m’mimba muzimuvuta. Ndiye zinangochitika kuti bambo ake anadwalanso mwakayakaya ndipo ankafunika kuthandizidwa.

Kodi n’chiyani chinathandiza John ndi banja lake kupirira? Iye anati: “Ngakhale kuti ndinkafooka, ndinkaonetsetsa kuti banja lathu likuchita zinthu zokhudza kulambira. Tinkapezeka pa misonkhano yonse, kulowa mu utumiki komanso kuchita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse.” John anaona kuti kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova kumathandiza kuti tipirire mavuto. Iye ananena kuti: “N’zoona kuti poyamba munthu angade nkhawa kwambiri. Koma kenako mtima umakhala m’malo. Izi zimachitika chifukwa chakuti Yehova amatikonda komanso amatipatsa mphamvu. Mulungu akhoza kukuthandizani ngati mmene wandithandizira ineyo.”

Tisakayikire kuti Yehova akhoza kutithandiza kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo panopa kapena m’tsogolo. Tiyeni tiziyesetsa kumudalira n’kumamupempha kuti atithandize. Tiziyesetsanso kupeza anzathu apamtima mumpingo komanso tizilola kuti akulu atithandize. Tiyeneranso kupitiriza kuchita zinthu zokhudza kulambira. Tikatero, tidzatha kutsatira mawu a Paulo akuti: “Mukufunika Kupirira.”

^ ndime 2 Mayina ena asinthidwa.