Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikhulupirira Yehova Nthawi Zonse

Muzikhulupirira Yehova Nthawi Zonse

“Mukhulupirireni nthawi zonse, anthu inu.”—SAL. 62:8.

1-3. Kodi n’chiyani chinachitikira mtumwi Paulo chomwe chinamuthandiza kukhulupirira kwambiri Yehova? (Onani chithunzi pamwambapa.)

AKHRISTU ankazunzidwa kwambiri mu ulamuliro wa Aroma. Iwo ananamiziridwa kuti awotcha mzinda wa Roma mu 64 C.E. ndiponso kuti amadana ndi anthu. Mukanakhalapo pa nthawiyi, tsiku lililonse bwenzi mukuopa kumangidwa kapena kuzunzidwa. Mukanachitanso mantha poona Akhristu anzanu akukhadzulidwa ndi mikango m’mabwalo a zamasewera, kukhomeredwa pamtengo kapena kuotchedwa.

2 Imeneyi ndi nthawi yomwe mtumwi Paulo anamangidwa kachiwiri ku Roma. Kodi zikanatheka kuti Akhristu anzake amupulumutse? Mwina mtumwi Paulo ankaona kuti palibe amene angamuthandize. Mwina n’chifukwa chake analembera Timoteyo kuti: “Pamene ndinali kudziteteza koyamba pa mlandu wanga, palibe amene anakhala kumbali yanga. Onse anandisiya ndekha. Ngakhale zinali choncho, usakhale mlandu kwa iwo.” Komabe iye anazindikira kuti akhoza kupeza thandizo chifukwa analemba kuti: “Koma Ambuye anaima pafupi ndi ine ndi kundipatsa mphamvu.” Yesu ndi amene anapereka mphamvu kwa mtumwiyu.  Kodi mtumwi Paulo anathandizidwadi? Iye anati: “Ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.”—2 Tim. 4:16, 17. *

3 Mtumwi Paulo ankalimbikitsidwa akamakumbukira zimenezi chifukwa ankaona kuti kukhulupirira Yehova kudzamuthandiza kupirira mayesero alionse. N’chifukwa chake anapitiriza kulemba kuti: “Ambuye adzandipulumutsa ku choipa chilichonse.” (2 Tim. 4:18) Apatu zikuonetseratu kuti Paulo anazindikira kuti Yehova ndi Yesu amatithandiza pamene tikuona kuti palibiretu mtengo wogwira.

MWAYI WOSONYEZA KUTI TIMAKHULUPIRIRA YEHOVA

4, 5. (a) Kodi ndani angatithandize pa nthawi ina iliyonse? (b) Kodi mungatani kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ulimbe kwambiri?

4 Kodi inunso munakumanapo ndi vuto lalikulu n’kumaona kuti palibe mtengo wogwira? Mwina simukupeza ntchito, mumanyozedwa kusukulu, muli ndi matenda ena ake kapena zinthu zina zikukudetsani nkhawa. N’kutheka kuti munapempha thandizo kwa anthu ena koma sanakuthandizeni. Kunena zoona anthu sangatithandize pa mavuto ena. Kodi ndi nzeru kutsatira malangizo akuti tizikhulupirira Yehova pa nthawi ngati imeneyi? (Miy. 3:5, 6) Inde. Tikutero chifukwa chakuti pali umboni wa m’Baibulo wosonyeza kuti Yehova amathandiza pa mavuto ngati amenewo.

5 Choncho tikakumana ndi vuto lalikulu tisamakwiye. Tiziona kuti tapeza mwayi wosonyeza kuti timakhulupirira Yehova ndiponso woti tione akutithandiza. Umu ndi mmene Paulo ankaonera mavuto ake. Mukatero ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimba kwambiri chifukwa choti mwayamba kumukhulupirira ndi mtima wonse.

MUZIKHULUPIRIRA YEHOVA KUTI MUKHALE NAYE PAUBWENZI

6. N’chifukwa chiyani nthawi zina timavutika kukhulupirira Yehova tikakumana ndi mavuto?

6 Mukakumana ndi vuto lalikulu muyenera kufotokozera Yehova m’pemphero. Mukatero mtima wanu uyenera kukhala m’malo podziwa kuti mwachita zonse zimene mukanatha ndipo mbali yotsalayo mwasiyira Yehova. (Werengani Salimo 62:8; 1 Petulo 5:7.) Munthu akamachita zimenezi, ubwenzi wake ndi Yehova umalimba kwambiri. N’zoona kuti nthawi zina zimativuta kukhulupirira zoti Yehova adzatipatsa zonse zofunika. Izi zingachitike chifukwa choti mapemphero ena sayankhidwa nthawi yomweyo.—Sal. 13:1, 2; 74:10; 89:46; 90:13; Hab. 1:2.

7. N’chifukwa chiyani mapemphero ena sayankhidwa nthawi yomweyo?

7 N’chifukwa chiyani nthawi zina mapemphero ena sayankhidwa nthawi yomweyo? Choyamba tiyenera kukumbukira kuti Yehova ali ngati bambo athu. (Sal. 103:13) Kodi ana ayenera kuyembekezera kuti bambo awo aziwapatsa chilichonse chimene apempha pa nthawi yomweyo? Nthawi zina ana amangopempha zinthu zosafunika kwenikweni zimene angozilakalaka pa nthawiyo. Ndiye pali zinthu zina zimene amapempha zomwe ayenera kudikira kaye. Koma amatha kupemphanso zinthu zimene sizingathandize iwowo kapena anthu ena. Ndipotu bambo atati azingopereka chilichonse kwa mwana, zikhoza kukhala ngati mwanayo ndi bwana ndipo bambowo ndi wantchito. Choncho m’pomveka kuti nthawi zina Yehova sayankha mapemphero athu nthawi yomweyo. Yehova ali ndi ufulu wochita zimenezi chifukwa chakuti iye ndi Atate wathu wachikondi komanso amene anatilenga. Atati azingopereka chilichonse pa nthawi imene tapempha  ndiye kuti sangakhale ndi ufulu umene bambo kapena mlengi amayenera kukhala nawo.—Yerekezerani ndi Yesaya 29:16; 45:9.

8. Kodi Yehova akutilonjeza chiyani poganizira mmene tilili?

8 Mfundo ina ndi yakuti Yehova amatidziwa bwino. (Sal. 103:14) Amadziwa kuti sitingapirire mavuto patokha ndipo ndiwokonzeka kutithandiza. N’zoona kuti nthawi zina timaona kuti sitingapirire. Koma Yehova amatitsimikizira kuti sangalole kuti atumiki ake ayesedwe kufika pamene sangapirire. Ndithu “iye adzapereka njira yopulumukira.” (Werengani 1 Akorinto 10:13.) Choncho tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kukhulupirira kuti Yehova amadziwa bwino mavuto amene tingathe kuwapirira ndiponso amene sitingathe kuwapirira.

9. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati mapemphero athu sakuyankhidwa?

9 Tiziyembekezera Yehova ngati tikuona kuti mapemphero athu sakuyankhidwa, chifukwa iye amadziwa nthawi imene angatithandize. Tiyeneranso kudziwa kuti iye amafunitsitsa kutithandiza koma amaleza mtima podikira nthawi yake. Paja Baibulo limati: “Yehova azidzayembekezera kuti akukomereni mtima ndipo adzanyamuka kuti akuchitireni chifundo, pakuti Yehova ndi Mulungu amene amaweruza mwachilungamo. Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezera.”—Yes. 30:18.

“M’KAMWA MWA MKANGO”

10-12. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasokoneze maganizo a Mkhristu amene akusamalira matenda aakulu? (b) Kodi kukhulupirira Yehova pa nthawi ya mavuto kumalimbitsa bwanji ubwenzi wathu ndi iye? Perekani chitsanzo.

10 Paulo atakumana ndi mavuto aakulu ankamva ngati ali pafupi kulowa m’kamwa mwa mkango.” Mavuto ena akhoza kukuchititsaninso kumva ngati kuti muli pafupi kulowa mkamwa mwa mkango kapena mungamve kuti mwalowa kale. Pa nthawi ngati imeneyi kukhulupirira Yehova kumakhala kovuta koma kofunika kwambiri. Tiyerekeze kuti mukusamalira wachibale wanu amene akudwala matenda aakulu. Mwina mwapempha Yehova kuti akupatseni nzeru ndiponso mphamvu. * Kodi zikatero mumakhala ndi mtendere mumtima podziwa kuti Yehova akuona zonse ndipo adzakupatsani zonse zofunika kuti mupirire?—Sal. 32:8.

11 Koma zochitika pa nthawi ya mavutoyi zikhoza kukusowetsani mtendere. Mwachitsanzo, madokotala osiyanasiyana akhoza kumapereka malangizo osiyanasiyananso. Apo ayi, achibale anu angamakusokonezeni m’malo mokuthandizani. Zikatero muyenera kudalira kwambiri Yehova n’kumayesetsa kuyandikana naye. (Werengani 1 Samueli 30:3, 6.) Ubwenzi wanu ndi Yehova umalimba kwambiri mukaona mmene wakuthandizirani.

12 Mlongo wina dzina lake Linda * anavomereza mfundoyi pa nthawi imene makolo ake ankadwala mwakayakaya. Iye anati: “Pa nthawiyo, ineyo, mwamuna wanga komanso mchimwene wanga tinkasowa mtengo wogwira. Nthawi zina tinkaona kuti palibiretu chabwino. Koma panopa tikamakumbukira, timaona kuti Yehova ankatithandiza kwambiri. Iye ankatilimbikitsa ndiponso kutipatsa zofunika pa nthawi yake ngakhale pamene tinkaona kuti zinthu zavutiratu.”

13. Kodi kukhulupirira Yehova kunathandiza bwanji mlongo wina amene anakumana ndi mavuto aakulu?

13 Mlongo wina dzina lake Rhonda anaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhani yokhulupirira  Yehova pa nthawi ya mavuto. Mwamuna wake sanali wa Mboni ndipo pa nthawi ina mwamunayo anaganiza zothetsa banja. Izi zili mkati, mchimwene wake anapezeka ndi matenda oopsa kwambiri. Patangopita miyezi yochepa, mulamu wake anamwalira. Ndiyeno atayesa kupeza mphamvu pambuyo pa mavuto onsewa, mlongoyu anayamba upainiya wokhazikika. Koma pasanapite nthawi yaitali, mayi ake anamwalira. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti apirire? Rhonda anati: “Ndimapemphera kwa Yehova tsiku lililonse ndiponso ndikamasankha zochita ngakhale pa nkhani zing’onozing’ono. Izi zandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova. Panopa ndaphunzira kudalira Yehova osati kudzidalira kapena kudalira anthu ena. Iye wandithandiza kwambiri ndipo ankandipatsa zonse zofunika. Yehova amakhala nane pa zonse zimene ndikuchita.”

Tingakumane ndi mavuto m’banja amene angasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova (Onani ndime 14 mpaka 16)

14. Kodi tiyenera kukhulupirira mfundo iti ngati m’bale wathu wachotsedwa?

14 Kukhulupirira Yehova kungatithandizenso pamene wachibale wathu wachotsedwa. Tonsefe timadziwa mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu ochotsedwa. (1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10) Nthawi zina tingaone kuti n’zovuta kapenanso zosatheka kutsatira malangizo okhudza ochotsedwa. * Koma tiyenera kukhulupirira kuti Yehova akhoza kutipatsa mphamvu kuti titsatire malangizo a m’Baibulo. Choncho ngati takumana ndi vutoli tiziona kuti tili ndi mpata wolimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova.

15. N’chifukwa chiyani Adamu sanamvere Yehova?

15 Zimene Adamu anachita zikhoza kutipatsa phunziro pa nkhaniyi. Kodi iye ankaganiza  kuti akhoza kukhalabe moyo pambuyo pochita zimene Mulungu anamuletsa? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti Baibulo limati: “Adamu sananyengedwe.” (1 Tim. 2:14) Nangano n’chiyani chinamuchititsa kuti achimwe? N’kutheka kuti anadya chipatsocho chifukwa chotengeka ndi mkazi wake. Iye anaona kuti ndi bwino kumvera mkaziyo osati Yehova Mulungu.—Gen. 3:6, 17.

16. Kodi tiyenera kukonda kwambiri ndani? Perekani chifukwa.

16 Kodi pamenepa tikuphunzira kuti tisamakonde achibale athu? Ayi, nkhani si imeneyo. Mfundo ndi yakuti tiyenera kukonda Yehova kuposa aliyense. (Werengani Mateyu 22:37, 38.) Kukonda kwambiri Yehova kungathandizenso achibale athuwo, kaya panopa akutumikira Yehova kapena ayi. Choncho yesetsani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova ndiponso kumukhulupirira. Koma ngati kuchotsedwa kwa m’bale wanu kukukupwetekani kwambiri muyenera kufotokozera Yehova nkhawa zanu zonse. * (Aroma 12:12; Afil. 4:6, 7) N’zoona kuti zimapweteka, koma muziona kuti umenewo ndi mwayi wanu woti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova. Zimenezi zidzakuthandizani kuti muziyembekezera Yehova kuti akuthandizeni.

ZIMENE TIYENERA KUCHITA PANOPA

Muzigwira ntchito yolalikira posonyeza kuti mumakhulupirira Yehova (Onani ndime 17)

17. Kodi tikamagwira ntchito yolalikira mwakhama, timasonyeza bwanji kuti timakhulupirira Yehova?

17 N’chifukwa chiyani Paulo anapulumutsidwa “mkamwa mwa mkango?” Iye anati: “Kuti kudzera mwa ine, ntchito yolalikira ichitidwe mokwanira, ndi kuti mitundu yonse ya anthu imve uthengawo.” (2 Tim. 4:17) Nafenso tikamayesetsa kugwira mwakhama ntchito yolalikira, Yehova adzaonetsetsa kuti tikupeza zinthu zina zofunika. (Mat. 6:33) Ndife “antchito anzake a Mulungu” ndipo iye “wationa kuti ndife oyenera kupatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino.” (1 Akor. 3:9; 1 Ates. 2:4) Choncho tikamagwira ntchito yolalikira mwakhama, zidzakhala zosavuta kuyembekezera kuti Yehova atithandize.

18. Kodi tingatani kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova ndiponso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye?

18 Choncho tiyeni tiyesetse panopa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu. Tikakumana ndi vuto lililonse lodetsa nkhawa, tiziona kuti ndi mwayi wathu woti tiyandikire Yehova. Tiziyesetsa kuphunzira Mawu a Mulungu, kupemphera mosalekeza ndiponso kuchita nawo zinthu zonse zokhudza kulambira. Tikamatero, Yehova adzatithandiza pa vuto lililonse limene tingakumane nalo panopa ngakhale m’tsogolo.

^ ndime 2 Mwina mtumwi Paulo anapulumutsidwadi “mkamwa mwa mkango” weniweni kapena ankangophiphiritsa.

^ ndime 10 Mabuku athu amapereka malangizo othandiza anthu amene akudwala kapena amene akusamalira odwala. Malangizo ena mungawapeze mu Galamukani! ya February 8, 1994; February 8, 1997; June 8, 2000 ndiponso ya February 8, 2001.

^ ndime 12 Mayina asinthidwa.

^ ndime 14 Onani nkhani yakuti “Kuchotsa Anthu Osalapa Kumathandiza” patsamba 29.

^ ndime 16 Mabuku athu amafotokoza zimene anthu angachite ngati wachibale wachotsedwa. Nkhani zoterezi mungazipeze mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 2006, tsamba 17 mpaka 21 ndi ya January 15, 2007, tsamba 17 mpaka 20.