Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani masiku ano mabuku athu safotokoza kwambiri kuti zinthu zosiyanasiyana zotchulidwa m’Baibulo zimaphiphiritsira zinazake?

Nsanja ya Olonda ya 1950, inanena kuti nthawi zina nkhani za m’Baibulo zimakhala zophiphiritsa. Mwachitsanzo, kale mabuku athu ankasonyeza kuti anthu okhulupirika monga Debora, Elihu, Yefita, Yobu, Rahabi ndi Rabeka ankaphiphiritsira odzozedwa kapena “khamu lalikulu.” (Chiv. 7:9) Ankanena kuti Yefita, Yobu ndi Rabeka ankaimira odzozedwa pomwe Debora ndi Rahabi ankaimira “khamu lalikulu.” N’chifukwa chiyani masiku ano mabuku athu sanena zinthu ngati zimenezi?

Malemba amasonyeza kuti anthu ena otchulidwa m’Baibulo ankaimira anthu ena. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ananena kuti nkhani imene anafotokoza pa Agalatiya 4:21-31 ili ndi “tanthauzo lophiphiritsira.” Iye ananena kuti mdzakazi wa Abulahamu dzina lake Hagara ankaimira mtundu wa Isiraeli. Yehova anachita pangano ndi mtunduwu ndipo unkayenera kutsatira Chilamulo cha Mose. Koma Sara “anali mfulu” ndipo ankaimira mkazi wa Mulungu kapena kuti mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. M’kalata yopita kwa Aheberi, Paulo anatchula za Melekizedeki. Iye anali mfumu komanso wansembe. Paulo anasonyeza kuti Melekizedeki ankaimira Yesu ndipo anasonyezanso kufanana kwawo. (Aheb. 6:20; 7:1-3) Paulo anasonyezanso kuti Yesaya ndi ana ake ankaimira Yesu ndi Akhristu odzozedwa. (Aheb. 2:13, 14) Timavomereza zonsezi chifukwa chakuti Paulo analemba mouziridwa ndi Mulungu.

 

Kodi nkhosa imene Aisiraeli ankapereka nsembe pa pasika inkaimira chiyani?—Num. 9:2

 

Paulo ananena kuti Khristu ndi “nsembe yathu ya pasika.”—1 Akor. 5:7

Choncho nthawi zina Baibulo limasonyeza kuti munthu wina amaimira winawake. Koma izi sizikutanthauza kuti zonse zimene zinachitika pa moyo wa munthuyo n’zophiphiritsira. Chitsanzo ndi nkhani ya Melekizedeki ija. N’zoona  kuti Paulo ananena kuti iye ankaimira Yesu. Koma pa nthawi ina Melekizedeki anakapatsa Abulahamu mkate ndi vinyo atagonjetsa mafumu 4 a ku Sinara. Paulo sananene kuti zimenezi zinkaimira zinazake. Choncho Malemba sasonyeza kuti zinali zophiphiritsira.—Gen. 14:1, 18.

Pambuyo pa imfa ya Yesu, anthu ena ankakonda kusonyeza kuti zinthu zambirimbiri zinkaimira zinazake. Buku lina lomasulira mawu a m’Baibulo linati anthu ngati Origen, Ambrose ndi Jerome ankakonda kuchita zimenezi. Limati kankhani kalikonse ka m’Malemba ankanena kuti kakuimira zinazake. Ngakhale zochitika wamba ankaziona kuti ndi zophiphiritsa. Bukulo limati ena anafika poganiza kuti nsomba 153, zimene ophunzira anagwira Yesu ataukitsidwa, zimaimira zinazake.

Nayenso Augustine wa ku Hippo anafotokoza zambirimbiri pa nkhani yoti Yesu anadyetsa anthu 5,000 powapatsa mikate 5 yabarele ndi nsomba ziwiri. Anthu ankaona kuti barele si wabwino akayerekezera ndi tirigu. Ndiyeno Augustine anati mikate 5 ya barele inkaimira mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo amene Mose analemba. Ndiyeno ankati izi zikusonyeza kuti “Chipangano Chakale” si chofunika kwambiri poyerekezera ndi “Chipangano Chatsopano.” Pa zifukwa zina, iye ankanenanso kuti nsomba ziwiri zinkaimira mfumu ndi wansembe. Munthu winanso wokonda kulemba zoterezi ananena kuti zimene Yakobo anachita pogula ukulu wa Esau ndi mphodza zofiira zinali zophiphiritsira. Anati zinkaimira zimene Yesu anachita pogula anthu ndi magazi ake ofiira kuti apite kumwamba.

Zimene anthuwa anafotokozazi n’zosamvetsetseka. Choncho tingaone kuti anthu paokha sangadziwe nkhani za m’Baibulo zimene zikuimira zinazake. Apa mfundo ndi yakuti: Ngati Malemba anena kuti izi zikuimira zakutizakuti, timavomereza. Koma ngati sanena, palibe chifukwa choganizira zimenezo.

Ndiyeno kodi nkhani za m’Baibulo zingatithandize bwanji? Pa Aroma 15:4, Paulo analemba kuti: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa chiyembekezo chifukwa malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.” Apa Paulo ankatanthauza kuti odzozedwa anzake pa nthawiyo akanatha kuphunzira mfundo zofunika mu nkhani za m’Baibulo. Koma anthu onse a Yehova pa nthawi iliyonse, kaya odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” akhoza kuphunzira zambiri pa nkhani za m’Baibulo “zimene zinalembedwa kalekale.”—Yoh. 10:16; 2 Tim. 3:1.

Choncho masiku ano gulu silikonda kunena kuti nkhani iyi ikukhudza odzozedwa, iyi ikukhudza a khamu lalikulu kapena kuti iyi ikukhudza anthu a pa nthawi yakutiyakuti. M’malomwake timaona kuti anthu onse a Mulungu akhoza kuphunzira zinazake pa nkhani za m’Baibulo. Mwachitsanzo, sitinganene kuti nkhani ya Yobu ikuimira mavuto amene odzozedwa anakumana nawo pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Atumiki a Mulungu ambirimbiri akumanapo ndi mavuto ngati a Yobu ndipo kenako anadzaona kuti “Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yak. 5:11) Ena mwa anthuwa ndi amuna, ena ndi akazi, ena ndi odzozedwa ndipo ena ndi a khamu lalikulu.

Inunso mukhoza kuvomereza kuti masiku ano m’mipingo yathu muli alongo achikulire okhulupirika ngati Debora, akulu achinyamata anzeru ngati Elihu komanso apainiya olimba mtima ndiponso akhama ngati Yefita. Mulinso abale ndi alongo okhulupirika ndiponso oleza mtima ngati Yobu. Timayamikira kuti Yehova anasunga “zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale” n’cholinga choti Malemba ‘azitilimbikitsa ndiponso kutipatsa chiyembekezo.’

Chifukwa cha mfundo zimene tanenazi, masiku ano gulu limafotokoza kwambiri zimene tikuphunzira pa nkhani za m’Baibulo osati kusonyeza kuti izi zikuimira zakutizakuti.