Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Ankadziwa Njira Yake’

‘Ankadziwa Njira Yake’

M’BALE GUY HOLLIS PIERCE, yemwe anali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anamaliza utumiki wake padziko lapansi Lachiwiri pa March 18, 2014. Pa nthawiyo anali ndi zaka 79 ndipo popeza ali m’gulu la abale a Khristu, iye anaukitsidwa n’kulandira mphoto yake kumwamba.—Aheb. 2:10-12; 1 Pet. 3:18.

M’baleyu anabadwa pa November 6, 1934 mumzinda wa Auburn, ku California m’dziko la United States. Iye anabatizidwa mu 1955. Mu 1977, anakwatira Penny ndipo analera naye ana angapo. Kusamalira banja lake kunamuthandiza kuti azithandiza anthu ngati mmene bambo amachitira. Pofika mu 1982, m’baleyu ndi mkazi wake ankachita upainiya ndipo mu 1986 anadzakhala woyang’anira dera ku United States. Anagwira ntchitoyi kwa zaka 11.

Mu 1997, M’bale Pierce ndi mkazi wake anayamba kutumikira pa Beteli ku United States. Poyamba, m’baleyu ankatumikira mu Dipatimenti ya Utumiki ndipo mu 1998 anasankhidwa kuti azithandizira mu Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli ya Bungwe Lolamulira. Ndiyeno pa October 2, 1999, pa msonkhano wapachaka, analengeza kuti m’baleyu wasankhidwa kuti akhale m’Bungwe Lolamulira. Zaka zapitazi, M’bale Pierce watumikira mu Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli, Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku, Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku ndiponso mu Komiti ya Ogwirizanitsa.

Anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana ankakonda M’bale Pierce chifukwa cha kumwetulira kwake komanso tinthabwala take. Koma ankakondedwa kwambiri chifukwa chakuti anali munthu wachikondi ndiponso wodzichepetsa. Ankalemekezanso kwambiri malamulo ndi mfundo za m’Baibulo komanso ankakhulupirira Yehova ndi mtima wonse. M’baleyu ankaona kuti mfundo yoti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake ndi yodalirika kwambiri kuposa yoti dzuwa litulukanso. Iye ankafunitsitsa kuti anthu onse adziwe zimenezi.

M’bale Pierce ankachita khama kwambiri potumikira Yehova moti ankadzuka m’mawa kwambiri ndipo nthawi zambiri ankaweruka usiku. Iye anayenda m’mayiko osiyanasiyana n’cholinga choti akalimbikitse abale ndi alongo. Koma akamayenda ankapezanso mpata wocheza ndi anthu a pa Beteli amene ankafuna kucheza naye, kufunsa malangizo kapena kupempha thandizo. Anthu ambiri amakumbukira kuti iye anali munthu wochereza alendo, wochezeka komanso wodziwa kugwiritsa ntchito Malemba polimbikitsa anthu.

M’baleyu wasiya mkazi, ana 6 komanso zidzukulu zambiri. Palinso anthu ambirimbiri amene ankamuona kuti ndi bambo wawo. M’bale Mark Sanderson, wa m’Bungwe Lolamulira, ndi amene anakamba nkhani ya maliro a m’baleyu ku Beteli ya ku Brooklyn, Loweruka pa March 22, 2014. M’nkhaniyo anatchulanso zoti m’baleyu ankayembekezera kupita kumwamba ndipo anawerenga mawu a Yesu akuti: “M’nyumba ya Atate wanga muli malo ambiri okhalamo. . . . Ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengerani kwathu, kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko. Ndipo kumene ndikupitako, inu njira yake mukuidziwa.”—Yoh. 14:2-4.

N’zoona kuti tidzamusowa M’bale Pierce. Koma tikusangalala kuti ‘ankadziwa njira’ ya ‘kumalo ake okhala’ kwamuyaya.