Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi mawu a Davide pa Salimo 37:25 komanso a Yesu pa Mateyu 6:33 amasonyeza kuti Yehova sadzalola kuti Mkhristu avutike ndi njala?

Davide analemba kuti: “Sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya.” Ananena zimenezi poganizira zimene zinachitika pa moyo wake. Iye ankadziwa kuti Mulungu amasamalira anthu ake nthawi zonse. (Sal. 37:25) Koma mawuwa sakutanthauza kuti palibe mtumiki wa Yehova amene angasowe zofunika pa moyo.

Davide nayenso ankavutika nthawi zina. Mwachitsanzo, pamene iye ankathawa Sauli, analibe chakudya chokwanira ndipo anapempha mkate kuti adye iyeyo ndi anzake. (1 Sam. 21:1-6) N’zoona kuti pa nthawiyo Davide ‘anapempha chakudya’ koma ankadziwa kuti Yehova sawasiya. Baibulo silinena kuti Davide ankapemphapempha chakudya kuti asafe ndi njala.

Pa Mateyu 6:33, Yesu anatitsimikizira kuti Mulungu adzathandiza atumiki ake kuti azipeza zofunika pa moyo ngati amaika zinthu za Ufumu patsogolo. Iye anati: “Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi [monga chakudya, madzi ndi zovala] zidzawonjezedwa kwa inu.” Koma Yesu anasonyezanso kuti “abale” ake akhoza kukhala ndi njala chifukwa chozunzidwa. (Mat. 25:35, 37, 40) Zimenezi zinachitikira mtumwi Paulo. Nthawi zina iye ankavutika ndi njala komanso ludzu.—2 Akor. 11:27.

Yehova watiuza kuti tikhoza kuzunzidwa m’njira zosiyanasiyana. Mwina angalole kuti tivutike pamene tikuthandiza nawo poyankha mabodza a Mdyerekezi. (Yobu 2:3-5) Mwachitsanzo, Akhristu ena anatsekeredwa m’ndende pa nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi ndipo ankavutika kwambiri. Asilikali ankawamana chakudya pofuna kuti asiye kukhala okhulupirika. Abale ndi alongo okhulupirika ankamverabe Yehova ndipo iye sanawasiye. Nthawi zina Yehova amalola kuti Akhristu akumane ndi mayesero osiyanasiyana. Koma sitiyenera kukayikira kuti Yehova amathandiza onse amene amavutika chifukwa cha dzina lake. (1 Akor. 10:13) Tingachite bwino kukumbukira mawu a pa Afilipi 1:29 akuti: “Munapatsidwa mwayi. Osati mwayi wokhulupirira Khristu wokha, komanso wovutika chifukwa cha iye.”

Yehova amalonjeza kuti azithandiza atumiki ake. Paja lemba la Yesaya 54:17 limati: “Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.” Malonjezo ngati amenewa amasonyeza kuti Mulungu aziteteza gulu lake. Koma Mkhristu aliyense payekha akhoza kukumana ndi mayesero ngakhale kuphedwa kumene.