Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mdani Wathu Womalizira Adzawonongedwa

Mdani Wathu Womalizira Adzawonongedwa

“Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.”—1 AKOR. 15:26.

1, 2. (a) Kodi zinthu zinali bwanji Adamu ndi Hava atangolengedwa kumene? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

ADAMU ndi Hava atalengedwa analibe mdani aliyense. Anali angwiro ndipo ankakhala m’Paradaiso. Ankagwirizana kwambiri ndi Mulungu moti anali ngati ana ake enieni. (Gen. 2:7-9; Luka 3:38) Zimene Mulungu anawauza kuchita zinasonyeza kuti tsogolo lawo linali labwino kwambiri. (Werengani Genesis 1:28.) Patapita nthawi, iwo ‘akanadzaza dziko lapansi.’ Anayeneranso kuyang’anira ‘cholengedwa chilichonse padziko lapansi.’ Koma kuti apitirize kuchita zimenezi, anafunika kukhala ndi moyo wosatha.

2 Ndiye kodi zinthu zinasintha bwanji? N’chifukwa chiyani anthu akuvutika ndi adani ambirimbiri? Kodi imfa, yomwe ndi mdani wamkulu, inayamba bwanji? Kodi Mulungu adzawononga bwanji adani onsewa? M’Baibulo tikhoza kupeza mayankho a mafunso ngati amenewa. Tiyeni tione mmene Baibulo limayankhira mafunsowa.

 ANAWACHENJEZA MWACHIKONDI

3, 4. (a) Kodi Mulungu anapereka lamulo liti kwa Adamu ndi Hava? (b) N’chifukwa chiyani iwo anayenera kumvera lamulolo?

3 Ngakhale kuti Adamu ndi Hava akanakhala ndi moyo wosatha, sikuti anali ndi moyo wosakhoza kufa. Iwo anayenera kupuma, kumwa, kugona ndiponso kudya kuti apitirize kukhala ndi moyo. Koma chofunika kwambiri kuti akhalebe ndi moyo chinali kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Deut. 8:3) Anayenera kutsatira malangizo ake kuti asafe komanso kuti azisangalala. Mulungu anaonetsetsa kuti Adamu adziwe zimenezi Hava asanalengedwe. Kodi anachita bwanji zimenezi? Baibulo limanena kuti: “Yehova Mulungu anapatsa munthuyo lamulo lakuti: ‘Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.’”—Gen. 2:16, 17.

4 “Mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa” unkasonyeza kuti Mulungu ndi amene ali ndi udindo wonena kuti ichi ndi chabwino, ichi ndi choipa. N’zoona kuti Adamu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu komanso anali ndi chikumbumtima choncho akanatha kudziwa kuti izi ndi zabwino, izi ndi zoipa. Koma mtengowu unkasonyeza kuti nthawi zonse Adamu ndi Hava ankafunika kutsatira malangizo a Mulungu. Kudya zipatso za mtengowu kukanasonyeza kuti anthuwo sakufuna kuti Mulungu aziwalamulira. Kuchita zimenezi kukanabweretsa mavuto aakulu kwambiri kwa iwowo ndiponso ana awo ndipo malinga ndi zimene Mulungu anawachenjeza, akanafa.

KODI IMFA INAYAMBA BWANJI?

5. N’chiyani chinachititsa kuti Adamu ndi Hava achimwe?

5 Hava atalengedwa, Adamu anamuuza lamulo la Mulungu lija. Havayo ankalidziwa bwino kwambiri lamuloli. Tikutero chifukwa chakuti pamene Satana Mdyerekezi anagwiritsa ntchito njoka pomulankhula iye analifotokoza ndendende mmene Adamu anamuuzira. (Gen. 3:1-3) Satana anali ndi mtima wofuna kudzilamulira komanso wolamulira ena. (Yerekezerani ndi Yakobo 1:14, 15.) Kuti zimene ankafunazo zitheke ananena kuti Mulungu ananamiza Adamu ndi Hava. Iye anauza Hava kuti ngati satsatira lamulo la Mulungu sadzafa koma adzayamba kufanana ndi Mulunguyo. (Gen. 3:4, 5) Hava anamukhulupirira ndipo anadya chipatso chimene Mulungu anawaletsa n’kunyengereranso Adamu kuti adye. (Gen. 3:6, 17) Hava ananamizidwa ndi Satana. (Werengani 1 Timoteyo 2:14.) Ndiyeno Adamu ‘anamvera mawu a mkazi wake.’ Mwina zinkaoneka ngati njokayo inkafuna kuwathandiza. Koma Satana Mdyerekezi anali mdani wawo yemwe ankadziwa bwino kuti akadya chipatsocho adzafa.

6, 7. Kodi Yehova anapereka bwanji chiweruzo kwa Adamu ndi Hava?

6 Yehova ankaona zonse zimene zinkachitika koma analola kuti anthuwo komanso Satana asonyeze ngati akumukonda kapena ayi. (1 Mbiri 28:9; werengani Miyambo 15:3.) N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava anapandukira Mulungu amene anawapatsa moyo ndi zinthu zina zonse. Monga Atate wawo, Yehova ayenera kuti zinamupweteka kwambiri mumtima pamene onse anasankha kuti asamumvere. (Yerekezerani ndi Genesis 6:6.) Kenako Mulungu anayenera kuwaweruza mogwirizana ndi zimene anali atawauza.

7 Mulungu anali atauza Adamu kuti: “Tsiku limene udzadya [zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa], udzafa ndithu.” N’kutheka kuti Adamu ankaganiza kuti ‘tsikulo’ linali tsiku lenileni la maola 24. Atadya chipatso choletsedwacho, mwina ankaganiza  kuti Yehova adzapereka chilangocho tsiku lomwelo dzuwa lisanalowe. Ndiyeno Yehova analankhula nawo madzulo ake kapena kuti “nthawi ya kamphepo kayeziyezi.” (Gen. 3:8) Iye anayamba kuwafunsa mafunso ngati ali m’khoti kuti adziwe bwinobwino maganizo awo. (Gen. 3:9-13) Kenako Mulungu anapereka chiweruzo choti adzafadi. (Gen. 3:14-19) Koma ngati Mulungu akanawawononga nthawi yomweyo, cholinga chake chokhudza ana a Adamu ndi Hava sichikanakwaniritsidwa. (Yes. 55:11) Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anayamba nthawi yomweyo kuvutika chifukwa cha uchimowo, Mulungu anawalola kubereka ana omwe anali ndi mwayi wodzalandira madalitso. Choncho pa tsiku lenilenilo limene anachimwa, zinali ngati Adamu ndi Hava anafa pa maso pa Mulungu. Komanso tinganene kuti anafadi pa tsikulo chifukwa anamwalira pasanathe “tsiku” limodzi la zaka 1,000.—2 Pet. 3:8.

8, 9. Kodi uchimo wa Adamu unakhudza bwanji ana ake? (Onani chithunzi patsamba 23.)

8 Kodi uchimo wa Adamu ndi Hava unakhudza bwanji ana awo? Lemba la Aroma 5:12 limafotokoza kuti: “Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” Mtumwi Paulo ananenanso kuti: “Mwa kusamvera kwa munthu mmodziyo, ambiri anakhala ochimwa.” (Aroma 5:19) Woyamba kumwalira anali Abele, yemwe anali wokhulupirika. (Gen. 4:8) Kenako ana ena a Adamu ndiponso zidzukulu zake, anadzakalamba n’kufa. Choncho uchimo ndi imfa zinakhala ngati adani omwe anthu sangathe kuwathawa. Sitingathe kufotokoza mmene Adamu anapatsira ana ake uchimo ndi imfa koma chimene tikudziwa n’chakuti aliyense amabadwa ndi uchimo basi.

9 Baibulo limafotokoza kuti uchimo ndi imfa zili ngati “chophimba chimene chikuphimba anthu onse, ndi nsalu imene yakuta mitundu yonse.” (Yes. 25:7) Tingati anthu onse akutiridwa munsalu kapena kuti chophimba chimenechi. Choncho chifukwa cha Adamu, anthu onse amafa. (1 Akor. 15:22) Funso limene tonsefe tingakhale nalo ndi limene Paulo anafunsa lakuti: “Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi?” Kodi panali munthu amene akanamupulumutsa? *Aroma 7:24.

UCHIMO NDI IMFA ZIDZAWONONGEDWA

10. (a) Kodi ndi malemba ati amene amasonyeza kuti Yehova adzawononga imfa imene tatengera kwa Adamu? (b) Kodi malembawa amasonyeza chiyani za Yehova ndi Mwana wake?

10 Yehova ndi amene akanapulumutsa Paulo. Paja Yesaya atangotchula za “chophimba,” analemba kuti: “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.” (Yes. 25:8) Bambo amafunitsitsa kuthetsa mavuto a ana ake ndiponso kupukuta misozi yawo. Nayenso Yehova adzasangalala kwambiri kuwononga imfa imene tinatengera kwa Adamu. Koma sadzachita yekha zimenezi. Paja lemba la 1 Akorinto 15:22 limati: “Mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” Paulo atafunsa kuti: “Ndani adzandipulumutse?” ananenanso kuti: “Mulungu adzatero kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:25) Choncho chikondi chimene chinachititsa Yehova kulenga anthu sichinazirale pamene Adamu ndi Hava anachimwa. Komanso Mwana wa Mulungu  amene anamuthandiza kulenga Adamu ndi Hava sanasiye kusangalala kwambiri ndi ana awo. (Miy. 8:30, 31) Koma kodi akanawapulumutsa bwanji?

11. Kodi Mulungu anachita zotani pofuna kuthandiza anthu?

11 Anthufe tinatengera uchimo kwa Adamu ndipo timafa chifukwa cha chilango chimene Mulungu anapereka. (Aroma 5:12, 16) Baibulo limati: “Mwa uchimo umodzi anthu kaya akhale amtundu wotani anaweruzidwa kukhala ochimwa.” (Aroma 5:18) Kodi Yehova akanachotsa bwanji chiweruzochi popanda kuphwanya mfundo zake za chilungamo? Yankho lake lili m’mawu a Yesu akuti: ‘Mwana wa munthu anabwera kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.’ (Mat. 20:28) Apa Yesu anasonyeza kuti anabwera padzikoli n’kudzapereka moyo wake wangwiro monga dipo. N’chifukwa chiyani tinganene kuti pamenepa mfundo za Mulungu za chilungamo zinatsatiridwa?—1 Tim. 2:5, 6.

12. Kodi Mulungu anatani kuti dipo likhale lokwanira ndendende?

12 Cholinga cha Yehova chinali choti dzikoli lidzaze ndi ana angwiro a Adamu. Chifukwa chokonda Yehova komanso anthu, Yesu anapereka moyo wake. Yesu anali wangwiro, ngati mmene Adamu analili asanachimwe. Choncho, Moyo umene anaperekawo unali wofanana ndendende ndi umene Adamu anataya. Kenako Yehova anaukitsa mwana wakeyo kuti akakhalenso kumwamba. (1 Pet. 3:18) Potsatira mfundo zake za chilungamo, Yehova analandira dipo la Yesu kuti awombole ana a Adamu n’kuwapatsa mwayi woti adzakhalenso ndi moyo wangwiro umene Adamu anatayawo. Tinganene kuti Yesu analowa m’malo mwa Adamu. N’chifukwa chake Paulo anafotokoza kuti: “Zinachita kulembedwa kuti: ‘Munthu woyambirira, Adamu, anakhala munthu wamoyo.’ Adamu womalizira anakhala mzimu wopatsa moyo.”—1 Akor. 15:45.

Abele anali woyamba kumwalira ndipo adzaukitsidwa chifukwa cha dipo la Yesu (Onani ndime 13)

13. Kodi “Adamu womalizira” adzathandiza bwanji akufa?

13 Nthawi idzafika yoti “Adamu womalizira” athandize anthu monga “mzimu wopatsa moyo.” Ana ambiri a Adamu anamwalira. Choncho adzayenera kuukitsidwa kapena kupatsidwanso moyo padzikoli.—Yoh. 5:28, 29.

14. Kodi Yehova wachita chiyani kuti athu adzamasulidwe ku uchimo umene tinatengera kwa Adamu?

14 Kodi Yehova wachita chiyani kuti anthu adzamasulidwe ku uchimo? Iye wakhazikitsa Ufumu ndipo olamulira ake ndi “Adamu womalizira” limodzi ndi anzake ena ochokera padzikoli. (Werengani Chivumbulutso 5:9, 10.) Olamulira anzake a Yesu kumwambako ndi anthu oti amadziwa bwino vuto lokhala ochimwa. Ndiyeno kwa zaka 1,000 adzathandiza anthu padzikoli kuti asinthe n’kukhala angwiro.—Chiv. 20:6.

15, 16. (a) Kodi ndi imfa iti imene idzawonongedwa ndipo zimenezi zidzachitika liti? (b) Malinga ndi 1 Akorinto 15:28, kodi Yesu adzachita chiyani?

15 Pa mapeto pa zaka 1,000, anthu omvera adzakhala opanda mavuto onse amene anabwera chifukwa cha kusamvera kwa Adamu. Paja Baibulo limati: “Monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo. Koma aliyense pamalo pake: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyambirira, kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake. Ndiyeno pa mapeto pake, adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake, atathetsa maboma onse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse. Pakuti ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Imfa nayonso, monga mdani womalizira,  idzawonongedwa.” (1 Akor. 15:22-26) Imfa imene idzawonongedwa ndi imene tinatengera kwa Adamu. Pa nthawi imeneyo, chophimba chimene chakuta anthu onse chidzachotsedwa ndipo sichidzakhalaponso.—Yes. 25:7, 8.

16 Mtumwi Paulo anamaliza mawu akewa ponena kuti: “Zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwanayonso adzadziika pansi pa amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.” (1 Akor. 15:28) Pa nthawiyo, cholinga cha ulamuliro wa Khristu chidzakhala chitakwaniritsidwa. Ndiyeno iye adzasangalala kubwezera ulamuliro wake kwa Yehova atamaliza kuthandiza anthu onse kuti akhale angwiro.

17. N’chiyani chidzachitikire Satana?

17 Koma kodi Satana amene anayambitsa mavuto onsewa adzangomusiyasiya? Yankho la funso limeneli tingalipeze pa Chivumbulutso 20:7-15. Choyamba, Satana adzaloledwa kuti ayese anthu angwiro komaliza. Kenako Mdyerekeziyo limodzi ndi anthu amene adzamutsatire adzawonongedwa kwamuyaya ndipo imeneyi imatchedwa “imfa yachiwiri.” (Chiv. 21:8) Imfa imeneyi sidzawonongedwa chifukwa chakuti anthu amene adzaphedwe ndi imfayi sadzakhalanso ndi moyo mpaka kalekale. Koma anthu amene amakonda Mulungu ndiponso kumutumikira sayenera kuopa imfa ‘yachiwiriyi’ chifukwa sidzawakhudza.

18. Kodi ntchito imene Mulungu anapatsa Adamu idzakwaniritsidwa bwanji?

18 Pa nthawiyo, anthu angwiro adzakhala oyenerera pa maso pa Yehova kuti alandire moyo wosatha ndipo sadzakhala ndi mdani wina aliyense. Ntchito imene Adamu anapatsidwa idzakwaniritsidwa ngakhale kuti iye sadzakhalapo. Ana ake adzadzaza dzikoli ndipo adzaliyang’anira n’kumasangalala ndi zamoyo zonse. Tiyeni tonse tiziyamikira kwambiri zimene Mulungu adzachite powononga imfa yomwe ndi mdani wathu womalizira.

^ ndime 9 Pa nkhani ya zimene asayansi akuchita kuti amvetse chifukwa chake timakalamba n’kufa, buku lakuti Insight on the Scriptures limati: “Iwo amalephera kuzindikira kuti Mlengi wathu ndi amene anapereka chilango cha imfa. Choncho n’zosatheka kuti amvetse zimene zimachitika.”—Voliyumu 2, tsamba 247.