Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Makolo, Muzisamalira Bwino Ana Anu

Makolo, Muzisamalira Bwino Ana Anu

“Uyenera kudziwa bwino maonekedwe a ziweto zako.”—MIY. 27:23.

1, 2. (a) Kodi abusa a ku Isiraeli ankayenera kuchita chiyani? (b) Kodi makolo amafanana bwanji ndi abusa?

NTCHITO yoweta nkhosa ku Isiraeli sinali yophweka. Abusa ankafunika kugwira ntchito pa nyengo yotentha komanso yozizira kwambiri. Iwo ankayenera kuteteza nkhosa kuti zisagwidwe kapena kubedwa. Ankayendera nkhosa zawo pafupipafupi n’kumathandiza zimene zikudwala kapena zavulazidwa. Iwo ankasamalira kwambiri ana a nkhosazo chifukwa amakhala opanda mphamvu.—Gen. 33:13.

2 Nawonso makolo achikhristu ayenera kusamalira ana awo ngati abusa abwino. Iwo ali ndi udindo wolera ana “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Udindo umenewu si wophweka. Ana amalimbana ndi mabodza a m’dziko la Satanali komanso zilakolako zawo zoipa. (2 Tim. 2:22; 1 Yoh. 2:16) Ngati muli ndi ana, kodi mungawathandize bwanji? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene mungachite. Zinthu zake ndi izi: Kuwadziwa bwino, kuwadyetsa bwino ndiponso kuwatsogolera.

 MUZIWADZIWA BWINO

3. Kodi makolo angatsatire bwanji lemba la Miyambo 27:23?

3 M’busa wabwino amayang’anitsitsa nkhosa iliyonse kuti adziwe ngati ili bwinobwino. Inunso makolo, muyenera kudziwa bwino ana anu. Paja Baibulo limati: “Uyenera kudziwa bwino maonekedwe a ziweto zako.” (Miy. 27:23) Kuti zimenezi zitheke, muyenera kuganizira zochita za ana anu, zimene amaganiza komanso mmene akumvera mumtima mwawo. Kodi mungadziwe bwanji zonsezi? Chofunika ndi kucheza nawo pafupipafupi.

4, 5. (a) Kodi makolo angatani kuti ana azimasuka nawo? (Onani chithunzi patsamba 17.) (b) Kodi inuyo mumachita zotani kuti ana anu azimasuka nanu?

4 Ana akayamba kukula, makolo ena amavutika kulankhula nawo. Nthawi zina, anawo safuna kucheza ndi makolo awo ndipo amachita manyazi kufotokoza zimene zili mumtima mwawo. Kodi izi n’zimene ana anu amachita? Ndiye mungawathandize bwanji? Si bwino kuwakakamiza kuti afotokoze maganizo awo. Chofunika n’kupeza nthawi yocheza nawo basi. (Deut. 6:6, 7) Muyenera kuyesetsa kuti muzichitira limodzi zinthu zina. Ndi bwino kungopeza nthawi yopita nawo koyenda, kusewera nawo kapena kugwira nawo ntchito zina zapakhomo. Pochita zinthu ngati zimenezi, achinyamatawo akhoza kumasuka n’kufotokoza zamumtima mwawo.

5 Koma bwanji ngati mwanayo sakumasukabe? Apa tsopano m’pofunika kuyesa njira zina. Mwachitsanzo, m’malo mofunsa kuti: “Zakuyendera bwanji lero?” mukhoza kungoyamba kufotokoza zimene zakuchitikirani inuyo pa tsikulo. Mwina nayenso akhoza kufotokoza zimene zamuchitikira. Kuti mudziwe maganizo a mwana wanu pa nkhani inayake, ndi bwino kumufunsa mwanzeru. Mwina mungamupemphe kuti anene zimene anzake amaganiza pa nkhaniyo. Kenako mungamufunse malangizo amene angapereke kwa anzakewo.

6. Kodi makolo ayenera kuchitanso chiyani kuti ana awo azimasuka?

6 Komabe pali zinthu zina zofunikanso kuti ana azimasuka kukufotokozerani za mumtima mwawo. Makolo akamasonyeza kuti alibiretu mpata wocheza ndi ana, anawo samasuka kufotokoza mavuto awo. Komanso si bwino kungouza ana kuti, “Ngati pali vutotu uzimasuka kundiuza.” Muyenera kusonyeza kuti mumaganizira kwambiri mavuto awo komanso simudzawakalipira akakuuzani. Makolo ambiri amachita bwino pa nkhani imeneyi. Mwachitsanzo, mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Kayla, anati: “Ndimamasuka kuuza bambo anga chilichonse. Sandidula mawu kapena kundiweruza ayi. Amangomvetsera basi. Ndiyeno ndikamaliza, amandipatsa malangizo abwino kwambiri.”

7. (a) Kodi makolo angatani kuti azikambirana ndi ana awo momasuka nkhani zokhudza chibwenzi? (b) Kodi makolo angakwiyitse bwanji ana awo mosazindikira?

7 Pokambirana ndi ana anu nkhani zina zovutirapo, muyenera kukhala osamala. Mwachitsanzo, pokambirana nkhani ya chibwenzi, si bwino kumangowauza kuti osachita zakutizakuti. M’malomwake, muyenera kuwauza zoyenera kuchita pa nkhaniyo. Tiyerekeze kuti mwapita kukagula mankhwala. Ndiyeno papaketi ya mankhwalawo angolembapo zinthu zoopsa zimene zingachitike ngati mutamwa, osafotokoza ubwino wake. Kodi simungasiye mankhwalawo n’kuyang’ana ena? Ana anunso akhoza kuchita zimenezi. Ngati atabwera kudzakufunsani malangizo, ndiyeno inu n’kungoyamba kuwachenjeza mwamphamvu zinthu zosayenera kuchita, sangakumvereni. (Werengani Akolose 3:21.) Chofunika n’kukambirana nawo n’kuona mbali zonse za nkhaniyo. Mtsikana wina dzina lake Emily anati: “Pokambirana  ndi makolo anga nkhani ya chibwenzi sasonyeza kuti n’zoipa. Iwo amasonyeza kuti zimakhala zosangalatsa ukamadziwana ndi munthu n’cholinga choti udzakhale naye pa banja. Izi zathandiza kuti ndizikambirana nawo nkhaniyi momasuka. Choncho ndikangoyamba kugwirizana kwambiri ndi mnyamata ndidzawauza kuti andithandize maganizo.”

8, 9. (a) Kodi kumvetsera moleza mtima ana athu akamalankhula n’kothandiza bwanji? (b) Kodi kumvetsera bwino ana anu akamalankhula kwakuthandizani bwanji?

8 Malinga ndi zimene Kayla ananena, mungachite bwino kumvetsera moleza mtima mwana wanu akamalankhula. (Werengani Yakobo 1:19.) Mlongo wina, amene akulera yekha mwana wamkazi, anati: “Poyamba sindinkaleza mtima mwana wanga akamalankhula. Ndinkakonda kumudula mawu. Nthawi zina ndinkakhala nditatoperatu koma pena ndinkangofuna kuti asandivutitse. Panopa ndasintha ndipo mwana wangayo wasinthanso. Nthawi zambiri amandimvera.”

Muziwamvetsera kuti muwadziwe bwino(Onani ndime 3 mpaka 9)

9 Zoterezi zinachitikiranso bambo wina dzina lake Ronald. Iye anati: “Mwana wanga atangondiuza kuti ali pa chibwenzi ndi mnyamata wina kusukulu ndinakwiya koopsa. Koma kenako ndinaganizira za kuleza mtima komanso kulolera kwa Yehova. Ndiyeno ndinaona kuti ndi bwino kulola mwana wangayo kufotokoza maganizo ake ndisanapereke malangizo alionse. Zimenezi zinathandiza kwambiri. Aka kanali koyamba kumvetsa mmene mwana wangayo ankamvera mumtima mwake. Atamaliza, sizinandivute kumulankhula mokoma mtima. Ndinadabwa kuona kuti anamvetsera kwambiri malangizo anga. Ananena kuchokera mumtima kuti asiya zimene ankachitazo.” Kulankhula ndi ana anu pafupipafupi kumathandiza kuti mudziwe zimene zili mumtima mwawo. Izi zingachititse kuti muziwathandiza kwambiri akamasankha zochita. *

MUZIWADYETSA BWINO

10, 11. Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti asatengeke ndi zinthu zoipa?

10 M’busa wabwino amadziwa kuti nkhosa ikhoza kusochera. Mwina ingatengeke pang’onopang’ono ndi msipu wobiriwira n’kusiyana ndi zinzake. Nayenso mwana akhoza  kutengeka pang’onopang’ono ndi anzake kapena zosangalatsa zoipa. (Miy. 13:20) Kodi mungatani kuti zimenezi zisachitike?

11 Mukazindikira kuti ana anu ayamba khalidwe linalake losayenera muziwathandiza mwamsanga kuti akhale ndi makhalidwe abwino. (2 Pet. 1:5-8) Mungachite zimenezi pa Kulambira kwa Pabanja. Utumiki wa Ufumu wa October 2008 unati: “Mitu ya mabanja iyenera kukwaniritsa udindo umene Yehova anawapatsa poonetsetsa kuti akuphunzira Baibulo ndi banja lawo nthawi zonse.” Kodi mukugwiritsa ntchito nthawi ya Kulambira kwa Pabanja kuti muzisamalira bwino ana anu? Dziwani kuti ana amayamikira kwambiri mukamayesetsa kuwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.—Mat. 5:3; Afil. 1:10.

Muziwadyetsa bwino (Onani ndime 10 mpaka 12)

12. (a) Kodi achinyamata ena athandizidwa bwanji ndi Kulambira kwa Pabanja? (Onaninso bokosi lakuti “ Amayamikira.”) (b) Nanga inuyo mwathandizidwa bwanji ndi Kulambira kwa Pabanja?

12 Mtsikana wina dzina lake Carissa anafotokoza mmene Kulambira kwa Pabanja kwathandizira banja lawo. Iye anati: “Zimandisangalatsa kwambiri tikakhala limodzi n’kumakambirana. Tikamachita zimenezi timasangalala kwambiri ndiponso timakhala ogwirizana. Bambo anga amaona kuti Kulambira kwa Pabanja n’kofunika kwambiri ndipo salola kuti tiphonye. Zimenezi zimandilimbikitsa kwambiri ndipo zimandichititsa kuona kuti kulambirako ndi kofunika. Izi zimandithandizanso kuwalemekeza kwambiri monga bambo anga komanso m’busa wanga.” Mtsikana wina dzina lake Brittney anati: “Kulambira kwa Pabanja kwandithandiza kugwirizana kwambiri ndi makolo anga. Ndimaona kuti amafunitsitsa kudziwa zimene zikundivutitsa komanso amandikonda kwambiri. Kulambirako kumathandiza kuti banja lathu likhale lolimba komanso logwirizana.” Choncho kuti mukhale m’busa wabwino, muyenera kudyetsa ana anu makamaka pochita Kulambira kwa Pabanja. *

MUZIWATSOGOLERA BWINO

13. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti adzatumikire Yehova?

13 M’busa wabwino amatsogolera komanso kuteteza nkhosa zake. Nthawi zambiri amazitsogolera ku “msipu wobiriwira.” (Ezek. 34:13, 14) Nawonso makolo ayenera kutsogolera ana awo kuti adzakhale atumiki a Yehova. Ayenera kuwathandiza kukhala ndi maganizo amene wamasalimo anali nawo. Paja iye anati: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.” (Sal. 40:8) Ana amene ali ndi maganizo amenewa amadzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. Koma amafunika kuchita zimenezi akafika msinkhu wotha kusankha okha zochita ndiponso chifukwa choti akufunitsitsa kutumikira Yehova.

14, 15. (a) Kodi makolo ayenera kuthandiza ana awo kuchita chiyani? (b) N’chiyani chingachititse mwana kuoneka ngati akukayikira zimene amaphunzitsidwa?

14 Kodi mungatani ngati mwana wanu akuoneka kuti sakufuna kutumikira Yehova? Chofunika ndi kumuthandiza kuti azikonda Yehova komanso kuyamikira zonse zimene wamuchitira. (Chiv. 4:11) Akatero, adzatha kusankha yekha kuti azimutumikira.

15 Koma kodi mungatani ngati akuoneka kuti akukayikira zimene akuphunzira m’Baibulo? Kodi mungamuthandize bwanji kuzindikira kuti kutumikira Yehova n’kwabwino komanso kungamuchititse kukhala wosangalala kwambiri? Choyamba, muyenera kufufuza zimene zikumuchititsa kukayikira. Kodi n’zoona kuti mwanayo sagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo kapena vuto ndi  loti satha kulimba mtima kuti afotokozere anzake zimene amakhulupirira? Kodi amakayikiradi zoti mfundo za Yehova n’zothandiza kapena vuto ndi loti amasalidwa chifukwa chosiyana ndi anzake?

Muziwatsogolera bwino(Onani ndime 13 mpaka 18)

16, 17. Kodi makolo angathandize bwanji ana kuti azikonda kutumikira Yehova?

16 Kaya vuto n’chiyani, mukhoza kuthandiza mwana wanu kuti asamakayikire zimene amaphunzira. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Makolo ena amakambirana ndi mwana wawo mafunso ngati awa: “Kodi umaona kuti kukhala Mkhristu kuli ndi ubwino uti? Nanga mavuto ake ndi ati? Kodi umaona kuti mavutowo ndi ochuluka kuposa zinthu zabwino zimene timapeza panopa komanso zimene tidzapeze m’tsogolo? N’chifukwa chiyani ukutero?” Pofunsa mafunsowa musachite kumupanikiza ngati kuti ndinu wapolisi. Mukhoza kuwasintha pena ndi pena kuti muwafunse mokoma mtima komanso m’njira yosangalatsa. Ana ena angakonde kulemba maganizo awo papepala. Mwina mbali ina angalembe ubwino wokhala Mkhristu mbali ina n’kulemba mavuto ake. Akaona zimene alembazo akhoza kumvetsa mavuto awo n’kudziwa zoyenera kuchita. Mwina mungakambirane nayenso lemba la Maliko 10:29, 30. Akhristufe timadziwa kuti m’pofunika kuphunzira ndi anthu ena buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani komanso lakuti Khalanibe M’chikondi cha Mulungu. Ndiye kodi zingakhale bwino kusiya ana athu enieni osawaphunzitsa?

17 N’zoona kuti pa nthawi ina, ana anu adzayenera kusankha okha kutumikira Mulungu kapena ayi. Koma musaiwale kuti mtima wa mnzako ndi tsidya lina choncho mfundo zimene mumakhulupirira sizingatsetsereke zokha n’kukalowa mumtima mwa anawo. Pamafunika kuchita khama kuti azikonda kutumikira Yehova. (Miy. 3:1, 2) Ngati mwana wanu akuoneka kuti sakufuna kutumikira Yehova, mwina mungayese kukambirana naye mfundo zoyambirira za m’Baibulo. M’thandizeni kuti azidzifunsa mafunso ngati awa: “N’chiyani chimanditsimikizira kuti Mulungu aliko? Nanga n’chiyani chimandichititsa kukhulupirira kuti Mulungu amandikonda kwambiri? Kodi ndimakhulupiriradi kuti kutsatira mfundo za Yehova kungandithandize?” Kuti mukhale m’busa wabwino, muyenera kutsogolera ana anu moleza mtima n’kuwathandiza kuzindikira zoti kutumikira Yehova n’kwabwino kwambiri. *Aroma 12:2.

18. Kodi makolo angatsanzire bwanji Yehova, yemwe ndi M’busa Wamkulu?

18 Tonsefe timafunitsitsa kutsanzira Yehova, yemwe ndi M’busa Wamkulu. (Aef. 5:1; 1 Pet. 2:25) Taona kuti makolo afunika kudziwa bwino ana awo ndiponso kuwatsogolera kuti adzalandire madalitso amene Yehova wawasungira. Choncho yesetsani kukhala abusa abwino n’kumathandiza ana anu kuti azikonda kutumikira Yehova.

^ ndime 12 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Kulambira kwa Pabanja N’kofunika Kwambiri Kuti Tidzapulumuke” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2009, tsamba 29 mpaka 31.