Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukuyenda Limodzi ndi Gulu la Yehova?

Kodi Mukuyenda Limodzi ndi Gulu la Yehova?

“Maso a Yehova ali pa olungama.”—1 PET. 3:12.

1. Kodi ndi gulu liti lomwe linalowa m’malo mwa Aisiraeli? (Onani chithunzi pamwambapa.)

YEHOVA ndi yemwe anakhazikitsa mpingo wachikhristu m’nthawi ya atumwi komanso kubwezeretsa kulambira koona m’masiku otsiriza ano. Monga tinaonera m’nkhani yapitayo, Aisiraeli atapanduka, Mulungu anasankha Akhristu oyambirira kukhala gulu la anthu odziwika ndi dzina lake. Mulungu ankadalitsa gulu lake latsopanoli ndipo anapulumutsa Akhristuwo pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E. (Luka 21:20, 21) Zimene zinachitika m’nthawiyo n’zofanana ndi zomwe zidzachitikire anthu a Yehova masiku ano. Posachedwapa, dziko la Satanali liwonongedwa koma gulu la Mulungu lidzapulumuka. (2 Tim. 3:1) Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?

2. (a) Kodi Yesu ananena zotani pa nkhani ya chisautso chachikulu? (b) Kodi chisautsochi chidzayamba bwanji?

2 Ponena za kukhalapo kwake komanso mapeto a dziko loipali, Yesu anati: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko  mpaka tsopano, ndipo sichidzachitikanso.” (Mat. 24:3, 21) Chisautsochi chidzayamba pamene Yehova adzagwiritsa ntchito maulamuliro andale kuti awononge “Babulo Wamkulu” amene akuimira zipembedzo zonse zonyenga. (Chiv. 17:3-5, 16) Kodi kenako kudzachitika zotani?

ZOMWE SATANA ADZACHITE ZIDZAYAMBITSA ARAMAGEDO

3. Zipembedzo zonyenga zikadzawonongedwa, kodi n’chiyani chidzachitikire anthu a Yehova?

3 Zipembedzo zonyenga zikadzawonongedwa, Satana limodzi ndi anthu ake m’dzikoli adzaukira atumiki a Yehova. Ponena za “Gogi wa kudziko la Magogi,” Malemba ananeneratu kuti: “Iwe udzabwera m’dzikolo ngati mphepo yamkuntho. Iweyo, magulu ako onse a asilikali, pamodzi ndi anthu ambiri a mitundu ina, mudzaphimba dzikolo ngati mitambo.” Popeza Mboni za Yehova zilibe asilikali ndipo ndi anthu amtendere kwambiri, iwo adzaoneka osavuta kuwagonjetsa. Koma akadzangoyesa kuwaukira, zidzawavuta.—Ezek. 38:1, 2, 9-12.

4, 5. Kodi Yehova adzachita chiyani Satana akadzayesa kuwononga anthu ake?

4 Kodi Mulungu adzachita chiyani Satana akadzayesa kuwononga anthu ake? Yehova adzasonyeza kuti ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse ndipo sadzalola zimenezi. Atumiki ake akaukiridwa, iye amaona kuti oukirawo akumuyamba. (Werengani Zekariya 2:8.) Choncho nthawi yomweyo, Atate wathu wakumwamba adzalowererapo kuti atipulumutse. Ndipo dziko la Satanali lidzawonongedwa pa Aramagedo, yomwe ndi ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’—Chiv. 16:14, 16.

5 Ulosi wa m’Baibulo umanena za Aramagedo kuti: “‘Yehova akufuna kuimba mlandu mitundu ya anthu. Iye mwini adzalimbana ndi anthu onse powaweruza. Anthu oipa adzawapha ndi lupanga,’ watero Yehova. Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Taonani! Tsoka likuyenda kuchokera mu mtundu wina kupita mu mtundu wina, ndipo mkuntho wamphamvu udzafika kuchokera kumalekezero a dziko lapansi. Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kufikanso kumalekezero ena a dziko lapansi. Sadzawalira maliro, kuwasonkhanitsa pamodzi, kapena kuwaika m’manda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.’” (Yer. 25:31-33) Pa Aramagedo dziko la Satanali lidzawonongedwa koma anthu amene ali m’gulu la Yehova adzapulumuka.

GULU LA YEHOVA LIKUKULA KWAMBIRI MASIKU ANO

6, 7. (a) Kodi anthu amene ali ‘m’khamu lalikulu’ akuchokera kuti? (b) Kodi gulu la Yehova lakula bwanji m’zaka za posachedwapa?

6 Padzikoli, zinthu zikuyenda bwino kwambiri m’gulu la Yehova chifukwa chakuti muli anthu amene Mulungu amawakonda. Paja Baibulo limanena kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo.” (1 Pet. 3:12) Ena mwa anthu olungamawa ndi amene amatchedwa “khamu lalikulu” ndipo adzapulumuka pa ‘chisautso chachikulu.’ (Chiv. 7:9, 14) Chochititsa chidwi n’chakuti pofotokoza za anthuwa, Baibulo silimangonena kuti “khamu,” koma limati “khamu lalikulu.” Izi zikutanthauza kuti ndi anthu ambirimbiri. Kodi inuyo mumafatsa n’kumayerekezera muli m’gulu la anthu opulumuka ‘chisautso chachikulu’?

7 Kodi anthu amene ali m’khamu lalikululi akuchokera kuti? Ntchito ina imene Yesu analosera kuti idzachitika m’nthawi ya kukhalapo kwake ndi imene ikuthandiza kuti anthuwa asonkhanitsidwe. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:14) Ntchito imeneyi ndi  imene gulu la Yehova likugwira kwambiri padziko lonse m’masiku otsiriza ano. Ndiyeno yathandiza anthu mamiliyoni ambiri kuti aphunzire kulambira Yehova “motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.” (Yoh. 4:23, 24) Mwachitsanzo, kuyambira m’chaka cha utumiki cha 2003 mpaka 2012, anthu oposa 2,707,000 anabatizidwa posonyeza kuti adzipereka kwa Yehova. Panopa, padziko lonse pali abale ndi alongo oposa 7,900,000 ndipo anthu ena mamiliyoni ambiri amasonkhana nawo makamaka pa mwambo wa Chikumbutso. Ndipo chaka chilichonse khamu lalikululi likuwonjezeka. Koma sitidzitama tikaona kuwonjezeka kwa anthuwa chifukwa chodziwa kuti ‘Mulungu ndi amene amakulitsa.’—1 Akor. 3:5-7.

8. N’chifukwa chiyani anthu akuwonjezeka kwambiri m’gulu la Yehova?

8 Anthu akuwonjezeka kwambiri m’gulu la Yehova chifukwa chakuti Yehovayo akulidalitsa. (Werengani Yesaya 43:10-12.) Baibulo linalosera kale zimenezi ponena kuti: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” (Yes. 60:22) M’mbuyomo, odzozedwa amene anali padzikoli anali ngati “wamng’ono” koma chiwerengero chawo chinawonjezeka pamene anthu ena odzozedwa anayamba kulowa m’gulu la Mulungu. (Agal. 6:16) Madalitso a Yehovawa achititsanso kuti khamu lalikulu lisonkhanitsidwe, ndipo gululi likukulabe.

ZIMENE YEHOVA AMAFUNA KUTI TIZICHITA

9. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzaone zinthu zimene Baibulo limalonjeza?

9 Kaya ndife odzozedwa kapena a khamu lalikulu, tikuyembekezera zinthu zosangalatsa zimene talonjezedwa m’Baibulo. Koma kuti tidzaone zinthuzo, tiyenera kuchita zimene Mulungu amafuna. (Yes. 48:17, 18) Nawonso Aisiraeli anayenera kumvera Chilamulo cha Mose. Cholinga chimodzi chimene Mulungu anaperekera Chilamulocho chinali choti ateteze Aisiraeli. Iye anapereka malamulo pa nkhani monga kugonana, malonda, kusamalira ana ndiponso mmene ayenera kuchitira zinthu ndi anzawo. (Eks. 20:14; Lev. 19:18, 35-37; Deut. 6:6-9) Ifenso timapindula tikamatsatira malamulo a Mulungu ndipo sitiona kuti kuchita zimene Mulungu amafuna ndi kovuta. (Werengani 1 Yohane 5:3.) Mofanana ndi Aisiraeli, tikamatsatira malamulo ndi mfundo za Yehova timatetezedwa komanso timakhala ndi “chikhulupiriro cholimba.”—Tito 1:13.

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kupeza nthawi yophunzira Baibulo ndiponso yopanga Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse?

10 Mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova ikuyenda mosabwerera m’mbuyo. Mwachitsanzo, nthawi zonse tikupitiriza kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo. Zimenezi n’zomveka chifukwa Baibulo limati: “Njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.” (Miy. 4:18) Koma tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikudziwa bwino mmene gulu likufotokozera mfundo za m’Baibulo masiku ano? Kodi ndimawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku? Kodi ndimakondadi kuwerenga mabuku athu? Kodi ine ndi banja langa timachita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse?’ Ambirife sitiona kuti kuchita zinthuzi n’kovuta. Apa nkhani ndi yongopeza nthawi yochita zinthuzo. Panopa chisautso chachikulu chikuyandikira kwambiri. Choncho tiyenera kuphunzira Baibulo mozama, kutsatira zimene taphunzira ndiponso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova.

11. Kodi zikondwerero zakale ndiponso misonkhano ya masiku ano zathandiza bwanji anthu a Mulungu?

11 Gulu la Yehova limatifunira zabwino, choncho limatilimbikitsa kutsatira malangizo  a mtumwi Paulo akuti: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.” (Aheb. 10:24, 25) Zikondwerero zimene Aisiraeli ankachita chaka ndi chaka ndiponso misonkhano ina zinkawathandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Komanso zochitika zina zapadera monga Chikondwerero cha Misasa chimene anachita m’nthawi ya Nehemiya zinali zosangalatsa kwambiri. (Eks. 23:15, 16; Neh. 8:9-18) Ifenso timapindula ndi misonkhano yathu yampingo ndiponso ikuluikulu. Tiyeni tiziyesetsa kupezeka ndi kupindula ndi misonkhano imeneyi kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba.—Tito 2:2.

12. Kodi tiyenera kuona bwanji ntchito yolalikira za Ufumu?

12 Ife amene tili m’gulu la Mulungu tili ndi mwayi wogwira nawo “ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu.” (Aroma 15:16) Ntchitoyi ndi “yopatulika” choncho tikamaigwira, timakhala “antchito anzake” a Yehova, yemwe ndi “Woyera.” (1 Akor. 3:9; 1 Pet. 1:15) Kulalikira uthenga wabwino kumathandiza kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. Ndipotu ndi mwayi wamtengo wapatali kwambiri kugwira ntchito yolalikira ‘uthenga wabwino waulemerero wochokera kwa Mulungu wachimwemwe.’—1 Tim. 1:11.

13. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhalebe ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso moyo?

13 Mulungu akufuna kuti tizikhala ndi chikhulupiriro cholimba, choncho amatilimbikitsa kukhala okhulupirika kwa iye ndiponso kuchita zambiri m’gulu lake. Mose anauza Aisiraeli kuti: “Ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero pamaso panu. Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu. Choncho inuyo ndi mbadwa zanu musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo. Musankhe moyo mwa kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake ndi kum’mamatira, chifukwa iye ndiye wokupatsani moyo ndi masiku ambiri kuti mukhale panthaka imene Yehova analumbira kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzawapatsa.” (Deut. 30:19, 20) Kuti tikhalabe ndi moyo, tiyenera kuchita zimene Yehova amafuna, kumukonda ndiponso kukhala okhulupirika kwa iye.

14. Kodi m’bale wina anaona bwanji gulu la Mulungu?

14 M’bale Pryce Hughes, yemwe anaphunzira choonadi chaka cha 1914 chisanafike, anakhala wokhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake kwa moyo wake wonse. Pofotokoza mbiri ya moyo wake ananena kuti chinthu chofunika kwambiri chimene anaphunzira chinali kufunika koyenda limodzi ndi gulu la Yehova osati kudalira nzeru za anthu. Izi zinamuthandiza kukhalabe wokhulupirika. M’bale Hughes ananena kuti munthu ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi gulu la Yehova ngati akufuna kuti Yehovayo azimudalitsa.

PITIRIZANI KUYENDA LIMODZI NDI GULU LA MULUNGU

15. Perekani chitsanzo cha m’Malemba chosonyeza kuti tiyenera kutsatira ngati gulu lasintha kafotokozedwe ka mfundo zina za m’Baibulo.

15 Ngati tikufuna kuti Yehova azitikonda komanso kutidalitsa, tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi gulu lake. Tiyeneranso kutsatira ngati gululo lasintha kafotokozedwe ka mfundo zina za m’Baibulo. Kumbukirani kuti Yesu ataphedwa, panali Akhristu achiyuda ambiri amene anali odzipereka pa nkhani yotsatira Chilamulo ndipo anavutika kuti asiye kuchitsatira. (Mac. 21:17-20) Koma Paulo anawathandiza kwambiri powalembera kalata. Ndipo iwo anamvetsa kuti machimo awo sanakhululukidwe chifukwa cha “nsembe  zimene zimaperekedwa malinga ndi Chilamulo” koma “kudzera m’thupi la Yesu Khristu loperekedwa nsembe kamodzi kokha.” (Aheb. 10:5-10) Mosakayikira, Akhristu achiyudawo anasintha mmene ankaonera zinthu ndipo anayamba kuyenda limodzi ndi gulu la Yehova. Ifenso tiyenera kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama. Komanso gulu likasintha kafotokozedwe ka malemba ena kapena zinthu zokhudza ntchito yolalikira, tiyenera kutsatira modzichepetsa.

16. (a) Kodi anthu adzasangalala ndi madalitso ati m’dziko latsopano? (b) Kodi n’chiyani chakusangalatsani pa zinthu zimene zidzachitike m’dziko latsopano?

16 Yehova amadalitsa atumiki ake omwe amakhalabe okhulupirika kwa iye komanso ku gulu lake. Akhristu odzozedwa adzakhala ndi mwayi wokalamulira ndi Khristu kumwamba. (Aroma 8:16, 17) Anthu omwe ali ndi chiyembekezo chokhala padziko lapansi adzasangalala kwambiri ndi moyo m’Paradaiso. Monga atumiki a Yehova, tili ndi mwayi wapadera wouza ena za dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. (2 Pet. 3:13) Lemba la Salimo 37:11 limati: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Anthu “adzamanga nyumba n’kukhalamo” ndipo iwo adzapindula “ndi ntchito ya manja awo.” (Yes. 65:21, 22) Sipadzakhalanso kuponderezana, umphawi komanso njala. (Sal. 72:13-16) Babulo Wamkulu sadzasocheretsanso anthu chifukwa adzakhala atawonongedwa. (Chiv. 18:8, 21) Anthu amene anamwalira adzaukitsidwa ndipo adzapatsidwa mwayi wokhala ndi moyo wosatha. (Yes. 25:8; Mac. 24:15) Anthu amene adzipereka kwa Yehova akuyembekezera zinthu zosangalatsa kwambiri. Kuti tidzalandire nawo madalitso amenewa, tiyenera kupitiriza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova komanso kuyendera limodzi ndi gulu lake.

Muziyerekezera muli m’Paradaiso (Onani ndime 16)

17. Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani pa nkhani ya kulambira Yehova komanso kumvera gulu lake?

17 Pamene mapeto ayandikira, tiyeni tiziyesetsa kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso tiziyamikira zimene Mulungu wachita potithandiza kuti tizimulambira moyenerera. Mmenemu ndi momwe Davide anamvera. Iye anaimba kuti: “Chinthu chimodzi chimene ndapempha kwa Yehova, chimenecho ndi chimene ndimachikhumba, n’chakuti, ndikhale m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kuti ndione ubwino wa Yehova, komanso kuti ndiyang’ane kachisi wake moyamikira.” (Sal. 27:4) Tiyeni tonse tipitirize kukhala okhulupirika kwa Mulungu komanso kuyendera limodzi ndi gulu lake.