Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Chakudya Changa N’kuchita Chifuniro cha Mulungu’

‘Chakudya Changa N’kuchita Chifuniro cha Mulungu’

Kodi n’chiyani chimakusangalatsani kwambiri? Ena amasangalala ndi zinthu monga kukhala pa banja, kulera ana kapena kukhala pa ubwenzi wabwino ndi anthu ena. Ambirife timasangalala kudya chakudya limodzi ndi anzathu. Koma atumiki a Yehovafe timasangalala kwambiri ndi kuchita chifuniro cha Mulungu, kuphunzira Mawu ake komanso kulalikira uthenga wabwino.

M’nyimbo ina yotamanda Mlengi, Mfumu Davide anaimba kuti: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.” (Sal. 40:8) Davide ankasangalala kwambiri kuchita zimene Mulungu amafuna ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto ambiri. Koma pali anthu enanso amene ankasangalala kwambiri kutumikira Mulungu woona.

Mtumwi Paulo anasonyeza kuti mawu a pa Salimo 40:8 amanena za Mesiya kapena kuti Khristu. Iye analemba kuti: “Chotero pobwera m’dziko iye [Yesu] anati: ‘“Nsembe ndiponso zopereka simunazifune, koma munandikonzera thupi. Nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zamachimo simunazivomereze.” Ndiyeno ndinati, “Taonani! Ine ndabwera (mumpukutu munalembedwa za ine) kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.”’”—Aheb. 10:5-7.

Pamene Yesu anali padzikoli, ankasangalala kwambiri kuona chilengedwe, kucheza ndi anzake ndiponso kudya nawo limodzi. (Mat. 6:26-29; Yoh. 2:1, 2; 12:1, 2) Koma chimene chinkamusangalatsa kwambiri ndi kuchita chifuniro cha Atate wake. Iye anati: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yoh. 4:34; 6:38) Iye anathandizanso ophunzira ake kudziwa zimene zingawathandize kukhala osangalala. Ophunzirawo ankasangalala kwambiri kuuza ena uthenga wa Ufumu ndipo ankachita zimenezi mwakhama.—Luka 10:1, 8, 9, 17.

“PITANI MUKAPHUNZITSE ANTHU”

Yesu anauza otsatira ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.  Ndipo dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:19, 20) Kuti tichite zimenezi, timafunika kupita kukafufuza anthu kulikonse kumene angapezeke, kuchita maulendo obwereza komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Kugwira ntchito imeneyi kumasangalatsa kwambiri.

Chikondi chingatithandize kulalikirabe ngakhale pamene anthu sakumvetsera uthenga wathu

Kaya anthu amvetsere uthenga wathu kapena ayi, tiyenera kukhalabe osangalala tikamalalikira. N’chifukwa chiyani timapitirizabe kulalikira ngakhale anthu ena samvetsera uthenga wabwino? Timachita zimenezi chifukwa timadziwa kuti kugwira ntchitoyi kumasonyeza kuti timakonda Mulungu komanso anthu anzathu. Tizikumbukiranso kuti moyo wathu komanso wa anthu ena uli pa ngozi. (Ezek. 3:17-21; 1 Tim. 4:16) Tiyeni tikambirane mfundo zina zimene zathandiza anzathu kugwirabe ntchitoyi m’madera ovuta.

MUZIGWIRITSA NTCHITO MPATA ULIWONSE

Kugwiritsa ntchito mafunso oyenera kumathandiza. Tsiku lina mlongo wina dzina lake Amalia, anaona bambo wina akuwerenga nyuzi pamalo enaake. Iye anafunsa bamboyo ngati wapeza nkhani iliyonse yabwino m’nyuziyo. Bamboyo atayankha kuti sanapezemo, Amalia ananena kuti: “Ine ndiye ndakubweretseranitu nkhani yabwino ya Ufumu wa Mulungu.” Bamboyo anachita chidwi ndipo anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Amalia anayambitsa maphunziro a Baibulo atatu pamalo amenewo.

Mlongo winanso dzina lake Janice amakonda kulalikira kuntchito. Mlonda wina komanso mnzake wogwira naye ntchito atachita chidwi ndi nkhani ina ya m’magazini a Nsanja ya Olonda, Janice anawauza kuti akhoza kumawapatsa magazini mwezi uliwonse. Ananenanso zimenezi kwa munthu wina yemwe anachita chidwi ndi nkhani zosiyanasiyana za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Izi zinachititsa kuti mayi winanso kuntchitoko apemphe magazini. Janice anati: “Ndikuona kuti Yehova wandidalitsa kwambiri.” Patapita nthawi, Janice anali ndi anthu 11 amene ankawapatsa magazini mwezi uliwonse kuntchitoko.

MUZIONA KUTI ALIYENSE ANGATHE KUPHUNZIRA

Woyang’anira woyendayenda wina ananena kuti abale sayenera kungouza anthu mu utumiki kuti adzabweranso tsiku lina. M’malomwake, angachite bwino kufunsa anthu kuti: “Kodi mungakonde kuona mmene timaphunzirira Baibulo ndi anthu?” kapena kuti: “Kodi mungafune kuti ndidzabwere liti kuti tidzakambiranenso?” Woyang’anira woyendayendayu ananena kuti pa mlungu wapadera kumpingo wina, abale ndi alongo anayambitsa maphunziro a Baibulo okwana 44 pogwiritsa ntchito mafunso amenewa.

Komanso kubwerera msanga kwa anthu kumathandiza kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti kuchita zimenezi kumasonyeza kuti tikufunitsitsa  kuthandiza anthu kuti aziphunzira Baibulo. Mayi wina atafunsidwa chifukwa chake anayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova, anayankha kuti: “Ndinayamba chifukwa nthawi zonse iwo ankasonyeza kuti amandiganizira ndiponso kundikonda.”

Mukhoza kufunsa munthu kuti: “Kodi mungakonde kuona mmene timaphunzirira Baibulo ndi anthu?”

Mlongo wina dzina lake Madaí atangomaliza Sukulu ya Utumiki Waupainiya anayambitsa maphunziro 20 ndipo 5 anawapereka kwa anthu ena. Pa anthu amene ankaphunzira nawo, ambiri anayamba kusonkhana. N’chiyani chinamuthandiza kuyambitsa maphunziro ambiri chonchi? Sukuluyo inamuthandiza kudziwa kufunika koyesetsa kubwerera kwa anthu amene anamvetsera mpaka atawapezanso. Mlongo wina amene wathandiza anthu ambiri kuphunzira Baibulo anati: “Ndaona kuti kuchita khama pochita maulendo obwereza n’kofunika kuti tizithandiza anthu kudziwa Yehova.”

Kubwerera mwamsanga kwa anthu amene akufuna kuphunzira Baibulo kumasonyeza kuti timawakonda

N’zoona kuti munthu ayenera kuchita khama kuti apange maulendo obwereza ndiponso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Komabe madalitso amene munthu amapeza ndi ambiri. Tikamachita khama mu utumiki, tikhoza kuthandiza anthu ena kuti akhale “odziwa choonadi molondola” n’kupulumuka. (1 Tim. 2:3, 4) Zimenezi zingatithandizenso kukhala osangalala kwambiri.