Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ufumu Umene Walamulira kwa Zaka 100 Umakukhudzani Bwanji?

Kodi Ufumu Umene Walamulira kwa Zaka 100 Umakukhudzani Bwanji?

“Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu, . . . Mfumu yamuyaya.—CHIV. 15:3.

1, 2. (a) Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani? (b) N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Ufumuwo udzabwera?

YESU KHRISTU anali paphiri lina pafupi ndi mzinda wa Kaperenao limodzi ndi ophunzira ake mu 31 C.E. Pa nthawiyo iye anawaphunzitsa kupemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere.” (Mat. 6:10) Masiku ano anthu ambiri amakayikira zoti Ufumuwo udzabweradi. Koma ife sitikayikira kuti Mulungu adzayankha mapemphero athu ochokera pansi pa mtima opempha kuti Ufumu wake ubwere.

2 Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumuwo pogwirizanitsa ana ake onse akumwamba ndiponso apadziko lapansi. Palibe chimene chingalepheretse cholinga cha Mulungu chimenechi. (Yes. 55:10, 11) Ndipotu panopa Yehova wayamba kale kukhala Mfumu. Umboni wake ndi zinthu zosangalatsa zimene zachitika m’zaka 100 zapitazi. Mulungu ali ndi anthu okhulupirika mamiliyoni ambiri ndipo akuwachitira zinthu zazikulu komanso zodabwitsa. (Zek. 14:9; Chiv. 15:3) N’zoona kuti Yehova anayamba kale kukhala Mfumu, koma zimenezi n’zosiyana ndi kubwera kwa Ufumu wa Mulungu umene Yesu anatiphunzitsa kuti tiziupempherera. Kodi ndi zosiyana m’njira iti, nanga ifeyo zikutikhudza bwanji?

MFUMU YOIKIDWA NDI YEHOVA INAYAMBA KUKONZA ZINTHU

3. (a) Kodi Yesu anaikidwa liti kukhala Mfumu ndipo zinachitikira kuti? (b) Kodi mungapereke umboni wotani wosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914? (Onani mawu a m’munsi.)

3 Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, Mulungu anayamba kuthandiza anthu ake kumvetsa ulosi umene Danieli analemba zaka zoposa 2,500 zapitazo. Ulosiwu umati: “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa  ku nthawi zonse.” (Dan. 2:44) Kwa zaka zambiri, Ophunzira Baibulo ankanena kuti chaka cha 1914 chidzakhala chapadera. Pa nthawiyo, anthu ambiri ankaganiza kuti zinthu ziyenda bwino moti munthu wina analemba kuti: “Mu 1914, anthu padzikoli ankaona kuti tsogolo lawo linali labwino kwambiri.” Koma ulosi wa m’Baibulo unakwaniritsidwa pamene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayambika chakumapeto kwa chakachi. Kenako padzikoli panayamba kuchitika zivomezi, miliri, njala komanso zinthu zina zimene zinakwaniritsa maulosi ena a m’Baibulo. Zonsezi zinapereka umboni wakuti Yesu Khristu anali atayamba kulamulira kumwamba mu 1914 monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. * Chifukwa choika Mwana wake kukhala Mfumu, tinganene kuti nayenso Yehova anakhala Mfumu m’njira yatsopano.

4. (a) Kodi Yesu anachita chiyani atangoikidwa kumene kukhala Mfumu? (b) Kodi kenako anayamba kuthandiza ndani?

4 Poyamba, Mfumu yoikidwa ndi Mulunguyo inayenera kumenya nkhondo ndi Satana, yemwe ndi Mdani wamkulu wa Atate wake. Yesu limodzi ndi angelo ake anachotsa Mdyerekezi ndi ziwanda zake kumwamba. Onse akumwamba anayamba kusangalala kwambiri koma padziko lapansi panayamba mavuto aakulu. (Werengani Chivumbulutso 12:7-9, 12.) Kenako Mfumuyi inayamba kuthandiza anthu ake padzikoli powayeretsa, kuwaphunzitsa ndiponso kusintha zinthu m’gulu lawo kuti azigwira bwino ntchito ya Mulungu. Tiyeni tikambirane zimene anthuwo anachita Yesu atawathandiza m’njira zitatu zimenezi. Tionanso zimene tingachite potsatira chitsanzo chawo chabwino.

MFUMU INAYERETSA ANTHU AKE OKHULUPIRIKA

5. Kodi n’chiyani chinachitika kuyambira m’chaka cha 1914 mpaka kumayambiriro kwa chaka cha 1919?

5 Yesu atachotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba, Yehova anamuuza kuti ayendere otsatira ake padziko lapansi ndi kuwayenga. Mneneri Malaki anafotokoza kuti zimenezi zikutanthauza kuwayeretsa mwauzimu. (Mal. 3:1-3) Pali umboni wosonyeza kuti zimenezi zinachitika m’chaka cha 1914 mpaka kumayambiriro kwa chaka cha 1919. * Choncho kuti tikhale m’banja la Yehova, tiyenera kukhala oyera. (1 Pet. 1:15, 16) Tiyenera kupewa kudetsedwa ndi ziphunzitso za zipembedzo zonyenga kapena ndale za m’dzikoli.

6. Kodi ndi ndani amene akutipatsa chakudya chauzimu, ndipo n’chifukwa chiyani chakudyachi n’chofunika kwambiri?

6 Kenako Yesu, monga Mfumu, anasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Kapolo ameneyu ali ndi udindo wopereka chakudya chauzimu kwa onse amene ali ‘m’gulu limodzi’ la nkhosa za Yesu. (Mat. 24:45-47; Yoh. 10:16) Kuyambira mu 1919, gulu laling’ono la abale odzozedwa lakhala likugwira mokhulupirika ntchito yaikuluyi yopereka chakudya kwa ‘antchito apakhomo.’ Chakudya chauzimu chimenechi chimatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Chimatithandizanso kukhala aukhondo komanso oyera pa nkhani ya kulambira kwathu, makhalidwe athu ndiponso zimene timaganiza. Chakudya chauzimuchi chimatiphunzitsa ndi kutithandiza kuti tizigwira kwambiri ntchito yofunika padziko lonse lapansi m’nthawi yathu ino. Kodi inuyo mukudya mokwanira chakudya chimenechi?

MFUMU IKUPHUNZITSA ANTHU AKE KUTI AZILALIKIRA PADZIKO LONSE

7. Kodi Yesu anayambitsa ntchito yofunika iti ali padzikoli, ndipo inayenera kuchitika mpaka liti?

7 Yesu atayamba utumiki wake padziko lapansi, anati: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Kwa zaka zitatu ndi hafu, ntchitoyi inali yofunika kwambiri pa moyo wa Yesu. Iye analangiza ophunzira ake kuti: “Pitani ndi kulalikira kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’” (Mat. 10:7) Yesu ataukitsidwa analosera kuti ophunzira ake adzalalikira uthengawu “mpaka kumalek ezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Iye anawalonjeza kuti adzawathandiza pa ntchitoyi mpaka m’masiku athu ano.—Mat. 28:19, 20.

8. Kodi Mfumu inalimbikitsa bwanji anthu ake kuti ayambe kugwira ntchito yolalikira?

8 Pofika m’chaka cha 1919, zinthu zinanso zokhudza ‘uthenga wabwino wa ufumu’ zinali zitayamba kukwaniritsidwa. (Mat. 24:14) Mfumu ya Ufumuwu inali itayamba kulamulira kumwamba ndiponso inali itasonkhanitsa ndi kuyeretsa gulu laling’ono la anthu ake padzikoli. Anthuwo anatsatira ndi mtima wonse malangizo a Yesu akuti: Lalikirani padziko lonse uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene wakhazikitsidwa. (Mac. 10:42) Mwachitsanzo, m’mwezi wa September mu 1922 anthu pafupifupi 20,000 amene anali ku mbali ya Ufumuwo anapezeka pa msonkhano wa mayiko mumzinda wa Cedar Point ku Ohio, m’dziko la United States. Tangoganizirani mmene iwo anasangalalira pamene M’bale Rutherford anakamba nkhani yakuti “Ufumu,” kenako n’kunena kuti: “Onani, Mfumu yayamba kale kulamulira ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza za ufumuwo. Choncho lengezani, lengezani, lengezani za Mfumu ndi ufumu wake.” Pa anthu amene anafika pa msonkhanowu, anthu 2,000 anamvera pempho limeneli poyenda mtunda wa makilomita 72 kuchokera pamalo a msonkhanowo kupita kukalalikira kunyumba ndi nyumba. Anachita zimenezi pa tsiku lapadera limene ankalitcha kuti “Tsiku la Utumiki.” M’bale wina amene analimbikitsidwa kwambiri pa msonkhanowu anati: “Sindidzaiwala pamene tinapemphedwa kulengeza Ufumu ndiponso mmene anthu onse anasonyezera kuti akufunadi kugwira ntchitoyi.” Anthu ena ambiri analimbikitsidwanso.

9, 10. (a) Kodi ndi sukulu ziti zimene zakhazikitsidwa kuti zizithandiza anthu olalikira Ufumu? (b) Kodi inuyo mwathandizidwa bwanji ndi maphunzirowa?

9 Pofika m’chaka cha 1922, panali anthu olengeza Ufumu oposa 17,000 m’mayiko 58. Koma iwo anafunika kuphunzitsidwa mmene angagwirire ntchitoyi. Pamene anali padziko lapansi, Yesu anapatsa ophunzira ake malangizo omveka bwino ofotokoza zimene ayenera kunena, kumene ayenera kukalalikira komanso mmene angachitire zimenezi. (Mat. 10:5-7; Luka 9:1-6; 10:1-11) Masiku anonso Yesu akuonetsetsa kuti anthu onse amene akugwira nawo ntchito yolalikirayi alandire malangizo ndiponso zonse zofunika kuti agwire bwino ntchitoyi. (2 Tim. 3:17) Yesu akuphunzitsa anthu ake utumiki umenewu kudzera mumpingo wake. Mwachitsanzo, akuwaphunzitsa pogwiritsa ntchito Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imene imachitika m’mipingo 111,000 padziko lapansi. Chifukwa cha sukulu imeneyi, anthu oposa 7 miliyoni athandizidwa kuti azilalikira ndiponso kuphunzitsa “anthu osiyanasiyana” mowafika pamtima.—Werengani 1 Akorinto 9:20-23.

10 Palinso sukulu zina zophunzitsa Baibulo zimene zakhazikitsidwa n’cholinga choti zizithandiza akulu  m’mipingo, apainiya, abale osakwatira, Akhristu apabanja, abale a m’Komiti ya Nthambi ndi akazi awo, oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo komanso amishonale. * Anthu ena amene anamaliza maphunziro m’Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja anayamikira kwambiri sukuluyi ponena kuti: “Maphunziro apadera amene talandira atithandiza kukonda kwambiri Yehova ndiponso kuti tizitha kuthandiza bwino anthu ena.”

11. N’chiyani chathandiza anthu a Mulungu kuti apitirize kulalikira za Ufumu ngakhale kuti amatsutsidwa?

11 Satana, yemwe ndi mdani wathu, akuona kuti tikugwira mwakhama ntchito yolalikira ndiponso yophunzitsa anthu. Choncho akuyesetsa kuletsa ntchito imeneyi kapena kuisokoneza m’njira zina. Koma zimene akuchitazi sizikuphula kanthu. Yehova waika Mwana wake “pamwambamwamba kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, amphamvu onse [ndiponso] ambuye onse.” (Aef. 1:20-22) Yesu amagwiritsa ntchito ulamuliro wake poteteza ndi kutsogolera ophunzira ake komanso poonetsetsa kuti cholinga cha Atate wake chikuchitika. * Uthenga wabwino ukulalikidwa komanso anthu mamiliyoni ambiri omwe akufuna kudziwa Yehova akuphunzitsidwa Mawu ake. Ndi mwayi waukulu kwambiri kugwira nawo ntchito yofunikayi.

MFUMU YASINTHA ZINTHU M’GULU LA ANTHU AKE KUTI AZICHITA ZAMBIRI

12. Fotokozani zinthu zina zimene zasintha m’gulu la Mulungu kuchokera pamene Ufumu unakhazikitsidwa.

12 Kuchokera pamene Ufumu unakhazikitsidwa mu 1914, Mfumu ya Ufumuwu yasintha zinthu zina m’gulu la atumiki ake kuti azikwaniritsa bwino cholinga cha Atate wake. (Werengani Yesaya 60:17.) Mu 1919, mumpingo uliwonse munaikidwa wotsogolera utumiki kuti azitsogolera pa ntchito yolalikira. Mu 1927, anakonza zoti mipingo izilalikira kunyumba ndi nyumba pa tsiku Lamlungu. Mu 1931, anthu amene anali kumbali ya Ufumu analimbikitsidwa kugwira ntchito mwakhama atalandira dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12) Mu 1938, anasiya kusankha oyang’anira mumpingo pochita voti ndipo anayamba kuikidwa poona ziyeneretso za m’Malemba. Mu 1972, anakhazikitsa mabungwe a akulu kuti aziyang’anira mipingo m’malo mwa woyang’anira mpingo mmodzi basi. Ndiyeno abale onse analimbikitsidwa kuti ayesetse kukhala oyenerera kuikidwa pa udindo kuti azithandiza ‘kuweta gulu la nkhosa za Mulungu.’ (1 Pet. 5:2) Mu 1976, anakhazikitsa makomiti 6 a Bungwe Lolamulira kuti aziyang’anira ntchito ya Ufumu padziko lonse. Zonsezi zikusonyeza kuti Mfumu yoikidwa ndi Yehova yakhala ikukonza zinthu m’gulu la anthu ake kuti azichita zinthu motsogoleredwa ndi Mulungu.

13. Kodi zimene Ufumu wa Mulungu wachita m’zaka 100 zapitazi zakhudza bwanji moyo wanu?

13 Taganizirani zimene Mfumu ya Ufumu wa Mulungu yachita m’zaka 100 zoyambirira za ulamuliro wake. Iye wayeretsa anthu odziwika ndi dzina la Yehova. Watsogolera pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’mayiko 239 ndipo waphunzitsa anthu mamiliyoni ambiri kuti azichita zofuna za Yehova. Iye wathandizanso anthu amene ali kumbali ya  Ufumu wake kuti akhale ogwirizana ndipo aliyense ndi wodzipereka ndi mtima wonse kuchita zimene Atate wake akufuna. (Sal. 110:3) Ndithudi, Yehova wachita zinthu zazikulu komanso zodabwitsa kwambiri pogwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya. Ndipo m’tsogolomu tikuyembekezera zinanso zodabwitsa kwambiri kuposa pamenepa.

MADALITSO AMENE UFUMU WA MESIYA UDZABWERETSE

14. (a) Kodi tikamapemphera kuti “Ufumu wanu ubwere,” timakhala tikupempha chiyani kwenikweni? (b) Kodi lemba lathu la chaka cha 2014 ndi liti, ndipo n’chifukwa chiyani ndi loyenerera?

14 N’zoona kuti Yehova anaika Mwana wake, Yesu Khristu, kukhala Mfumu ya Ufumu wake mu 1914. Koma zimenezi sizinakwaniritse mbali zonse za pemphero lathu lakuti “ufumu wanu ubwere.” (Mat. 6:10) Baibulo linaneneratu kuti Yesu ‘adzapita kukagonjetsa anthu pakati pa adani ake.’ (Sal. 110:2) Koma maboma a anthu, omwe akutsogoleredwa ndi Satana, amatsutsanabe ndi Ufumu wa Mulungu. Tikamapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere, tikupempha kuti Mulungu agwiritse ntchito Ufumu wake pochotsa ulamuliro wa anthu ndiponso onse otsutsa Ufumuwo. Mulungu adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito Mfumu imene iye wasankha ndiponso olamulira anzake. Zimenezi zidzakwaniritsa mawu a pa Danieli 2:44 akuti Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo.” Ufumu wa Mulungu udzawononga anthu onse andale amene amadana ndi Ufumuwu. (Chiv. 6:1, 2; 13:1-18; 19:11-21) Zimenezi zichitika posachedwapa. M’pake kuti lemba lathu la chaka cha 2014 ndi Mateyu 6:10 lomwe limati: “Ufumu wanu ubwere.” Lembali ndi loyenereranso chifukwa chakuti tsopano padutsa zaka 100 kuchokera pamene Ufumuwu unakhazikitsidwa kumwamba.

Lemba lathu la chaka cha 2014 ndi lakuti: “Ufumu wanu ubwere.”—Mateyu 6:10

15, 16. (a) Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zimene zidzachitike mu Ulamuliro wa Zaka 1,000? (b) Kodi ndi chinthu chomaliza chiti chimene Yesu adzachite monga Mfumu? (c) Kodi zimenezi zidzakwaniritsa bwanji cholinga cha Mulungu chokhudza ana ake onse?

15 Mfumuyo ikadzawononga adani a Mulungu, idzaponya Satana ndi ziwanda zake m’phompho kwa zaka 1,000. (Chiv. 20:1-3) Adani amenewa atachotsedwa, Ufumuwu udzathandiza anthu kupindula ndi dipo la Yesu komanso udzathetseratu mavuto obwera chifukwa cha uchimo wa Adamu. Mfumuyo idzaukitsa anthu mamiliyoni ambiri amene ali m’manda ndipo idzakhazikitsa ntchito yaikulu yophunzitsa anthuwo za Yehova. (Chiv. 20:12, 13) Dziko lonse lidzakhala Paradaiso ngati mmene unalili munda wa Edeni. Ndipo anthu onse okhulupirika adzakhala angwiro.

16 Pofika kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, Ufumu wa Mesiya udzakhala utakwaniritsa cholinga chake. Kenako Yesu adzabweza Ufumuwu kwa Atate wake. (Werengani 1 Akorinto 15:24-28.) Sipadzafunikanso mkhalapakati pakati pa Yehova ndi ana ake padziko lapansi. Ana a Mulungu onse kumwamba ndiponso padziko lapansi adzakhala ogwirizana ndi Atate wawo monga banja limodzi.

17. Kodi mukufunitsitsa kuchita chiyani pa nkhani ya Ufumu?

17 Zinthu zosangalatsa zimene Ufumu wa Mulungu wachita pa zaka 100 zapitazi, zimatitsimikizira kuti Yehova akulamulira. Zimatitsimikiziranso kuti cholinga chake chokhudza dziko lapansi chidzakwaniritsidwa. Tiyeni tipitirize kukhala okhulupirika kwa Mulungu ndiponso kulengeza za Mfumu ndi Ufumu wake. Tizichita zimenezi ndi chikhulupiriro chonse kuti posachedwapa Yehova ayankha pemphero lathu lochokera pansi pa mtima lakuti: “Ufumu wanu ubwere.”

^ ndime 10 Onani nkhani yakuti “Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu Zimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda” mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2012, tsamba 13 mpaka 17.

^ ndime 11 Mutha kuwerenga za milandu imene a Mboni awina m’mayiko osiyanasiyana mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1998, tsamba 19 mpaka 22.