Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ufumu wa Mulungu Ubwera Liti?

Kodi Ufumu wa Mulungu Ubwera Liti?

“Mukadzaona zinthu zonsezi, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni.”—MAT. 24:33.

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chingatichititse kuti tisaone zinthu zinazake? (b) Kodi tikudziwa chiyani zokhudza Ufumu wa Mulungu?

MWINA mwaonapo kuti anthu angapo akaona zinazake zikuchitika amazifotokoza mosiyana. Anthu sangakumbukirenso zonse zimene dokotala wanena powauza za matenda awo. Munthu amathanso kufufuza makiyi kapena magalasi koma osawaona, ngakhale kuti ali pafupi. Akatswiri ena ofufuza chifukwa chake zinthu zonsezi zimachitika amanena kuti umenewu ndi mtundu wina wa khungu la m’maganizo. Sitiona zinthu kapena timaiwala zinthu zina chifukwa chakuti pa nthawiyo tikuganiziranso zinazake. Iwo amanena kuti ubongo wathu sutha kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi.

2 Anthu ambiri masiku ano sadziwa tanthauzo la zimene zikuchitika m’dzikoli ndipo zili ngati ali ndi khungu la mtundu umenewu. Iwo angavomereze kuti zinthu zasintha kwambiri m’dzikoli kungoyambira mu 1914, koma sadziwa chifukwa chake. Popeza ife timaphunzira  Baibulo, tikudziwa kuti Ufumu wa Mulungu unabwera mu 1914 pamene Yesu anakhala Mfumu kumwamba. Koma tikudziwanso kuti pali zinthu zina zimene Mulungu adzachite poyankha pemphero lakuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mat. 6:10) N’zodziwikiratu kuti zimenezi zikuphatikizapo kuwonongedwa kwa dzikoli. Izi zikadzachitika m’pamene chifuniro cha Mulungu chidzachitike padziko lapansi monga kumwamba.

3. Kodi kuphunzira Mawu a Mulungu kwatithandiza bwanji?

3 Chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse, tikuona kuti ulosi ukukwaniritsidwa panopa. Koma anthu ena saona zimenezi. Iwo amatanganidwa kwambiri ndi zinthu zina moti saona umboni wooneka bwino wakuti Khristu wakhala akulamulira kuyambira mu 1914 ndipo posachedwapa apereka chiweruzo cha Mulungu. Koma ngati mwakhala mukutumikira Mulungu kwa zaka zambiri mungadzifunse kuti, Kodi ndikukhulupirira kuti mapeto ali pafupi kwambiri ngati mmene ndinkaonera zaka zambiri zapitazo? Ngati mwayamba kumene kutumikira Mulungu, dzifunseni kuti, Kodi ndimatanganidwa ndiponso kuganizira kwambiri za chiyani? Kaya yankho lathu ndi lotani, tiyeni tione zifukwa zitatu zotichititsa kukhulupirira ndi mtima wonse kuti posachedwapa Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ionetsetsa kuti chifuniro cha Mulungu chachitika padziko lapansi.

ANTHU OKWERA PAMAHATCHI AKUTHAMANGA

4, 5. (a) Kodi Yesu wakhala akuchita chiyani kuyambira mu 1914? (Onani chithunzi patsamba 27.) (b) Kodi masomphenya a anthu atatu okwera pamahatchi akuimira chiyani? (c) Kodi masomphenyawa akukwaniritsidwa bwanji?

4 M’masomphenya, Yohane anaona Yesu Khristu atakwera pahatchi yoyera ndipo anapatsidwa chisoti chachifumu. Iye anapatsidwa chisoticho kumwamba mu 1914. Nthawi yomweyo, anapita kukagonjetsa dziko loipa la Satanali. (Werengani Chivumbulutso 6:1, 2.) Ulosi wa mu chaputala 6 cha Chivumbulutso umasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu utakhazikitsidwa panayenera kukhala mavuto ambiri padzikoli monga nkhondo, njala, miliri ndiponso zinthu zina zimene zimapha anthu. Anthu ena atatu okwera pamahatchi omwe akutsatira Yesu Khristu ndi amene akusonyeza kuti mavutowa ayenera kuchitika.—Chiv. 6:3-8.

5 Mogwirizana ndi ulosiwu, mtendere ‘unachotsedwa padziko lapansi’ ngakhale kuti mayiko ankalonjeza kuti akhazikitsa mgwirizano padziko lonse. Zinthu zimene zachitika padzikoli posachedwapa zikusonyeza kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse inali chiyambi chabe cha nkhondo zikuluzikulu. Komanso anthu akuvutika kwambiri ndi njala padzikoli ngakhale kuti kuchokera mu 1914, anthu ena aphunzira zambiri pa nkhani ya zachuma ndiponso zasayansi. Tonsefe tikudziwanso kuti matenda, masoka a chilengedwe ndiponso ‘miliri yakupha’ zikuwononga anthu mamiliyoni ambiri chaka chilichonse. Zinthuzi zikuchitika kwambiri komanso zikuwononga zinthu ndiponso anthu ambiri kuposa kale lonse. Kodi mukuzindikira tanthauzo la zimenezi?

Anthu okwera pamahatchi akuthamangabe, ndipo zinthu m’dzikoli zikuipiraipira (Onani ndime 4 ndi 5)

6. Kodi ndani amene anazindikira kuti ulosi wa m’Baibulo ukukwaniritsidwa, ndipo anachita chiyani?

6 Anthu padzikoli anasokonezeka kwambiri chifukwa cha nkhondo yoyamba ya padziko lonse komanso matenda oopsa a chimfine amene anapha anthu ambiri. Koma Akhristu odzozedwa ankayembekezera kutha kwa ‘nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu ina’ mu 1914. (Luka 21:24) Iwo sankadziwa bwinobwino zimene zidzachitike m’chakachi. Koma ankadziwa kuti padzachitika zinthu zina zapadera zokhudza ulamuliro wa Mulungu. Atangozindikira kuti ulosi wa m’Baibulo ukukwaniritsidwa, anayamba kuuza anthu ena molimba mtima kuti Ufumu wa Mulungu wayamba kulamulira. Koma chifukwa chochita zimenezi mwakhama, anayamba kuzunzidwa kwambiri. Komabe chizunzo chimene Akhristuwo anakumana nacho m’mayiko ambiri chinakwaniritsanso ulosi. M’zaka zotsatira, adani a Ufumu ankayesetsa ‘kuyambitsa mavuto popanga malamulo.’ Adaniwo ankamenyanso abale athu komanso kuwatsekera m’ndende. Ankawaphanso powamangirira, kuwaombera kapena kuwadula mitu.—Sal. 94:20; Chiv. 12:15.

7. N’chifukwa chiyani anthu ambiri sakudziwa tanthauzo la zimene zikuchitika m’dzikoli?

7 Pali umboni wochuluka wosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kale kumwamba. Ngati zili choncho, n’chifukwa chiyani anthu ambiri sadziwa tanthauzo la zimenezi? N’chifukwa chiyani satha kuona kugwirizana pakati pa zinthu zoipa za padzikoli ndi maulosi a m’Baibulo amene anthu a Mulungu akhala akufotokoza kwa nthawi yaitali?  Mwina ndi chifukwa chakuti anthu ambiri akungoganizira zinthu zimene zikuoneka ndi maso. (2 Akor. 5:7) Kodi kutanganidwa kwambiri ndi zochitika za m’dzikoli kukuwachititsa khungu kuti asaone zimene Mulungu akuchita? (Mat. 24:37-39) Kapena kodi anthu ena akusokonezedwa ndi mabodza a Satana? (2 Akor. 4:4) Munthu ayenera kukhala ndi chikhulupiriro komanso kumvetsa Mawu a Mulungu kuti adziwe zimene Ufumu wa Mulungu ukuchita. Ndife osangalala kwambiri kuti tilibe khungu, ndipo tikutha kuzindikira zimene zikuchitika.

ZINTHU ZIKUIPIRAIPIRABE

8-10. (a) Kodi lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 likukwaniritsidwa bwanji? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zinthu zikuipiraipirabe?

8 Pali chifukwa chinanso chimene chikutichititsa kukhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu uyamba kulamulira dziko lonse lapansi posachedwapa. Chifukwa chake n’choti zochita za anthu zikuipiraipirabe. Kwa zaka pafupifupi 100, zimene lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 likunena zakhala zikuchitika ndipo zikuwonjezekawonjezeka. Kodi inunso simukuvomereza kuti panopa pakuchitika zinthu zambiri zokwaniritsa ulosi umenewu? Tiyeni tione zitsanzo zingapo zomwe zikusonyeza zimenezi.—Werengani 2 Timoteyo 3:1, 13.

9 Taganizirani zimene anthu ankadana nazo pa nkhani ya zosangalatsa, masewera kapena kavalidwe m’ma 1940 kapena m’ma 1950. N’zosiyana kwambiri ndi mmene zilili masiku ano. Panopa, anthu azolowera kwambiri chiwawa ndiponso chiwerewere. Ambiri amayesetsa kuti apose anzawo pa nkhani yokhala oopsa, okonda zachiwerewere ndiponso ankhanza. Mapulogalamu a pa TV omwe anthu m’ma 1950 ankaona kuti ndi oipa, masiku ano anthu amaona kuti palibe vuto ngati aliyense m’banja atawaonera. Mutha kuonanso kuti anthu ogonana ndi amuna kapena akazi anzawo amalimbikitsa kwambiri anthu kutengera khalidwe lawo kudzera m’mafashoni kapena zosangalatsa. Koma ife ndife osangalala kwambiri kuti timadziwa mmene Mulungu amaonera zinthu zimenezi.—Werengani Yuda 14, 15.

 10 Mkhristu akhozanso kuyerekezera makhalidwe oipa amene achinyamata ankachita m’ma 1950 ndi zimene zikuchitika masiku ano. Makolo ankadera nkhawa kuti mwina ana awo akusuta, kumwa mowa kapena kuvina motayirira. Ndipo m’pake kuti ankadera nkhawa zimenezi. Koma masiku ano, timamva nthawi ndi nthawi za zinthu zodabwitsa zimene ana akuchita. Mwachitsanzo, mwana wazaka 15 anawombera ana anzake kusukulu ndipo anapha ana awiri n’kuvulaza ena 13. Komanso gulu la achinyamata oledzera linapha mwankhanza mtsikana wina wazaka 9 ndipo anamenya kwambiri bambo ake ndi wachibale wake wina. Kudziko lina la ku Asia, achinyamata ndi amene anapalamula hafu ya milandu imene inachitika m’zaka 10 zapitazi. Kodi pali munthu amene angakane kuti zinthu zikuipiraipirabe?

11. N’chifukwa chiyani anthu ambiri sazindikira kuti zinthu zikuipiraipira?

11 Mtumwi Petulo ananena mfundo yoona yakuti: “M’masiku otsiriza kudzakhala onyodola amene azidzatsatira zilakolako zawo, amene azidzati: ‘Kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti? Taonani, kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira, zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi ngati mmene zakhalira kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe.’” (2 Pet. 3:3, 4) N’chifukwa chiyani anthu ena amachita zimenezi? Zikuoneka kuti anthu saona vuto ndi zinthu zimene anazizolowera kwambiri. Anthu akhoza kudabwa kwambiri akaona kuti munthu amene amadziwana naye kwambiri wasintha mwamsanga mmene amachitira zinthu. Koma makhalidwe a m’dzikoli akamalowa pansi mwapang’onopang’ono, anthu sadabwa nazo kwambiri ngakhale kuti zimenezi n’zoopsa.

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhumudwa ndi zimene zikuchitika m’dzikoli? (b) N’chiyani chingatithandize kupirira masiku ovutawa?

12 Mtumwi Paulo anati “masiku otsiriza” adzakhala ‘ovuta.’ (2 Tim. 3:1) Koma n’zotheka kuwapirira. Tikhoza kuthana ndi mavuto kapena zinthu zochititsa mantha chifukwa timathandizidwa ndi Yehova, mzimu wake ndiponso mpingo wake. N’zotheka kuti tikhalebe okhulupirika chifukwa Mulungu amatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.”—2 Akor. 4:7-10.

13 Kumbukirani kuti Paulo anayamba kufotokoza ulosi wonena za masiku otsiriza ndi mawu akuti “dziwa kuti.” Mawu amenewa akutsimikizira kuti zimene ananena pambuyo pake zinali zoti zidzachitikadi. Sitiyenera kukayikira kuti dziko loipali lidzaipiraipirabe mpaka Yehova atalithetsa. Pofotokoza za maufumu ena amene anagwa, akatswiri a mbiri yakale amanena kuti maufumuwo asanagwe, choyamba makhalidwe a anthu awo analowa pansi kwambiri. Panopa makhalidwe a anthu padziko lonse lapansi aipa kwambiri kuposa kale lonse. Anthu ambiri sadziwa tanthauzo la zimenezi. Koma zimene zakhala zikuchitika kuyambira mu 1914 zingatithandize kukhulupirira ndi mtima wonse kuti Ufumu wa Mulungu uthetsa mavuto onsewa posachedwapa.

M’BADWO UWU SUDZATHA WONSE

14-16. Kodi chifukwa chachitatu chimene chikutichititsa kukhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ‘ubwera’ posachedwapa ndi chiti?

14 Pali chifukwa chachitatu chimene chimatichititsa kukhulupirira kuti mapeto ali pafupi. Zimene zachitika pakati pa anthu a Mulungu ndi umboni wa zimenezi. Mwachitsanzo, Ufumu wa Mulungu usanakhazikitsidwe kumwamba, panali Akhristu ena odzozedwa amene anali kutumikira Mulungu mokhulupirika. Kodi iwo anachita chiyani ataona kuti zinthu zina zimene ankayembekezera mu 1914 sizinachitike? Ambiri anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ngakhale pamene ankazunzidwa kapena kukumana ndi mayesero. Ambiri mwa Akhristu odzozedwa amenewa, anapitiriza kutumikira Mulungu mokhulupirika  mpaka atamaliza moyo wawo padziko lapansi.

15 Mu ulosi wake wofotokoza mwatsatanetsatane za mapeto a nthawi ino, Yesu ananena kuti: “M’badwo uwu sudzatha wonse kuchoka kufikira zinthu zonsezi zitachitika.” (Werengani Mateyu 24:33-35.) Tikudziwa kuti ponena kuti “m’badwo uwu,” Yesu ankanena magulu awiri a Akhristu odzozedwa. Gulu loyamba ndi la odzozedwa amene analipo mu 1914, ndipo anamvetsa tanthauzo la chizindikiro cha kukhalapo kwa Khristu m’chaka chimenecho. Akhristu a m’gulu limeneli anali ndi moyo mu 1914, komanso anadzozedwa n’kukhala ana a Mulungu m’chakachi kapena chisanafike.—Aroma 8:14-17.

16 Gulu lachiwiri la odzozedwa amene akupanga “m’badwo uwu,” ndi amene anakhala ndi moyo anthu a m’gulu loyambalo asanamwalire. Sikuti anangokhala ndi moyo pamene a m’gulu loyamba aja analinso ndi moyo koma anadzozedwa ndi mzimu woyera anthu a m’gulu loyambawo adakali padziko lapansi. Choncho sikuti wodzozedwa aliyense masiku ano ali nawo mu “m’badwo uwu” umene Yesu anatchula. Masiku ano, amene ali m’gulu lachiwirili ndi okalamba. Komabe zimene Yesu ananena pa Mateyu 24:34 zimatitsimikizira kuti ena amene ali mu “m’badwo uwu” adzaona kuyambika kwa chisautso chachikulu asanamwalire. Zimenezi zikutitsimikiziranso kuti patsala nthawi yochepa kuti Mfumu ya Ufumu wa Mulungu iwononge oipa ndi kubweretsa dziko latsopano lolungama.—2 Pet. 3:13.

POSACHEDWAPA KHRISTU APAMBANA PA NKHONDO

17. Kodi zifukwa zitatu zimene takambiranazi zingatithandize kuzindikira chiyani?

17 Kodi zifukwa zitatu zimene takambiranazi zikusonyeza chiyani? Yesu ananena kuti sitingadziwe “tsiku kapena ola lake.” (Mat. 24:36; 25:13) Ngakhale zili choncho, timadziwa “nyengo” yake ndipo izi zikugwirizana ndi zimene Paulo ananena. (Werengani Aroma 13:11.) Panopa tikukhala m’nyengo imeneyo kapena kuti m’masiku otsiriza. Tiyenera kuganizira kwambiri ulosi wa m’Baibulo ndiponso zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu akuchita. Tikatero sitingalephere kuona umboni wamphamvu wakuti mapeto a dziko loipali ali pafupi kwambiri.

18. Kodi n’chiyani chidzachitikire anthu amene amakana kugonjera Ufumu wa Mulungu?

18 Yesu Khristu akuthamanga atakwera pahatchi yoyera ndipo posachedwapa apambana nkhondo. Pa nthawiyo, anthu onse amene amakana kugonjera ulamuliro umene Mulungu anapatsa Yesu Khristu adzakakamizidwa kuzindikira kuti ankalakwitsa. Anthuwo sadzatha kuthawa ndipo ambiri adzafuula mwamantha kuti: “Ndani angaimirire pamaso pawo?” (Chiv. 6:15-17) Chaputala 7 cha buku la Chivumbulutso chimayankha funsoli. Chimasonyeza kuti Akhristu odzozedwa limodzi ndi anthu omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli ndi amene adzathe ‘kuimirira pamaso pawo.’ Izi zidzachitika chifukwa ali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Kenako “khamu lalikulu” la nkhosa zina lidzapulumuka pa chisautso chachikulu.—Chiv. 7:9, 13-15.

19. Kodi inuyo mukuyembekezera zinthu zosangalatsa ziti?

19 Tingachite bwino kuganizira kwambiri zimene zikuchitika masiku ano pokwaniritsa maulosi a m’Baibulo. Tikachita zimenezi sitidzasokonezedwa ndi zinthu za m’dziko la Satanali komanso tidzamvetsa tanthauzo la zimene zikuchitika m’dzikoli. Posachedwapa, Khristu adzamenya nkhondo yomaliza mwachilungamo ndipo adzagonjetsa anthu onse osaopa Mulungu. (Chiv. 19:11, 19-21) Baibulo limalonjeza kuti kenako tidzasangalala kwambiri ndi zinthu zabwino zimene Ufumu wa Mulungu udzabweretse.—Chiv. 20:1-3, 6; 21:3, 4.