Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani ‘Kuyembekezera Moleza Mtima’

Pitirizani ‘Kuyembekezera Moleza Mtima’

“Ndidzayembekezera moleza mtima.”MIKA 7:7.

1. N’chifukwa chiyani anthufe tikhoza kutopa kuyembekezera mapeto?

NTHAWI ya mapeto a dziko la Satanali inayamba pamene Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa mu 1914. Pa nkhondo imene inachitika kumwamba, Yesu anaponya Mdyerekezi ndi ziwanda zake padzikoli. (Werengani Chivumbulutso 12:7-9.) Satana amadziwa kuti “wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chiv. 12:12) Koma panopa kwadutsa zaka zambiri, choncho ena angaone kuti ‘kanthawiko’ katalika kwambiri. Kodi ifeyo tatopa kuyembekezera kuti Yehova akonze zinthu?

2. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?

2 Munthu akatopa kuyembekezera akhoza kuchita zinthu mopupuluma. Kodi tingatani kuti tipitirize kuyembekezera moleza mtima? Nkhaniyi itithandiza kuchita zimenezi poyankha mafunso awa: (1) Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Mika? (2) N’chiyani chidzasonyeze kuti mapeto akufika? (3) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira kuleza mtima kwa Yehova?

KODI TIKUPHUNZIRA CHIYANI PA CHITSANZO CHA MIKA?

3. Kodi zinthu zinali bwanji mu Isiraeli m’masiku a Mika?

3 Werengani Mika 7:2-6. Mneneri Mika anaona zinthu zikusokonekera mu Isiraeli pa nkhani yotumikira Yehova. Zinafika poipa kwambiri mu ulamuliro wa Mfumu Ahazi yomwe inali yoipa kwambiri. Mika ananena kuti Aisiraeli osakhulupirikawo anali ngati “chitsamba chaminga” ndiponso “mpanda wa mitengo yaminga.” Munthu amene amadutsa paminga amabayidwa. Ndi mmene zinalili ndi Aisiraeli chifukwa munthu aliyense amene ankachita nawo zinthu, sizinkamuyendera bwino. Anthuwo anali achinyengo kwambiri moti sankagwirizananso ngakhale ndi achibale awo. Popeza Mika ankadziwa kuti sangathe kusintha zinthu, anapemphera kwa Yehova ndi mtima wonse. Ndiyeno  ankayembekezera moleza mtima kuti Mulungu athetse mavutowo. Iye sankakayikira zoti Yehova akonza zinthu pa nthawi yake.

4. Kodi Akhristufe timakumana ndi mavuto ati?

4 Masiku ano, m’dzikoli mulinso anthu odzikonda. Ambiri ndi ‘osayamika, osakhulupirika ndiponso osakonda achibale awo.’ (2 Tim. 3:2, 3) Zimatipweteka kwambiri tikaona kuti anzathu akuntchito, kusukulu, komanso aneba athu ndi omva zawo zokha. Koma atumiki a Mulungu ena amakumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Yesu ananena kuti Akhristu adzatsutsidwa ndi achibale awo. Iye anagwiritsa ntchito mawu ofanana ndi amene ali pa Mika 7:6 pofotokoza zimene zizidzachitika anthu akamva uthenga wake. Yesu anati: “Ndinabwera kudzagawanitsa anthu. Ndinabwera kudzachititsa munthu kutsutsana ndi bambo ake, mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake, ndiponso mtsikana wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi. Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.” (Mat. 10:35, 36) Zimakhala zopweteka kwambiri ngati munthu akunyozedwa komanso kutsutsidwa ndi achibale ake osakhulupirira. Ngati zoterezi zitachitika, tiyeni tisabwerere m’mbuyo. M’malomwake, tikhalebe okhulupirika kwa Yehova n’kumayembekezera moleza mtima kuti akonze zinthu. Tikamamupempha nthawi zonse kuti atithandize, adzatipatsa mphamvu komanso nzeru kuti tipirire.

5, 6. (a) Kodi Yehova anadalitsa bwanji Mika? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene Mika sanaone zikukwaniritsidwa?

5 Yehova anadalitsa Mika chifukwa choyembekezera moleza mtima kuti Yehova akonze zinthu. Mika anaona ulamuliro wa Ahazi ukutha. Anaonanso mwana wa Ahazi, dzina lake Hezekiya, akulowa ufumu n’kuyambitsanso kulambira koyera. Kudzera mwa Mika, Yehova anapereka uthenga wa chiweruzo wokhudza Samariya ndipo izi zinakwaniritsidwa pamene Asuri anawononga ufumu wakumpoto wa Isiraeli.—Mika 1:6.

6 Komatu Mika sanaone zinthu zonse zimene Yehova anamuuza kuti alosere zikukwaniritsidwa. Mwachitsanzo, iye analemba kuti: “M’masiku otsiriza, phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa nsonga za mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa mapiri ang’onoang’ono. Mitundu ya anthu idzakhamukira kumeneko. Anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana adzabwera n’kunena kuti: ‘Bwerani anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova.’” (Mika 4:1, 2) Mika anamwalira kutatsala zaka zambiri kuti ulosiwu ukwaniritsidwe. Komabe iye anakhala wokhulupirika kwa Yehova mpaka pamene anafa ngakhale kuti anthu ena ankachita zoipa. Ndiyeno pa nkhani imeneyi, Mika analemba kuti: “Mtundu uliwonse wa anthu udzayenda m’dzina la mulungu wake. Koma ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.” (Mika 4:5) Mika anayembekezera moleza mtima chifukwa chakuti ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake onse. Mneneri wokhulupirikayu ankadalira kwambiri Yehova.

7, 8. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kwambiri Yehova? (b) N’chiyani chingathandize kuti nthawi yomwe yatsalayi tisaione kuchedwa?

7 Kodi nafenso timakhulupirira kwambiri Yehova? Palitu zifukwa zotichititsa kumukhulupirira. Taona ulosi wa Mika ukukwaniritsidwa. “M’masiku otsiriza” ano, anthu mamiliyoni ochokera m’mitundu, mafuko ndi zinenero zonse akukhamukira ‘kuphiri la nyumba ya Yehova.’ Ngakhale kuti amachokera m’mitundu imene imadana, iwo asula “malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo” ndipo amakaniratu ‘kuphunzira nkhondo.’ (Mika 4:3) Ndi mwayi waukulutu kukhala m’gulu la anthu a Yehova okonda mtendere.

8 M’pomveka kuti timafuna Yehova atawononga dziko loipali mwamsanga. Koma kuti  tiyembekezere moleza mtima, tiyenera kuona zinthu mmene Yehova amazionera. Yehova wakonza tsiku limene adzaweruza anthu onse ndipo wasankha Yesu Khristu kuti adzagwire ntchito imeneyi. (Mac. 17:31) Koma panopa, Mulungu akupereka mwayi kwa anthu onse kuti adziwe “choonadi molondola” n’kusintha moyo wawo kuti apulumuke. Moyo wa anthu ambiri, womwe ndi wamtengo wapatali, uli pangozi. (Werengani 1 Timoteyo 2:3, 4.) Tikamatanganidwa kwambiri kuphunzitsa anthu kuti adziwe bwino Mulungu, nthawi yomwe yatsalayi izidutsa mofulumira kwambiri. Posachedwapa, ndiponso mwina mosayembekezereka, tidzangoona kuti basi yatha. Pa nthawiyo, tidzasangalala kwambiri podziwa kuti tinachita khama pa ntchito yolalikira.

N’CHIYANI CHIDZASONYEZE KUTI MAPETO AKUFIKA?

9-11. Kodi lemba la 1 Atesalonika 5:3 lakwaniritsidwa? Fotokozani.

9 Werengani 1 Atesalonika 5:1-3. Posachedwapa anthu adzanena kuti: “Bata ndi mtendere!” Kuti tisapusitsidwe ndi mawu amenewa, tiyenera ‘kukhalabe maso ndiponso oganiza bwino.’ (1 Ates. 5:6) Tiyeni tikambirane zinthu zimene zikusonyeza kuti anthu adzanena mawuwo posachedwapa. Kukambirana zimenezi kungatithandize kukhalabe maso.

10 Nkhondo ziwiri zapadziko lonse zitatha, anthu ankanenanena za mtendere. Mwachitsanzo, nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha, bungwe la League of Nations linakhazikitsidwa n’cholinga choti pakhale mtendere. Kenako pambuyo pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, bungwe la United Nations linakhazikitsidwa ndipo anthu ankaganiza kuti libweretsa mtendere. Maboma ambiri komanso atsogoleri azipembedzo akhala akudalira mabungwe amenewa kuti abweretse mtendere. Umboni wake ndi wakuti mu 1986, bungwe la United Nations linalengeza kuti chaka chimenechi ndi chaka chamtendere padziko lonse. Ndiyeno m’chakachi, atsogoleri a mayiko ambiri komanso azipembedzo anapita ku Assisi m’dziko la Italy kukapempherera mtendere limodzi ndi mtsogoleri wa tchalitchi cha Katolika.

 11 Koma zimene zinachitika mu 1986 komanso pa nthawi zina sizinakwaniritse ulosi wa pa 1 Atesalonika 5:3. Tikutero chifukwa chakuti “chiwonongeko chodzidzimutsa” sichinafikebe.

12. Kodi timadziwa chiyani zokhudza kunena kuti: “Bata ndi mtendere”?

12 Kodi ndi ndani amene adzanene kuti: “Bata ndi mtendere”? Kodi atsogoleri a matchalitchi amene amati ndi achikhristu komanso a zipembedzo zina adzachita chiyani? Nanga atsogoleri a maboma adzachita zotani pa nthawi imeneyo? Malemba safotokoza zimenezi. Koma chimene tikudziwa n’chakuti kaya adzanena bwanji, mawuwo sadzakhala oona. Dziko loipali lidzakhalabe m’manja mwa Satana. Tingati lawoleratu ndipo silidzasintha. Zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati Mkhristu angakhulupirire mawu abodza ochokera kwa Satana amenewa n’kuyamba kulowerera m’nkhani za m’dzikoli.

13. N’chifukwa chiyani angelo akugwira mphepo zowononga kuti zisawombe padziko lapansi?

13 Werengani Chivumbulutso 7:1-4. Pamene tikudikira kuti lemba la 1 Atesalonika 5:3 likwaniritsidwe, angelo amphamvu akugwira mphepo za chisautso chachikulu kuti zisawombe padziko lapansi. Kodi angelowo akudikira chiyani? Yohane ananena kuti chinthu chimodzi chimene akudikira n’chakuti “akapolo a Mulungu wathu,” omwe ndi odzozedwa, adindidwe chidindo chomaliza. * Zimenezi zikadzachitika, angelowo adzasiya mphepozo kuti ziwombe. Ndiyeno kodi chidzachitike n’chiyani?

14. N’chiyani chikusonyeza kuti Babulo Wamkulu watsala pang’ono kuwonongedwa?

14 Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga, adzawonongedwa. Pa nthawi imene adzawonongedwe, anthu sadzatha kumuthandiza. Ngakhale panopa, umboni woti adzawonongedwa posachedwapa ukuoneka. (Chiv. 16:12; 17:15-18; 18:7, 8, 21) Nkhani za m’nyuzipepala ndiponso pa TV zikusonyeza kuti anthu ayamba kale kudana ndi zipembedzo ndiponso atsogoleri ake. Komabe atsogoleri a Babulo Wamkulu amaganiza kuti zinthu zili bwinobwino. Koma adzadabwa. Mawu akuti “Bata ndi mtendere!” akadzanenedwa, atsogoleri andale a m’dziko la Satanali adzaukira zipembedzo zonyenga mwadzidzidzi n’kuziwononga. Amenewo adzakhala mapeto a Babulo Wamkulu. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene zonsezi zidzachitike.—Chiv. 18:8, 10.

KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI TIMAYAMIKIRA KULEZA MTIMA KWA YEHOVA?

15. N’chifukwa chiyani Yehova sanawononge dzikoli mwamsanga?

15 Anthu akhala akunyoza kwambiri dzina la Yehova, koma iye akuyembekezera moleza mtima nthawi imene adzakonze zinthu. Yehova sakufuna kuti anthu amtima wabwino awonongedwe. (2 Pet. 3:9, 10) Kodi nafenso tili ndi maganizo amenewa? Tiyeni tikambirane zimene tingachite posonyeza kuti timayamikira kuleza mtima kwa Yehova pamene tsiku lake likuyandikira.

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza anthu amene asiya kutumikira Yehova? (b) N’chifukwa chiyani anthu amene asiya kutumikira Yehova ayenera kubwerera mwamsanga?

16 Thandizani anthu amene asiya kutumikira Mulungu. Yesu ananena kuti kumwamba kumakhala chisangalalo chachikulu nkhosa imodzi yotayika ikapezeka. (Mat. 18:14; Luka 15:3-7) Umenewutu ndi umboni wakuti Yehova amaganizira kwambiri anthu amene anasonyeza kuti amakonda dzina lake, ngakhale amene panopa sakumutumikira. Tikamathandiza anthu oterewa kuti abwerere m’gulu la Yehova, timachititsa kuti Yehova ndi angelo ake asangalale.

17 Kodi inuyo munasiya kutumikira Yehova? N’kutheka kuti munasiya kusonkhana ndi  gulu la Yehova chifukwa chakuti m’bale kapena mlongo wina anakukhumudwitsani. Ndiye poti nthawi yadutsa tsopano, ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi panopa zinthu zikundiyendera bwino kwambiri ndipo ndikusangalala kuposa kale? Kodi amene anandilakwira ndi Yehova kapena ndi munthu winawake yemwe si wangwiro? Kodi Yehova anachitapo chilichonse chondipweteka?’ Kunena zoona, Yehova amatichitira zabwino nthawi zonse. Ngakhale pamene sitikukwaniritsa zimene tinamulonjeza podzipereka kwa iye, amatipatsabe zinthu zabwino. (Yak. 1:16, 17) Panopa tsiku la Yehova layandikira kwambiri. Ino ndi nthawi yoti tibwerere kwa Atate wathu wachikondi Yehova komanso mumpingo wake. Ngati tikufuna kukhala otetezeka m’masiku otsiriza ano, tiyenera kuchita zimenezi.—Deut. 33:27; Aheb. 10:24, 25.

Atumiki a Yehova amachita khama kwambiri pothandiza anthu kuti abwerere kwa Yehova (Onani ndime 16 ndi 17)

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera amene akutsogolera mumpingo?

18 Muzimvera amene akutsogolera mumpingo. Yehova ndi M’busa wachikondi amene amatitsogolera ndiponso kutiteteza. Iye wasankha Mwana wake kuti akhale M’busa Wamkulu wa nkhosa zake. (1 Pet. 5:4) M’mipingo yoposa 100,000, akulu amaweta nkhosa iliyonse ya Mulungu. (Mac. 20:28) Tikamamvera amene akutsogolera mumpingo, timasonyeza kuti timayamikira kwambiri zimene Yehova ndi Yesu amatichitira.

19. Kodi tingatsanzire bwanji zimene asilikali amachita?

19 Muzigwirizana kwambiri ndi Akhristu anzanu. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi? Gulu la asilikali likakumana ndi adani, asilikaliwo amayandikana kwambiri. Izi zimathandiza kuti azitetezana ndipo sagonjetsedwa. Panopa Satana akuukira kwambiri anthu a Mulungu. Ino si nthawi yoti tizilimbana ndi Akhristu anzathu. Ndi nthawi yoti tizigwirizana kwambiri, tiziiwala zimene ena atilakwira ndipo tizisonyeza kuti timadalira Yehova yemwe akutitsogolera.

Ino ndi nthawi yoti tiziyandikana kwambiri kuti tithe kulimbana ndi Satana ndi ziwanda zake (Onani ndime 19)

20. Kodi panopa tiyenera kuchita chiyani?

20 Tiyeni tonse tikhalebe maso ndipo tiziyembekezera Yehova. Tizidikira moleza mtima nthawi imene anthu adzanene mawu akuti “Bata ndi mtendere!” ndiponso pamene odzozedwa adzadindidwa chidindo chomaliza. Zikatero, angelo adzasiya mphepo zowononga kuti ziwombe padzikoli ndipo Babulo Wamkulu adzawonongedwa. Pamene tikuyembekezera zonsezi, tiyeni tizimvera amene akutsogolera m’gulu la Yehova. Tiyeni tiziyandikana kwambiri kuti tithe kulimbana ndi Mdyerekezi ndi ziwanda zake. Ino ndi nthawi yotsatira malangizo a wamasalimo akuti: “Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu, inu nonse amene mukuyembekezera Yehova.”—Sal. 31:24.

^ ndime 13 Kuti mudziwe zambiri zokhudza kusiyana pakati pa kudindidwa koyamba kwa adzozedwa ndiponso komaliza, onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 2007, tsamba 30 ndi 31.