Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzimvera Abusa Amene Yehova Watipatsa

Muzimvera Abusa Amene Yehova Watipatsa

“Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu.”—AHEB. 13:17.

1, 2. N’chifukwa chiyani m’pomveka kuti Yehova amadziyerekezera ndi m’busa?

YEHOVA amadziyerekezera ndi m’busa. (Ezek. 34:11-14) M’pomveka kudziyerekezera chonchi chifukwa zimatithandiza kudziwa mmene iye alili. M’busa amene amakonda nkhosa zake amasamalira bwinobwino nkhosazo. Iye amapita nazo kubusa ndiponso kumadzi (Sal. 23:1, 2); amazilondera usana ndi usiku (Luka 2:8); amaziteteza kuti zisagwidwe ndi nyama zolusa (1 Sam. 17:34, 35); amanyamula tiana ta nkhosa (Yes. 40:11); amafufuza nkhosa zotayika komanso amasamalira zimene zavulala.—Ezek. 34:16.

2 Kalelo, anthu a Yehova ambiri anali alimi ndipo ankaweta ziweto. Choncho zinali zosavuta kuti amvetse mfundo yoti Yehova Mulungu ali ngati m’busa wabwino. Iwo ankadziwa kuti nkhosa sizingakhale bwinobwino popanda kusamaliridwa. Ndi mmene zililinso ndi anthu pa nkhani yolambira Mulungu. (Maliko 6:34) Zinthu siziyenda bwino ngati anthu sakusamaliridwa ndiponso kutsogoleredwa. Iwo amatha kusokonezeka mosavuta komanso kulowerera. Amakhala ngati “nkhosa zopanda m’busa” zimene zabalalika. (1 Maf. 22:17) Koma Yehova amasamalira anthu ake mwachikondi.

3. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?

3 Masiku anonso Yehova ali ngati m’busa. Iye amasamalirabe anthu ake. Tiyeni tione zimene amachita potsogolera ndiponso kusamalira nkhosa zake masiku ano. Tionanso zimene tiyenera kuchita Yehova akamatisamalira mwachikondi.

M’BUSA WABWINO AMATIPATSA ABUSA AANG’ONO

4. Kodi Yesu ali ndi udindo wotani posamalira nkhosa za Yehova?

4 Yehova wasankha Yesu kukhala Mutu wa mpingo  wachikhristu. (Aef. 1:22, 23) Yesu, yemwe ndi “m’busa wabwino,” ali ndi makhalidwe ndiponso zolinga zofanana ndi za Atate wake. Iye anafika ‘potaya moyo wake chifukwa cha nkhosa.’ (Yoh. 10:11, 15) Dipo la Khristu ndi dalitso lalikulu kwambiri kwa anthu. (Mat. 20:28) Cholinga cha Yehova n’chakuti “aliyense wokhulupirira [Yesu] asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yoh. 3:16.

5, 6. (a) Kodi Yesu wasankha ndani kuti azisamalira nkhosa zake ndipo nkhosazo ziyenera kuchita chiyani? (b) Kodi ndi mfundo iti imene iyenera kutilimbikitsa kwambiri kumvera akulu mumpingo?

5 Kodi nkhosa zimasonyeza bwanji kuti Yesu ndi M’busa wawo? Yesu anati: “Nkhosa zanga zimamva mawu anga. Ine ndimazidziwa, ndipo izo zimanditsatira.” (Yoh. 10:27) Kumva mawu a M’busa Wabwino kumatanthauza kutsatira malangizo ake nthawi zonse. Zimenezi zikutanthauzanso kumvera abusa aang’ono amene iye watipatsa. Yesu anasonyeza kuti atumwi ndiponso ophunzira ake ayenera kupitiriza ntchito imene iye anayambitsa. Iwo anayenera ‘kuphunzitsa’ ndiponso ‘kudyetsa ana a nkhosa a Yesu.’ (Mat. 28:20; werengani Yohane 21:15-17.) Uthenga wabwino utafalikira kwambiri ndiponso ophunzira atachuluka, Yesu anakonza zoti pakhale akulu kuti aziweta nkhosa m’mipingo.—Aef. 4:11, 12.

6 Mtumwi Paulo anauza oyang’anira mumpingo wa ku Efeso kuti mzimu woyera ndi umene unawaika kukhala oyang’anira ‘kuti awete mpingo wa Mulungu.’ (Mac. 20:28) Masiku anonso oyang’anira mumpingo amasankhidwa chifukwa chotsatira mfundo za m’Malemba amene anauziridwa ndi mzimu woyera. Choncho tikamamvera oyang’anira mumpingo timasonyeza kuti timalemekeza Yehova ndi Yesu amene ndi Abusa aakulu. (Luka 10:16) Mfundo imeneyi ndi imene iyenera kutilimbikitsa kwambiri kugonjera akulu. Komabe tiyenera kuwamvera pa zifukwa zinanso.

7. Kodi akulu amakuthandizani bwanji kuti mukhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova?

7 Akulu amalimbikitsa ndiponso kulangiza Akhristu anzawo pogwiritsa ntchito Baibulo kapena mfundo za m’Malemba. Popereka malangizowo sakhala ndi cholinga choti azilamulira abale awo. (2 Akor. 1:24) Koma amafuna kuthandiza kuti mumpingo mukhale mtendere ndiponso kuti abale azisankha mwanzeru zochita. (1 Akor. 14:33, 40) Akulu “amayang’anira miyoyo” yathu poyesetsa kuthandiza aliyense mumpingo kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. N’chifukwa chake amafulumira kuthandiza m’bale kapena mlongo amene watsala pang’ono ‘kupatuka’ kapena amene wapatuka kale. (Agal. 6:1, 2; Yuda 22) Izitu ndi zifukwa zomveka zotichititsa ‘kumvera amene akutsogolera.’—Werengani Aheberi 13:17.

8. Kodi akulu amateteza bwanji nkhosa za Mulungu?

8 Mtumwi Paulo yemwenso anali m’busa, analembera abale a ku Kolose kuti: “Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.” (Akol. 2:8) Chenjezo limeneli limasonyeza chifukwa chinanso chotichititsa kutsatira malangizo a m’Malemba amene akulu angatipatse. Akuluwo amateteza abale powachenjeza za anthu amene angasokoneze chikhulupiriro chawo. Mtumwi Petulo anachenjeza za “aneneri onyenga” ndiponso “aphunzitsi onyenga” amene “amakopa anthu apendapenda” kuti achite zoipa.  (2 Pet. 2:1, 14) Masiku anonso akulu ayenera kuchenjeza abale ngati pakufunika kutero. Akuluwo amakhala kuti akudziwa zambiri. Komanso asanakhale akulu anali atasonyeza kuti amadziwa bwino Malemba ndipo akhoza kuphunzitsa zolondola. (1 Tim. 3:2; Tito 1:9) Iwo amatha kupereka malangizo mwaluso chifukwa chakuti ndi odziwa zambiri, ali ndi nzeru zochokera m’Malemba komanso sachita zinthu monyanyira.

Mofanana ndi m’busa, akulu amateteza nkhosa zimene akuyang’anira (Onani ndime 8)

M’BUSA WABWINO AMADYETSA NKHOSA NDIPONSO KUZITETEZA

9. Kodi Yesu amachita zotani potsogolera ndiponso kudyetsa mpingo masiku ano?

9 Yehova amagwiritsa ntchito gulu lake kuti apereke chakudya chauzimu chochuluka kwa Akhristu onse padziko lapansi. Timalandira malangizo ambiri ochokera m’Baibulo kudzera m’mabuku amene gululi limafalitsa. Koma nthawi zina gulu limapereka malangizo apadera kwa akulu pogwiritsa ntchito makalata kapena oyang’anira oyendayenda. Zonsezi zimathandiza kuti nkhosa zilandire malangizo omveka bwino.

10. Kodi akulu ayenera kuchita chiyani nkhosa zina zikapatuka?

10 Akulu alinso ndi udindo woteteza ndiponso kusamalira abale ndi alongo makamaka amene afooka kapena amene achita machimo enaake. (Werengani Yakobo 5:14, 15.) Mwina abale ndi alongo ena apatuka n’kusiya kutumikira Mulungu. Izi zikachitika, mkulu wachikondi ayenera kuchita  zonse zimene angathe kuti apeze nkhosa yotayikayo n’kuikusira m’khola kapena kuti mumpingo. Yesu anati: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”—Mat. 18:12-14.

KODI TIZIONA BWANJI ZIMENE ABUSA AANG’ONO AMALAKWITSA?

11. N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta nthawi zina kutsatira malangizo a akulu?

11 Yehova ndi Yesu ndi Abusa angwiro. Koma abusa aang’ono amene atipatsa kuti asamalire mipingo si angwiro. Choncho nthawi zina zingakhale zovuta kutsatira malangizo a akuluwo. Anthu ena angaganize kuti: ‘Akulu nawonso si angwiro. Ndiye palibe chifukwa choti tizitsatira malangizo awo.’ N’zoona kuti akulu si angwiro koma tiyenera kuona moyenera zofooka ndi zolakwa zawo.

12, 13. (a) Kodi anthu ena amene anali ndi udindo wotsogolera anthu a Mulungu analakwitsa zinthu ziti? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anachititsa kuti zolakwa za anthu amene ankawagwiritsa ntchito zilembedwe m’Baibulo?

12 Malemba amafotokoza mosapita m’mbali zolakwa za anthu amene Yehova anasankha kuti azitsogolera anthu ake. Mwachitsanzo, Davide anasankhidwa kukhala mfumu ndiponso mtsogoleri wa Isiraeli. Koma iye anachita chigololo ndiponso anapha munthu. (2 Sam. 12:7-9) Chitsanzo china ndi mtumwi Petulo. Ngakhale kuti anapatsidwa udindo waukulu mumpingo, analakwitsa zinthu zikuluzikulu. (Mat. 16:18, 19; Yoh. 13:38; 18:27; Agal. 2:11-14) Kuyambira nthawi imene Adamu ndi Hava anachimwa, Yesu yekha ndi amene anali wangwiro padzikoli.

13 N’chifukwa chiyani Yehova anachititsa kuti olemba Baibulo alembe zolakwa za anthu amene ankawagwiritsa ntchito? Chifukwa chimodzi n’chakuti ankafuna kusonyeza kuti akhoza kugwiritsa ntchito anthu amene si angwiro kuti azitsogolera anthu ake. Kuyambira kale wakhala akugwiritsa ntchito anthu otere. Choncho sitiyenera kung’ung’udza za anthu amene akutitsogolera kapena kunyalanyaza malangizo awo chifukwa cha zimene iwowo amalakwitsa. Yehova amafuna kuti tizilemekeza abalewo ndiponso kuwamvera.—Werengani Ekisodo 16:2, 8.

14, 15. Kodi tikuphunzira chiyani tikaona mmene Yehova ankaperekera malangizo kwa anthu ake m’mbuyomu?

14 Kumvera abale amene akutsogolera mumpingo n’kofunika kwambiri. Taganizirani mmene Yehova ankaperekera malangizo kwa anthu ake pa nthawi zovuta m’mbuyomu. Pamene Aisiraeli ankachoka ku Iguputo, Mulungu ankawapatsa malangizo kudzera mwa Mose ndi Aroni. Aisiraeli anayenera kumvera malangizo oti adye chakudya chapadera ndiponso kuwaza magazi a nkhosa pamafelemu a pakhomo kuti apulumuke mliri wa nambala 10. Mulungu sanapereke yekha malangizo amenewa kuchokera kumwamba. Aisiraeliwo anayenera kumvera akuluakulu awo omwe analandira malangizowo kuchokera kwa Mose. (Eks. 12:1-7, 21-23, 29) Pa nthawiyo, Mose ndiponso akuluakuluwo anali oimira Yehova popereka malangizo kwa anthu ake. Masiku ano, akulu mumpingo amagwiranso ntchito yofunika imeneyi.

15 Mosakayikira mungakumbukire za nthawi zina m’Baibulo pamene Yehova anagwiritsa ntchito angelo kapena anthu ena popereka malangizo othandiza kuti anthu apulumuke. Pa nthawi zonsezi Yehova sanapereke yekha malangizowo koma anagwiritsa ntchito anthu kapena angelo. Iwo  ankaimira Yehova ndipo anauza atumiki ake zimene ayenera kuchita kuti apulumuke. Kodi mukuganiza kuti Yehova sadzachitanso zimenezi pa nthawi ya Aramagedo? Choncho akulu amene apatsidwa mwayi woimira Yehova kapena gulu lake masiku ano ayenera kusamala kwambiri kuti asamagwiritse ntchito mosayenera udindo wawo.

“GULU LIMODZI NDI M’BUSA MMODZI”

16. Kodi tikuyenera kumvera “mawu” ati?

16 Anthu a Yehova ali ‘m’gulu limodzi’ ndipo ali ndi “m’busa mmodzi,” yemwe ndi Yesu Khristu. (Yoh. 10:16) Yesu ananena kuti adzakhala ndi ophunzira ake “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Iye tsopano ndi Mfumu kumwamba, ndipo zonse zimene ziyenera kuchitika dziko la Satanali lisanawonongedwe zili m’manja mwake. Kuti tikhalebe ogwirizana komanso otetezeka m’gulu la Mulungu, tiyenera kumvera ‘mawu akumbuyo kwathu’ otiuza njira yoyenera kupita. “Mawu” amenewo akuphatikizapo zimene mzimu wa Mulungu ukunena kudzera m’Baibulo komanso zimene Yehova ndi Yesu akunena kudzera mwa abale amene awasankha kuti akhale abusa aang’ono.—Werengani Yesaya 30:21; Chivumbulutso 3:22.

Akulu amayesetsa kuthandiza makolo amene akulera okha ana kuti anawo asamacheze ndi anthu olakwika (Onani ndime 17 ndi 18)

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani anthu a Yehova ayenera kukhala tcheru? (b) Kodi sitiyenera kukayikira lonjezo liti? (c) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

17 Baibulo limanena kuti Satana akuyendayenda “ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Pet. 5:8) Iye ali ngati chilombo cholusa komanso chanjala ndipo akuwenderera aliyense wofooka kapena amene wasochera kuti amumbwandire. N’chifukwa chake sitiyenera kuchoka ngakhale pang’ono m’gulu la Mulungu n’kusiyana ndi ‘m’busa wathu ndi woyang’anira miyoyo yathu.’ (1 Pet. 2:25) Ponena za anthu amene adzapulumuke chisautso chachikulu, lemba la Chivumbulutso 7:17 limanena kuti: “Mwanawankhosa [Yesu] . . . adzawaweta ndi kuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo. Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.” Limenelitu ndi lonjezo losangalatsa zedi.

18 M’nkhaniyi takambirana udindo waukulu umene akulu ali nawo mumpingo monga abusa aang’ono. Koma funso ndi lakuti, Kodi akulu amenewa angatani kuti azisamalira bwino nkhosa za Yesu? Tidzakambirana yankho lake m’nkhani yotsatira.