Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MBIRI YA MOYO WATHU

Tachita Utumiki wa Nthawi Zonse kwa Zaka 50 Kumpoto Kwenikweni

Tachita Utumiki wa Nthawi Zonse kwa Zaka 50 Kumpoto Kwenikweni

Tsiku lina tinauza mnzathu kuti: “Iwe upainiya sungakuvute. Makolo ako onse ndi Mboni ndipo amakuthandiza.” Koma iye anayankha kuti: “Atsikana inu, tonsefetu tili ndi Bambo mmodzi.” Zimene ananenazi zinatikumbutsa mfundo yofunika yakuti: Atate wathu wakumwamba amasamalira ndiponso kulimbikitsa atumiki ake. Pa moyo wathu taona umboni wa mfundo imeneyi.

 TINABADWIRA kudera lakumpoto m’dziko la Finland. M’banja lathu tinalimo ana 10 ndipo tinkakhala pafamu inayake. Pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkachitika, ifeyo tinali ana. Ngakhale kuti anthu ankamenyana kutali ndi nyumba yathu, tinkadziwa kuti anthu akuvutika kwambiri. Tsiku lina usiku, tinangoona kuwala kofiira kumwamba pamene mabomba anaponyedwa m’mizinda ya Oulu ndi Kalajoki. Makolo athu anatiuza kuti tizibisala tikaona ndege zankhondo zikudutsa. Mchimwene wathu wamkulu, dzina lake Tauno, atatiuza za nthawi imene dzikoli lidzakhala paradaiso komanso lopanda mavuto, tinkafuna kudziwa zambiri.

Tauno anaphunzira choonadi ali ndi zaka 14. Iye ankawerenga mabuku ochokera kwa Ophunzira Baibulo. Pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayamba, iye anakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo. Choncho anamangidwa ndipo kundendeko anazunzidwa kwambiri. Izi zinangochititsa kuti azikonda kwambiri kutumikira Yehova ndipo atatuluka, ankalalikira mwakhama kwambiri. Zochita za mchimwene wathuyu zinatilimbikitsa kuti tizipita ku misonkhano ya Mboni imene inkachitika kumudzi wina wapafupi. Tinkapitanso ku misonkhano ikuluikulu ngakhale kuti zinali zovuta kuti tipeze ndalama zokwanira ulendowo. Kuti tipeze ndalama, tinkalima anyezi, kugulitsa zipatso komanso kusokera anthu zovala. Pafamu yathu pankakhala ntchito yaikulu choncho ikafika nthawi ya misonkhano, wina ankatsala.

Kuchokera kumanzere: Matti (bambo), Tauno, Saimi, Maria Emilia (mayi), Väinö (mwana), Aili ndi Annikki mu 1935

Zimene tinaphunzira zokhudza Yehova ndi zolinga zake zinatichititsa kumukonda kwambiri ndipo tinadzipereka kwa iye. Ndiyeno tinabatizidwa mu 1947. (Pa nthawiyi, Annikki anali ndi zaka 15 ndipo Aili anali ndi zaka 17.) Mchemwali wathu, dzina lake Saimi, anabatizidwanso chaka chomwecho. Tinkaphunziranso Baibulo ndi mchemwali wathu wina, dzina lake Linnea, yemwe pa nthawiyo anali pa banja. Iye ndi banja lake anadzakhalanso Mboni za Yehova. Titangobatizidwa, tinkafuna kuchita upainiya wothandiza nthawi ndi nthawi.

TINAYAMBA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE

Kuchokera kumanzere: Eeva Kallio, Saimi Mattila-Syrjälä, Aili, Annikki, ndi Saara Noponen mu 1949

Mu 1955, tinasamukira chakumpoto mumzinda wa Kemi. Ngakhale kuti tonse tinkagwira ntchito, tinkafunabe kuchita upainiya. Koma tinkaopa kuti sitingapeze ndalama zokwanira tikachepetsa masiku amene tinkagwira ntchito. Ndiyeno tinkaganiza kuti tiyambe tasunga kaye ndalama. Iyi ndi nthawi imene tinakambirana ndi mnzathu uja. Zimene iye ananena zinatithandiza kuona kuti Yehova ndi amene angatithandize kuchita utumiki wa nthawi zonse. Tinaona kuti sitiyenera kudzidalira tokha kapena kudalira achibale.

Tikupita ku msonkhano ku Kuopio mu 1952. Kuchokera kumanzere: Annikki, Aili, ndi Eeva Kallio

Pa nthawiyo, tinali ndi ndalama zokwanira kugula zofunika pa miyezi iwiri. Choncho mu May 1957, tinafunsira upainiya wa miyezi iwiri koma tinkachita mantha. Tinachita upainiyawo kumpoto kwenikweni,  mumzinda wa Pello kudera la Lapland. Koma pamene miyezi iwiriyo inkatha, tinali tisanagwiritse ntchito ndalama zathuzo. Choncho tinafunsira miyezi iwiri inanso. Pamene miyezi iwiriyi inkathanso, ndalamazo zinalipobe. Apa tsopano tinadziwa kuti Yehova adzatisamaliradi. Ndalamazo zilipobe ngakhale kuti tachita upainiya kwa zaka 50 tsopano. Timaona ngati Yehova anatigwira manja n’kutiuza kuti: ‘Musachite mantha. Ineyo ndikuthandizani.’—Yes. 41:13.

Ndalama zija zilipobe ngakhale kuti tachita upainiya kwa zaka 50 tsopano

Kaisu Reikko ndi Aili akulalikira

Mu 1958, woyang’anira dera wathu anatipempha kukatumikira monga apainiya apadera kutauni ina (Sodankylä) m’dera la Lapland. Pa nthawiyo, m’dera lonselo munali Mboni imodzi yokha ndipo anali mlongo. Iye anaphunzira choonadi m’njira yochititsa chidwi. Mwana wake wamwamuna anapita ndi kalasi yake kumzinda wa Helsinki, womwe ndi likulu la dziko la Finland. Pamene anawo anali kuyenda mumzindawo, mwanayu anali kumapeto. Ndiyeno mlongo wina wachikulire anapereka Nsanja ya Olonda kwa mwanayo n’kumuuza kuti akapereke kwa mayi ake. Mayiyo ataiwerenga, anadziwiratu kuti apeza choonadi.

Kumzindawo, tinkachita lendi chipinda chinachake m’nyumba yochekera matabwa. Tinkachita misonkhano m’nyumba imeneyi. Poyamba, tinkasonkhana ife awiri, mlongo uja ndi mwana wake wamkazi basi. Tinkangowerengera limodzi nkhani zimene tinkayenera kuphunzira mlungu umenewo. Kenako mwamuna wina amene ankaphunzira Baibulo ndi Mboni anabwera kudzagwira ntchito yocheka matabwa. Iye ndi banja lake anayamba kusonkhana nafe. Patapita nthawi, iye ndi mkazi wake anabatizidwa. M’baleyu anayamba kutsogolera zinthu pa misonkhano yathu. Amuna ena amene ankagwiranso ntchito komweko anayambanso kusonkhana nafe ndipo anadzakhala Mboni. Patapita zaka zochepa, mpingo unakhazikitsidwa.

MAVUTO AMENE TINAKUMANA NAWO

Tinkayenda maulendo ataliatali kuti tikalalikire. M’nyengo yotentherapo tinkayenda wapansi, panjinga kapena paboti. Njinga zathu zinkatithandiza kwambiri. Tinkazigwiritsanso ntchito popita ku misonkhano ikuluikulu komanso pokaona makolo athu omwe ankakhala pa mtunda wa makilomita mahandiredi angapo. M’nyengo yozizira, tinkakwera basi m’mawa kwambiri kupita kumudzi winawake kenako n’kumayenda nyumba ndi nyumba. Tikamaliza mudzi umodzi, tinkayenda wapansi kupita kumudzi wina. Kunkakhala chipale chofewa  chambiri ndipo nthawi zina misewu sinkaoneka. Nthawi zambiri tinkangotsatira tinjira topangidwa ndi ngolo zokokedwa ndi mahatchi. Koma kukagwa chipale chofewa china, tinjirato sitinkaonekanso. Nyengo ikayamba kutentherapo chipalecho chinkayamba kusungunuka ndiye zinkakhala ngati tikuyenda m’matope.

Tikulalikira, kunja kukuzizira koopsa

Popeza kuderali kunali kozizira kwambiri, tinkavala zovala zotenthera bwino. Tinkavala mapeyala angapo a sokosi komanso nsapato zofika m’mawondo. Koma nthawi zambiri chipale chofewacho chinkalowabe m’nsapatozo. Tikafika panyumba tinkavula nsapatozo n’kukutumula chipale chofewacho. Majasi athu ankanyowanso m’munsi tikamadutsa m’chipale chofewa. Kukazizira kwambiri mbali yonyowayo inkauma gwa. Tsiku lina tinayenda mtunda wa makilomita 11 kuti tikafike kunyumba ina ndipo mayi amene tinamupeza anati: “Koma ndiye muli ndi chikhulupiriro chenichenitu. Kulolera kuyenda kunjaku kuli chonchi?”

Nthawi zambiri tinkapempha malo ogona kwa anthu amene tinkawalalikira m’madera akutali. Tinyumba take tinali ting’onoting’ono koma anthu ake anali odziwa kulandira alendo. Iwo ankatipatsa malo ogona komanso chakudya. Nthawi zambiri tinkagona pa zikopa za mphalapala kapena za chimbalangondo. Koma nthawi zina tinkapeza zinthu zabwino. Mwachitsanzo, mayi wina anali ndi nyumba yaikulu ndipo anatilola kuti tigone m’chipinda china cham’mwamba chomwe chinali ndi bedi lokongola komanso nsalu zoyalapo zabwino kwambiri. Nthawi zambiri tinkaphunzira Baibulo ndi anthu mpaka usiku. Kunyumba ina tinkagona m’chipinda chimodzi ndi eni nyumbayo, iwo mbali ina ife mbali ina. Mwamuna akafunsa funso, mkazinso ankafunsa lake. Tinkakambirana nawo Malemba mpaka pakati pa usiku mwinanso m’bandakucha.

UTUMIKI UNALI WOSANGALATSA

Dera la Lapland ndi lokongola kwambiri. Koma ife chimene chinkatisangalatsa kwambiri ndi anthu amene tinkaphunzira nawo za Yehova. Anthu ena amene tinkawalalikira anali azibambo obwera kudzadula mitengo ku Lapland. Nthawi zina, awirife tikalowa m’nyumba tinkapeza kuti muli azibambo ambirimbiri. Koma chosangalatsa n’chakuti ankamvetsera uthenga wathu wochokera m’Baibulo komanso ankalandira mabuku athu.

Pali zinthu zambiri zosangalatsa zimene zinkachitika. Tsiku lina, basi yathu inatithawa chifukwa chakuti wotchi ya pasiteji inkafulumira ndi maminitsi 5. Ndiyeno tinaganiza zongokwera basi yopita kumudzi wina. Aka kanali koyamba kukafika kumudzi umenewo. Titafika panyumba yoyamba, tinapeza mayi wina amene anati: “E! Eee! Mwafika atsikana. Kuteroku ndimakudikiranitu.” Tinkaphunzira Baibulo ndi mchemwali wake. Ndiyeno mayiyo anali atamupempha mchemwali wakeyo kuti atiuze kuti tipite kunyumbayo tsiku limenelolo koma sanatiuze. Tinayamba kuphunzira Baibulo ndi mayiyo komanso achibale ake amene ankakhala pafupi.  Pasanapite nthawi yaitali, tinauza anthuwo kuti tiziphunzirira pamodzi moti linali phunziro la anthu 12. Panopa, anthu ambiri m’banja limeneli ndi Mboni za Yehova.

Mu 1965, tinapemphedwa kuti tikatumikire chakum’mwera, ku mpingo wa Kuusamo, ndipo n’kumene tili mpaka pano. Pa nthawiyo, mu mpingowo munali ofalitsa ochepa kwambiri ndipo gawo limene tinkalalikira linkaoneka lovuta. Anthu ake anali achipembedzo ndipo ankadana ndi ntchito yathu. Koma ubwino wake ndi wakuti ambiri ankalemekeza Baibulo ndipo izi zinkathandiza kuti tiziona poyambira. Pang’ono ndi pang’ono tinayamba kuzolowerana ndi anthuwo ndipo pambuyo pa zaka ziwiri, sitinkavutikanso kuyambitsa maphunziro a Baibulo.

TIKUCHITABE KHAMA MU UTUMIKI

Anthu ena amene tinaphunzira nawo Baibulo

Masiku ano, tilibe mphamvu yoti tizilowa mu utumiki tsiku lonse koma timalowabe nthawi yochepa pafupifupi tsiku lililonse. Kulalikira kumadera akutali kwaphweka tsopano chifukwa chakuti mwana wa mchimwene wathu analimbikitsa Aili kuti aphunzire kuyendetsa galimoto. Aili anapeza laisensi mu 1987 pamene anali ndi zaka 56. Zinthu zinatiyenderanso bwino pamene Nyumba ya Ufumu yatsopano inamangidwa. Anatipempha kuti tizikhala m’kanyumba ka pa Nyumba ya Ufumuyo.

Tikusangalala kwambiri kuti anthu ambiri kumpoto kwa Finland alowa m’choonadi. Pamene tinkayamba utumiki wa nthawi zonse, m’dera lalikululi munali Mboni zochepa zokha. Panopa kuli mipingo yambiri. Nthawi zambiri, ku misonkhano ikuluikulu anthu amatifunsa kuti: “Kodi mukundikumbukira?” Nthawi zina amakhala anthu amene tinkaphunzira ndi makolo awo iwowo ali ana. Mbewu zimene tinabzala kalekalelo zabala zipatso.—1 Akor. 3:6.

Timasangalala kulalikira ngakhale kukugwa mvula

Mu 2008, tinakwanitsa zaka 50 tikuchita upainiya wapadera. Timathokoza Yehova kuti watithandiza kuti tizilimbikitsana kupirira m’ntchito imeneyi. Takhala moyo wosalira zambiri koma sitinasowepo kanthu kalikonse. (Sal. 23:1) Panopa timadziwa kuti sitinayenera kukayikakayika poyamba paja. Pa zaka zonsezi, Yehova watilimbikitsa mogwirizana ndi lonjezo lake la pa Yesaya 41:10 lakuti: “Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.”