Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Kuti Muzipindula Powerenga Baibulo

Zimene Mungachite Kuti Muzipindula Powerenga Baibulo

“Ndimasangalala kwambiri ndi chilamulo cha Mulungu.”—AROMA 7:22.

1-3. Kodi kuwerenga Baibulo ndiponso kutsatira zimene tikuphunzira kungatithandize bwanji?

MLONGO wina wachikulire anati: “Ndimathokoza Yehova m’mawa uliwonse chifukwa chondithandiza kumvetsa Baibulo.” Mlongoyu wawerenga Baibulo maulendo oposa 40 ndipo akuwerengabe. Mtsikana wina analemba kuti kuwerenga Baibulo kwamuthandiza kum’dziwa bwino Yehova. Izi zachititsa kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Atate wake wakumwamba. Iye anati: “Sindinakhalepo wosangalala chonchi pa moyo wanga.”

2 Mtumwi Petulo anatilimbikitsa ‘kulakalaka mkaka wosasukuluka umene uli m’mawu a Mulungu.’ (1 Pet. 2:2) Tikamaphunzira Baibulo ndiponso kutsatira zimene timaphunzira, timakhala ndi chikumbumtima choyera ndiponso moyo wosangalala. Zimatithandizanso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi anthu ena omwe amakonda ndiponso kutumikira Mulungu woona. Izitu ndi zifukwa zomveka zotichititsa ‘kusangalala kwambiri ndi chilamulo cha Mulungu.’ (Aroma 7:22) Koma kodi Baibulo lingatithandizenso m’njira zina ziti?

3 Mukamaphunzira za Yehova ndi Mwana wake, mumawakonda kwambiri ndiponso kukonda anthu ena. Kudziwa Malemba molondola kungakuthandizeni kuzindikira mmene Mulungu adzapulumutsire anthu omvera m’dziko loipali. Zimenezi zimachititsa kuti mukhale ndi uthenga wabwino woti muuze anthu mu utumiki. Ndipotu Yehova adzakudalitsani mukamaphunzitsa anthu ena zimene mwaphunzira m’Mawu ake.

MUZIWERENGA NDIPONSO KUSINKHASINKHA

4. Kodi kusinkhasinkha kumatanthauza chiyani?

4 Yehova safuna kuti tiziwerenga Mawu ake mothamanga. Iye anauza Yoswa kuti: “Buku la malamulo ili lisachoke pakamwa pako, uziliwerenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku.” (Yos. 1:8; Sal. 1:2) Kodi malangizo amenewa  akutanthauza kuti tizitchula mokweza mawu onse a m’Baibulo tikamawerenga? Ayi. Kusinkhasinkha kumatanthauza kuwerenga mosathamanga kuti muzikhala ndi mpata woganizira zimene mukuwerengazo. Mukamawerenga Baibulo m’njira imeneyi, mumatha kuganizira kwambiri mfundo zimene zingakuthandizeni ndiponso kukulimbikitsani pa nthawiyo. Mukapeza mfundo zoterezi, muyenera kuziwerenga pang’onopang’ono mwinanso kuzitchula mwapansipansi. Mukamatero, mumakhudzidwa kwambiri ndi mfundozo. Kodi zimenezi n’zofunika bwanji? Munthu akamvetsa malangizo a Mulungu m’njira imeneyi, amafunitsitsa kuwatsatira.

5-7. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kusinkhasinkha Mawu a Mulungu kungakuthandizeni (a) kutsatira malamulo a Mulungu; (b) kulankhula anthu ena mokoma mtima; (c) kudalira Yehova ngakhale pa nthawi yovuta.

5 Kusinkhasinkha kumathandiza kwambiri mukamawerenga mabuku a m’Baibulo omwe si ozolowereka. Mwachitsanzo, tiyeni tiyerekezere zochitika zitatu izi. Tinene kuti mnyamata wina akuwerenga Baibulo ndipo wafika pa ulosi wa Hoseya. Atawerenga mosamala chaputala 4 vesi 11 mpaka 13, akuima kaye kuti asinkhesinkhe. (Werengani Hoseya 4:11-13.) Iye akutero chifukwa chakuti kusukulu amayesedwa kwambiri kuti achite zinthu zoipa. Akuganizira kwambiri mavesiwa n’kumadziuza kuti: ‘Yehova amaona zinthu zoipa zimene anthu amachita ngakhale zobisika. Ine sindifuna kumukhumudwitsa.’ Ndiyeno mnyamatayo akutsimikiza mumtima mwake kuti akhalebe woyera pamaso pa Mulungu.

6 Tiyerekezenso kuti mlongo wina akuwerenga ulosi wa Yoweli ndipo wafika pa chaputala 2 vesi 13. (Werengani Yoweli 2:13.) Ndiyeno pamene akuwerenga lembali mosamala, akuganizira zimene angachite kuti atsanzire Yehova, yemwe ndi “wachisomo, wachifundo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.” Kenako akuona kuti nthawi zina amalankhula mwamuna wake komanso anthu ena mwachipongwe ndiponso mwaukali choncho akufuna kusiya zimenezo.

7 Pomaliza, tiyerekeze kuti bambo amene wachotsedwa ntchito akuda nkhawa akaganizira mmene angasamalirire mkazi ndi ana. Ndiyeno akuwerenga mosamala Nahumu 1:7 pamene pali mawu akuti Yehova “amadziwa amene amathawira kwa iye” ndipo ali ngati “malo achitetezo pa tsiku la nsautso.” Mfundo imeneyi ikumukhazika mtima pansi. Iye akuzindikira kuti Yehova ndi wachikondi kwambiri ndipo nkhawa yake ikuchepa. Ndiyeno akuwerenga mosamala vesi 15. (Werengani Nahumu 1:15.) M’baleyo akuona kuti kulalikira pa nthawi yovutayo kungasonyeze kuti iye amaona kuti Yehova ndi malo ake achitetezo. Iye akuona kuti ndi bwino kuti pamene akufufuza ntchito, azilowanso mu utumiki mkati mwa mlungu.

8. Tchulani zinthu zamtengo wapatali zimene munapeza powerenga Baibulo.

8 Taonani kuti mfundo zothandiza zimene takambiranazi tazipeza m’mabuku a m’Baibulo amene ena amawaona kuti ndi ovuta kuwamvetsa. Tikapeza mavesi olimbikitsa m’mabuku ngati Hoseya, Yoweli ndi Nahumu, tidzafunitsitsa kuwerenga mavesi ena mosamala. Mfundo zake zikhoza kutilimbikitsa kwambiri komanso kutipatsa nzeru. Koma dziwani kuti mabuku onse a m’Baibulo akhoza kutithandizanso chonchi. Baibulo lili ngati mgodi umene tingapezemo miyala yamtengo wapatali. Chitani khama pokumba mumgodiwu. Muziwerenga Baibulo lonse n’cholinga choti mupeze mfundo zolimbikitsa komanso malangizo amtengo wapatali.

MUZIYESETSA KUMVETSA ZIMENE MUKUWERENGA

9. Kodi tingatani kuti timvetse bwino Baibulo?

9 Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse n’kofunika kwambiri. Koma muyenera kuyesetsa kumvetsa bwino zimene mukuwerenga. Choncho muzifufuza za anthu, malo kapena zochitika zimene mukuwerenga pogwiritsa ntchito mabuku amene gulu la Yehova limatipatsa. Ngati  mukufuna kudziwa mmene mungagwiritsire ntchito mfundo inayake imene munawerenga m’Baibulo, mungafunse mkulu kapena Mkhristu wina wodziwa zambiri kuti akuthandizeni. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Mkhristu wina m’nthawi ya atumwi, dzina lake Apolo. Iye anafunika kuthandizidwa kuti amvetse mfundo zina za choonadi.

10, 11. (a) Kodi Apolo anathandizidwa bwanji kuti aphunzitse molondola uthenga wabwino? (b) Kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani ya Apolo? (Onani bokosi lakuti, “Kodi Mumaphunzitsa Zolondola?”)

10 Apolo anali Mkhristu wachiyuda amene anali “kuwadziwa bwino Malemba” komanso “wodzipereka kwambiri chifukwa chakuti anali ndi mzimu woyera.” Ponena za iye, buku la Machitidwe limati: “Anali kulankhula ndi kuphunzitsa molondola za Yesu. Koma anali kudziwa za ubatizo wa Yohane wokha basi.” Apolo sankadziwa kuti zimene ankaphunzitsa pa nkhani ya ubatizo si zolondola. Purisikila ndi Akula atamva Apolo akuphunzitsa ku Efeso, anamufotokozera “njira ya Mulungu molondola.” (Mac. 18:24-26) Kodi zimenezi zinathandiza bwanji Apolo?

11 Apolo atalalikira ku Efeso, anapita ku Akaya. “Iye atafika kumeneko, anathandiza kwambiri anthu amene anali atakhulupirira chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. Pakuti mwamphamvu, iye anawatsimikizira Ayuda poyera kuti anali olakwa, ndipo anasonyeza mwa Malemba kuti Yesu ndiyedi Khristu.” (Mac. 18:27, 28) Pa nthawi imeneyo, Apolo ankaphunzitsa zolondola zokhudza ubatizo wachikhristu. Chifukwa chodziwa zolondola, iye “anathandiza kwambiri” anthu kulambira Mulungu m’njira yoyenera. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Ifenso tiziyesetsa kumvetsa zimene timawerenga m’Baibulo. Komabe ngati Mkhristu mnzathu wodziwa zambiri akutithandiza mmene tingaphunzitsire bwino, tiziyamikira n’kutsatira malangizowo modzichepetsa. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tikhale aphunzitsi abwino.

 ZIMENE MWAPHUNZIRA M’BAIBULO MUZITHANDIZA NAZO ENA

12, 13. Perekani chitsanzo cha mmene mungagwiritsire ntchito Malemba mwaluso kuti muthandize ophunzira Baibulo kusankha kulambira Yehova.

12 Nafenso tikhoza kuthandiza anthu ena ngati mmene anachitira Akula, Purisikila ndi Apolo. Kodi mumamva bwanji ngati mwalimbikitsa munthu amene akuphunzira Baibulo kuthana ndi vuto linalake kuti ayambe kutumikira Yehova? Ngati ndinu mkulu, kodi mumamva bwanji Mkhristu wina akakuyamikirani chifukwa choti munamupatsa malangizo ochokera m’Malemba amene anamuthandiza pa nthawi yovuta? Kunena zoona, kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pothandiza anthu ena kusintha moyo wawo kumasangalatsa kwambiri. * Tiyeni tikambirane mmene tingachitire zimenezi.

13 M’masiku a Eliya, Aisiraeli ambiri anali asanasankhe pakati pa kulambira koona ndi konyenga. Malangizo amene Eliya anawapatsa akhoza kuthandiza wophunzira Baibulo yemwe sanasankhebe kutumikira Yehova. (Werengani 1 Mafumu 18:21.) Bwanji ngati munthu amene akuphunzira Baibulo amaopa zimene anzake kapena achibale ake anganene? Mukhoza kumulimbikitsa kuti asankhe kulambira Yehova pokambirana naye lemba la Yesaya 51:12, 13.—Werengani.

14. Kodi mungatani kuti muzikumbukira malemba oti mugwiritse ntchito pothandiza ena?

14 Baibulo lili ndi mawu ambiri amene amatilimbikitsa ndiponso kutilangiza. Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingadziwe bwanji malemba oyenera kugwiritsa ntchito pa nthawi inayake?’ Muyenera kuwerenga Baibulo tsiku lililonse ndiponso kusinkhasinkha zimene mwawerenga. Mukamatero, mudzayamba kudziwa bwino Malemba ndipo mzimu woyera ungakuthandizeni kukumbukira pa nthawi yake mawu amene munawerenga m’Baibulo.—Maliko 13:11; werengani Yohane 14:26. *

15. N’chiyani chingakuthandizeni kumvetsa bwino Mawu a Mulungu?

15 Mofanana ndi Mfumu Solomo, muzipempha Yehova kuti akupatseni nzeru kuti muthe kukwaniritsa maudindo anu m’gulu la Yehova. (2 Mbiri 1:7-10) Tsanzirani aneneri akale amene ‘anafufuza mwakhama ndi mosamala’ m’Mawu a Mulungu kuti adziwe bwino Yehova ndiponso zimene iye amafuna. (1 Pet. 1:10-12) Mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteyo kuphunzira “mawu a chikhulupiriro ndiponso chiphunzitso chabwino.” (1 Tim. 4:6) Mukamatero, mudzatha kuthandiza bwino ena kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso mudzalimbitsa chikhulupiriro chanu.

MAWU A MULUNGU AMATITETEZA

16. (a) Kodi kufufuza Malemba mosamala tsiku ndi tsiku kunathandiza bwanji Ayuda a ku Bereya? (b) Kodi kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku n’kofunika bwanji masiku ano?

16 Ayuda omwe ankakhala mumzinda wa Bereya ku Makedoniya anali ndi chizolowezi choti ‘tsiku ndi tsiku ankafufuza Malemba mosamala.’ Pamene Paulo ankalalikira uthenga wabwino kwa Ayuda amenewa, iwo ankayerekezera uthenga wakewo ndi zimene ankadziwa kale kuchokera m’Malemba. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Ambiri anazindikira kuti iye ankaphunzitsa choonadi ndipo “anakhala okhulupirira.” (Mac. 17:10-12) Izi zikusonyeza kuti kuwerenga Baibulo tsiku lililonse kumathandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova. Chikhulupiriro chimenechi, kapena kuti “chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa,” n’chofunika kwambiri kuti tipulumuke  n’kulowa m’dziko latsopano la Mulungu.—Aheb. 11:1.

17, 18. (a) Kodi chikhulupiriro cholimba komanso chikondi zimateteza bwanji mtima wathu wophiphiritsa? (b) Kodi chiyembekezo chimatiteteza bwanji?

17 Paulo analemba kuti: “Koma ife amene tili a usana, tikhalebe oganiza bwino ndipo tivale chodzitetezera pachifuwa chachikhulupiriro ndi chikondi. Tivalenso chiyembekezo chachipulumutso monga chisoti.” (1 Ates. 5:8) Msilikali amafunika kuteteza mtima wake kuti asaphedwe. Mtima wophiphiritsa wa Akhristu umafunikanso kutetezedwa kuti usawonongedwe ndi uchimo. Kodi chimachitika n’chiyani ngati mtumiki wa Yehova amakhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu, amamukonda ndiponso amakonda anthu ena? Iye amakhala ngati wavala chovala cholimba kwambiri choteteza pachifuwa. Si zapafupi kuti munthu wotereyu achite zinthu zimene zingawononge ubwenzi wake ndi Yehova.

18 Paulo ananenanso kuti “chiyembekezo cha chipulumutso” chili ngati chisoti. Kale, msilikali ankaphedwa mosavuta ngati sanateteze mutu wake. Koma akavala chisoti cholimba, iye sankavulala kwambiri akamenyedwa m’mutu. Tikamaphunzira Mawu a Mulungu, timakhala ndi chiyembekezo champhamvu chakuti Yehova adzatipulumutsa. Chiyembekezo champhamvuchi chimatithandiza kuti tipewe anthu ampatuko komanso ‘nkhani zawo zopeka’ zomwe ndi zoipa ndipo zimafala mwamsanga. (2 Tim. 2:16-19) Chiyembekezo chathu chingatithandizenso kukana ngati anthu ena akutilimbikitsa kuchita zinthu zimene Yehova amadana nazo.

BAIBULO LIMATITHANDIZA KUTI TIDZAPULUMUKE

19, 20. N’chifukwa chiyani timaona Mawu a Mulungu kukhala ofunika kwambiri? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timawayamikira? (Onani bokosi lakuti, “Yehova Amadziwa Zimene Ndikufunika, N’kundipatsa.”)

19 Pamene tikuyandikira mapeto m’pamenenso tiyenera kudalira kwambiri Mawu a Yehova. Malangizo amene timapeza m’Mawu a Mulungu amatithandiza kusintha makhalidwe oipa ndiponso kulimbana ndi mtima wolakalaka zoipa. Mawu a Mulungu amatilimbikitsa ndiponso kutitonthoza kuti tipirire mayesero ochokera kwa Satana ndi dziko lakeli. Malangizo a m’Mawu a Yehova angatithandize kuyendabe panjira yopita ku moyo.

20 Musaiwale kuti cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke.” Anthu amene akunenedwa pa lembali akuphatikizapo atumiki a Yehova komanso anthu amene timawaphunzitsa Baibulo. Koma anthu onse amene akufuna kupulumuka ayenera “kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Choncho kuti tipulumuke, tiyenera kuwerenga Baibulo ndiponso kutsatira malangizo ake. Tikamawerenga Baibulo tsiku lililonse, timasonyeza kuti Mawu a Yehova, omwe ndi choonadi, ndi amtengo wapatali kwa ife.—Yoh. 17:17.

^ ndime 12 Koma sikuti tizigwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo pokakamiza ena kuchita zinazake kapena powasonyeza kuti iwo ndi oipa. Tiyenera kukhala oleza mtima ndiponso kukomera mtima anthu amene tikuphunzira nawo Baibulo ngati mmene Yehova amachitira ndi ifeyo.—Sal. 103:8.

^ ndime 14 Kodi mungatani ngati mukukumbukira mawu enaake a m’Baibulo koma mwaiwala buku, chaputala ndi vesi? Mwina mukhoza kupeza lembalo mutafufuza mawuwo mu kalozera wa mawu a m’Baibulo kumapeto kwa Baibulo la Dziko Latsopano kapena mu Watchtower Library.