Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ukhale Wolimba Mtima Chifukwa Yehova Ali Nawe

Ukhale Wolimba Mtima Chifukwa Yehova Ali Nawe

“Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. . . . Yehova Mulungu wako ali nawe.”—YOS. 1:9.

1, 2. (a) Kodi ndi makhalidwe ati amene angatithandize kupirira mavuto? (b) Kodi chikhulupiriro n’chiyani? Perekani chitsanzo.

KUTUMIKIRA Yehova kumatithandiza kukhala achimwemwe. Komabe mofanana ndi anthu onse, timakumana ndi mavuto. Tikhozanso kuvutika chifukwa chochita zinthu mwachilungamo. (1 Pet. 3:14; 5:8, 9; 1 Akor. 10:13) Kuti tipirire mavuto amenewa, tiyenera kulimba mtima ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro.

2 Kodi chikhulupiriro n’chiyani? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa, umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheb. 11:1) Baibulo lina limati: “Chikhulupiriro ndicho chikalata chaumboni cha zinthu zimene tikuyembekezera. Chikhulupiriro ndi kukhala otsimikiza kuti zinthu zimene sitingazione zilipo ndithu.” Chikalata chaumboni n’chimene chimasonyeza kuti ndife eni ake a chinthu kapena malo. Timakhulupirira kuti nthawi zonse Mulungu amachita zimene wanena. Choncho zili ngati tapatsidwa chikalata chaumboni wa chinthu chamtengo wapatali. Chikhulupiriro chimatithandiza kuti tisamakayikire kuti tidzaonadi zimene Mulungu walonjeza. Sitikayikiranso mawu a m’Baibulo, ngakhale onena za zinthu zimene sitingazione.

3, 4. (a) Kodi kulimba mtima n’kutani? (b) N’chiyani chingatithandize kukhala olimba mtima ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chathu?

3 Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limanena kuti kulimba mtima kumatanthauza “kulankhula ndiponso kuchita zinthu mopanda mantha ukakumana ndi mavuto kapena zinthu zoopsa.” Ngati ndife olimba mtima timakhala amphamvu, opanda mantha komanso okonzeka kuvutika chifukwa cha zimene timakhulupirira.—Maliko 6:49, 50; 2 Tim. 1:7.

4 Chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima ndi makhalidwe abwino kwambiri. Koma bwanji ngati tikuona kuti  chikhulupiriro chathu n’chochepa ndiponso kuti sindife olimba mtima? M’Baibulo muli anthu ambiri amene anasonyeza makhalidwe amenewa. Choncho kukambirana zitsanzo za anthu ngati amenewa kungatithandize kukhala olimba mtima ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chathu.

YEHOVA ANALI NDI YOSWA

5. Kodi Yoswa anafunika chiyani kuti atsogolere bwino anthu a Mulungu?

5 Tiyeni tikambirane zimene zinachitika pafupifupi zaka 3,500 zapitazo. Pa nthawiyi, panali patadutsa zaka 40 kuchokera pamene Yehova analanditsa Aisiraeli ku ukapolo ku Iguputo. Mneneri Mose ndi amene ankawatsogolera. Ndiyeno ali ndi zaka 120, iye anaona Dziko Lolonjezedwa ali pamwamba pa phiri la Nebo ndipo anamwalira pomwepo. Analowedwa m’malo ndi Yoswa, yemwe anali “wodzazidwa ndi mzimu wa nzeru.” (Deut. 34:1-9) Apa n’kuti Aisiraeli atangotsala pang’ono kulanda dziko la Kanani. Yoswa anafunika nzeru yochokera kwa Mulungu kuti atsogolere bwino anthuwo. Iye anafunikanso kukhulupirira Yehova, kukhala wolimba mtima ndiponso kuchita zinthu mwamphamvu.—Deut. 31:22, 23.

6. (a) Mogwirizana ndi Yoswa 23:6, timafunika kulimba mtima kuti tichite chiyani? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa lemba la Machitidwe 4:18-20 ndi Machitidwe 5:29?

6 Aisiraeli ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ataona nzeru, kulimba mtima ndiponso chikhulupiriro zimene Yoswa anasonyeza. Iye anasonyeza makhalidwewa pa nthawi yonse imene ankagonjetsa dziko la Kanani. Aisiraeli ankafunika kukhala olimba mtima kuti amenye nkhondo komanso kuchita zimene Yoswa anawauza. Yoswa atatsala pang’ono kumwalira, anauza Aisiraeli kuti: “Tsopano khalani olimba mtima kwambiri, kuti musunge ndi kuchita zonse zimene zinalembedwa m’buku la chilamulo cha Mose, posapatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere.” (Yos. 23:6) Ifenso tiyenera kulimba mtima kuti tizimvera Yehova nthawi zonse. Tiyenera kuchita zimenezi ngakhale pamene anthu atipempha kuchita zosemphana ndi zofuna za Mulungu. (Werengani Machitidwe 4:18-20; 5:29.) Ngati tidalira Yehova n’kupemphera kwa iye, adzatithandiza kulimba mtima.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIKHALE NDI MOYO WOPAMBANA

7. Kodi Yoswa anafunika kutani kuti akhale wolimba mtima ndiponso kuti zinthu zimuyendere bwino?

7 Kuti tikhale olimba mtima n’kumachita zofuna za Mulungu, tiyenera kuphunzira ndiponso kutsatira Mawu ake. Izi n’zimene Yoswa anauzidwa kuchita atalowa m’malo mwa Mose. Anauzidwa kuti: “Iwe khala wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula. . . . Buku la malamulo ili lisachoke pakamwa pako, uziliwerenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatira zonse zolembedwamo. Pakuti ukatero, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzachita zinthu mwanzeru.” (Yos. 1:7, 8) Yoswa anatsatira malangizo amenewa ndipo anakhala ndi “moyo wopambana.” Nafenso tikatero, tidzakhala olimba mtima ndipo zinthu zidzatiyendera bwino potumikira Mulungu.

Lemba lathu la chaka cha 2013 ndi lakuti: “Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. . . . Yehova Mulungu wako ali nawe.”—Yoswa 1:9

8. Tchulani lemba la chaka cha 2013. Kodi mukuganiza kuti lemba limeneli likuthandizani bwanji?

8 Yoswa ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri atamva mawu a Yehova akuti: “Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.” (Yos. 1:9) Ifenso Yehova ali nafe. Choncho  kaya tikumane ndi mavuto otani, ‘tisachite mantha kapena kuopa.’ M’malomwake, tiyenera kuganizira kwambiri mawu akuti: “Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. . . . Yehova Mulungu wako ali nawe.” Mawu amenewa a pa Yoswa 1:9 ndi amene asankhidwa kukhala lemba la chaka cha 2013. M’miyezi ikubwerayi, tilimbikitsidwa kwambiri ndi mawu amenewa ndiponso mawu komanso zochita za anthu amene anasonyeza chikhulupiriro ndi kulimba mtima.

ANTHU AMENE ANACHITA ZINTHU MOLIMBA MTIMA

9. Kodi Rahabi anasonyeza bwanji kulimba mtima ndiponso chikhulupiriro?

9 Yoswa atatuma anthu awiri kukazonda dziko la Kanani, Rahabi anawabisa n’kunamiza adani awo kuti azondiwo achoka. Chifukwa cha chikhulupiriro komanso kulimba mtima, Rahabi ndi banja lake anapulumuka pamene Aisiraeli ankawononga mzinda wa Yeriko. (Aheb. 11:30, 31; Yak. 2:25) Rahabi anasiyanso uhule kuti azisangalatsa Yehova. Chifukwa cha chikhulupiriro, anthu enanso masiku ano analimba mtima n’kusiya makhalidwe ngati amenewa n’cholinga choti azisangalatsa Mulungu.

10. Kodi Rute anasonyeza bwanji kulimba mtima? Nanga Yehova anamudalitsa bwanji?

10 Yoswa atamwalira, mkazi wina wachimowabu dzina lake Rute analimba mtima n’kuyamba kulambira Yehova. Popeza mwamuna wake amene anamwalira anali Mwisiraeli, n’kutheka kuti ankadziwa zina zokhudza Yehova. Apongozi a Rute, dzina lawo Naomi, ankakhalanso ku Mowabu. Koma anaganiza zobwerera ku Betelehemu m’dziko la Isiraeli. Ndiyeno ali panjira, Naomi anachonderera Rute kuti abwerere kwawo koma iye anayankha kuti: “Musandichonderere kuti ndikusiyeni, kuti ndibwerere ndisakutsatireni . . . Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Rute sanasinthe maganizo akewa. Kenako anadzakwatiwa ndi wachibale wa Naomi, dzina lake Boazi, n’kubereka mwana wamwamuna. Rute anadzakhala kholo la Davide ndiponso Yesu. Apa n’zoonekeratu kuti Yehova amadalitsa anthu amene amachita zinthu molimba mtima ndiponso mwachikhulupiriro.—Rute 2:12; 4:17-22; Mat. 1:1-6.

ANTHU AMBIRI ANAIKA MOYO WAWO PA NGOZI

11. Kodi Yehoyada ndi Yoseba anasonyeza bwanji kulimba mtima? Nanga zotsatira zake zinali zotani?

11 Pali anthu amene amachita zofuna za Mulungu ndiponso kuthandiza Akhristu anzawo. Timalimba mtima ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu tikaona kuti Yehova akuwathandiza. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Mkulu wa Ansembe Yehoyada ndi mkazi wake Yoseba. Mfumu Ahaziya itamwalira, Ataliya, yemwe anali amayi ake, anapha ana onse a mfumuyi, kupatula Yoasi, n’kuyamba kulamulira. Koma Yehoyada ndi Yoseba anaika moyo wawo pa ngozi posunga mwana wina wa Ahaziya, dzina lake Yoasi, kwa zaka 6. Ndiye m’chaka cha 7, Yehoyada anaika Yoasi kukhala mfumu ndipo analamula kuti Ataliya aphedwe. (2 Maf. 11:1-16) Patapita nthawi, Yehoyada anathandiza Mfumu Yoasi kukonza kachisi. Yehoyada anamwalira ali ndi zaka 130 ndipo anaikidwa m’manda limodzi ndi mafumu “chifukwa anachita zabwino mu Isiraeli ndiponso kwa Mulungu woona ndi nyumba Yake.” (2 Mbiri 24:15, 16) Chifukwa cha kulimba mtima kwa Yehoyada ndi mkazi wake, banja lachifumu limene Mesiya anayenera kubadwira linatetezedwa.

12. Kodi Ebedi-meleki anasonyeza bwanji kulimba mtima?

12 Chitsanzo china ndi Ebedi-meleki, yemwe ankatumikira m’nyumba ya Mfumu Zedekiya. Iye anaika moyo wake pa ngozi kuti apulumutse Yeremiya. Mfumu Zedekiya inapereka Yeremiya m’manja mwa akalonga a Yuda omwe anamuimba mlandu wabodza woukira boma. Kenako akalongawa anamuponya m’chitsime chamatope kuti afe. (Yer. 38:4-6) Anthu ambiri ankamuda Yeremiya choncho kumuthandiza kunali koopsa. Koma Ebedi-meleki anakapempha Zedekiya kuti akapulumutse Yeremiya. Mfumuyi inamvera ndipo inamupatsa anthu 30 kuti akamupulumutse. Kudzera mwa mneneriyu, Mulungu anauza  Ebedi-meleki kuti sadzaphedwa pa nthawi imene Ababulo azidzawononga Yerusalemu. (Yer. 39:15-18) Mulungu amadalitsa kwambiri anthu amene amalimba mtima pochita zofuna zake.

13. Kodi Aheberi atatu anasonyeza bwanji kulimba mtima? Nanga chitsanzo chawo chingatithandize bwanji?

13 M’zaka za m’ma 600 B.C.E., Yehova anadalitsa atumiki ake atatu achiheberi omwe anasonyeza chikhulupiriro komanso kulimba mtima. Mfumu Nebukadinezara inasonkhanitsa akuluakulu a mu ufumu wa Babulo n’kulamula kuti alambire chifano cha golide. Inanena kuti aliyense wosalambira chifanochi adzaponyedwa m’ng’anjo ya moto. Aheberi atatuwa anauza Nebukadinezara mwaulemu kuti: “Mulungu wathu amene tikumutumikira akhoza kutipulumutsa. Iye atipulumutsa m’ng’anjo yoyaka moto ndiponso m’manja mwanu mfumu. Koma ngati satipulumutsa, dziwani mfumu kuti ife sititumikira milungu yanu, ndipo sitilambira fano limene mwaimika.” (Dan. 3:16-18) Pa Danieli 3:19-30, timawerenga nkhani yosangalatsa ya mmene Mulungu anawapulumutsira m’ng’anjoyo. Sikuti ifenso tingaopsezedwe kuti tiponyedwa m’ng’anjo ya moto. Koma tikamayesedwa kuti tisakhulupirike kwa Yehova, tisamakayikire zoti iye adzatidalitsa ngati tikhala ndi chikhulupiriro n’kuchita zinthu molimba mtima.

14. Malinga ndi Danieli chaputala 6, kodi Danieli anasonyeza bwanji kulimba mtima? Kodi zotsatira zake zinali zotani?

14 Nayenso Danieli anasonyeza chikhulupiriro ndi kulimba mtima. Pa nthawi ina, adani a Danieli anaumiriza Mfumu Dariyo kukhazikitsa lamulo ‘loletsa munthu aliyense kupemphera kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense kwa masiku 30, kupatulapo kwa mfumuyo.’ Ananena kuti: “Aliyense amene samvera lamulo limeneli aponyedwe m’dzenje la mikango.” Danieli atangodziwa kuti lamulo limeneli lasainidwa, “analowa m’nyumba mwake, ndipo mawindo a nyumba yake oyang’ana ku Yerusalemu anali otsegula. M’nyumbamo, iye anali kugwada ndi kupemphera kwa Mulungu wake ndi kumutamanda katatu pa tsiku, monga mmene anali kuchitira nthawi zonse lamuloli lisanasainidwe.” (Dan. 6:6-10) Danieli anaponyedwadi m’dzenje la mikango koma Yehova anamupulumutsa.—Dan. 6:16-23.

15. (a) Kodi Akula ndi Purisikila anasonyeza bwanji chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima? (b) Kodi mawu a Yesu pa Yohane 13:34, amatanthauza chiyani? Nanga Akhristu ambiri asonyeza bwanji chikondi choterechi?

15 Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza zimene zinachitika, limatiuza kuti Akula ndi Purisikila ‘anaika miyoyo yawo pachiswe chifukwa cha moyo wa Paulo.’ (Mac. 18:2; Aroma 16:3, 4) Iwo analimba mtima n’kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana.” (Yoh. 13:34) Chilamulo cha Mose chinkanenanso kuti munthu azikonda mnzake ngati mmene amadzikondera yekha. (Lev. 19:18) Koma tingati lamulo la Yesu linali latsopano. Tikutero chifukwa chakuti limalimbikitsa  anthu kukonda anzawo mpaka kufika popereka moyo wawo chifukwa cha anzawowo ngati mmene Yesu anachitira. Akhristu ambiri asonyeza chikondi choterechi ‘poika miyoyo yawo pachiswe.’ Iwo achita zimenezi kuti ateteze abale awo kwa adani ofuna kuwazunza kapena kuwapha.—Werengani 1 Yohane 3:16.

Akhristu oyambirira sanalolere kugonja

16, 17. Kodi Akhristu oyambirira anakumana ndi mayesero ati? Nanga Akhristu a m’nthawi yathu ino akumananso ndi mayesero ati?

16 Mofanana ndi Yesu, Akhristu oyambirira ankalambira Yehova yekha molimba mtima. (Mat. 4:8-10) Iwo anakaniratu kufukiza zonunkhira polemekeza mfumu ya Roma. (Onani chithunzi.) Munthu wina analemba m’buku lake kuti: “Ndi Akhristu ochepa kwambiri amene anagonja ngakhale kuti malo ofukizirawo nthawi zambiri ankakhala pabwalo pomwepo. Mkaidi ankangofunika kuponya tizofukiza tochepa pamoto kuti apatsidwe chikalata chom’masula. Ankafotokozeredwa kuti kuchita zimenezi si kulambira mfumu koma kungovomereza kuti mfumuyo ndi mulungu chifukwa chakuti ndi yolamulira ufumu wa Roma. Koma ndi Akhristu ochepa kwambiri amene analolera kuchita zimenezi kuti amasulidwe.”—Those About to Die.

17 Akhristu amene anali kundende mu ulamuliro wa chipani cha Nazi ankapatsidwa mwayi woti asaine chikalata chonena kuti asiya kulambira Yehova. Munthu akasaina chikalatacho, ankamasulidwa ndipo sankaphedwa. Koma ndi ochepa okha amene anasaina. Posachedwapa, pa nthawi ya nkhondo yapachiweniweni ku Rwanda, Akhristu omwe ndi Atutsi ndi Ahutu anaika miyoyo yawo pa ngozi pofuna kutetezana. Munthu ayenera kukhala ndi chikhulupiriro komanso kulimba mtima kuti apirire mavuto ngati amenewa.

KUMBUKIRANI KUTI YEHOVA ALI NAFE

18, 19. Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zimene zingatithandize kukhala ndi chikhulupiriro komanso kulimba mtima polalikira?

18 Panopa tili ndi mwayi wogwira nawo ntchito yaikulu imene atumiki a Mulungu a padziko lapansi apatsidwa. Ntchitoyi ndi yolalikira Ufumu ndi kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Timayamikira kwambiri kuti Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. Iye ankayenda “mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Ifenso timafunika chikhulupiriro komanso kulimba mtima kuti tizilalikira uthenga wa Ufumu. Mulungu akhoza kutithandiza kukhala olimba mtima ngati Nowa. Iye anali “mlaliki wa chilungamo . . . padziko la anthu osaopa Mulungu,” limene linali litatsala pang’ono kuwonongedwa ndi chigumula.—2 Pet. 2:4, 5.

19 Pemphero limatithandiza kuti tizigwira bwino ntchito yolalikira. Akhristu ena amene ankazunzidwa atapempha kuti ‘alankhule mawu a Mulungu molimba mtima,’ pemphero lawo linayankhidwa. (Werengani Machitidwe 4:29-31.) Ngati inunso mumaopa kulalikira kunyumba ndi nyumba, Yehova adzayankha mukamupempha kuti akuthandizeni kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu ndiponso kulimba mtima.—Werengani Salimo 66:19, 20. *

20. Kodi atumiki a Yehovafe tili ndi thandizo liti?

20 Kupitiriza kuchita zimene Mulungu akufuna pokumana ndi mavuto m’dziko loipali si kophweka. Komabe sitili tokha chifukwa Mulungu ali nafe. Nayenso Mwana wake, amene ndi Mutu wa mpingo, ali nafe. Palinso Mboni za Yehova zinzathu padziko lonse lapansi zoposa 7,000,000. Pamodzi ndi anzathu amenewa, tiyeni tipitirize kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso kulengeza uthenga wabwino. Tizikumbukiranso lemba la chaka cha 2013 lakuti: “Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. . . . Yehova Mulungu wako ali nawe.”—Yos. 1:9.

^ ndime 19 Onani zitsanzo zina za anthu olimba mtima mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2012 pa mutu wakuti, “Khalani Olimba Mtima Kwambiri Ndipo Muchite Zinthu Mwamphamvu.”