Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kuyandikira Yehova

Pitirizani Kuyandikira Yehova

“Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—YAK. 4:8.

1, 2. (a) Kodi Satana amapusitsa bwanji anthu? (b) N’chiyani chingatithandize kuyandikira Mulungu?

YEHOVA MULUNGU analenga anthu ndi mtima woti azifuna kumuyandikira. Koma Satana amafuna kuti tikhale ndi maganizo ake akuti sitifunika kuyandikira Yehova. Limeneli ndi bodza limene Satana anapusitsa nalo Hava m’munda wa Edeni ndipo akupitirizabe mpaka pano. (Gen. 3:4-6) Kuyambira nthawi imeneyo, anthu ambiri akhala akuganiza kuti safunika kuyandikira Mulungu.

2 Koma tikhoza kupewa misampha ya Satana chifukwa “tikudziwa bwino ziwembu zake.” (2 Akor. 2:11) Satana amatilimbikitsa kusankha zinthu zolakwika n’cholinga choti tisokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Koma malinga ndi nkhani yapita ija, tikhoza kusankha bwino ntchito, zosangalatsa komanso zoyenera kuchita ndi anthu a m’banja lathu. M’nkhani ino, tiona zimene tiyenera kuchita kuti zipangizo zamakono, thanzi lathu, ndalama komanso kunyada zisatilepheretse ‘kuyandikira Mulungu.’—Yak. 4:8.

ZIPANGIZO ZAMAKONO

3. Kodi zipangizo zamakono zingakuthandizeni bwanji nanga zingakusokonezeni bwanji?

3 Masiku ano, zipangizo zamakono zili ponseponse. Ngati titazigwiritsa ntchito bwino, zikhoza kutithandiza. Koma kupanda kuzigwiritsa ntchito bwino, zikhoza kutisokonezera ubwenzi wathu ndi Atate wathu wakumwamba. Mwachitsanzo, tiyeni tikambirane za makompyuta. Magazini imene mukuwerengayi inalembedwa ndiponso kusindikizidwa pogwiritsa ntchito kompyuta. Pa kompyuta, munthu ukhoza kufufuza zinthu, kulankhulana ndi anthu komanso kupeza zinthu zosangalatsa zabwino. Koma n’zothekanso kutengeka kwambiri ndi makompyuta. Otsatsa malonda amayesetsa kuchititsa anthu kuganiza kuti afunika kupeza zipangizo zamakono zimene zangotuluka kumene. Mnyamata wina ankafunitsitsa kwambiri kakompyuta kenakake kam’manja moti anazemba n’kukagulitsa impso yake kuti agule kakompyutako. Kumenekutu n’kupusa kwambiri.

4. Kodi Mkhristu wina anathana bwanji ndi vuto lotengeka kwambiri ndi kompyuta?

 4 Koma kulola kuti zipangizo zamakono zisokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova n’koopsa kwambiri. M’bale wina wa zaka 28, dzina lake Jon, * anati: “Ndimadziwa kuti Baibulo limati ‘tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu’ n’cholinga choti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova. Koma pa nkhani ya makompyuta munthune ndili ndi vuto lalikulu kwabasi.” Jon ankakhala pa Intaneti mpaka pakati pa usiku. Iye anati: “Makamaka ndikatopa kwambiri m’pamene zinkandivuta kusiya kucheza ndi anthu pa Intaneti kapena kuonera mavidiyo, omwe nthawi zina sanali abwino.” Kuti athane ndi vutoli, anakonza zoti kompyuta yakeyo izizima yokha ikafika nthawi yoti akagone.—Werengani Aefeso 5:15, 16.

Makolo ayenera kuthandiza ana awo kugwiritsa ntchito mwanzeru zipangizo zamakono

5, 6. (a) Kodi makolo ali ndi udindo wotani kwa ana awo? (b) Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti azicheza ndi anthu oyenera?

5 Ngati ndinu kholo, sikuti mumafunika kuona chilichonse chimene ana anu akuchita. Komabe mumafunika kuona mmene akuchitira zinthu pa kompyuta. Musamangowalekerera akuonera zinthu zachiwerewere, zachiwawa, zamizimu kapena kucheza ndi anthu oipa. Imeneyi si njira yowatangwanitsira kapena yowachititsa kuti asakuvutitseni. Ngati mutawalekerera, akhoza kumaganiza kuti ndi zabwinobwino. Muli ndi udindo woteteza ana anu, ngakhale akuluakulu, kuti china chilichonse chisasokoneze ubwenzi wawo ndi Yehova. Pajatu ngakhale nyama zimateteza ana awo. Kodi mukuganiza kuti chimbalangondo chachikazi chingatani ngati munthu wina akufuna kupha tiana take?—Yerekezerani ndi Hoseya 13:8.

6 Muzithandiza ana anu kuti azicheza ndi Akhristu achitsanzo chabwino komanso amisinkhu yosiyanasiyana. Musaiwale kuti inuyo mumafunika kucheza mokwanira ndi ana anu. Muzipeza nthawi yochitira limodzi zinthu monga kuseka, kusewera, kugwira ntchito ndiponso ‘kuyandikira Mulungu.’ *

THANZI

7. N’chifukwa chiyani tonse timafuna kukhala ndi thanzi labwino?

7 Nthawi zina timamva munthu akufunsa mnzake kuti, “Mukupeza bwanji?” M’pake kufunsa chonchi chifukwa chakuti kungoyambira pamene Adamu ndi Hava anamvera Satana n’kusokoneza ubwenzi wawo ndi Yehova, anthufe timadwala. Satana amasangalala akaona kuti tikudwala chifukwa zimakhala zovuta kutumikira Yehova. Ndipo ngati titafa ndiye kuti sitim’tumikiranso. (Sal. 115:17) N’chifukwa chake timayesetsa kusamalira moyo wathu. * Tiyeneranso kuganizira thanzi la abale ndi alongo athu.

8, 9. (a) Kodi tingapewe bwanji kuchita zinthu mopitirira malire pa nkhani ya thanzi lathu? (b) Kodi mtima wosangalala umathandiza bwanji?

8 Koma si bwino kuchita zinthu mopitirira malire. Anthu ena amangokhalira kukamba za kadyedwe koyenera, mankhwala oyenera kapena zinthu zina zothandiza kuti azioneka bwino. Amakamba kwambiri za zimenezi kusiyana ndi  mmene amakambira za Ufumu wa Mulungu. Mwina amaganiza kuti akuthandiza anzawo. Komatu tikakhala pa misonkhano, si bwino kutsatsa malonda kapena kulimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito mankhwala enaake kapena zinthu zina zodzikongoletsera. N’chifukwa chiyani tikutero?

9 Akhristufe timasonkhana kuti tikambirane za Yehova ndiponso kuti tizikhalabe achimwemwe chifukwa chotsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Agal. 5:22) Kaya wina watipempha kapena ayi, kupereka malangizo okhudza mankhwala kapena zinthu zina zodzikongoletsera si kwabwino pamene tili pa misonkhano. Kungasokoneze cholinga cha misonkhano ndiponso kungachititse ena kukhumudwa. (Aroma 14:17) Munthu aliyense ayenera kusankha yekha zochita pa nkhani ya mankhwala. Ndipotu palibe aliyense amene angapeze njira yothetsera matenda onse. Ngakhale madokotala apamwamba amadwala, kukalamba ndiponso kufa. Kudera nkhawa kwambiri za thanzi lathu sikungatalikitse moyo. (Luka 12:25) Koma “mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.”—Miy. 17:22.

10. (a) Kodi Yehova amaona kuti ndi makhalidwe ati amene amakongoletsa munthu? (b) Kodi ndi liti pamene tidzakhale ndi thanzi langwiro?

10 M’pomveka kuganiziranso za maonekedwe athu. Koma si bwino kumangoganizira zimene tingachite kuti tifufute zizindikiro zonse za ukalamba. Zizindikiro zoterezo zikhoza kusonyeza kuti ndife anzeru, olemekezeka komanso kuti munthu wamkati ndi wokongola. Pajatu Baibulo limati: “Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero zikapezeka m’njira yachilungamo.” (Miy. 16:31) Umu ndi mmene Yehova amationera ndipo ifenso tizidziona choncho. (Werengani 1 Petulo 3:3, 4.) Chotero kodi ndi bwino kuchititsa maopaleshoni oopsa kapena kuyamba kugwiritsa ntchito mankhwala oopsa n’cholinga choti tizingooneka okongola? “Chimwemwe chimene Yehova amapereka” n’chimene chimakongoletsa munthu ngakhale wokalamba kapena wodwala chifukwa chakuti chimachokera mumtima. (Neh. 8:10) M’dziko latsopano ndi mmene tidzakhala ndi thanzi langwiro ndiponso kuoneka okongola ngati kamwana. (Yobu 33:25; Yes. 33:24) Podikira nthawi imeneyo, tiyeni tizichita zinthu mwanzeru ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu. Kuchita zimenezi kungatithandize kuyandikirabe Yehova ndiponso kukhala ndi moyo wabwino ngakhale panopa.—1 Tim. 4:8.

NDALAMA

11. Kodi ndalama zingasokoneze bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?

11 Ndalama pazokha zilibe vuto ndipo si kulakwa kuchita bizinezi mwachilungamo. (Mlal. 7:12; Luka 19:12, 13) Koma “kukonda ndalama” kumasokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Tim. 6:9, 10) “Nkhawa za moyo wa m’nthawi ino,” kapena kuti kudera nkhawa kwambiri mmene tingapezere zinthu zofunika pa moyo, kungasokonezenso ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndi mmene zililinso ndi “chinyengo champhamvu cha chuma.” Munthu akhoza kumaganiza kuti ndalama zingam’pangitse kukhala wotetezeka ndiponso wosangalala mpaka kalekale. Koma zimenezi si zoona. (Mat. 13:22) Pa nkhaniyi, Yesu ananena momveka bwino kuti munthu “sangatumikire” Mulungu ndi chuma pa nthawi imodzi.—Mat. 6:24.

12. Kodi anthu amachita zotani kuti apeze ndalama zambiri pa nthawi yochepa? Kodi tingapewe bwanji zimenezi?

12 Kuona kuti ndalama n’zofunika kwambiri kungatipangitse kuchita zinthu zolakwika. (Miy. 28:20) Ena pofuna kupeza ndalama mwamsangamsanga, afika pogula matikiti otchovera juga kapena kuyamba mabizinezi oti alemere mwachangu. Ena afika mpaka ponyengerera anzawo mu mpingo kuti nawonso akhoza kupeza ndalama zambiri. Ena apusitsidwa pouzidwa kuti akongoze anthu ena ndalama ndipo adzawabwezera chiwongola dzanja chochuluka. Mtima wadyera ungachititse kuti tipusitsidwe n’kutaya ndalama zambiri. Choncho tiyenera kusamala kuti tisayambe mtima umenewu. Tiyeni tizichita zinthu mwanzeru. Tizizindikira kuti nthawi zambiri  n’zosatheka kupeza ndalama zambirimbiri pa nthawi yochepa.

13. Kodi maganizo a Yehova amasiyana bwanji ndi a anthu a m’dzikoli pa nkhani ya ndalama?

13 Tikamaika ‘ufumu ndi chilungamo cha Mulungu’ pa malo oyamba, Yehova amatidalitsa pamene tikamagwira ntchito mwakhama kuti tipeze zofunika pa moyo. (Mat. 6:33; Aef. 4:28) Iye safuna kuti tiziwodzera pa misonkhano chifukwa chogwira ntchito kwambiri. Safunanso kuti tikakhala pa misonkhano tizidera nkhawa za ndalama. Koma anthu ambiri m’dzikoli amaganiza kuti afunika kudzipereka kwambiri kuti apeze ndalama zochuluka n’cholinga choti adzakhale ndi moyo wabwino m’tsogolo. Ndiye amalimbikitsa ana awo kukhala ndi moyo wokonda chuma umenewu. Yesu anasonyeza kuti maganizo amenewa ndi osathandiza. (Werengani Luka 12:15-21.) Nkhani imeneyi ikutikumbutsa za Gehazi. Iye ankaganiza kuti akhoza kumachita zinthu mwadyera uku akutumikira Yehova.—2 Maf. 5:20-27.

14, 15. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudalira ndalama? Perekani chitsanzo.

14 Pali nkhwazi zina zimene zimamira m’nyanja n’kufa chifukwa chosafuna kusiya nsomba zolemera kwambiri zimene zagwira. Zinthu ngati zimenezi zikhoza kuchitikiranso Mkhristu. M’bale wina yemwe ndi mkulu mu mpingo, dzina lake Alex, anati: “Ndimayesetsa kwambiri kuti ndisawononge ndalama. Ngakhale pa zinthu ngati mankhwala a tsitsi, ndimasamala. Ngati ndapungula ambiri, ndimabwezeretsa ena n’kungogwiritsa ntchito ochepa.” Koma m’bale yemweyu anayamba bizinezi ina yotentha kwambiri. Iye ankafuna kuti akapeza ndalama zambiri, asiye ntchito n’kuyamba upainiya. Ndiye anayamba kutanganidwa kwambiri ndi bizinezi yakeyo. Anafika mpaka potenga ndalama zake zonse ndiponso kubwereka zina poganiza kuti apeza phindu lalikulu. Tsoka ndi ilo analuza nazo kwambiri. Alex anati: “Ndinayesetsa kuti ndalama zanga zibwerere. Ndinkaganiza kuti ndikadikira pang’ono zinthu ziyamba kuyenda bwino.”

15 Kwa miyezo ingapo, Alex ankangoganiza za bizinezi yake basi. Ankalephera kuganiza za zinthu zimene zingalimbitse ubwenzi wake ndi Yehova ndiponso ankalephera kugona. Koma zinthu sizinayambebe kuyenda bwino ngati mmene ankaganizira. Ndalama zake zonse zinatha ndipo anagulitsa nyumba yake. Iye anati: “Ndinazunzitsa banja langa.” Koma zimene zinachitikazi zinam’pangitsa kuphunzira zinthu zina zofunika kwambiri. Anati: “Tsopano ndazindikira kuti aliyense wodalira dziko la Satanali, amagwiritsidwa fuwa lamoto.” (Miy. 11:28) Kudalira ndalama zimene tili nazo kapena luso lathu lopeza ndalama m’dzikoli kuli ngati kudalira Satana, yemwe ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akor. 4:4; 1 Tim. 6:17) Alex anasintha zinthu pa moyo wake “chifukwa cha uthenga wabwino” ndipo tsopano akukhala moyo wosalira zambiri. Kuchita zimenezi kwathandiza iye ndi banja lake kukhala osangalala komanso kuyandikira Yehova.—Werengani Maliko 10:29, 30.

KUNYADA

16. Kodi ndi zinthu ngati ziti zimene tinganyadire? Kodi chingachitike n’chiyani ngati timadziona kuti ndife apamwamba kapena anzeru kwambiri?

16 Kunyadira zinthu zabwino kulibe vuto lililonse. Mwachitsanzo, tiyenera kunyadira kuti ndife Mboni za Yehova. (Yer. 9:24) Kusadzikayikira kumathandizanso munthu kusankha bwino zinthu ndiponso kutsatira mfundo zapamwamba za Mulungu. Koma kudziona ngati ndife apamwamba kapena anzeru kwambiri kukhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova.—Sal. 138:6; Aroma 12:3.

M’malo molakalaka udindo mu mpingo, muzisangalala ndi utumiki

17, 18. (a) Tchulani anthu a m’Baibulo amene anali odzichepetsa ndiponso amene anali onyada. (b) Kodi m’bale wina anachita chiyani n’cholinga choti kunyada kusasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova?

17 M’Baibulo muli zitsanzo za anthu onyada komanso odzichepetsa. Davide anali wodzichepetsa ndipo ankadalira Yehova kuti amutsogolere. Choncho Yehova anamudalitsa. (Sal. 131:1-3) Koma Yehova analanga Mfumu Nebukadinezara ndi Belisazara chifukwa anali odzikuza. (Dan. 4:30-37; 5:22-30) Masiku anonso, zingativute  nthawi zina kukhala odzichepetsa. Mtumiki wothandiza wina wa zaka 32, dzina lake Ryan, anasamukira ku mpingo wina. Iye anati: “Ndinkaganiza kuti posachedwa ndikhala mkulu koma chaka chathunthu chinadutsa.” Kodi Ryan anakwiya poganiza kuti akulu sakumulemekeza? Kodi anasiya kusonkhana n’kulola kuti kunyada kusokoneze ubwenzi wake ndi Yehova ndiponso anthu ake? Kodi mukanakhala inuyo mukanatani?

18 Ryan ananena kuti: “Ndinawerenga nkhani zonse zimene ndinapeza m’mabuku athu zokhudza kulephereka kwa zinthu zimene tikuyembekezera.” (Miy. 13:12) Ananenanso kuti: “Ndinazindikira kuti ndinafunika kukhala woleza mtima ndiponso wodzichepetsa. Ndinayenera kulola kuti Yehova andiphunzitse.” Ryan anasiya kudziganizira kwambiri n’kuyamba kuganizira ndiponso kuthandiza anthu ena mu mpingo komanso mu utumiki. Pasanapite nthawi, anali kuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri. Iye anati: “Ndinaikidwa kukhala mkulu patapita chaka ndi hafu ndipo pa nthawiyi, ndinali ndisakuyembekeza n’komwe. Ndinali nditasiya kuganizira kwambiri zimenezi chifukwa ndinkasangalala kwambiri mu utumiki.”—Werengani Salimo 37:3, 4.

PITIRIZANI KUKHALA PAFUPI NDI YEHOVA

19, 20. (a) Kodi tingatani kuti zinthu zimene timachita tsiku lililonse zisasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova? (b) Perekani zitsanzo za anthu amene anakhalabe pafupi ndi Yehova.

19 Zinthu 7 zimene takambirana m’nkhani ino ndiponso yapita ija pazokha si zolakwika. Timanyadira kuti ndife Mboni za Yehova. Banja losangalala ndiponso thanzi labwino ndi mphatso zamtengo wapatali zochokera kwa Yehova. Timadziwa kuti ntchito ndiponso ndalama zimatithandiza kupeza zofunika pa moyo wathu. Timadziwanso kuti zosangalatsa zimatitsitsimula ndipo zipangizo zamakono zingatithandize. Koma tikamachita chilichonse pa nthawi yolakwika kapena m’njira yolakwika, tikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova.

Musalole chilichonse kusokoneza ubwenzi wanu ndi Yehova

20 Satana angasangalale kwambiri ubwenzi wathu ndi Yehova utasokonezeka. Koma n’zotheka inuyo ndi banja lanu kupewa zimenezi. (Miy. 22:3) Muziyandikira Yehova n’kukhalabe naye pafupi. Tili ndi zitsanzo zambiri m’Baibulo zimene zingatithandize. Mwachitsanzo, Inoki ndi Nowa “anayenda ndi Mulungu woona.” (Gen. 5:22; 6:9) Nayenso Mose “anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Aheb. 11:27) Mulungu ankathandiza Yesu chifukwa iyeyo ankachita zosangalatsa Atate wake wakumwamba nthawi zonse. (Yoh. 8:29) Yesetsani kutsanzira anthu ngati amenewa. “Muzikhala okondwera nthawi zonse. Muzipemphera mosalekeza. Muziyamika pa chilichonse.” (1 Ates. 5:16-18) Musalole chilichonse kusokoneza ubwenzi wanu ndi Yehova.

^ ndime 4 Mayina asinthidwa.

^ ndime 6 Onani Galamukani! ya October 2011 ya mutu wakuti, “Kodi Mungalere Bwanji Ana Anu Kuti Akule Bwino?”

^ ndime 7 Onani Galamukani! ya March 2011 ya mutu wakuti, “Mfundo Zisanu Zokuthandizani Kukhala ndi Thanzi Labwino”