Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Musalole Chilichonse Kusokoneza Ubwenzi Wanu ndi Yehova

Musalole Chilichonse Kusokoneza Ubwenzi Wanu ndi Yehova

“Sankhani lero amene mukufuna kum’tumikira.”—YOS. 24:15.

1-3. (a) N’chifukwa chiyani Yoswa ndi chitsanzo chabwino? (b) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tisanasankhe zochita?

ZINTHU zimene timasankha pa moyo wathu zikhoza kukhala ndi zotsatira zabwino kapena zoipa. Choncho kusankha zochita ndi udindo waukulu. Zimakhala ngati munthu amene akuyenda ndipo wafika pamphambano. Amafunika kusankha njira. Njira imodzi ikhoza kukamufikitsa kumene akupita koma ina ikhoza kumusocheretsa.

2 M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anayenera kusankha zochita. Mwachitsanzo, Kaini anayenera kusankha kulamulidwa ndi mkwiyo kapena kuulamulira. (Gen. 4:6, 7) Yoswa anayenera kusankha kulambira Mulungu woona kapena milungu yonyenga. (Yos. 24:15) Yoswa ankafuna kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova choncho anasankha zinthu zimene zikanamuthandiza kuchita zimenezo. Koma Kaini analibe cholinga chimenechi choncho anasankha zinthu zimene zinasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova.

3 Nthawi zina, ifenso tiyenera kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Zikatero, kumbukirani cholinga chanu chomwe ndi kulemekeza Yehova pa zonse zimene mumachita ndiponso kupewa chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wanu ndi iye. (Werengani Aheberi 3:12.) M’nkhani ino ndiponso yotsatira tikambirana zinthu 7 zimene tiyenera kusankha mwanzeru kuti tisasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.

NTCHITO

4. Kodi kugwira ntchito n’kofunika bwanji?

4 Akhristu amafunika kupeza zofunika pa moyo wawo komanso wa banja lawo. Baibulo limasonyeza kuti munthu amene safuna kusamalira banja lake amakhala woipa kuposa wosakhulupirira. (2 Ates. 3:10; 1 Tim. 5:8) Ntchito  ndi yofunika kwambiri pa moyo wathu koma ngati sitisamala, ikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi ingasokoneze bwanji?

5. Kodi muyenera kuganizira mfundo ziti mukamasankha ntchito?

5 Tiyerekeze kuti mukufufuza ntchito. Ngati m’dera lanu ntchito zimasowa kwambiri, mukhoza kungovomera ntchito iliyonse imene mungaipeze. Koma bwanji ngati ntchitoyo ndi yosemphana ndi mfundo za m’Baibulo? Nanga bwanji ngati ntchitoyo ndi yopanikiza kapena muzifunika kuyendayenda moti izikulepheretsani kuchita zinthu zina ndi mpingo kapena banja lanu? Kodi mudzayambabe ntchitoyo poganiza kuti kugwira ntchito zoterezi n’kwabwino kusiyana ndi kukhala pa ulova? Kumbukirani kuti ngati mutasankha molakwika, mukhoza kusokoneza ubwenzi wanu ndi Yehova. (Aheb. 2:1) N’chiyani chingakuthandizeni kusankha mwanzeru pofufuza ntchito kapena poona ngati ntchito imene mukugwira ili yabwino?

6, 7. (a) Kodi anthu amakhala ndi zolinga zotani akamagwira ntchito? (b) Nanga ndi cholinga chiti chimene chingakuthandizeni kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova? Perekani chifukwa.

6 Monga tanenera poyamba paja, muyenera kukumbukira cholinga chanu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikufuna kuti ntchitoyi indithandize kuchita chiyani?’ Ngati cholinga chanu ndi kupeza zofunika pa moyo wanu kapena wa banja lanu kuti muzitumikira bwino Yehova, iye adzakuthandizani. (Mat. 6:33) Iye amadziwa mmene angakuthandizireni ngakhale pamene ntchito yatha kapena ngati chuma cha dziko sichikuyenda bwino. (Yes. 59:1) Yehova “amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.”—2 Pet. 2:9.

7 Koma bwanji ngati cholinga chanu n’kungofuna kulemera basi? Mwina mukhoza kulemeradi. Koma kugwira ntchito n’cholinga chimenechi kungakugwetseni m’mavuto aakulu. (Werengani 1 Timoteyo 6:9, 10.) Kuika patsogolo ndalama kapena ntchito kungasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova.

8, 9. Kodi makolo ayenera kuganizira zinthu ziti pa nkhani ya ntchito? Fotokozani.

8 Ngati ndinu kholo, muyenera kuganizira mmene zosankha zanu zingakhudzire ana anu. Kodi iwo amaona kuti mumaika patsogolo chiyani? Ntchito kapena ubwenzi wanu ndi Yehova? Ngati amaona kuti mumaika patsogolo chuma, kutchuka kapena moyo wapamwamba, nawonso akhoza kukutsatirani pa njira yoopsa imeneyi. Apo ayi akhoza kusiya kukulemekezani. Mlongo wina wachitsikana anati: “Kuyambira kalekale bambo anga amatanganidwa kwambiri ndi ntchito yawo. Poyamba tinkaganiza kuti akuchita zimenezi pofuna kupezera banja lathu zinthu zabwino kwambiri. Tinkaona kuti akungofuna kutisamalira bwino. Koma m’zaka zaposachedwapa, tikuona kuti zinthu zasintha. Iwo amangokhalira kugwira ntchito n’cholinga choti azitibweretsera zinthu zapamwamba osati zofunika pa moyo. Panopa anthu amangoona kuti banja lathu ndi lolemera osati lolimbikitsa ena kutumikira Yehova. Ndingakonde bambo anga atamatitsogolera potumikira Yehova osati kumangotipezera ndalama.”

9 Makolo, musalole kuti ntchito isokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova. Muzipereka chitsanzo chabwino kwa ana anu. Asonyezeni kuti kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ndi chuma chamtengo wapatali kwambiri kuposa ndalama kapena katundu.—Mat. 5:3.

10. Kodi wachinyamata amene akuganizira ntchito yoti adzagwire ayenera kukumbukira chiyani?

10 Ngati ndinu wachinyamata ndipo mukuganizira ntchito yoti mudzagwire, kodi mungatani kuti musankhe bwino? Monga tanenera kale, muyenera kukumbukira cholinga chanu pa moyo. Kodi kuphunzira ndiponso kugwira ntchito imene mukuiganizirayo kudzakuthandizani kuika patsogolo kutumikira  Yehova? Kapena kodi kudzasokoneza ubwenzi wanu ndi iye? (2 Tim. 4:10) Kodi mudzalola kutengera anthu amene amasangalala pokhapokha ngati ali ndi ndalama? Kapena kodi mudzatsanzira Davide amene analemba kuti: “Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya”? (Sal. 37:25) Kumbukirani kuti njira ina imakhala yosocheretsa pomwe ina imakuthandizani kukhala pa ubwenzi ndi Yehova n’kumasangalala. (Werengani Miyambo 10:22; Malaki 3:10.) Kodi inuyo mudzasankha njira iti? *

ZOSANGALATSA

11. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya zosangalatsa? Koma kodi tiyenera kukumbukira chiyani?

11 Baibulo sililetsa kusangalala. Silinenanso kuti munthu akamachita zosangalatsa ndiye kuti akungotaya nthawi. Paja Paulo anauza Timoteyo kuti: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Tim. 4:8) Baibulo limanenanso kuti pali “nthawi yoseka” ndi “nthawi yodumphadumpha mosangalala.” Limatilimbikitsanso kupeza nthawi yopuma. (Mlal. 3:4; 4:6) Koma ngati sitisamala, zosangalatsa zikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Pali njira ziwiri. Njira yoyamba ndi kusankha zosangalatsa zolakwika ndipo yachiwiri ndi kuthera nthawi yambiri mukuzichita.

Zosangalatsa zimakhala bwino ngati zili zoyenera ndiponso sizikukutherani nthawi yambiri

12. Kodi muyenera kuganizira zinthu ziti posankha zosangalatsa?

12 Choyamba tiyeni tikambirane mtundu wa zosangalatsa zimene timasankha. Zosangalatsa zabwino zilipo ndithu. Koma zosangalatsa zambiri zimalimbikitsa zinthu zimene Mulungu amadana nazo monga chiwawa, kukhulupirira mizimu ndiponso chiwerewere. Choncho ndi bwino kuganizira kwambiri mtundu wa zosangalatsa zimene mumakonda. Kodi zimakuchititsani kukhala munthu wotani? Kodi zimakuchititsani kukhala ndi mtima wachiwawa, wampikisano kapena wokondetsa dziko lanu? (Miy. 3:31) Kodi zimakuwonongerani ndalama zambiri? Kodi zingakhumudwitse anthu ena? (Aroma 14:21) Kodi zosangalatsa zanu zimachititsa kuti muzicheza ndi anthu otani? (Miy. 13:20) Kodi zimakulimbikitsani kuchita zinthu zoipa?—Yak. 1:14, 15.

13, 14. Kodi muyenera kukumbukira mfundo ziti mukamaganizira nthawi imene mungathere pochita zosangalatsa?

 13 Tiyenera kuganiziranso za kuchuluka kwa nthawi imene timathera pochita zosangalatsa. Ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimatha nthawi yambiri ndikuchita zosangalatsa moti sindikhala ndi nthawi yokwanira yochitira zinthu monga kulalikira ndi kusonkhana?’ Kutha nthawi yaitali tikuchita zosangalatsa kumapangitsanso kuti tisasangalale nazo kwenikweni. Nthawi zambiri, anthu amene satha nthawi yaitali akuchita zosangalatsa ndi amene amasangalala nazo kwambiri. Tikutero chifukwa amakhala atachitiratu zinthu zonse “zofunika kwambiri.” Choncho ikafika nthawi yochita zosangalatsa sadziimba mlandu.—Werengani Afilipi 1:10, 11.

14 Ngakhale kuti kuchita zosangalatsa kwa nthawi yaitali kungaoneke kosangalatsa, kukhoza kutisokonezera ubwenzi wathu ndi Yehova. Umboni wake ndi zimene zinachitikira mlongo wina wa zaka 20 dzina lake Kim. Iye anati: “Ndinkakonda kupita kulikonse kumene anthu akunjoya. Kumapeto kwa mlungu uliwonse kunkachitika zinazake kuyambira Lachisanu mpaka Lamlungu. Koma panopa ndazindikira kuti pali zinthu zina zofunika kwambiri zimene ndingamachite. Panopa ndikuchita upainiya ndipo ndimadzuka 6 koloko m’mawa kuti ndipite mu utumiki choncho n’zosatheka kuti ndizikhala konjoya mpaka 1 koloko kapena 2 koloko usiku. Kucheza ndi anzathu kulibe vuto koma ngati sitisamala kukhoza kutisokoneza. Tiyenera kukhala ndi malire ngati mmene timachitira ndi zinthu zina.”

15. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti azisangalala ndi zinthu zabwino?

15 Makolo afunika kupezera banja lawo zinthu zofunika. Amafunikanso kuthandiza aliyense m’banja kuti azikhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, kukhala wosangalala ndiponso kudzimva kuti amakondedwa. Ngati ndinu kholo musakhale ndi mtima woona kuti kusangalala n’kulakwa. Koma muzisamalanso kuti banja lanu lisamasangalale ndi zinthu zoipa. (1 Akor. 5:6) Ngati mungasankhe mosamala, mukhoza kupeza zosangalatsa zabwino za banja lanu. * Kuchita zimenezi kungathandize kuti banja lanu lonse likhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.

ANTHU A M’BANJA LATHU

16, 17. Kodi makolo ambiri akumana ndi vuto liti? Nanga tikudziwa bwanji kuti Yehova amamvetsa mmene zikuwapwetekera?

16 Ubwenzi wa pakati pa makolo ndi ana umakhala wamphamvu kwambiri moti Yehova anauyerekezera ndi mmene amakondera anthu ake. (Yes. 49:15) Choncho m’pomveka kuti timamva chisoni kwambiri ngati munthu wina m’banja lathu wasiya Yehova. Mlongo wina amene mwana wake wamkazi anachotsedwa anati: “Zinandipweteka koopsa. Ndinkadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani wasiya Yehova?’ Ndinkadziimba mlandu kwambiri.”

17 Yehova amadziwa mmene zikukupwetekerani. Iyenso “zinam’pweteka kwambiri mumtima” pamene mwana wake woyamba padziko lapansi anamupandukira komanso pamene anthu ena ambiri anachita zimenezi Chigumula chisanafike. (Gen. 6:5, 6) Anthu amene sanakumanepo ndi zimenezi sangamvetse bwino mmene zimapwetekera. Komabe, si bwino kulola zochita za munthu amene wachotsedwa kuti zisokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi mungatani ngati mukumva chisoni chifukwa choti munthu wina m’banja lanu wasiya Yehova?

18. N’chifukwa chiyani makolo sayenera kudziimba mlandu ngati mwana wawo wasiya Yehova?

18 Musamadziimbe mlandu pa zimene zinachitika. Yehova wapereka ufulu wosankha kwa anthu. Munthu aliyense m’banja, amene  wadzipereka n’kubatizidwa, ali ndi udindo “wonyamula katundu wake.” (Agal. 6:5) Yehova amaona kuti wochimwa aliyense ayenera kudziyankhira pa zimene wasankha. Iye sangakuimbeni mlandu inuyo. (Ezek. 18:20) Si bwinonso kuimba mlandu anthu ena. Muziona kuti chilango chimene Yehova wapereka n’choyenera. Muzilimbana ndi Mdyerekezi osati akulu amene akuyesa kuteteza mpingo.—1 Pet. 5:8, 9.

Si kulakwa kuyembekezera kuti m’bale wanu amene anachotsedwa adzabwerera kwa Yehova

19, 20. (a) Kodi makolo a mwana amene wachotsedwa angatani kuti apirire chisoni chawo? (b) Kodi makolo oterewa ayenera kuyembekezera chiyani?

19 Koma ngati mungakwiyire Yehova, dziwani kuti ubwenzi wanu ndi iye usokonezeka. Munthu wa m’banja lanu yemwe wasiya Yehova akufunikira kuona kuti mumafunitsitsa kusangalatsa Yehova kuposa wina aliyense, ngakhale a m’banja lanu. Choncho kuti mukwanitse kupirira, yesetsani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Musamadzipatule, koma muzicheza ndi abale ndi alongo okhulupirika. (Miy. 18:1) Muzimuuza Yehova nkhawa zanu zonse m’pemphero. (Sal. 62:7, 8) Musamafufuze zifukwa zochezera ndi wachibale wanu amene wachotsedwa, kulemberana naye makalata, kutumizirana mauthenga a pafoni kapena pa Intaneti. (1 Akor. 5:11) Muzitanganidwa ndi zinthu zimene zingalimbitse ubwenzi wanu ndi Mulungu. (1 Akor. 15:58) Mlongo amene tamutchula uja anati: “Ndikudziwa kuti ndiyenera kutumikira Yehova mwakhama ndiponso kulimbitsa ubwenzi wanga ndi iye n’cholinga choti mwana wanga akadzabwezeretsedwa, ndidzathe kumuthandiza.”

20 Baibulo limanena kuti chikondi “chimayembekezera zinthu zonse.” (1 Akor. 13:4, 7) Si kulakwa kuyembekezera kuti m’bale wanu amene anachotsedwa adzabwezeretsedwa. Chaka chilichonse anthu ochimwa ambiri amalapa n’kubwerera m’gulu la Yehova. Yehova sanyinyirika akaona kuti alapa. M’malomwake, amakhala “wokonzeka kukhululuka.”—Sal. 86:5.

SANKHANI MWANZERU

21, 22. Kodi mukufunitsitsa kusankha bwanji zinthu pa moyo wanu?

21 Yehova wapatsa anthu ufulu wosankha. (Werengani Deuteronomo 30:19, 20.) Koma ufulu umenewu umabwera limodzi ndi udindo waukulu. Mkhristu aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuyenda panjira iti? Kodi ndalola zinthu monga ntchito, zosangalatsa kapena anthu a m’banja langa kusokoneza ubwenzi wanga ndi Yehova?’

22 Yehova sadzasiya kukonda anthu ake. Koma kusankha zolakwika n’kumene kumasokoneza ubwenzi wathu ndi iye. (Aroma 8:38, 39) Tisalole kuti zimenezi zitichitikire. Tsimikizani mumtima mwanu kuti china chilichonse chisasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova. M’nkhani yotsatira tiona zinthu zina zinayi zimene tiyenera kusankha mwanzeru kuti tisasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.

^ ndime 10 Kuti mumve zambiri pa nkhani yosankha ntchito, onani mutu 38 m’buku lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri.