Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tisamagwiritse Ntchito Baibulo Ngati Chithumwa

Tisamagwiritse Ntchito Baibulo Ngati Chithumwa

“MAWU a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” (Aheb. 4:12) Ponena mawu amenewa, Paulo ankasonyeza kuti mawu a Mulungu ali ndi mphamvu zofika munthu pa mtima komanso kumusintha.

Koma atumwi atamwalira, mpatuko unayamba ndipo anthu anayamba kukhulupirira zinthu zolakwika pa nkhani ya mphamvu za uthenga wa m’Baibulo. (2 Pet. 2:1-3) Patapita nthawi, atsogoleri a matchalitchi anayamba kuphunzitsa kuti Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu zamatsenga. Pulofesa wina analemba za “mphamvu zamatsenga za malemba achikhristu.” Iye anafotokoza kuti m’zaka za m’ma 200, mtsogoleri wina wa matchalitchi dzina lake Origen anaphunzitsa kuti “kungomva chabe mawu opatulika kukhoza kuthandiza munthu.” Iye ananenanso kuti: “Ngati mawu ogwiritsidwa ntchito m’zamatsenga ali ndi mphamvu, ndiye kuli bwanji mawu a m’malemba ochokera kwa Mulungu.” Munthu wina dzina lake John Chrysostom, yemwe anakhalapo m’zaka za m’ma 300, analemba kuti: “Mdyerekezi sangalowe n’komwe m’nyumba yomwe muli Baibulo.” Iye anafotokozanso kuti anthu ena ankavala m’khosi mavesi ena a mu Uthenga Wabwino monga chithumwa chowateteza. Pulofesa uja ananenanso kuti mtsogoleri wina wa chipembedzo cha Katolika, dzina lake Augustine, ankaphunzitsa kuti “ngati munthu akudwala mutu, akamagona akhoza kuika mawu a Uthenga Wabwino wa Yohane pansi pa pilo wake.” Pa zifukwa zimenezi, anthu ankagwiritsa ntchito Baibulo monga chithumwa. Nanga kodi inuyo, mumaona kuti Baibulo ndi chithumwa chomwe chingakutetezeni ku zinthu zoipa?

Pali njira inanso yoipa imene anthu ambiri amagwiritsira ntchito Baibulo. Iwo amakhulupirira kuti kungotsegula Baibulo paliponse n’kuwerenga vesi limene ayambirira kuona kukhoza kuwathandiza. Mwachitsanzo, pulofesayu ananena kuti tsiku lina Augustine anamva mwana wa aneba akuti: “Tenga uwerenge, tenga uwerenge.” Iye atamva zimenezi, anaganiza kuti Mulungu akumuuza kuti atsegule Baibulo n’kuwerenga vesi limene maso ake ayambirire kuona.

Kodi mwamvapo za anthu amene akakumana ndi vuto amapemphera kwa Mulungu kenako n’kutsegula Baibulo pena paliponse pokhulupirira kuti vesi limene ayambirire kuona liwathandiza pa vuto lawolo? Anthuwo akhoza kukhala ndi cholinga chabwino pochita zimenezi, koma Akhristu sayenera kufufuza malangizo a m’Malemba m’njira imeneyi.

Yesu analonjeza ophunzira ake kuti adzawatumizira “mthandizi, amene ndi mzimu woyera.” Ponena za mthandiziyo, iye anawauza kuti: “Adzakuphunzitsani zinthu zonse ndi kukukumbutsani zonse zimene ndinakuuzani.” (Yoh. 14:26) Choncho Baibulo limatithandiza tikamagwiritsa ntchito zimene taphunzira m’Baibulolo osati kungotsegula paliponse n’kuwerenga.

Ngakhale kuti anthu ambiri amagwiritsa ntchito Baibulo ngati chithumwa, Mawu a Mulungu amaletsa kuombeza kapena kuchita zamatsenga. (Lev. 19:26; Deut. 18:9-12; Mac. 19:19) N’zoona kuti “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu” koma kuti atithandize, tiyenera kuwagwiritsa ntchito bwino. Baibulo silitithandiza tikaligwiritsa ntchito ngati chithumwa. Koma tikaliphunzira bwino m’pamene lingatithandize pa moyo wathu. Kudziwa bwino Baibulo kwathandiza anthu ambiri kukhala ndi makhalidwe abwino, kusiya zinthu zoipa, kulimbitsa mabanja awo ndiponso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, yemwe analilemba.