Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wabwino Kwambiri

Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wabwino Kwambiri

“Ukatero, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzachita zinthu mwanzeru.”—YOS. 1:8.

1, 2. (a) Kodi anthu ambiri amaona kuti moyo wabwino ndi wotani? (b) Kodi mungadziwe bwanji moyo umene mumaona kuti ndi wabwino?

KODI moyo wabwino umatanthauza chiyani? Ngati mutafunsa anthu angapo funso limeneli, mayankho awo akhoza kukhala osiyanasiyana. Ambiri amaganiza kuti moyo umakhala wabwino ngati munthu ali ndi chuma, ntchito yapamwamba kapena ngati ndi wophunzira kwambiri. Ena amaganiza kuti moyo umakhala wabwino ngati amagwirizana ndi a m’banja lawo, anzawo kapena akuntchito kwawo. Atumiki ena a Mulungu angaganize kuti moyo umakhala wabwino ngati ali ndi udindo mu mpingo kapena ngati athandizapo anthu kuphunzira choonadi.

2 Kuti mudziwe moyo umene mumaganiza kuti ndi wabwino, lembani mayina a anthu angapo amene mumawalemekeza kwambiri. Kodi anthuwa amafanana m’njira ziti? Kodi ndi achuma kapena otchuka? Kodi mwina ali ndi udindo winawake? Mayankho anu angasonyeze zimene zili mumtima mwanu zomwe zingakutsogolereni posankha zochita.—Luka 6:45.

3. (a) Kodi Yoswa anafunika kuchita chiyani kuti akhale ndi moyo wopambana? (b) Kodi tikambirana za chiyani?

3 Koma chofunika kwambiri ndi kukhala ndi moyo umene Yehova amaona kuti ndi wabwino. Tikutero chifukwa chakuti popanda kumusangalatsa sitingapitirize kukhala ndi moyo. Pamene Yehova ankapereka kwa Yoswa udindo waukulu wotsogolera Aisiraeli kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, anamuuza kuti aziwerenga Chilamulo cha Mose “usana ndi usiku.” Anamuuzanso kuti aonetsetse kuti akutsatira zonse zolembedwamo. Kenako Mulungu anamuuza kuti: “Ukatero, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzachita zinthu mwanzeru.” (Yos. 1:7, 8) Inunso mukudziwa kuti Yoswa zinthu zinamuyendera bwino. Koma bwanji ifeyo? Kodi tingadziwe bwanji ngati maganizo athu akufanana ndi  a Mulungu pa nkhani ya moyo wabwino? Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambirane za anthu awiri otchulidwa m’Baibulo.

KODI SOLOMO ANALI NDI MOYO WABWINO?

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zinthu zinkamuyendera bwino Solomo?

4 Zinthu zambiri zinkamuyendera bwino Solomo. Zinali choncho chifukwa chakuti iye anamvera ndiponso kuopa Mulungu kwa zaka zambiri ndipo Yehova ankamudalitsa kwambiri. Yehova atamuuza kuti apemphe zimene akufuna, iye anapempha nzeru kuti athe kutsogolera anthu a Mulungu. Ndiyeno Mulungu anamudalitsa pomupatsa nzeru komanso chuma. (Werengani 1 Mafumu 3:10-14.) Nzeru za Solomo “zinaposa nzeru za anthu onse a Kum’mawa ndi nzeru zonse za ku Iguputo.” Iye “anatchuka m’mitundu yonse yozungulira.” (1 Maf. 4:30, 31) Anali ndi chuma chambiri moti chaka chilichonse ankalandira matani pafupifupi 25 a golide. (2 Mbiri 9:13) Iye anali ndi luso lomanga, la zamalonda ndiponso lotha kugwirizana ndi mafumu anzake. Pa nthawi imene Solomo anali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, zinthu zinkamuyendera bwino.—2 Mbiri 9:22-24.

5. Kodi Solomo anazindikira chiyani za anthu amene ali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu?

5 Zimene Solomo analemba m’buku la Mlaliki zimasonyeza kuti iye ankadziwa kuti si anthu achuma kapena otchuka okha amene zinthu zimawayendera bwino. Iye analemba kuti: “Ndazindikira kuti palibe chabwino kuposa kuti iwo asangalale ndiponso azichita zabwino pamene ali ndi moyo, komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Mlal. 3:12, 13) Iye anazindikiranso kuti munthu amene ali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu ndi amene amasangalala kwambiri ndi zinthu zimenezi. Solomo ananena zoona pamene anati: “Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.”—Mlal. 12:13.

6. Kodi chitsanzo cha Solomo chingatithandize bwanji kudziwa tanthauzo la moyo wabwino?

6 Kwa zaka zambiri, Solomo ankaopa Mulungu. Malemba amanena kuti: “Anapitiriza kukonda Yehova mwa kuyenda motsatira malamulo a Davide bambo ake.” (1 Maf. 3:3) Kodi si zoona kuti umenewu unali moyo wabwino? Solomo atauzidwa ndi Mulungu, anamanga kachisi wokongola kwambiri kuti anthu azigwiritsa ntchito pomulambira. Anamuuzanso kulemba mabuku atatu a m’Baibulo. Mwina sitingachite zinthu zofanana ndi Solomo. Koma kodi chitsanzo chake pamene anali wokhulupirika kwa Mulungu chingatithandize bwanji? Chingatithandize kudziwa tanthauzo la moyo wabwino kuti nafenso zinthu zizitiyendera bwino. M’dzikoli anthu amaona kuti moyo umakhala wabwino ngati munthu ndi wotchuka, ali ndi chuma, nzeru kapena udindo. Koma Solomo anauziridwa kulemba kuti zinthu zimenezi ndi zachabechabe ndipo kuzifufuza kuli ngati “kuthamangitsa mphepo.” Mwina mwaona kuti anthu okonda chuma sakhutira ndipo nthawi zambiri amangodera nkhawa chuma chimene ali nacho. Komanso tsiku lina, chuma chawo chidzakhala cha anthu ena.—Werengani Mlaliki 2:8-11, 17; 5:10-12.

7, 8. Kodi Solomo analephera bwanji kukhala wokhulupirika? Kodi zotsatira zake zinali zotani?

7 Patapita nthawi, Solomo anasiya kumvera Mulungu mokhulupirika. Baibulo limati: “Pamene iye anali kukalamba, akazi ake anali atapotoza mtima wake moti iye anali kutsatira milungu ina. Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu monga mmene anachitira Davide bambo ake. . . . Solomo anayamba kuchita zinthu zimene zinali zoipa m’maso mwa Yehova.”—1 Maf. 11:4-6.

8 Yehova sanasangalale nazo ndipo anauza Solomo kuti: “Chifukwa chakuti . . . sunasunge pangano langa ndi malamulo amene ndinakulamula, ndidzang’amba ufumuwu kuuchotsa  kwa iwe, ndipo ndithu ndidzaupereka kwa mtumiki wako.” (1 Maf. 11:11) Izitu zinali zomvetsa chisoni. Ngakhale kuti zinthu zambiri zinkamuyendera bwino, patapita nthawi, Solomo anakhumudwitsa Yehova. Iye analephera kuchita chinthu chofunika kwambiri, chomwe ndi kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wofunitsitsa kuti zimene ndaphunzira kwa Solomo zindithandize kukhala ndi moyo wabwino?’

MOYO WABWINO KWAMBIRI

9. Kodi anthu a m’dzikoli angaone kuti Paulo anali ndi moyo wabwino? Fotokozani.

9 Moyo wa Paulo unali wosiyana kwambiri ndi wa Mfumu Solomo. Iye sankakhala pampando wachifumu wopangidwa ndi minyanga ya njovu kapena kudya limodzi ndi mafumu. M’malomwake, nthawi zina ankavutika ndi njala, ludzu, kuzizidwa komanso kukhala wosavala. (2 Akor. 11:24-27) Paulo atangovomereza zoti Yesu ndi Mesiya, anasiya kukhala wolemekezeka m’chipembedzo chachiyuda. M’malomwake, atsogoleri a chipembedzo chachiyuda anayamba kudana naye. Iye anamangidwa, kukwapulidwa, kumenyedwa ndi ndodo ndiponso kuponyedwa miyala. Paulo ananena kuti iye limodzi ndi Akhristu anzake ankaneneredwa zachipongwe, kuzunzidwa ndiponso kunyozedwa. Iye analemba kuti: “Mpaka tsopano, takhala ngati zinyalala za dziko, nyansi za zinthu zonse.”—1 Akor. 4:11-13.

10. N’chifukwa chiyani anthu ena mwina anaona kuti Paulo wataya moyo wabwino?

10 Pa nthawi imene Paulo anali wachinyamata n’kumadziwika ndi dzina loti Saulo, zinkaoneka ngati ali ndi tsogolo lowala kwambiri. N’kutheka kuti anabadwira m’banja lotchuka. Komanso anaphunzitsidwa ndi mphunzitsi wolemekezeka kwambiri dzina lake Gamaliyeli. Pa nthawi ina analemba kuti: “Ndinali kupita patsogolo kwambiri m’Chiyuda kuposa anzanga ambiri.” (Agal. 1:14) Iye ankadziwa bwino Chiheberi ndi Chigiriki ndipo anali ndi mwayi komanso ufulu wambiri chifukwa chokhala nzika ya Roma. Akanapitiriza zimene ankachitazo, akanakhala munthu wolemekezeka kwambiri komanso wachuma. Koma anasankha moyo umene anthu ena, mwinanso achibale ake, anaona kuti ndi wachabechabe. N’chifukwa chiyani anatero?

11. Kodi ndi zinthu ziti zimene Paulo ankaona kuti ndi zofunika kwambiri ndipo n’chifukwa chiyani?

11 Paulo ankakonda kwambiri Yehova kuposa chuma ndi kutchuka. Iye ankafunitsitsa kusangalatsa Mulungu. Paulo ataphunzira choonadi anadziwa kufunika kwa dipo, utumiki wachikhristu ndiponso chiyembekezo cha moyo wakumwamba. Zinthu zimenezi ndi zimene anthu ambiri m’dzikoli amazinyalanyaza. Paulo ankadziwa zoti pali nkhani inayake yofunika kuthetsedwa.  Pajatu Satana ananena kuti akhoza kuchititsa anthu kusiya kutumikira Mulungu. (Yobu 1:9-11; 2:3-5) Ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto ambiri, Paulo ankafunitsitsa kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ndiponso kupirirabe pomulambira. Koma anthu m’dzikoli saganizira zinthu zimenezi akamayesetsa kuti akhale ndi moyo wabwino.

12. N’chifukwa chiyani inuyo mwasankha kudalira Mulungu m’malo mwa zinthu za m’dzikoli?

12 Kodi inuyo muli ndi maganizo ngati a Paulo? Ngakhale kuti kukhala wokhulupirika si kophweka, timadziwa kuti Mulungu amatidalitsa ndiponso kukondwera nafe tikamachita zimenezi. Madalitso a Yehova ndi amene amachititsa munthu kukhala ndi moyo wabwino. (Miy. 10:22) Tikakhala okhulupirika, zinthu zimatiyendera bwino panopa komanso tidzalandira madalitso m’tsogolo. (Werengani Maliko 10:29, 30.) Choncho chiyembekezo chathu sichiyenera kukhala pa ‘chuma chosadalirika, koma tizidalira Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.’ Tiyeni ‘tizisunga maziko a tsogolo lathu monga chuma, kuti tigwire mwamphamvu moyo weniweniwo.’ (1 Tim. 6:17-19) Tikatero, m’tsogolomu pambuyo pa zaka 100 kapena 1,000, tizidzayang’ana m’mbuyo n’kumati, “Ndinasankhadi moyo wabwino kwambiri.”

KUMENE KULI CHUMA CHANU

13. Kodi Yesu anapereka malangizo otani pa nkhani ya chuma?

13 Pa nkhani ya chuma, Yesu anati: “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma unjikani chuma chanu kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge, ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba. Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.”—Mat. 6:19-21.

14. N’chifukwa chiyani si nzeru kufunafuna chuma cha m’dzikoli?

14 Chuma chotchulidwa pa lembali chikhoza kuimira zambiri osati ndalama zokha. Chingaimire zinthu zimene Solomo anatchula, zomwe anthu amaona kuti munthu amene ali nazo ndiye kuti akukhala moyo wabwino. Ndi zinthu monga kutchuka kapena udindo. Yesu ananena mawu ena ofanana ndi zimene Solomo ananena zokhudza chuma. Iye anasonyeza kuti chuma cha m’dzikoli n’chosakhalitsa. Mwina inunso mwadzionera nokha kuti chuma choterechi chimatha mosavuta. Pulofesa wina analemba kuti: “N’zosachita kufunsa kuti kutchuka kumakhala kwakanthawi. Munthu amene anali wotchuka mlungu watha, amanyozeka pasanapite nthawi. Munthu amene ali ndi chuma chaka chino, chaka chamawa akhoza kukhala mphawi. . . . [Yesu] amakonda kwambiri anthu. Iye amawauza zinthu zomwe zingawathandize kuti asagwiritsidwe mwala ndi ulemerero wosakhalitsa ndi wakanthawi basi. Yesu safuna kuti ophunzira [ake] akhumudwe. ‘Tsiku lililonse dzikoli limafulatira anthu amene poyamba anali olemekezeka.’” Ngakhale kuti anthu ambiri amavomereza mfundo zimene pulofesayu ananena, safuna  kusintha maganizo ndi zolinga zawo. Kodi inuyo mukhoza kusintha?

15. Kodi tiyenera kuyesetsa kukhala ndi moyo wotani?

15 Atsogoleri ena achipembedzo amanena kuti n’kulakwa kuyesetsa kuti tikhale ndi moyo wabwino. Komatu Yesu sananene zimenezi. Iye anangolimbikitsa anthu kuti m’malo moyesetsa kukhala ndi chuma cha m’dzikoli aziyesetsa kuunjika chuma chosawonongeka kumwamba. Tiyeni tizikhala ndi mtima wofunitsitsa kukhala ndi moyo wabwino pa maso pa Yehova. Mawu a Yesu amatikumbutsa kuti tili ndi ufulu wosankha zinthu zimene tingamaike patsogolo. Koma tisaiwale kuti munthu amaika patsogolo zinthu zimene zili mumtima mwake kapena zimene amaona kuti ndi zofunika kwambiri.

16. Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?

16 Ngati tili ndi mtima wofuna kusangalatsa Yehova, iye adzatipatsa zinthu zofunika pa moyo wathu. N’zoona kuti angalole kuti tivutike kwakanthawi ndi njala kapena ludzu ngati mmene zinalili ndi Paulo. (1 Akor. 4:11) Koma sitikayikira malangizo anzeru amene Yesu anapereka akuti: “Choncho musamade nkhawa n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi. Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mat. 6:31-33.

KHALANI NDI MOYO UMENE MULUNGU AMAONA KUTI NDI WABWINO

17, 18. (a) Kodi moyo wabwino umadalira chiyani? (b) Nanga moyo wabwino sudalira chiyani?

17 Mfundo yofunika kuikumbukira ndi iyi: Moyo wabwino sudalira pa mmene anthu m’dzikoli amationera. Komanso kukhala ndi udindo m’gulu la Yehova pakokha si umboni woti munthuyo ali ndi moyo wabwino. Munthu amakhala ndi moyo wabwino ngati amamvera Mulungu ndipo ndi wokhulupirika kwa iye. Madalitso ena, ngati udindo, akhoza kubwera ngati akuchita zimenezi. Paja mawu a Mulungu amati: “Chofunika kwa woyang’anira ndicho kukhala wokhulupirika.” (1 Akor. 4:2) Tiyenera kukhalabe okhulupirika ndiponso kupirira. Yesu anati: “Yekhayo amene adzapirire mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.” (Mat. 10:22) Kupulumuka kudzakhala umboni wosatsutsika wakuti munthu ali ndi moyo wabwino.

18 Malinga ndi zimene takambirana, tingaone kuti udindo, maphunziro, chuma kapena kutchuka si umboni woti munthu ndi wokhulupirika kwa Mulungu. Nzeru kapena luso linalake sizichititsanso munthu kukhala wokhulupirika. Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tikhoza kukhala okhulupirika kwa Mulungu. M’nthawi ya atumwi, anthu ena a Mulungu anali olemera pamene ena anali osauka. Paulo analangiza anthu olemerawo kuti: “Azichita zabwino, akhale olemera pa ntchito zabwino, owolowa manja, okonzeka kugawira ena.” Olemera ndi osauka omwe akanatha ‘kugwira mwamphamvu moyo weniweniwo.’ (1 Tim. 6:17-19) Ndi mmene zililinso masiku ano. Tonsefe tili ndi mwayi ndiponso udindo wofanana. Tiyenera kukhalabe okhulupirika ndiponso kukhala “olemera pa ntchito zabwino.” Tikamatero, timakhala ndi moyo wabwino pa maso pa Mlengi wathu ndiponso timakhala osangalala chifukwa chodziwa kuti tikumukondweretsa.—Miy. 27:11.

19. Kodi ndinu wofunitsitsa kukhala ndi moyo wotani?

19 Zinthu zina pa moyo wanu zimakhala zosapeweka koma mukhoza kupewa kusokonezeka nazo. Kaya zili bwanji pa moyo wanu, yesetsani kukhala okhulupirika. Simudzanong’oneza bondo. Dziwani kuti Yehova adzakudalitsani panopa komanso mpaka kalekale. Musaiwale mawu amene Yesu anauza Akhristu odzozedwa akuti: “Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa, ndipo ndidzakupatsa mphoto ya moyo.” (Chiv. 2:10) Munthu wotsatira mawu amenewa angakhaledi ndi moyo wabwino.