Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Cholinga cha Nsanja ya Olonda ya M’Chingelezi Chosavuta

Cholinga cha Nsanja ya Olonda ya M’Chingelezi Chosavuta

KWA zaka zambiri, anthu padziko lonse akhala akupindula ndi mfundo zochokera m’Baibulo zimene zimapezeka m’magazini ya Nsanja ya Olonda. Mu July 2011, Nsanja ya Olonda yophunzira ya m’Chingelezi chosavuta inayamba kusindikizidwa. Magazini ya mwezi umenewu inati: “Tiyesa kuchita zimenezi kwa chaka chimodzi ndipo tikaona kuti ikuthandiza tipitiriza.”

Tsopano ndife osangalala kulengeza kuti tipitiriza kusindikiza magaziniyi. Komanso m’tsogolomu, Nsanja ya Olonda ya Chifulenchi, Chipwitikizi ndiponso Chisipanishi chosavuta iyamba kusindikizidwa.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU AMBIRI AKUIKONDA?

Anthu ambiri a kuzilumba za kum’mwera kwa nyanja ya Pacific atalandira magazini ya m’Chingelezi chosavutayi, anati: “Panopa abale akutha kumvetsa bwino nkhani za mu Nsanja ya Olonda.” Kalata ina inati: “M’mbuyomu, tinkathera nthawi yambiri pofufuza matanthauzo a mawu koma tsopano nthawiyo timaigwiritsa ntchito poyesetsa kumvetsa malemba ndiponso cholinga cha malembawo m’nkhani.”

Mlongo wina amene anaphunzira mpaka ku yunivesite anati: “Kwa zaka 18, ndakhala ndikulankhula ndiponso kulemba mawu ovuta kumva amene anthu ophunzira amakonda kugwiritsa ntchito. Ndinali ndi chizolowezi cholankhula ndiponso kuganiza m’njira yovuta. Ndinazindikira kuti ndiyenera kusintha mmene ndimaganizira ndiponso kulankhulira.” Iye analembanso kuti: “Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavuta yandithandiza kusintha. Chingelezi chake chimandithandiza kudziwa mmene ndinganenere zinthu m’njira yosavuta.” Tsopano mlongoyu amatha kulalikira mogwira mtima.

Ponena za Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavutayi, mlongo wina wa ku England, amene anabatizidwa mu 1972, analemba kuti: “Nditawerenga magazini yoyambirira, ndinamva ngati Yehova ali pambali pangapa ndipo wakoloweka dzanja lake paphewa langa n’kumawerenga nane limodzi magaziniyo. Zinali ngati bambo akuwerengera mwana wake kankhani asanagone.”

Mlongo wina amene amatumikira ku Beteli ya ku United States, yemwe anabatizidwa zaka zoposa 40 zapitazo, ananena kuti magazini imeneyi yamuthandiza kumvetsa bwino zinthu zina m’Baibulo. Mwachitsanzo, bokosi lakuti “Matanthauzo a Mawu Ena” m’magazini ya September 15, 2011, linafotokoza mawu akuti “mtambo wa mboni” pa Aheberi 12:1 kuti: “Zinali mboni zambirimbiri zosatheka kuziwerenga.” Iye anati: “Tanthauzo limeneli linandithandiza kumvetsa vesili.” Ponena za Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu ndi mlungu, ananenanso kuti: “Ngakhale mwana akamayankha pongowerenga kuchokera m’magaziniyi, yankho lake limakhala losiyana ndi mawu amene ali mu Nsanja ya Olonda ya nthawi zonse. Choncho limakhala lochititsa chidwi.”

Mlongo wina wa ku Beteli analemba kuti: “Ndimasangalala kwambiri kumva ndemanga za ana ku mpingo. Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavutayi yawathandiza kuyankha mochokera mumtima. Ndemanga zawo zimandilimbikitsa kwambiri.”

Mlongo amene anabatizidwa mu 1984 anayamikira magaziniyi ponena kuti: “Ndimaona kuti analembera ineyo. Imandithandiza kumvetsetsa zimene ndikuwerenga. Tsopano ndimatha kuyankha molimba mtima pa Phunziro la Nsanja ya Olonda.”

IKUTHANDIZA KWAMBIRI MAKOLO

Mlongo wina amene ali ndi kamnyamata ka zaka 7 anati: “Kale ndinkayenera kumufotokozera zambiri pokonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda. Zimenezi zinkatenga nthawi yaitali ndipo ndinkatopa kwambiri.” Kodi magazini ya m’Chingelezi chosavuta yawathandiza bwanji? Iye analemba kuti: “Panopa n’zodabwitsa kuti mwana wanga amatha kuthandiza nawo kuwerenga ndime ndiponso amamvetsa bwino zimene akuwerengazo. Popeza kuti mawu ake ndi osavuta ndiponso ziganizo zake n’zazifupi, iye amasangalala nayo kwambiri. Tsopano amakonzekera yekha zoti akayankhe ku misonkhano. Komanso tikakhala pa Phunziro la Nsanja ya Olonda, amagwiritsa ntchito magaziniyi ndipo amakhala tcheru mpaka phunziro lonse kutha.”

Mlongo wina, amene ali ndi mtsikana wa zaka 9, analemba kuti: “Kale tinkamuthandiza kukonzekera ndemanga zake. Koma tsopano amakonzekera yekha. Panopa sitivutikanso kwambiri kumufotokozera mawu ovuta. Popeza kuti amatha kumvetsa zimene akuwerenga m’magaziniwa, amasangalala kwambiri ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda.”

ZIMENE ANA AKUNENA

Ana ambiri amamva ngati Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavuta anaipangira iwowo. Mtsikana wina wa zaka 12 dzina lake Rebecca anapempha kuti: “Chonde musasiye kusindikiza magaziniyi.” Iye ananenanso kuti: “Ndimakonda kwambiri mbali yakuti ‘Matanthauzo a Mawu Ena.’ Ndi yosavuta kwa anafe.”

Mtsikana wina wa zaka 7 dzina lake Nicolette amaona chimodzimodzi. Iye anati: “M’mbuyomu, ndinkavutika kumvetsa Nsanja ya Olonda. Koma panopa ndimatha kuyankha mafunso ambiri ndekha.” Mtsikana winanso wa zaka 9 dzina lake Emma analemba kuti: “Magaziniyi yathandiza kwambiri ineyo ndiponso mchimwene wanga wa zaka 6. Timatha kumvetsa zinthu zambiri mosavuta. Zikomo kwambiri.”

Zikuonekeratu kuti anthu ambiri akupindula ndi Nsanja ya Olonda imeneyi chifukwa imagwiritsa ntchito mawu ndiponso ziganizo zosavuta. Popeza kuti magaziniyi ndi yothandiza kwambiri, ipitirira kusindikizidwa limodzi ndi Nsanja ya Olonda ya nthawi zonse, yomwe yakhala ikuthandiza anthu kuyambira mu 1879.