Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amasonkhanitsa Anthu Ake Osangalala

Yehova Amasonkhanitsa Anthu Ake Osangalala

“Sonkhanitsani anthu, amuna, akazi, ana ndi alendo.”—DEUT. 31:12.

1, 2. Kodi tikambirana chiyani pa nkhani ya misonkhano?

KWA zaka zambiri, Mboni za Yehova zakhala zikusonkhana pa misonkhano ya mayiko ndi yachigawo. Ambirife tapezeka pa misonkhano yosangalatsayi kangapo mwinanso maulendo ambirimbiri.

2 Zaka masauzande ambiri m’mbuyomo, anthu a Mulungu ankachitanso misonkhano yopatulika. Tiyeni tikambirane misonkhano yakale yotchulidwa m’Baibulo, n’kuona kufanana kwake ndi misonkhano ya masiku ano. Tionanso ubwino wopezeka pa misonkhano imeneyi.—Sal. 44:1; Aroma 15:4.

MISONKHANO YOSAIWALIKA YA NTHAWI ZAKALE NDIPONSO YA MASIKU ANO

3. (a) Kodi chinachitika n’chiyani pa msonkhano woyamba kutchulidwa m’Baibulo wa anthu a Yehova? (b) Kodi Aisiraeli ankaitanidwa bwanji kuti asonkhane?

3 Msonkhano waukulu woyamba kutchulidwa m’Baibulo unachitika m’mphepete mwa phiri la Sinai. Pa nthawi imeneyi, Aisiraeli analandira malangizo ochokera kwa Mulungu. Msonkhanowu unali wosaiwalika m’mbiri ya anthu a Mulungu. Pa msonkhano wosangalatsa umenewu, Yehova anasonyeza Aisiraeli mphamvu zake ndiponso kuwapatsa malamulo. (Eks. 19:2-9, 16-19; werengani Ekisodo 20:18; Deuteronomo 4:9, 10.) Pa tsiku limenelo, Yehova anasintha mmene ankachitira zinthu ndi Aisiraeli. Kenako Yehova anauza Mose njira yosonkhanitsira anthu. Anamuuza kuti apange malipenga awiri asiliva kuti aziwagwiritsa ntchito “poitanitsa msonkhano” kuti ubwere “pakhomo la chihema chokumanako.” (Num. 10:1-4) Taganizirani mmene zinalili zosangalatsa pamene ankasonkhana pamodzi.

4, 5. N’chifukwa chiyani misonkhano imene Mose ndi Yoswa anachititsa inali yofunika kwambiri?

4 Chakumapeto kwa ulendo wa zaka 40 wa Aisiraeli m’chipululu, Mose anawasonkhanitsa. Zimenezi zinachitika pa nthawi yofunika kwambiri kwa Aisiraeli. Iwo anali atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Inali nthawi yoyenera kuti Mose akumbutse abale ake zinthu zonse zimene Yehova anawachitira ndiponso zimene ankayembekeza kuwachitira.—Deut. 29:1-15; 30:15-20; 31:30.

5 Mwina pa msonkhanowu, Mose anawafotokozera zoti azisonkhana ndi kuphunzira za Mulungu. Pakapita zaka 7, amuna, akazi, ana ndiponso alendo okhala mu Isiraeli ankafunika kusonkhana pamalo omwe Yehova anasankha kuti achite Chikondwerero cha Misasa. Ankatero ‘kuti amvetsere ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu ndiponso kutsatira mosamala mawu onse a m’chilamulo.’ (Werengani Deuteronomo 31:1, 10-12.) Apatu n’zoonekeratu kuti Yehova ankafuna kuti anthu ake azisonkhana kuti aphunzire mawu ake ndiponso zolinga zake. Aisiraeli atagonjetsa mitundu imene inali m’Dziko Lolonjezedwa, Yoswa anawasonkhanitsa. Pa nthawi imeneyi, iwo anali atazunguliridwa ndi mitundu ina yosadziwa Mulungu choncho Yoswa ankafuna kuwalimbikitsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. Atalimbikitsidwa, anthuwo analumbira kuti adzatumikira Mulungu.—Yos. 23:1, 2; 24:1, 15, 21-24.

6, 7. Tchulani misonkhano yofunika kwambiri imene yachitika masiku ano.

6 Masiku ano, anthu a Yehova akhala akuchitanso misonkhano yosaiwalika. Pa misonkhano imeneyi, amalengeza zinthu monga kusintha kwa zinthu m’gulu la Yehova kapena mmene timamvera malemba ena. (Miy. 4:18) Pambuyo pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, msonkhano waukulu woyamba wa Ophunzira Baibulo unachitika mu 1919, mumzinda wa Cedar Point, ku Ohio m’dziko la United States. Pa msonkhanowu panafika anthu okwana 7,000 ndipo analengeza zoti Akhristu afunika kuchita khama kwambiri pa ntchito yolalikira padziko lonse. Mu 1922, pamalo omwewo panachitika msonkhano wa masiku 9. Pa msonkhanowu, M’bale Joseph F. Rutherford analimbikitsa anthu kugwira ntchito yolalikira. Iye anati: “Mukhale mboni za Ambuye zokhulupirika komanso zoona. Pitirizani kumenya nkhondo mpaka mbali iliyonse ya Babulo itawonongedwa. Lengezani uthengawu kwina kulikonse. Dziko lonse lidziwe kuti Yehova ndiye Mulungu ndipo Yesu Khristu ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. Lero ndi tsiku lalikulu kuposa masiku onse. Onani, Mfumu yayamba kale kulamulira ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza za ufumuwo. Choncho lengezani, lengezani, lengezani za Mfumu ndi ufumu wake.” Anthu amene anasonkhana komanso anthu padziko lonse anatsatira mawu amenewa ndi mtima wonse.

7 Mu 1931, panachitika msonkhano mumzinda wa Columbus, ku Ohio. Pa msonkhanowu, Ophunzira Baibulo anasangalala kwambiri kumva kuti azidziwika ndi dzina loti Mboni za Yehova. Pa msonkhano wa mu 1935 ku Washington, D.C., M’bale Rutherford anafotokoza za “khamu lalikulu” lomwe buku la Chivumbulutso limanena kuti ‘linali litaimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.’ (Chiv. 7:9-17) Mu 1942, pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, M’bale Nathan H. Knorr anakamba nkhani yakuti, “Kodi Padzikoli Padzakhala Mtendere?” Iye anafotokoza za ‘chilombo chofiira kwambiri’ chotchulidwa m’Chivumbulutso chaputala 17. Anasonyezanso kuti nkhondo ikatha, padzakhalabe ntchito yaikulu yolalikira.

8, 9. Tchulani zinthu zimene zachititsa misonkhano ina kukhala yosangalatsa kwambiri.

8 Nkhani ina yolimbikitsa inakambidwa ndi M’bale Knorr pa msonkhano womwe unachitika mu 1946 mumzinda wa Cleveland, ku Ohio. Mutu wa msonkhanowo unali wakuti “Mitundu Yosangalala” ndipo nkhaniyo inali yofotokoza za kumanganso ndiponso kukuza nyumba za ku Beteli. M’bale wina amene analipo anafotokoza mmene anthu anasangalalira atamvetsera nkhaniyi. Iye analemba kuti: “Ndinali ndi mwayi wokhala ndi m’baleyu papulatifomu pa nthawi imene ankakamba nkhaniyi. Iye ananena za ntchito yolalikira ndiponso mapulani okulitsa nyumba ya Beteli ku Brooklyn limodzi ndi fakitale. Atanena zimenezi, anthu anaomba m’manja mosalekeza. Ngakhale kuti zinali zovuta kuona nkhope za anthu kuchokera kupulatifomu, zinali zosavuta kuzindikira kuti iwo anali osangalala kwambiri.” Pa msonkhano wa mayiko mu 1950 ku New York City, anthu anasangalala kulandira Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu. Limeneli linali gawo loyamba la Baibulo lonse lolembedwa m’Chingelezi chamakono. M’Baibuloli, anabwezeretsa dzina la Mulungu m’malo ake.—Yer. 16:21.

9 Misonkhano yakhala ikuchitika kumayiko kumene Mboni za Yehova zinkazunzidwa kapena kumene ntchito yawo inaletsedwa. Mwachitsanzo, Adolf Hitler ankafuna kupha Mboni za Yehova zonse ku Germany. Koma mu 1955, Mboni za Yehova zokwana 107,000 zinapezeka pa msonkhano umene unachitika mumzinda wa Nuremberg, ku Germany, pabwalo limene Hitler ankachitira misonkhano yake. Anthu ambiri amene anapezekapo anayamba kulira chifukwa cha chisangalalo. Mu 1989, kudziko la Poland kunachitika misonkhano itatu ya mutu wakuti, “Kudzipereka Kwaumulungu.” Pa misonkhanoyi, panapezeka anthu okwana 166,518 ndipo ambiri anali ochokera kumayiko omwe ankatchedwa Soviet Union ndi Czechoslovakia komanso mayiko ena a kum’mawa kwa Ulaya. Kwa ena, inali nthawi yoyamba kusonkhana ndi anthu a Mulungu oposa 15 kapena 20. Mu 1993, anthu anasangalalanso kwambiri pa msonkhano wa mayiko wakuti “Chiphunzitso Chaumulungu” umene unachitikira mumzinda wa Kiev ku Ukraine. Pa msonkhanowu, panabatizidwa anthu okwana 7,402. Palibe nthawi ina imene anthu anabatizidwa ambiri chonchi pa msonkhano wa Mboni za Yehova.—Yes. 60:22; Hag. 2:7.

10. Kodi ndi misonkhano iti imene ndi yosaiwalika kwa inu ndipo n’chifukwa chiyani?

10 Mwina pali misonkhano yachigawo kapena ya mayiko imene simuiiwala. Kodi mumakumbukira msonkhano woyamba umene munapezekapo kapena umene munabatizidwa? Tingati misonkhano imeneyi ndi yofunika kwambiri ndiponso yosaiwalika kwa inu.—Sal. 42:4.

ZIKONDWERERO ZAPACHAKA

11. Kodi Mulungu anauza Aisiraeli kuti azichita zikondwerero ziti?

11 Yehova anauza Aisiraeli kuti azisonkhana ku Yerusalemu katatu pa chaka. Ankasonkhana pa Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa, pa Chikondwerero cha Masabata (chimene kenako chinkatchedwa Pentekosite) ndiponso pa Chikondwerero cha Misasa. Mulungu anawalamula kuti: “Katatu pa chaka mwamuna aliyense pakati panu azionekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova.” (Eks. 23:14-17) Podziwa kuti zikondwerero zimenezi zinali zofunika kwambiri pa kulambira kwawo, amuna ambiri ankapita limodzi ndi anthu onse a m’banja lawo.—1 Sam. 1:1-7; Luka 2:41, 42.

12, 13. Kodi Aisiraeli ena ankachita chiyani kuti akapezeke pa zikondwerero zapachaka?

12 Ndiye tangoganizani zimene ankafunika kuchita kuti banja lawo lipite ku Yerusalemu. Mwachitsanzo, Yosefe ndi Mariya ankayenda ulendo wa makilomita 100 kuchokera ku Nazareti kupita ku Yerusalemu. Kodi mukuganiza kuti ankayenda nthawi yaitali bwanji kuti akafike limodzi ndi ana awo aang’ono? Ulendo wa Yesu ku Yerusalemu, pa nthawi imene anali kamnyamata, umasonyeza kuti anthu ankayenda limodzi ndi anzawo komanso achibale awo. Taganizirani mmene zinkakhalira poyenda, kukonza chakudya ndiponso kukonza malo abwino oti agone kudera lachilendo. Koma ulendowu sunkakhala woopsa kwambiri chifukwa Yesu, ali ndi zaka 12 zokha, ankaloledwa kuchita zinthu zina payekha. Anthu onse, makamaka ana, ayenera kuti sankaiwala maulendo ngati amenewa.—Luka 2:44-46.

13 Pa nthawi ina, Aisiraeli anabalalika n’kusamukira m’mayiko ena. Choncho pa zikondwererozi pankakhala anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Mwachitsanzo, pa Pentekosite mu 33 C.E., Ayuda ndi anthu olowa Chiyuda, omwe ankaona kuti zikondwererozi n’zofunika, anapita ku Yerusalemu. Iwo anali ochokera kumadera ngati Italiya, Libiya, Kerete, Asia Minor ndiponso Mesopotamiya.—Mac. 2:5-11; 20:16.

14. Kodi Aisiraeli ankamva bwanji akapezeka pa zikondwerero zapachaka?

14 Aisiraeli okhulupirika ankaona kuti chinthu chofunika komanso chosangalatsa kwambiri pa maulendowa chinali kulambira Yehova limodzi ndi anzawo masauzande ambiri. Kodi anthu opezeka pa zikondwererozi ankamva bwanji? Tingapeze yankho pa zimene Yehova anauza anthu ake zokhudza Chikondwerero cha Misasa. Iye anati: “Ndipo uzisangalala pa chikondwerero chimenecho, iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi, Mlevi, mlendo wokhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye, amene ali mumzinda wanu. Uzichitira Yehova Mulungu wako chikondwerero chimenecho masiku 7 pamalo amene Yehova adzasankhe. Uzichita chikondwerero chimenecho chifukwa Yehova Mulungu wako adzakudalitsa pa zokolola zako zonse ndi pa chilichonse chimene dzanja lako likuchita, ndipo iwe uzikhala wosangalala basi.”—Deut. 16:14, 15; werengani Mateyu 5:3.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUYAMIKIRA MISONKHANO?

15, 16. Kodi inuyo mumachita zotani kuti mukapezeke pa misonkhano? Kodi ubwino wake ndi wotani?

15 Zikondwerero zimenezi ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu a Mulungu masiku ano. Ngakhale kuti zinthu zina zasintha, mbali zikuluzikulu za misonkhano sizinasinthe. Kalelo anthu ankafunika kuchita khama ndiponso kudzipereka kuti akapezeke ku zikondwerero. Ndi mmene zililinso masiku ano koma ubwino wake ndi wambiri. Misonkhano ndi yofunikabe pa kulambira kwathu. Pa misonkhanoyi, timalandira malangizo ofunika kwambiri kuti tikhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Timalimbikitsidwa kutsatira zimene timaphunzira ndiponso timathandizidwa kupewa mavuto. Pa misonkhanoyi, timalimbikitsidwanso kuchita zinthu zimene zingatitsitsimule osati zimene zingatifooketse.—Sal. 122:1-4.

16 Anthu opezeka pa misonkhano amakhala osangalala. Ponena za msonkhano umene unachitika mu 1946, lipoti lina linati: “Zinali zosangalatsa kuona a mboni masauzande ambirimbiri atasonkhana pamodzi. Zinkasangalatsa kwambiri kumva gulu lina lalikulu likuimba zida zoimbira, anthu ena onse n’kumatsatira poimba nyimbo za Ufumu zabwino kwambiri zotamanda Yehova.” Lipotili linanenanso kuti: “Anthu ankalembetsa mayina awo ku Dipatimenti ya Antchito Odzipereka n’cholinga choti athandize madipatimenti osiyanasiyana pa msonkhanowu. Anachita zimenezi chifukwa chofunitsitsa kutumikira a mboni anzawo.” Kodi inunso mumasangalala mukakhala pa msonkhano wachigawo kapena wa mayiko?—Sal. 110:3; Yes. 42:10-12.

17. Kodi ndi zinthu ziti zokhudza misonkhano zimene zasintha masiku ano?

17 Zinthu zina zokhudza misonkhano zasintha. Mwachitsanzo, kale msonkhano wachigawo unkakhala wa masiku 8. Kunkakhala chigawo cham’mawa, chamasana ndi chamadzulo. Pankakhalanso ntchito yolalikira. Nthawi zina, msonkhano unkayamba 9 koloko m’mawa mpaka 9 koloko usiku. Anthu odzipereka ankagwira ntchito mwakhama kuti akonzere anthu opezeka pa msonkhano chakudya cham’mawa, chamasana ndiponso chamadzulo. Koma masiku ano, misonkhano imakhala ya masiku ochepa ndipo aliyense amakonzeratu kwawo chakudya. Zimenezi zimathandiza kuti aliyense amvetsere bwinobwino msonkhano.

18, 19. Kodi inuyo mumayembekezera kwambiri zinthu ziti pa misonkhano ndipo n’chifukwa chiyani?

18 Pali zinthu zina zochitika pa misonkhano zimene sizinasinthe ndipo timaziyembekezera kwambiri. Mwachitsanzo, timalandira ‘chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera’ chimene chimatithandiza kumvetsa bwino maulosi ndiponso mfundo za m’Baibulo. Timalandira chakudyachi m’nkhani zimene zimakambidwa komanso m’mabuku amene amatulutsidwa pa misonkhanoyi. (Mat. 24:45) Mabuku ambiri amene timalandira amatithandiza pophunzitsa ena choonadi cha m’Baibulo. Masewero ochokera m’Baibulo amalimbikitsa achinyamata ndi achikulire omwe kukhala ndi zolinga zabwino potumikira Mulungu ndiponso kupewa maganizo oipa a m’dzikoli. Nkhani ya ubatizo imatithandiza tonsefe kuganizira kwambiri zimene tikuika pa malo oyamba. Timasangalalanso kuona anthu ena akubatizidwa posonyeza kuti adzipereka kwa Yehova.

19 Misonkhano yakhala mbali ya kulambira koona kwa zaka zambirimbiri. Imatithandiza kukhala osangalala ndiponso kutumikira Yehova mokhulupirika komanso mwakhama ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto. Imatipatsa mwayi wopeza anzathu atsopano ndiponso wodziwa kuti tili pa ubale wa padziko lonse. Misonkhano ndi njira yofunika kwambiri imene Yehova amatidalitsira ndiponso kutisamalira. Choncho aliyense ayenera kuyesetsa kuti azipezeka pa chigawo chilichonse cha misonkhano yonse.—Miy. 10:22.